-
1 Akorinto 4:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Mpaka pano tikadali anjala,+ aludzu+ ndiponso ausiwa. Tikumenyedwabe,+ tikusowabe pokhala 12 ndipo tikugwirabe ntchito mwakhama ndi manja athu.+ Akamatinenera zachipongwe, timadalitsa+ ndipo akamatizunza, timapirira moleza mtima.+ 13 Akamatinenera zoipa, timayankha mofatsa.+ Mpaka pano, tikuonedwa ngati zinyalala za dziko ndiponso nyansi za zinthu zonse.
-