Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Chikumbumtima Changa Chimandivuta?
SORAYA wazaka khumi ndi zitatu zakubadwa anapitirizabe kumawonda—koma osati chifukwa cha mtundu woipa wa chakudya. Soraya akufotokoza kuti: “Ndinaphatikizidwa m’khamu loipa pasukulu. Ndinadziwa bwinopo, koma panali chisonkhezero chosalekeza cha anzanga. Mwamsanga ndinali ndi bwenzi lachinyamata limene linkagwiritsira ntchito anamgoneka.” Ndipo kodi zimenezi zinali ndi chochita chirichonse chotani ponena za kuwonda kwake? “Chikumbumtima changa chinandivuta kwambiri chakuti sindikanatha kudya.”
Alex wazaka zisanu ndi ziwiri zakubadwa anadzipeza kukhala akumadzizunza. Iye anali atathira mpunga pansi ndipo anali kugwada pamenepo momva ululu kwambiri ndi mawondo ake osavekedwa. Chifukwa ninji? Alex anali atapalamula kwa makolo ake ndipo anali atasankha kudzilanga.
Achichepere onse awiriwo anali kuchitapo kanthu—momvetsa ululu kufika pamenepo—ku kanthu kena kamene Baibulo limakatcha chikumbumtima, mawu amkati amene anazunza ngakhale atumiki a Mulungu pamene anali atachita cholakwa. “Mulibe mtendere m’mafupa anga,” analemba motero Davide pambuyo pooti wachita chigololo. (Salmo 38:3, NW) Mofananamo abale a Yosefe anavutika ndi malingaliro aliwongo pambuyo pooti iwo, pokhala mu mkhalidwe wa ukali wochititsidwa ndi nsanje, anamgulitsa muukapolo. Zaka zoposa 20 pambuyo pake, iwo akanatha kukumbukirabe mmene ‘Yosefe anali kuwapembera chifundo.’ Ha mmene chimenecho chinayenera kukhalira chikumbukiro chomvetsa ululu kwambiri nanga!—Genesis 37:18-36; 42:21.
Inde, chikumbumtima choipa chingathe kubweretsa chiwawo ndi chipsinjo chamaganizo. Mosiyana, chikumbumtima chabwino chimabweretsa chikhutiro ndi chisangalalo! Mosakaikira chimenechi ndicho chifukwa chimene, m’kupenda kwa m’Soviet kochitidwa pa achichepere zikwi zochuluka ponena za zofunika zawo m’moyo, “chikumbumtima choyera chinalembedwa kukhala chofunika kopambana.” (Soviet Monthly Digest, July 1983) Komabe, chodetsa nkhawa kopambana kwa Akristu, ndicho chenicheni chakuti Baibulo limalankhula za “kukhala nacho chikumbumtima chabwino.” (1 Petro 3:16) Koma kodi ndimotani mmene mungachitire zimenezo? Choyamba, muyenera kumvetsetsa chimene chikumbumtima chiri ndi mmene chimagwirira ntchito.
Chikumbumtima—Kodi Icho Nchiyani?
Zaka zoposa zana zapitazo, mlembi Wachitaliyana Carlo Collodi analemba nthanthi yotchuka ya ana ake ya Pinocchio—kamnyamata kachidole kopangidwa ndi matabwa kokhala ndi luso lolowera m’mavuto. Kaŵirikaŵiri panali kachilombo kolankhula kulangira ndi kuwongolerera Pinocchio, kotchedwa Jiminy Cricket. Kunena zowona, iko kanali chikumbumtima cha Pinocchio. Mofananamo, inu mungathe kuyerekezera chikumbumtima chanu ndi mawu kapena mfuu imene imapita pambuyo poti mwachita choipa kapena chabwino kapena musanachite.
Wopanga zinthu zatsopano wina wagwiritsira ntchito molakwa lingaliro limeneli ndi chipangizo chotchedwa kuti chikumbumtima cha chakudya. Ndiko kanthu kamene kamagwira ntchito mothandizidwa ndi mabatire kamene kamaikidwa mkati mwa firiji kapena pachitseko cha chosungira zikho za m’khitcheni. Nthawi iriyonse pamene chitsekocho chimatsekulidwa mawu onenedwa amanena kuti: “Kodi mukudyanso? Nzachisoni kwa inu.”
Koma mosafanana ndi Jiminy Cricket kapena chipangizo chopangidwa ndi munthu, chikumbumtima chanu ndicho kanthu kena mkati mwanu. Baibulo limafotokoza chikumbumtima monga ‘wochitira umboni wamkati, yemwe amachitira umboni kukhala wabwino kapena woipa kwa mchitidwe wakutiwakuti. (Aroma 2:15) Koma kodi nkuti kumene mphamvu yamaganizo ya chikumbumtima imeneyi imachokera?
