Mika
1 M’masiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda,+ Yehova analankhula ndi Mika+ wa ku Moreseti kudzera m’masomphenya. M’masomphenyawo anamuuza zokhudza Samariya+ ndi Yerusalemu+ kuti:
2 “Tamverani anthu nonsenu. Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi anthu onse okhala mwa iwe.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani pa zimene mukuchita.+ Yehova akutsutseni ali m’kachisi wake woyera.+ 3 Tamverani! Yehova akuchoka pamalo ake,+ ndipo atsika ndi kupondaponda m’malo okwezeka a padziko lapansi.+ 4 Mapiri asungunuka kumapazi ake+ ndipo zigwa zigawanika. Zonsezi zisungunuka ngati phula losungunuka ndi moto+ ndipo ziyenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.
5 “Izi zichitika chifukwa cha kupanduka kwa Yakobo ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi wachititsa kupanduka kwa Yakobo ndani? Kodi si anthu a ku Samariya?+ Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+ Si anthu a ku Yerusalemu kodi? 6 Samariya ndidzamusandutsa bwinja+ ndi malo oyenera kubzalapo mpesa. Miyala yake ndidzaiponya m’chigwa ndipo maziko ake ndidzawafukula n’kuwasiya pamtunda.+ 7 Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa n’kukhala zidutswazidutswa+ ndipo mphatso zonse zimene ankalandira monga malipiro zidzatenthedwa pamoto.+ Mafano ake onse ndidzawawononga. Samariya anapeza zinthu zonsezi ndi ndalama zimene anapeza pochita uhule. Ndipo tsopano zitengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”+
8 Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+ Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+ Ndidzalira ngati mimbulu ndi kumva chisoni ngati nthiwatiwa zazikazi. 9 Zilonda zake n’zosachiritsika+ ndipo zafalikira mpaka kukafika ku Yuda.+ Mliri umenewu wakafika pachipata cha anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+
10 “Anthu inu musanene zimenezi ku Gati ndipo asakuoneni mukulira.+
“Gubudukani pafumbi+ m’nyumba ya Afira. 11 Iwe mkazi wokhala ku Safiri tuluka m’dziko lako uli maliseche mochititsa manyazi.+ Mkazi wokhala ku Zaanana sanachoke m’dziko lake. Beti-ezeli anali malo anu othawirako, koma tsopano kuzingomveka kulira kokhakokha. 12 Mkazi wokhala ku Maroti anali kuyembekezera zinthu zabwino,+ koma zoipa zochokera kwa Yehova zafika pachipata cha Yerusalemu.+ 13 Iwe mkazi wokhala ku Lakisi,+ mangirira galeta ku gulu la mahatchi.* Mzinda umenewu ndiwo unayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,+ pakuti kupanduka kwa Isiraeli kwapezeka mwa iwe.+ 14 Choncho iwe udzapereka mphatso zotsanzikirana kwa Moreseti-gati.+ Nyumba za Akizibu+ zinali chinthu chokhumudwitsa kwa mafumu a Isiraeli. 15 Iwe mkazi wokhala ku Maresha+ ndidzakubweretsera wolanda zinthu za ena.+ Ulemerero wa Isiraeli udzafika ku Adulamu.+ 16 Meta mpala ndi kuchotsa tsitsi lonse chifukwa cha ana ako aamuna amene unali kuwakonda.+ Meta mpala mpaka ufanane ndi wa chiwombankhanga, chifukwa chakuti ana akowo akusiya ndipo apita kudziko lina.”+
2 “Tsoka kwa anthu amene amati akagona pabedi, amakonza chiwembu ndiponso kuganiza mmene angachitire zoipa.+ M’mawa kukangocha, iwo amazichitadi+ chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.+ 2 Iwo alakalaka minda ya anthu ena ndipo ailanda.+ Alakalakanso nyumba za anthu ena n’kuzitenga kukhala zawo.+ Atenga mwachinyengo cholowa cha munthu ndi cha banja lake.+
