Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 Nahum 1:1-3:19
  • Nahumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nahumu
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nahumu

Nahumu

1 Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi:

2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+

3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+ komatu Yehova salephera kulanga wolakwa.+

Njira yake ili mumphepo yowononga ndi mumphepo yamkuntho. Mitambo ndilo fumbi lopondapo mapazi ake.+

4 Amadzudzula nyanja+ ndi kuiphwetsa ndipo amaumitsa mitsinje yonse.+

Basana ndi Karimeli afota+ ndipo maluwa a mitengo ya ku Lebanoni nawonso afota.

5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+

Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+

6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+

Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye.

7 Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo+ pa tsiku la nsautso.+

Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+

8 Adzafafaniza mzinda umenewo+ ndi madzi osefukira ndipo mdima udzathamangitsa adani ake.+

9 Kodi anthu inu mungakonze chiwembu chotani kuti muukire Yehova?+ Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso.

Sipadzakhalanso nsautso.+

10 Ngakhale kuti iwo alukanalukana ngati minga+ ndipo aledzera ngati kuti amwa mowa,+ adzatenthedwa ngati mapesi ouma.+

11 Mwa iwe mudzatuluka wina amene akuganiza zochitira Yehova zoipa+ ndi kulangiza anthu zinthu zopanda pake.+

12 Yehova wanena kuti: “Ngakhale kuti iwo anali achikwanekwane ndiponso anali ndi mphamvu zambiri, adzadulidwa+ ndipo wina adzawaukira. Pamenepo ndidzakusautsa kufikira pamene sudzafunikiranso kusautsidwa.+ 13 Tsopano ndidzathyola goli lake lonyamulira katundu ndi kulichotsa pa iwe,+ ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo.+ 14 Koma ponena za iwe, Yehova walamula kuti, ‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako.+ Ndidzadula zifaniziro zosema ndi zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndipo ndidzazitaya kunja kwa nyumba za milungu yako. Ndidzakukonzera manda+ chifukwa ndiwe wopanda pake.’

15 “Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.+ Iye akulengeza za mtendere. Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza+ chifukwa palibe munthu aliyense wopanda pake amene adzadutsa pakati pako.+ Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”+

2 Womwaza wafika pamaso pako.+ Teteza malo amene ali ndi mpanda wolimba kwambiri. Londera njira yako. Konzekera kumenya nkhondo.* Kunga mphamvu zako zonse.+

2 Pamenepo Yehova adzakweza ulemu wa Yakobo+ ndi kubwezeretsa ulemerero wa Isiraeli. Pakuti owononga awawononga,+ ndipo mphukira zawo zasakazidwa.+

3 Amuna amphamvu ovala zovala zofiira kwambiri afika. Anyamula zishango zonyika mu ututo wofiira.+ Pokonzekera nkhondo, iwo akukweza mikondo yawo yokhala ndi zogwirira zamtengo.+ Zida zawo zankhondo zachitsulo zimene zili pamagaleta awo zili waliwali ngati moto. 4 Magaleta awo ankhondo akuyenda mothamanga kwambiri m’misewu.+ Iwo akuthamangira uku ndi uku m’mabwalo a mzinda, ndipo akuoneka ngati zounikira zamoto. Magaletawo akuderukaderuka ngati mphezi.+

5 Mfumu idzakumbukira asilikali ake amphamvu.+ Iwo adzathamangira kumpanda wa mzinda ndipo pamene akutero adzakhala akupunthwa.+ Pamenepo mpanda wachitetezo udzakhala ndi chitetezo champhamvu. 6 Zotsekera madzi a m’mitsinje zidzatsegulidwa, ndipo nyumba yachifumu idzawonongedwa. 7 Nkhani imeneyi yatsimikiziridwa. Mzindawo udzavulidwa ndi kuchititsidwa manyazi, ndipo anthu ake adzatengedwa.+ Akapolo ake aakazi adzakhala akulira ngati nkhunda+ ndipo adzadziguguda pachifuwa.+ 8 Kuchokera pamene Nineve anakhalapo,+ iye wakhala ngati dziwe la madzi,+ koma tsopano anthu ake akuthawa. Ena akufuula kuti: “Imani amuna inu! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.+

9 Funkhani siliva amuna inu, funkhani golide,+ pakuti iwo ali ndi zinthu zochuluka kwambiri. Ali ndi zinthu zosiririka zosiyanasiyana zadzaoneni.+

10 Mzindawu auchititsa kukhala wopanda kanthu ndipo ausandutsa bwinja.+ Mitima yawo yasungunuka ndi mantha.+ Mawondo awo akunjenjemera+ ndipo akumva ululu thupi lonse.+ Nkhope zawo zonse zili ndi nkhawa.+ 11 Kodi malo obisalamo mikango, phanga la mikango yamphamvu, malo amene mkango unali kuyenda ndi kulowa,+ malo amene munali mwana wa mkango, mmene mikango inali kukhala popanda woiwopsa, ali kuti?+ 12 Mkango unali kukhadzulakhadzula nyama yokwanira kuti udyetse ana ake ndipo unali kupha nyama kuti upatse mikango yaikazi. Mapanga ake anali kukhala odzaza ndi nyama, ndipo malo ake obisalamo anali ndi nyama zokhadzulakhadzula.+

