Salimo
Nyimbo ya Davide.
Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu komanso chilungamo chanu.
2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,
Chifukwa palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+
3 Mdani akundifunafuna.
Iye wandipondereza ndipo wandigonjetsa.
Wandichititsa kuti ndikhale mumdima ngati anthu amene anafa kalekale.
5 Ndikukumbukira masiku akale.
Ndimaganizira mozama zochita zanu zonse.+
Ndimaganizira* ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.
6 Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.
Ndikuyembekezera inu ngati dziko louma limene likuyembekezera kuti mvula igwe.+ (Selah)
Musandibisire nkhope yanu,+
Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+
8 Mʼmawa ndichititseni kumva za chikondi chanu chokhulupirika,
Chifukwa ndimadalira inu.
9 Ndipulumutseni kwa adani anga, inu Yehova.
Ine ndikudalira inu kuti munditeteze.+
Mzimu wanu ndi wabwino.
Unditsogolere mʼmalo otetezeka.*
11 Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha dzina lanu.
Ndipulumutseni mʼmavuto anga, chifukwa ndinu wachilungamo.+