3 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndikuganiza zobweretsa tsoka pa banja ili.+ Tsoka+ limenelo simudzatha kulipewa,+ moti anthu inu simudzayendanso modzikuza+ chifukwa idzakhala nthawi ya tsoka.+ 4 Pa tsikulo munthu adzanena mwambi+ wokhudza anthu inu ndipo ndithu adzakuimbirani nyimbo ya maliro.+ Anthu adzanena kuti: “Ife talandidwa zinthu zathu!+ Cholowa cha anthu amtundu wathu chaperekedwa kwa anthu ena.+ Talandidwa cholowa chathu. Iye wapereka minda yathu kwa anthu osakhulupirika.” 5 Choncho mumpingo wa Yehova simudzapezeka aliyense amene azidzayeza ndi chingwe malo ogawidwa mwa kuchita maere.+ 6 Anthu inu musalosere.+ Aneneri amalosera koma sadzalosera zokhudza tsoka limeneli. Ndithu zochititsa manyazi zidzawagwera.+
7 “‘Inu a nyumba ya Yakobo,+ kodi mukunena kuti: “Kodi mzimu wa Yehova sukukhutira, kapena kodi izi ndiye zochita zake?”+ Kodi mawu anga sapindulitsa+ munthu woyenda mowongoka mtima?+
8 “‘Dzulo anthu anga enieni andiukira ngati mdani weniweni.+ Anthu amene akuyenda molimba mtima, ngati anthu obwera kuchokera kunkhondo, muwavule mkanjo wawo wokongola kwambiri umene avala pamwamba pa zovala zawo. 9 Inu mwathamangitsa akazi pakati pa anthu anga, m’nyumba imene mkazi aliyense anali kusangalala kukhalamo. Mwalanda ana awo zinthu zonse zaulemerero+ zimene ndinawadalitsa nazo ndipo simudzazibwezanso mpaka kalekale.*+ 10 Nyamukani,+ chokani chifukwa ano si malo opumulirako.+ Dzikoli liwonongedwa chifukwa chakuti ladetsedwa+ ndipo kuwonongedwako kukhala kopweteka.+ 11 Munthu wolondola zinthu zopanda pake ndi zachinyengo akanena bodza lakuti:+ “Ndidzakulosererani zokhudza vinyo ndi chakumwa choledzeretsa,” ndiye adzakhale mneneri wa anthu awa.+
12 “‘Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.+ Ndidzasonkhanitsa otsala a Isiraeli.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola, komanso ngati gulu la ziweto limene lili pamalo amsipu.+ Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+
13 “Ndithu wogumula mpanda adzawatsogolera.+ Iwo adzadutsa pogumukapo. Adzatuluka kudutsa pachipata.+ Mfumu yawo idzakhala patsogolo pawo ndipo Yehova adzawatsogolera.”+
3 Ine ndinapitiriza kunena kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo?+ 2 Inu mumadana ndi zinthu zabwino+ ndi kukonda zinthu zoipa.+ Mumasenda khungu la anthu ndi kuchotsa mnofu pamafupa awo.+ 3 Mwadya mnofu wa anthu anga+ ndipo mwasenda khungu lawo. Mwaswa mafupa awo kukhala zidutswazidutswa. Mwawaphwanyaphwanya ngati mafupa ndi mnofu zimene zili mumphika wakukamwa kwakukulu komanso ngati nyama imene ili mumphika.+ 4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+
5 “Yehova wanena zimene zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+ Aneneri amenewo akutafuna chakudya ndi mano awo+ n’kumanena kuti, ‘Mtendere!’+ Koma munthu akapanda kuika chakudya m’kamwa mwawo, amakonzekera kumuthira nkhondo.+ Kwa iwo Mulungu wanena kuti, 6 ‘Choncho anthu inu usiku udzakufikirani,+ ndipo simudzaonanso masomphenya.+ Mudzangoona mdima wokhawokha moti simudzaloseranso. Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera ndipo mdima udzawagwera masanasana.+ 7 Oona masomphenya+ adzachita manyazi+ ndipo olosera+ adzakhumudwa ndithu. Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamlomo+ chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”+
8 Koma ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu+ kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.+
9 Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo komanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+ amene mukuipidwa ndi chilungamo ndiponso amene mukupotoza chilichonse chowongoka.+ 10 Inu mukumanga Ziyoni ndi ntchito zokhetsa magazi ndipo mukumanga Yerusalemu mwa kuchita zinthu zopanda chilungamo.+ 11 Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+ 12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.
