12 Komabe onse amene anamulandira, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu,+ chifukwa choti ankakhulupirira dzina lake.+ 13 Iwowa sanabadwe kuchokera mwa anthu kapena chifukwa cha kufuna kwa anthu kapenanso chifukwa cha kufuna kwa munthu, koma anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+