Yona
1 Yehova anayamba kulankhula ndi Yona+ mwana wa Amitai, kuti: 2 “Nyamuka upite kumzinda waukulu wa Nineve.+ Kumeneko ukadzudzule anthu a mumzindawo ndi kuwauza kuti ine ndaona zoipa zimene akuchita.”+
3 Pamenepo Yona ananyamuka n’kulowera ku Tarisi,+ kuthawa Yehova.+ Kenako anafika ku Yopa+ ndipo kumeneko anapeza chombo chopita ku Tarisi. Iye analipira malipiro a ulendowo n’kukwera chombocho kuti apite ku Tarisi limodzi ndi anthu amene anali m’chombomo, kuthawa Yehova.
4 Ndiyeno Yehova anabweretsa chimphepo champhamvu panyanjapo,+ ndipo panachita mkuntho wamphamvu.+ Chotero chombocho chinatsala pang’ono kusweka. 5 Zitatero oyendetsa chombo anayamba kuchita mantha ndipo aliyense anayamba kufuulira mulungu wake+ kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya m’nyanja katundu amene anali m’chombomo kuti chipepukidwe.+ Apa n’kuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho, pakuti chinali ndi zipinda zapansi. Kumeneko Yona anagona tulo tofa nato.+ 6 Kenako woyendetsa chombocho anafika pamene Yona anagonapo n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukungogona? Dzuka ufuulire mulungu wako!+ Mwina Mulungu woona atikomera mtima ndipo sitifa.”+
7 Ndiyeno anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tichite maere+ kuti tidziwe amene wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere.”+ Iwo anachitadi maere ndipo maerewo anagwera Yona.+ 8 Choncho anamufunsa kuti: “Tiuze, ndani wachititsa kuti tsoka limeneli litigwere?+ Umagwira ntchito yanji ndipo ukuchokera kuti? Kwanu n’kuti ndipo ndiwe wa mtundu uti?”
9 Iye anayankha kuti: “Ndine Mheberi,+ ndipo ndimaopa+ Yehova Mulungu wakumwamba,+ amene anapanga nyanja ndi mtunda.”+
10 Pamenepo anthuwo anachita mantha kwambiri, ndipo anamufunsa kuti: “Wachitiranji zimenezi?”+ Anthuwo anamufunsa choncho chifukwa anadziwa kuti Yona akuthawa Yehova, pakuti iye anali atawauza zimenezo. 11 Kenako anamufunsa kuti: “Ndiye tichite nawe chiyani+ kuti nyanjayi ikhale bata?” Apa n’kuti mkuntho wamphamvu uja ukukulirakulira. 12 Iye anawayankha kuti: “Mundinyamule n’kundiponya m’nyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Chifukwa ndikudziwa kuti mkunthowu ukuchitika chifukwa cha ine.”+ 13 Koma anthuwo anayesetsa kuti adutse mafunde amphamvuwo ndi kukakocheza kumtunda. Koma sanakwanitse chifukwa mkunthowo unali kuwonjezeka kwambiri.+
14 Pamenepo anthuwo anafuulira Yehova ndi kunena kuti:+ “Chonde inu Yehova, musalole kuti tiwonongeke chifukwa cha munthu uyu! Musaike pa ife mlandu wa magazi a munthu wosalakwa,+ chifukwa zonsezi zachitika pokwaniritsa chifuniro chanu, inu Yehova!”+ 15 Kenako ananyamula Yona ndi kum’ponya m’nyanja. Atatero nyanjayo inakhala bata.+ 16 Zimenezi zitachitika anthuwo anayamba kuopa Yehova kwambiri.+ Choncho anapereka nsembe kwa Yehova+ ndi kuchita malonjezo.+
17 Tsopano Yehova anatumiza chinsomba chachikulu kuti chikameze Yona,+ moti Yona anakhala m’mimba mwa nsomba masiku atatu, usana ndi usiku.+
2 Tsopano Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali m’mimba mwa chinsombacho,+ 2 kuti:
“Pamene ndinali m’masautso ndinaitana Yehova,+ ndipo anandiyankha.+
Ndinafuula kupempha thandizo ndili m’Manda* akuya.+
Ndipo inu munamva mawu anga.+
3 Pamene munandiponya m’malo ozama, pansi penipeni pa nyanja yakuya,+
Madzi amphamvu anandimiza.