4 M’masiku otsiriza,+ phiri+ la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu ya anthu idzakhamukira kumeneko.+ 2 Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+ Iye akatiphunzitsa njira zake,+ ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+ 3 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu yakutali.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+ 4 Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu+ ndipo sipadzakhala wowaopsa,+ pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu panena zimenezi.+
5 Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake.+ Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu+ mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.+
6 Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzasonkhanitsa anthu amene anali kuyenda motsimphina.+ Anthu amene anamwazikana ndidzawasonkhanitsa pamodzi.+ Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amene ndawasautsa. 7 Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+
8 “Koma iwe nsanja ya gulu la nkhosa, malo okwera a mwana wamkazi wa Ziyoni,+ ulamuliro udzabwerera kwa iwe. Ulamuliro woyamba, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu,+ udzabwerera kwa iwe.+
9 “Tsopano n’chifukwa chiyani ukufuula kwambiri?+ Kodi mwa iwe mulibe mfumu, kapena kodi alangizi ako awonongedwa? Kodi n’chifukwa chake zowawa ngati za mkazi amene akubereka zakugwira?+ 10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu waukulu ngati mkazi amene akumva kupweteka kwambiri pobereka.+ Tsopano uchoka m’tauni ndipo ukakhala kumudzi.+ Ukafika mpaka ku Babulo+ koma kumeneko udzapulumutsidwa.+ Kumeneko Yehova adzakuwombola m’manja mwa adani ako.+
11 “Tsopano mitundu yambiri ya anthu idzasonkhana kuti ikuukire. Mitunduyo ikunena kuti, ‘Tiyeni timuwononge ndipo maso athu aone kuwonongeka kwa Ziyoni.’+ 12 Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova. Iwo sakumvetsa cholinga chake+ pakuti adzawasonkhanitsa ndithu ndi kuwaika pamalo opunthira ngati mmene munthu amasonkhanitsira tirigu amene angomumweta kumene.+
13 “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,+ nyamuka upunthe tirigu pakuti nyanga* yako ndidzaisandutsa chitsulo. Ziboda zako ndidzazisandutsa mkuwa ndipo udzanyenyanyenya mitundu yambiri ya anthu.+ Phindu lawo limene apeza mwachinyengo udzalipereka kwa Yehova monga chinthu chopatulika.+ Zinthu zawo udzazipereka kwa Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.”+
5 “Iwe mzinda wogonjetsedwa, tsopano udzichekecheke.+ Adani atizungulira kuti atiukire.+ Iwo adzamenya woweruza wa Isiraeli patsaya ndi ndodo.+
2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+
3 “Choncho Mulungu adzapereka ana a Isiraeli kwa adani awo+ mpaka pamene mkazi amene adzabereke atabereka.+ Ndipo abale ake onse a munthuyo adzabwerera kwa ana a Isiraeli.
4 “Iye adzaimirira n’kuyamba kuweta nkhosa mu mphamvu ya Yehova+ ndiponso m’dzina lalikulu la Yehova Mulungu wake.+ Anthuwo azidzakhala kumeneko motetezeka,+ pakuti iye adzakhala wamkulu mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ 5 Ameneyu adzabweretsa mtendere.+ Msuri akadzalowa m’dziko lathu, akadzaponda nsanja zathu zokhalamo,+ ife tidzamutumizira abusa 7, inde atsogoleri 8 a anthu kuti akathane naye. 6 Atsogoleriwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.+ Adzalanganso dziko la Nimurodi+ m’njira zake zonse zolowera m’dzikolo. Wolamulirayo adzatipulumutsa kwa Msuri.+ Adzatipulumutsa Msuriyo akadzangofika m’dziko lathu ndi kuponda nthaka yathu.