Mphamvu Yamaganizo Yobadwa Nayo
Nzowona kuti timaphunzira zochuluka ponena za chabwino ndi choipa kuchokera kwa makolo athu ndi ena. Mosasamala kanthu za zimenezo, Baibulo limasonyeza kuti chikumbumtima nchobadwa nacho. Pa Aroma 2:14, limalankhula za mmene “anthu a mitundu . . . [amachitira] mwachibadwidwe zinthu zalamulo.”—NW.
Chotero, miyezo ya malamulo amakhalidwe abwino yamaziko, imawonekera kukhala ikumapangidwa mkuganiza kwa munthu. Kumbukirani, munthu anapangidwa “m’chifanizo cha Mulungu,” akumasonyeza nzeru yaumulungu ndi chiweruzo cholungama kumlingo wakutiwakuti. (Genesis 1:27) Mosakaikira chimenechi ndicho chifukwa chake mitundu padziko lonse lapansi yapangira malamulo otsutsana ndi zinthu zonga kupha mwambanda, kuba, ndi kugonana ndi wachibale.
Ngakhale m’nkhani zazing’onozing’ono mfuwu ya chikumbumtima ingathe kumvedwa. Chotero sitolo ina yaikulu inapempha chikhumbumtima cha anthu mwa kugulitsa zikwama zogulira m’kachipinda kakang’ono kosatsekedwa. Pamwamba pa kauntala ya wosintha ndalama panalenjekeka chikwangwani chomwe chinalembedwa kuti: “Chikumbumtima chanu ndiye mtetezi wanga yekha.” Inde, chenicheni chakuti anthu ochulukitsitsa ali ndi chikumbumtima chogwira ntchito chimatipindulitsa. Apo phuluzi, miyoyo yathu ndi chuma zikanakhala mungozi yoipitsitsa!
Chiphunzitseni!
Ngakhale kuti nchobadwa nacho, chikumbumtima sichili chosalakwa konse. Mwachitsanzo, Baibulo limalankhula za awo omwe ali ndi chikumbumtima “chofowoka.” (1 Akorinto 8:7) Chifukwa cha chidziwitso cholakwika, oterowo angakhoterere ku kuchita mopambanitsa pamikhalidwe yakutiyakuti ndi kuvutika ndi mfuwu yosafunikira. Kumbali ina, ena ali “olotchedwa m’chikumbumtima mwawo monga ndi chitsulo chamoto.” (1 Timoteo 4:2) Chikumbumtima chawo sichimalabadira, mofanana ndi thupi lolotchedwa ndi chitsulo chofiira ndi moto.
Talingalirani za Adolf Eichmann, mpandu wa mu nkhondo ya Chinazi yemwe anagwidwa ndi kunyongedwera kukhala ndi phande m’kuphedwa mwambanda kwa Ayuda mamiliyoni asanu ndi imodzi. Kodi iye anakhalapo ndi malingaliro aliwongo? Katswiri wanthenda zamaganizo I. S. Kulscar anamfunsa funso limenelo kumene, limene Eichmann anayankha kuti: “Inde, kamodzi kapena kaŵiri, chifukwa cha kulumpha sukulu.” Ha mmene ziliri zosiyana nanga! Mwachiwonekere Eichmann anali ataphunzira kulinganiza chikumbumtima chake. Ndipo katswiri wodziwa maganizo mwa kupenda Willard Gaylin akunena kuti: “Kulephera kumva kukhala waliwongo ndicho cholakwa chamaziko mwa munthu wosokonezeka maganizo kapena wotsutsana ndi kuyanjana.”
Pamenepa, kodi ndimotani mmene inu mungatsimikizirire, kuti chikumbumtima chanu chikugwira ntchito moyenelera? Choyamba, chiyenera kuphunzitsidwa moyenelera. Motani? Mwa kuphunzira ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu. Uku kumakuthandizani kulinganiza bwino lomwe chikumbumtima chanu mwa kuphunzira miyezo ya Mulungu ndi ‘kukonzanso maganizo anu.’ (Aroma 12:2) Pamene chaphunzitsidwa moyenelera, chikumbumtima chanu chimachita zoposa kukulangani chabe pambuyo poti mwachita choipa. Chimakuthandizani kupewa kuchita choipa pasadakhale—ngakhale ngati palibe aliyense chapafupi woti avomereze kapena kusavomereza zochita zanu.
Chimvetsereni!
Komabe, kungodziwa kokha chabwino ndi choipa, sikokwanira. Kuti chikumbumtima chikuthandizeni, inu mufunikira kuphunzira kuchimvetsera! Ndithudi, izi sizitanthauza kuyendayenda nthawi zonse mukumamva kukhala waliwongo kapena kudzilanga mopambanitsa. Mosakanika, ndife opanda ungwiro. Koma Baibulo limati pa Salmo 103:13: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa Iye.” Chifundo cha Mulungu ndi chikhululukiro zimatithandiza kukhala ndi moyo m’kupanda ungwiro kwathu.
Komabe, panthawi zina, mfuwu za chikumbumtima chathu ziyenera kutisonkhezera kutenga kachitidwe koyenelera. Lester David akulemba kuti mu Senior Scholastic: “Kodi munaswa pangano, kuswa lamulo, kuswa lamulo lachipembedzo kapena lafuko, kuvulaza wina wake, kunama, kunyengeza? . . . Pemphani chikhululukiro ngati mungathe, wongolerani mchitidwe wolakwikawo mwanjira iriyonse imene iri yoyenelera. Lankhulani za uwo ndi munthu wina wake.” Zimenezi ndizo zimene Soraya, wotchulidwa pachiyambiyambi pankhaniyi, anachita. Mmalo mwa kungomva chabe kukhala waliwongo, iye analankhula nkhaniyo ndi makolo ake. Iye akusimba kuti anayamba “kumva bwinopo kwambiri” pamene anagwiritsira ntchito uphungu wa makolo ake.
Inde, pali pamene muchitapo kanthu pa zisonkhezero za chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo kuti mungathe kupindula nacho. Mwachitsanzo, mwamuna wina wachichepere wotchedwa Bill, anafikira pophatikizidwa ndi kagulu ka azaka 13-19. Koma pamenepo, akutero Bill, “Ndinawona mmodzi wa mabwenzi anga akumapita kundende chifukwa cha kupha mwambanda. Tsopano chikumbumtima changa chinandiuza kuti zonsezo zinali utsiru—osati za ine!” Koma kodi Bill anangomva kukhala waliwongo chabe ndi kusiya nkhaniyo? Ayi, iye akuti, “Ndinasiyana ndi kaguluko.”
Mwamuna wina wachichepere wotchedwa dzina lake Tony analola chikumbumtima chake kumthandiza m’njira ina yakenso. Tony ndimmodzi wa Mboni za Yehova. Chikumbumtima chake chinamsonkhezera kuwonongera maora okwanira 90 modzifunira mwezi uliwonse akumafikira anthu m’zinyumba mwawo, kuwaphunzitsa Baibulo. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) “Ndinasangaliradi kukumana ndi anthu,” akufotokoza motero Tony. “Ndiponso ndinali ndi ntchito yaganyu yabwino ndipo galimoto yanga, ndi ine tinakonda kumene ndinkakhala. Komabe ndinayamba kulingalira kukhala waliwongo chifukwa cha kusachita zochulukirapo—kutumikira kumene kunali kusowa kokulirapo kaamba ka amuna achichepere ofanana ndi ine.”
Ha mmene chiliri chisonyezero chamkhalidwe wapamwamba nanga wa chikumbumtima! Mochilabadira, Tony analemba chifunsiro chopempha kukatumikira pamalikulu apadziko lonse a Mboni za Yehova, kumene Mabaibulo ndi zothandizira maphunziro Abaibulo—zonga magazine ano—zimapangidwa. Iye wakhala akumatumikira konko kwazaka zisanu ndi zinayi zapita.
Kodi mumamvetsera chikumbumtima chanu? Chingakhoze, monga momwe wachichepere wina akunenera, kukhala chofanana ndi “bwenzi lowona lomwe limawononga nthawi ndi kuyesayesa kukuwongolerani.” Chingakusonkhezereninso kukwaniritsa mathayo aumwini ndi Achikristu. Koma muyenera kuchiphunzitsa moyenerera ndi kuchimvera! Zowonadi, chikumbumtima ndimphatso yodabwitsa. Chilemekezeni ndi kuchigwiritsira ntchito bwino lomwe.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Ngakhale kuti nchobadwa nacho, chikumbumtima sichiri chosakhoza kulakwa konse. Chiyenera kuphunzitsidwa moyenelera
[Chithunzi patsamba 13]
Chikumbumtima chaliwongo chingachititse chipsinjo chachikulu chamalingaliro