Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Atesalonika 3
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la 1 Atesalonika

      • Paulo anapitiriza kukhala ku Atene podikira lipoti lochokera ku Tesalonika (1-5)

      • Timoteyo anabweretsa lipoti lolimbikitsa (6-10)

      • Anapempherera Atesalonika (11-13)

1 Atesalonika 3:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 17:15

1 Atesalonika 3:2

Mawu a M'munsi

  • *

    Mabaibulo ena amati, “yemwe ndi wantchito mnzake wa Mulungu.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 16:1, 2; Aro 16:21; 1Ak 16:10

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    5/15/2009, tsa. 14

    10/1/1986, ptsa. 10-23

1 Atesalonika 3:3

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “amene wasochera.”

  • *

    Kapena kuti, “mukudziwa kuti tikuyenera kukumana ndi zimenezi.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 14:22; 1Ak 4:9; 1Pe 2:21

1 Atesalonika 3:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 2:14

1 Atesalonika 3:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 3:2
  • +Mt 4:3; 2Ak 11:3

1 Atesalonika 3:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 18:5

1 Atesalonika 3:7

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “pa zosowa zathu zonse.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2At 1:4

1 Atesalonika 3:8

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “timakhala ndi moyo.”

1 Atesalonika 3:10

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti tidzaone nkhope zanu.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2At 1:3

1 Atesalonika 3:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1At 4:9; 2At 1:3

1 Atesalonika 3:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 1:8
  • +1At 2:19; 5:23; 2At 2:1, 2

Kalozera

  • Buku Lofufuzira Nkhani

    Nsanja ya Olonda,

    10/1/1986, tsa. 23

Mabaibulo Ena

Dinani pa nambala ya vesi kuti muone mavesi a m'Baibulo lina ofanana ndi vesilo.

Malemba Ena

1 Ates. 3:1Mac 17:15
1 Ates. 3:2Mac 16:1, 2; Aro 16:21; 1Ak 16:10
1 Ates. 3:3Mac 14:22; 1Ak 4:9; 1Pe 2:21
1 Ates. 3:41At 2:14
1 Ates. 3:51At 3:2
1 Ates. 3:5Mt 4:3; 2Ak 11:3
1 Ates. 3:6Mac 18:5
1 Ates. 3:72At 1:4
1 Ates. 3:102At 1:3
1 Ates. 3:121At 4:9; 2At 1:3
1 Ates. 3:131Ak 1:8
1 Ates. 3:131At 2:19; 5:23; 2At 2:1, 2
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Werengani mu Baibulo la Dziko Latsopano
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Atesalonika 3:1-13

Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika

3 Choncho pamene sitinathenso kupirira, tinaona kuti ndi bwino kuti tipitirize kukhala ku Atene.+ 2 Ndiye tinatumiza Timoteyo+ mʼbale wathu, yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani nʼcholinga choti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba. 3 Tinachita zimenezi kuti pasapezeke aliyense amene chikhulupiriro chake chafooka* ndi masautso amenewa. Chifukwa inunso mukudziwa kuti sitingapewe kukumana ndi mavuto ngati amenewa.*+ 4 Chifukwa pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.+ 5 Nʼchifukwa chake pamene sindinathenso kupirira, ndinatuma Timoteyo kwa inu kuti ndidziwe za kukhulupirika kwanu.+ Ndimadera nkhawa kuti mwina Woyesayo+ anakuyesani ndipo nʼkutheka kuti ntchito imene tinagwira mwakhama inangopita pachabe.

6 Koma Timoteyo wangofika kumene kuno kuchokera kumeneko+ ndipo watiuza nkhani yabwino yokhudza kukhulupirika kwanu ndi chikondi chanu. Watiuza kuti mukupitiriza kutikumbukira ndipo mumatikonda komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ifenso tikulakalakira kukuonani. 7 Nʼchifukwa chake abale, mʼmavuto athu onse* komanso mʼmasautso athu onse tatonthozedwa chifukwa cha inu komanso chifukwa cha kukhulupirika kumene mukusonyeza.+ 8 Chifukwa ife timapeza mphamvu* inu mukakhala olimba mwa Ambuye. 9 Kodi Mulungu tingamuthokoze bwanji kuti timubwezere chifukwa cha chimwemwe chachikulu chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usiku ndi masana timapemphera mopembedzera kuchokera pansi pamtima kuti tidzakuoneni pamasomʼpamaso* nʼkukupatsani zimene zikufunika kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba.+

11 Tsopano Mulungu amenenso ndi Atate wathu komanso Ambuye wathu Yesu, atithandize kuti zitheke kubwera kwa inu. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muzikondana kwambiri ndiponso kuti muzikonda anthu ena+ ngati mmene ife timakukonderani. 13 Achite zimenezi kuti alimbitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera pamaso pa Mulungu+ amene ndi Atate wathu, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu,+ limodzi ndi oyera ake onse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena