-
1 Akorinto 13:4-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Chikondi+ nʼcholeza mtima+ ndiponso nʼchokoma mtima.+ Chikondi sichichita nsanje,+ sichidzitama, sichidzikuza,+ 5 sichichita zosayenera,*+ sichisamala zofuna zake zokha,+ sichikwiya+ ndipo sichisunga zifukwa.+ 6 Sichisangalala ndi zosalungama,+ koma chimasangalala ndi choonadi. 7 Chimakwirira zinthu zonse,+ chimakhulupirira zinthu zonse,+ chimayembekezera zinthu zonse+ komanso chimapirira zinthu zonse.+
-