Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Tiyenera Kupita ku Chikondwerero Chosonkhezera Timu Lasukulu?
‘LIMBIKANI timu lathu, limbikani!’ ‘Mukagonjetse, mukapambane, mukalakike!’ Mfuuzo zimayimbidwa mobwerezabwereza ndi chikondwerero chachikulu ndi changu monga ngati chachipembedzo. Holo yamaseŵera injenjemera ndi nyimbo zoimbidwa mosalekeza ndi kutimba ng’oma. Asungwana ndi anyamata ovala mochotitsa kaso akutsogolera mfuuzo ndi nyimbo zachilakiko, panthaŵi imodzimodziyo akuchititsa chidwi anzawo ndi kuseŵera kwaukatswiri ndi kuvina kotenga maganizo. Aphunzitsi a timulo ndi oyang’anira maseŵera apereka zitsimikizo zakulakika monyada. Kenako, timu la pasukulupo litulukira, kuchititsa owachemerera awo kukweza mfuu zawo. Khamulo limwerekera m’chisangalalo chachikulu, ndipo chisangalalocho chifika pachimake. Gululo nlokhutira kuti timu lawo lidzalakika!
M’sukulu zambiri, zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zimayembekezeredwa ndi chidwi chachikulu. Ndipo pamene kuli kwakuti nthaŵi ndi nthaŵi, zikondwerero zina zimachitidwa kukulitsa chidwi cha maprojekiti osiyanasiyana pasukulu, zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zimachitidwa kukonzekera maseŵera otsatira omwe ali pafupi kuchitika monga: rugby, mpira wachitanyu, baseball, basketball. Kwa achichepere ambiri chikondwerero chosonkhezera timu lasukulu chimatanthauza zoposa kupuma chabe ku programu yanthaŵi zonse yasukulu. Chimakhala mpata wakuchirikiza timu lasukulu, kusonkhezera ngwazi zawo zamaseŵera, kuchichiza timu kuti lilakike! Zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zimaperekanso mzimu wakudalirana ndi kugwirizana pakati pa ana asukulu.
Kunena zowona, sialiyense amene amawona maseŵera kukhala ofunika. Ana asukulu ena amangosangalala ndi nyonga, kusanguluka, ndi chimwemwe chokhala ku zikondwererozo. “Ndinthaŵi yakumasuka ndi kuchita mmene ufunira,” akutero wachichepere wina. Kwa ena, zikondwerero zamaseŵera zimakhala mpata wakuphonya kalasi—kapena wakuyanjana momasuka ndi osiyana nawo ziŵalo. “Ndinthaŵi yakusangalala pamodzi kwa zitsamwali za asungwana ndi anyamata,” akutero mnyamata wina wausinkhu wazaka zapakati pa 13 ndi 19.
Mulimonse mmene zingakhalire, aphunzitsi ambiri amakhulupirira kuti kuchirikiza maseŵera apasukulu kuli mbali yofunika ya kaphunziridwe. M’bukhu lake lakuti The High School Survival Guide—An Insider’s Guide to Success, Barbara Mayer analemba kuti: “Mwana wasukulu aliyense amene amamaliza maphunziro asekondale popanda . . . kukhala m’malo a openyerera ndi kukuŵirira timu lakwawo . . . waphonya nthaŵi yosangalatsa koposa ndi mipata yaikulu koposa yakukula imene angaipeze mwakanthaŵi.” Nkosadabwitsa kuti m’sukulu zina, zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zimaloledwa kuchitika m’nthaŵi ya makalasi olinganizidwa a nthaŵi zonse.
Ngati zoterozo zimachitika kusukulu kwanu, mwina munaganizapo za kukapezekako. Ndithudi, mungakakamizike kupitako. Kulephera kupezekako kungachititse ena kukuyesani mbutuma kapena wosakhulupirika. Ngakhale ndi tero, pali zifukwa zabwino zimene achichepere Achikristu sayenera kupezekerako.
Kodi Nchisangalalo Chachikulu Kapena Nkutengeka Maganizo Konkhitsa?