7 “Otsala a Yakobo,+ pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzakhala ngati mame ochokera kwa Yehova.+ Iwo adzakhala ngati mvula yamvumbi imene ikuwaza pazomera,+ yomwe sidalira munthu kapena kuyembekezera ana a anthu ochokera kufumbi.+ 8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu. Iwo adzakhala ngati mkango pakati pa nyama zakutchire. Adzakhala ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa, umene umati ukadutsa pakati pa nkhosazo, ndithu umazimbwandira ndi kuzikhadzula+ ndipo sipakhala wozipulumutsa. 9 Dzanja lanu lidzakhala pamwamba pa adani anu,+ ndipo adani anu onse adzaphedwa.”+
10 Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzapha mahatchi anu ndipo magaleta anu ndidzawawononga.+ 11 Ine ndidzagwetsa mizinda ya m’dziko lanu. Ndidzagumula malo anu onse amene ali ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 12 Amatsenga onse m’dziko lanu ndidzawapha, ndipo pakati panu sipadzapezekanso anthu ochita zamatsenga.+ 13 Ndidzagwetsa zifaniziro zanu zogoba ndi zipilala zopatulika zimene zili pakati panu, ndipo simudzagwadiranso ntchito za manja anu.+ 14 Ndidzazula mizati yanu yopatulika+ imene ili pakati panu ndi kuwononga mizinda yanu. 15 Ndidzabwezera mokwiya ndiponso mwaukali mitundu ya anthu imene sinandimvere.”+
6 Anthu inu imvani zimene Yehova akunena.+ Nyamukani mukanene mlandu wanu kwa mapiri ndipo zitunda zikamve mawu anu.+ 2 Inu mapiri, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake. Inu matanthwe okhazikika, tamverani. Mvetserani inu maziko a dziko lapansi,+ pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake. Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+
3 “Inu anthu anga,+ ndakulakwirani chiyani? Kodi ndakutopetsani mwa njira yanji?+ Perekani umboni wonditsutsa.+ 4 Ine ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo,+ ndipo ndinakuwombolani m’nyumba ya akapolo.+ Ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.+ 5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani+ zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite+ ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+ Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+ Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”+
6 Kodi nditenge chiyani popita kukakumana+ ndi Yehova? Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba?+ Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu+ ndi ana a ng’ombe achaka chimodzi? 7 Kodi Yehova adzakondwera ndi masauzande a nkhosa zamphongo? Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande makumimakumi?+ Kapena kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa chifukwa cha cholakwa changa?+ Kodi ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa? 8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+
9 Mawu a Yehova akumveka mumzinda.+ Munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu.+ Anthu inu, mverani mawu a ndodo ndi a amene anaisankha.+ 10 Kodi m’nyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo,+ ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wosaloleka? 11 Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu?+ 12 Anthu olemera a mumzindawo amakonda kuchita zachiwawa. Anthu okhalamo akulankhula zonama+ ndipo lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.+
13 “Ine ndidzakumenyani mpaka kukudwalitsani,+ ndipo mudzawonongedwa chifukwa cha machimo anu.+ 14 Inuyo mudzadya koma simudzakhuta ndipo mudzamvabe njala.+ Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino koma simudzatha kuziteteza. Zinthu zilizonse zimene mudzazitenge, ine ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.+ 15 Mudzabzala mbewu koma simudzakolola. Mudzaponda maolivi koma simudzadzola mafuta. Mudzaponda mphesa koma simudzamwa vinyo wotsekemera.*+ 16 Anthu inu mukutsatira zochita za Omuri.+ Zochita zonse za anthu a nyumba ya Ahabu, inunso mukuzichita+ ndipo mukuyendera maganizo awo.+ Pa chifukwa chimenechi ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa ndipo anthu a mumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+ Inuyo mudzatonzedwa ndi mitundu ina ya anthu.”+
