Luka 23:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Ndiyeno atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamukhomerera pamtengo limodzi ndi zigawenga zija. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ Machitidwe 5:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pamtengo.+ Machitidwe 7:52 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Iwo anapha anthu amene analengezeratu za kubwera kwa wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndiponso kumupha.+
33 Ndiyeno atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamukhomerera pamtengo limodzi ndi zigawenga zija. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+
52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Iwo anapha anthu amene analengezeratu za kubwera kwa wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndiponso kumupha.+