Sikuti Baibulo limatsutsa maseŵera. Baibulo limavomereza kuti “maseŵera olimbitsa thupi amapindula pang’ono.” (1 Timoteo 4:8, Today’s English Version) Akristu ambiri—achichepere ndi achikhulire—amakonda zonse ziŵiri kuwonerera ndi kutenga mbali m’maseŵera. Ngati achitidwa mwachikatikati, maseŵera angakhale osangalatsa, ndi opindulitsa.a
Komabe, zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zingasinthe chisangalalo chabwino cha maseŵera kukhala kutengeka maganizo kwaupandu. Malinga ndi bukhu lakuti Sports and Games in the Ancient World, m’Roma wamakedzana, “kuwomba m’manja kosalamulirika, kufuula ndi kukuŵirira kunkamveka” pamaseŵera Achiroma. Pamenepo, nzosadabwitsa kuti “kutengeka maganizo kunafalikira mosapeŵeka.” M’maseŵera akulimbana ndi zida, “ochemerera anali kufuula kuti ‘Muphe! Menya! Kantha!,’” osasamala kuti anali kusonkhezera kuphedwa kwa munthu mnzawo.
Kutengeka maganizo konkhitsa kwa maseŵera nkowanda lerolinonso koma nkoipa. Pambuyo pa maseŵera ampira wachitanyu a ku Ulaya kumene anthu 38 anaphedwa ndi ochemerera achiwawa, magazini a Discover anafotokoza kuti choputira chinali “lingaliro lakuti mpanduyo sadzadziŵika” limene limakhalapo pamene wina ali m’gulu. Chotero, munthuyo samadzimva kukhala waliŵongo kwenikweni pazochita zake. Komabe, Baibulo limachenjeza pa Eksodo 23:2 kuti: ‘Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.’ Koma kodi kungochemerera ndi kukuŵirira timu lanu kungakhaledi koipa motero? Inde. Magazini a Discover ananena kuti “kuchemerera ndi kukuŵirira pamaseŵera kuli mtundu wa kuukira kwa mawu kumene, kwa anthu ena, kungasinthe mosavuta ndikukhala kuukira kwakuthupi.”
Pamenepa, kodi kungakhale kopindulitsa kuyimba mfuu m’mavume ndi kuyimba nyimbo zimene zimachirikiza oseŵerawo kukantha opikisana nawo? Gerald wachichepere akukumbukira zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu zimene ankapezekako kuti: “Panali kukhala phokoso ndi kukuwa kwakukulu. Nthaŵi zina gululo linachitadi phokosolo mwachipongwe. Zikondwererozo zinali ngati madzoma ankhondo omwe anatisonkhezera kuchita chiwawa. Mawu monga ‘muphe,’ ‘mponde,’ ndi ‘mgwetse’ anagwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza.” Nthaŵi zina mawuwo anakhala zochitika zenizeni. Perry wachichepere akukumbukira chikondwerero kumene “aliyense ananyamula mtengo nayamba kumenya chifaniziro cha ngwazi ya timu lopikisana nalo. Pamene chikondwererocho chinatha, chifanizirocho chinawonongedwa kotheratu.”
Kodi ndani wosatha kuyambukiridwa ndi mzimu wamphamvu kwambiri wachiwawa wotero? Pazifukwa zabwino, Baibulo limachenjeza kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Mwana wasukulu wina wachichepere akuvomerezeradi kuti: “Sungachitire mwina kusiyapo kusonkhezeredwa kuchita zimene aliyense akuchita.” Ndipo ngati mutengamo mbali m’chiwawa, pangakhale zotulukapo zowopsa. Kumbukirani kuti Aedomu amakedzana anachemerera pamene Ababulo anafunkha Yerusalemu. “Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake,” anafuula motero Aedomu. (Salmo 137:7) Komabe, Mulungu anatsutsa kotheratu mzimu wawo wachiwawa, ndi wakubwezera. (Obadiya 1:1, 8, 12) Kodi wina akhoza kuchita zofananazo lerolino ndi kuloledwa ndi Mulungu?
Zowonadi, sizikondwerero zonse zosonkhezera timu lasukulu—ndipo simaseŵera onse—amene ali achiwawa. Koma ngakhale ngati paliko mzimu wabata, kodi nkoyenerera kwa Mkristu kung’ung’uza nyimbo zimene zimasonyeza mkhalidwe wochirikiza motengeka maganizo kapena ngakhale wakutamanda sukulu kapena timu lamaseŵera? (Yerekezerani ndi Eksodo 20:5.) Kodi kufuula mawu otonza kumagwirizana ndi uphungu wopezeka pa Aefeso 4:29, 31? Timaŵerenga kuti: ‘[Mawu, NW] onse ovunda asatuluke m’kamwa mwanu, . . . Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.’ Kodi kupezeka pachikondwerero chosonkhezeredwa ndi kutengeka maganizo kudzakuthandizani kukulitsa zipatso za mzimu wa Mulungu, zimene zimaphatikizapo ‘chifatso’ ndi ‘chiletso’? (Agalatiya 5:22, 23) Kapena kodi kudzangodzutsa mzimu wauchiŵanda wa mpikisano wa wafawafa?—Yerekezerani ndi Afilipi 2:3.