13 Yehova wa makamu akuti, “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo nditentha magaleta ako ankhondo moti padzakhala utsi wambiri.+ Lupanga lidzadya mikango yako yamphamvu.+ Sudzasakanso nyama padziko lapansi,* ndipo mawu a amithenga ako sadzamvekanso.”+

3 Tsoka mzinda wokhetsa magazi.+ Mzindawo wadzaza ndi chinyengo ndi chifwamba, moti nthawi zonse umafunkha zinthu za anthu ena. 2 Kukumveka kulira kwa mkwapulo,+ kulira kwa mawilo, mgugu wa mahatchi* ndi kudumpha kwa magaleta.+ 3 Komanso pali asilikali okwera pamahatchi, malupanga a moto walawilawi, mikondo yowalima ngati mphezi,+ anthu ambiri ophedwa ndiponso mulu waukulu wa mitembo moti pena paliponse pali mitembo yosawerengeka. Anthu akupunthwa pamitembo ya anthu awo. 4 Zimenezi zili choncho chifukwa cha kuchuluka kwa zochita zake zauhule+ ndi kukongola kwake kochititsa kaso. Iye ndi mkazi waluso lamatsenga ndipo amakopa mitundu ya anthu ndi zochita zake zauhule, amakopa mitundu ya anthu ndi zochita zake zamatsenga.+

5 Yehova wa makamu wanena kuti: “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo ndidzakuvula siketi yako ndi kukuphimba nayo kumaso moti ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ione maliseche ako+ ndi kutinso maufumu aone manyazi ako. 6 Ndidzakuponyera zinthu zonyansa+ ndipo ndidzakuchititsa kukhala chinthu chonyozeka ndiponso choopsa.+ 7 Aliyense wokuona adzakuthawa+ ndipo adzanena kuti, ‘Nineve wasakazidwa! Ndani adzamuchitira chisoni?’ Kodi anthu oti akutonthoze ndiwapeza kuti? 8 Kodi iwe uli pabwino kuposa No-amoni+ amene anali pafupi ndi ngalande zochokera mumtsinje wa Nailo?+ Iye anali wozunguliridwa ndi madzi. Chuma chake chinali kuchokera m’nyanja, ndipo nyanjayo ndiyo inali khoma lake. 9 Mphamvu zake zonse zinali kuchokera ku Itiyopiya komanso ku Iguputo,+ ndipo zinali zopanda malire. Anthu a ku Puti komanso a ku Libiya anali kumuthandiza.+ 10 Koma nayenso No-amoni anayenera kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo. Ana ake anaphwanyidwaphwanyidwa m’misewu yake yonse+ ndipo anthu ake olemekezeka anawachitira maere.+ Anthu ake onse otchuka anamangidwa m’matangadza.+

11 “Chotero iwenso udzaledzera,+ ndipo udzabisala.+ Iwenso udzafunafuna malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri kuti utetezeke kwa mdani.+ 12 Malo ako onse okhala ndi mpanda wolimba kwambiri ali ngati mitengo ya mkuyu imene ili ndi nkhuyu zoyambirira kupsa. Munthu akagwedeza mitengoyo, nkhuyu zakezo zimagwera m’kamwa mwa munthu wozidya.+

13 “Taona! Anthu ako ali ngati akazi.+ Zipata za dziko lako zidzatsegulidwa kuti adani ako alowemo. Moto udzanyeketsa mipiringidzo ya mzinda wako.+ 14 Tunga madzi kuti upange chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Limbitsa malo ako okhala ndi mpanda wolimba kwambiri.+ Lowa m’matope ndi kupondaponda dothi. Gwira chikombole. 15 Koma ngakhale utero, moto udzakunyeketsa. Lupanga lidzakuduladula+ ndipo lidzakudya ngati mmene ana a dzombe oyenda pansi amadyera zomera.+ Dzichulukitseni ngati ana a dzombe oyenda pansi, dzichulukitseni ngati dzombe. 16 Iwe wachulukitsa anthu ako amalonda kuposa nyenyezi zakumwamba.+

“Ana a dzombe oyenda pansi amafundula ndipo kenako amaulukira kutali. 17 Alonda ako ali ngati dzombe ndipo akapitawo ako olemba anthu usilikali ali ngati gulu la dzombe. Pa tsiku lozizira limabisala m’makoma. Dzuwa likawala, dzombelo limauluka ndi kuthawira kutali ndipo silidziwika kuti lili kuti.+

18 “Abusa ako ayamba kuwodzera,+ iwe mfumu ya Asuri, ndipo anthu ako olemekezeka akungokhala m’nyumba zawo.+ Anthu ako amwazikana pamapiri ndipo palibe amene akuwasonkhanitsa pamodzi.+ 19 Masoka ako sadzakupatsa mpata wopuma. Chilonda chako chakhala chosachiritsika.+ Kodi pali amene sunamuvutitse ndi zoipa zako nthawi zonse?+ N’chifukwa chake onse amene adzamva za iwe adzakuwombera m’manja.”+

Mawu ake enieni, “Limbitsa chiuno chako.”

Mawu ake enieni, “Ndidzadula nyama zimene umagwira padziko lapansi.”

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena