-
Genesis 12:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Choncho Abulamu ananyamuka monga mmene Yehova anamuuzira, ndipo Loti ananyamuka naye limodzi. Pamene ankachoka ku Harana, Abulamu anali ndi zaka 75.+ 5 Abulamu anatenga mkazi wake Sarai,+ Loti mwana wa mʼbale+ wake ndi chuma chawo chonse+ komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana. Iwo ananyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani.+ Atafika ku Kanani,
-