Ndithudi, mikhalidwe imasiyana. Nthaŵi zina limakhala lamulo kuti aliyense ayenera kupezeka pamisonkhano yapasukulu, ndipo chikondwerero chosonkhezera timu lasukulu chingakhale mbali ya programuyo. Zikondwerero zingasiyane mumkhalidwe wake ndi zoloŵetsedwamo. Ndipo pamene kuli kwakuti sitingaike lamulo lachindunji lokhwima pakupezekako, wachichepere Wachikristu angachite mwanzeru kukambitsirana nkhani zotero ndi makolo ake ndi kupenda mfundo zosiyanasiyana zophatikizidwa. (Onani Miyambo 24:6.) Ngati mwasankha kusadziloŵetsa m’zikondwerero zosonkhezera timu lasukulu, mwina mungafunikire kulimbana ndi chitsenderezo champhamvu cha ausinkhu wanu. Koma kumbukirani nthaŵi zonse kuti kukhulupirika kwanu koyamba kuli kwa Mulungu—osati sukulu kapena timu.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mpambo wa nkhani zakuti “Maseŵera—Kodi Ali ndi Malo Anji?” m’kope la Galamukani! la September 8, 1991.
[Bokosi patsamba 16]
‘Ndifuna Kukhala Wotsogolera Ochemerera!’
Asungwana ambiri—ndi anyamata—amalakalaka ulemu, kuzindikiridwa, ndi kutchuka zimene kukhala wotsogolera ochemerera kumadzetsa. “Kusonkhezera ndi kukondweretsa anthu kumawonjezera chimwemwe cha munthuwe,” anatero Lisa, msungwana wogwidwa mawu m’magazini a Seventeen. “Ndipo umadzimva kukhala kanthu kupenyedwa ndi aliyense!” Achichepere ena amakopeka ndi kudziŵana ndi anthu ambiri ngati akhala otsogolera ochemerera. Pamene olemba anthu anayesa kusainitsa Hannah wachichepere kuti akayesedwe, anamuuza kuti: “Udzakhala wotchuka ndipo kudzakupangitsa kumayanjana ndi anyamata.” Asungwana ena amanena kuti kukhala wotsogolera ochemerera kwawonjezera ulemu wawo.
Komabe, moyo wa wotsogolera ochemerera uli nzambiri koposa zokopazo. Kaŵirikaŵiri pamakhala mpikisano wa wafawafa pamayeso; kukanidwa kungakhale koswa maganizo. Pangakhale chidani chowopsa pakati pa magulu ochemerera a sukulu zopikisana nazo. Ndiponso, ntchito yocholoŵana yakutsogolera ochemerera ya lerolino imafuna akatswiri amaseŵera a Olympic. Kuvulala nkofala. Chotero otsogolera ochemerera ayenera kuthera maola ochuluka mlungu uliwonse akuyeseza. Monga momwe bukhu lamalangizo a wotsogolera ochemerera limanenera, munthuyo ayenera “kukhala wodzipereka kutsogolera ochemerera ndi kuyimba monga njira ya moyo.”
Kodi Mkristu akhoza kukhaladi “wodzipereka” ku kanthu kena kopanda pake monga kuchirikiza sukulu? Kutalitali; ndiponso sikukakhala koyenerera kwa wachichepere Wachikristu kufulumiza khamu kutchula mawu m’mavume kapena kuyimba nyimbo zimene zimasonkhezera chiwawa kapena kupembedza timu ndi ngwazi zamaseŵera. Ndipo, monga momwe tanenera poyamba, upandu wa “mayanjano oipa” ndiwo nkhaŵa yaikulu. (1 Akorinto 15:33) Ndiponso, tisaiŵale mavuto odziŵikiratu amene tingadzipalamulire mwakudziwonetsera—ndi kuvina—m’zovala zosayenera zimene otsogolera ochemerera amafunika kuvala.—1 Timoteo 2:9.
Pokhala kuti zonse zalingaliridwa, nkwachiwonekere kuti kutsogolera ochemerera kuli kosayenerera wachichepere Wachikristu. Kudzipereka kwake kwa Yehova nkofunika koposa.
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mzimu wokhala pazikondwerero zosonkhezera timu lasukulu umagwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino Achikristu?