Mafunde anu amphamvu anadutsa pamwamba panga.+
6 Ndinatsikira m’tsinde mwenimweni mwa mapiri.
Zotsekera za dziko lapansi zinanditsekereza kuti ndikhale komweko mpaka kalekale.*
Koma inu Yehova Mulungu wanga, munanditulutsa m’dzenje ndili wamoyo.+
7 Pamene ndinalefuka kwambiri,+ ndinakumbukira Yehova.+
Ndipo pemphero langa linafika kwa inu, m’kachisi wanu woyera.+
8 Anthu okhulupirira mafano, amaleka kusonyeza kukoma mtima kwawo kosatha.+
9 Koma ine, ndidzakutamandani ndi kupereka nsembe kwa inu.+
Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.+ Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”+
10 Kenako Yehova analamula chinsombacho, ndipo chinalavula Yona kumtunda.+
3 Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+ 2 “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve, ndipo kumeneko ukalalikire+ zimene ndikuuze.”
3 Pamenepo Yona ananyamuka ndi kupita ku Nineve mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu pamaso pa Mulungu,+ ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu. 4 Kenako Yona analowa mumzindawo ndi kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye anali kulalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”+
5 Anthu a ku Nineve anayamba kukhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli.*+ 6 Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve,+ mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu ndi kuvula chovala chake chachifumu. Ndiyeno inavala chiguduli ndi kukhala paphulusa.+ 7 Kuwonjezera pamenepo, mfumu ndi akuluakulu ake analamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti:
“Munthu aliyense, chiweto, ng’ombe ndi nkhosa iliyonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi.+ 8 Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu ndi mphamvu zawo zonse, ndipo aliyense asiye njira zake zoipa+ ndi zinthu zonse zachiwawa zimene amachita. 9 Ndani angadziwe? Mwina Mulungu woona satigwetsera tsoka ndipo asintha maganizo+ ndi kubweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga.”+
10 Ndiyeno Mulungu woona anaona ntchito zawo.+ Anaona kuti alapa ndi kusiya njira zawo zoipa.+ Choncho, Mulungu woona anasintha maganizo ake+ pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.+
4 Koma zimenezi sizinamusangalatse m’pang’ono pomwe Yona + ndipo anakwiya nazo koopsa. 2 Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? N’chifukwa chaketu ine ndinathawa kupita ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga, wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ komanso mumatha kusintha maganizo pa tsoka limene mumafuna kubweretsa.+ 3 Tsopano inu Yehova, chotsani moyo wanga,+ pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.”+
4 Poyankha, Yehova anati: “Kodi pali chifukwa chilichonse choti ukwiyire?”+
5 Kenako, Yona anatuluka mumzindawo ndi kukakhala pansi kumbali ya kum’mawa kwa mzindawo. Kumeneko anamanga chisimba* kuti akhale pamthunzi+ kufikira ataona zimene zichitikire mzindawo.+ 6 Ndiyeno Yehova Mulungu anameretsa chomera cha mtundu wa mphonda kuti chiyange pamene Yona anakhala ndi kum’chitira mthunzi. Anachita zimenezi kuti amupulumutse ku masautso ake.+ Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha chomeracho.
7 Kenako Mulungu woona anatumiza mbozi+ m’bandakucha wa tsiku lotsatira, kuti ikawononge chomera cha mtundu wa mphonda chija, moti chomeracho chinafota.+ 8 Dzuwa litatuluka, Mulungu anatumiza mphepo yotentha yochokera kum’mawa.+ Dzuwalo linamutentha Yona pamutu moti anangotsala pang’ono kukomoka.+ Choncho Yona anapempha mobwerezabwereza kuti angofa. Iye anali kunena kuti: “Kuli bwino ndife kusiyana n’kuti ndikhale ndi moyo.”+
9 Pamenepo Mulungu anafunsa Yona kuti: “Kodi pali chifukwa chilichonse chokwiyira ndi chomera cha mtundu wa mphondachi?”+
Yona anayankha kuti: “Ndikuyeneradi kukwiya moti ndikufuna kufa chifukwa cha mkwiyowo.” 10 Koma Yehova anati: “Iwe ukumvera chisoni chomera cha mtundu wa mphondachi, chimene sunachivutikire kapena kuchikulitsa, chimene changomera usiku umodzi wokha n’kufa usiku umodzi. 11 Kodi ine sindikuyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Nineve,+ mmene muli anthu oposa 120,000, omwe sadziwa kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere? Kodi sindiyenera kumveranso chisoni ziweto zambiri zimene zili mmenemo?”+
Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “masaka.”
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”