11 Ndinu osangalala pamene anthu akukunyozani,+ kukuzunzani komanso kukunamizirani+ zoipa zilizonse chifukwa cha ine.+ 12 Sangalalani ndi kukondwera+ kwambiri chifukwa mphoto+ imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu, ndipo umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.+