7 Tsoka kwa ine,+ chifukwa ndakhala ngati munthu wanjala amene sanapeze zipatso kuti adye.+ Ndakhala ngati munthu amene sanapeze nkhuyu zoyambirira zimene anali kuzilakalaka, nthawi yokolola zipatso za m’chilimwe* ndi mphesa itatha.+ 2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi, ndipo pakati pa anthu palibe munthu wowongoka mtima.+ Onse amadikirira anzawo kuti akhetse magazi.+ Aliyense amasaka m’bale wake ndi ukonde.+ 3 Manja awo amachita zoipa ndipo amazichita bwino kwambiri.+ Kalonga amalamula kuti amupatse mphatso, ndipo woweruza amalandira chiphuphu poweruza.+ Munthu wotchuka amangolankhula zolakalaka za mtima wake+ ndipo onsewa amakonzera limodzi chiwembu. 4 Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati chitsamba chaminga, ndipo munthu wowongoka mtima kwambiri pakati pawo ndi woipa kwambiri kuposa mpanda wa mitengo yaminga.+ Tsiku limene mudzapatsidwe chilango, limene alonda anu ananena, lidzafika ndithu.+ Pa tsikulo anthu adzathedwa nzeru.+
5 Musamakhulupirire anzanu. Musamadalire mnzanu wapamtima.+ Samala zonena zako polankhula ndi amene umagona naye pafupi.+ 6 Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake+ ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi.+ Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.+
7 Koma ine ndidzadikirira Yehova.+ Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.+ Mulungu wanga adzandimvera.+
8 Iwe mdani wanga,+ usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira. Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka ndithu.+ Ngakhale kuti ndili mumdima,+ Yehova adzakhala kuwala kwanga.+ 9 Mkwiyo waukulu wa Yehova ndiupirira chifukwa ndamuchimwira.+ Ndiupirirabe kufikira ataweruza mlandu wanga mondikomera ndi kundichitira chilungamo.+ Iye adzandipititsa pamalo owala ndipo ndidzaona kulungama kwake.+ 10 Mdani wanga adzaona zimenezi, ndipo amene anali kunena kuti: “Yehova Mulungu wako ali kuti?”+ adzachita manyazi.+ Maso anga adzamuyang’ana.+ Iye adzakhala malo opondedwapondedwa ngati matope a mumsewu.+
11 Pa tsiku lomanga mpanda wako wamiyala lamulo lokhudza iwe lidzachotsedwa.*+ 12 Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe kuchokera ku Asuri ndi kumizinda ya Iguputo. Anthu ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje*+ adzabwera kwa iwe. Adzabwera kuchokera m’malo onse apakati pa nyanja imodzi ndi nyanja ina, komanso pakati pa phiri limodzi ndi phiri lina.+ 13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+
14 Weta anthu ako ndi ndodo yako.+ Weta gulu la nkhosa zomwe ndi cholowa chako, zimene zinali kukhala zokhazokha m’nkhalango pakati pa mitengo ya zipatso.+ Uzilole kuti zikadyere ku Basana ndi ku Giliyadi+ ngati mmene zinali kuchitira masiku akale.+
15 “Anthu inu ndidzakusonyezani zinthu zodabwitsa ngati mmene ndinachitira m’masiku amene munali kuchokera ku Iguputo.+ 16 Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ali ndi mphamvu.+ Adzagwira pakamwa+ ndipo makutu awo adzagontha. 17 Adzanyambita fumbi ngati njoka.+ Adzatuluka m’malo awo obisalamo+ ngati zokwawa zapadziko lapansi ali ndi mantha. Adzabwera kwa Yehova Mulungu akunjenjemera ndipo adzachita nanu mantha.”+
18 Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu+ amene amakhululukira zolakwa+ ndi machimo a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+ Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale, pakuti kusonyeza kukoma mtima kosatha kumakusangalatsani.+ 19 Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzapondaponda zolakwa zathu.+ Machimo athu onse mudzawaponya pakati pa nyanja yozama.+ 20 Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
‘Muyezo wa efa’ ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Ena amati “wonzuna.”
Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.
Mawu ake enieni, “Pa tsikulo lamulo lidzakhala kutali.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.