-
Luka 6:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndinu osangalala anthu akamadana nanu,+ kukusalani,+ kukunyozani komanso kukana* dzina lanu nʼkumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu. 23 Sangalalani pa tsiku limenelo ndipo mudumphedumphe mokondwera, chifukwa mphoto imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu,* popeza zinthu zimenezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri.+
-