Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g86 10/8 tsamba 10
  • Mmene Mungathetsere Chizolowezicho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungathetsere Chizolowezicho
  • Galamukani!—1986
  • Nkhani Yofanana
  • Kusuta—Kawonedwe Kachikristu
    Galamukani!—1989
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Kusuta—Maupanduwo
    Galamukani!—1989
  • Kodi Kusuta Kulidi Koipa Motero?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1986
g86 10/8 tsamba 10

Mmene Mungathetsere Chizolowezicho

MUSAYESE kuthetsa mwapang’onopang’ono: Kumatalikitsa nthawi yamavuto akuchira.

MUSAWONONGE ndarama zanu kugulira mankhwala othetsa kusuta okwera mtengowo: “Popanda chosiyidwa, zithandizozo zimene pakali pano ziri pamisika sizimapereka chithandizo chenicheni kwa wosutayo,” ikusimba motero New Scientist. Ndipo World Health ikunena kuti: “Chinthu chachikulu m’chipambano . . . nthawi zonse chidzakhala chifuno cha wosuta ameneyo. Zotsala zonsezo nzongothandizira chabe.”

VOMEREZANI thayo lanu, koma vomerezaninso chithandizo: Mabwenzi ochilikiza omwe iwo eniwo aleka kusuta ali othandiza. Pempherani. Chikhumbo chowona mtima cha kukondweretsa Mulungu ndi kuchita chifuniro chake chimachita zodabwitsa.—Afilipi 2:4; 4:6, 13.

DZIWANI mapindu a kusasuta: Kumachepetsa kukhala kwanu m’ngozi ya imfa (yochititsidwa ndi nthenda yamtima, sitoroko, chifuwa, zotupatupa, kapena kensa); kukhazikitsa chitsanzo chabwino; kusunga ndalama kumasuka kuzonyansazo, kununkha, zosayenera, ndi ukapolo wa chizolowezicho.

MVETSETSANI Kupweteka kwanu kwa kuchirako: Mkati mwa maora 12 pambuyo pa ndudu yanu yotsirizira, mtima wanu ndi mapapu zimayamba kudzikonza zokha. Mlingo wa carbon monoxide yanu ndi chikonga zimatsika mofulumira. Koma pamene thupi lanu likuchira, zimapweteka. Mungawone kukhala wofulumira kukwiyitsidwa kapena wamtima wapachala, koma inu simufunikira ndudu kuti mukhazikitse minyewa yanu. Zosayenera zakanthawi zimenezi ziri chiyambi cha moyo wathanzi labwino koposerapo.

MVETSETSANI chitokosocho: Yembekezerani mavuto. Pewani kudzimvera chifundo ndi kugonjera. Koma musakaikire konse, inu mungathe kuthetsa chizolowezicho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena