Kodi Mudziwa Zimene Ana Anu Amamvetsera?
Mwana wamkazi wazaka 15 wa mlemmbiyo Kandy Stroud anati, “Muyenera kumvetsera ku iyi, Amayi!” Ndiyeno anawonjezera kuti, “Koma musamvetsere kumawu.” Iye analiza nyimbo ya ngwazi yotchuka ya roko. Amake anamvetsera, ndipo pamwamba pamalimbawo anamva mawu. Nyimboyo inali kunena za msungwana yemwe anali kuchita psotopsoto m’hotera.
Kandy Stroud, polemba mu Newsweek, akupitirizabe kunena kuti: “Nyimbo zolankhula za zakugona mopanda manyazi zonga zimenezi . . . zimapanga chakudya cha nyimbo kwa mamiliyoni ochuluka a ana amene tsopano amachidya pamakonsati, pa maulbum, pa wailesi ndi pa MTV [ngalande ya TV imene iri katswiri m’nyimbo za roko m’United States].”
Iye anawonjezera kuti: “Popeza kuti ndiri ponse pawiri kholo ndi woimba nyimbo ndiri wodera nkhawa ponena za chiwerengero cha nyimbo zotchuka zimene zingatchedwe kokha kukhala nyimbo za roko zodzazidwa ndi za kugonana, ndi za mkhalidwe wakugonana wosakondweretsa, zoyerekezera ndi zoimbidwa popanda chifukwa choyenera chirichonse zikumakhathamira m’mafunde a mpweya ndi kudzaza m’zinyumba zathu.”
Monga kholo, kodi inu muli wodera nkhawa ponena za mtundu wanyimbo zimene zikusonkhezera ana anu, kapena mtundu wanyimbo zimene ana anu akusankha? Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika? Chifukwa chakuti zingathe kukuuzani kanthu kena ponena za njira imene mwana wanu amalingalira ndi chimene mtima wake walingapo. Monga momwe Newsweek inasimbira, Dr. Joseph Novello, dairekitala wa programu ya anamgoneka, akufunsa odwala m’chipatala azaka 13-19 zakubadwa ponena za zimene amakonda m’nyimbo. “Mosasamala kanthu kuti iyo iri yausatana, ya zakugonana kapena yonena za anamgoneka—imamuuza kanthu kena ponena za mkhalidwe wamaganizo wa mwana.”
Kodi mwapenda mkhalidwe wamaganizo wa mwana wanu posachedwapa? Kodi mukudziwa mtundu wanyimbo imene iye amamvetsera panyumba kapena kwina kulikonse? Ngati mugamula kuti nyimboyo siiri yomangilira, kodi mudzasamalira motani nkhaniyo? Ndi chidzudzulo champhamvu kodi kapena ndi kulingalira kosamalitsa ndi chilango? Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Kachiwirinso, atate, inu simuyenera kukakamiza ana anu kuwachititsa kukhumudwa, koma apatseni malangizo, ndi chiwongolero, zimene ziri za kumangilira Kwachikristu.”—Aefeso 6:4, The New English Bible.
Pali mawu anyimbo osiyanasiyana mokwanira ooti munthu akhale wokhoza kupeza nyimbo zokondweretsa ndi zoyera. Mwinamwake ena afunikira kusintha mtundu wa nyimbo, koma monga momwe Mkristu amalingalirira imeneyo ndi mbali yofunika ya ‘kuvala umunthu watsopano wonga wa Kristu.’ Pokhala ndi chikhumbo ndi chisonkhezero choyenera, zingathe kuchitidwa.—Aefeso 4:20-24.