Lingaliro la Baibulo
Kodi Nthaŵi Zonse Kumakhala Kulakwa Kukwiya?
“MKWIYO ndiwo kupenga kwakanthaŵi.” Mwa kunena zimenezi, Horace, wolemba ndakatulo wamakedzana Wachiroma anatchula za lingaliro lofala lonena za mtundu wina wa malingaliro amphamvu koposa. Pamene kuli kwakuti si aliyense amavomereza kuti mkwiyo uli mtundu wa kupenga kwakanthaŵi, ambiri amauona kukhala chibadwa choipa. Ngakhale kalelo m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi C.E., odzipatulira Achikatolika anasonkhanitsa mpambo wotchuka wotchedwa “machimo oipitsitsa asanu ndi aŵiri.” Mosadabwitsa, mkwiyo unali pa ndandandayo.
Nkosavuta kuona chifukwa chake analingalira mwanjirayi. Baibulo limanenadi kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo.” (Salmo 37:8) Ndipo mtumwi Paulo analangiza mpingo wa ku Efeso kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.”—Aefeso 4:31.
Komabe mungazizwe kuti, ‘Kodi ndizokhazo zimene Baibulo limanena pa lingaliro lake la mkwiyo? Ndi iko komwe, kodi Paulo sanaloserenso kuti “masiku otsiriza” ano amene tikukhalamo akakhala “oŵaŵitsa”?’ (2 Timoteo 3:1-5) Kodi Mulungu amatiyembekezeradi kukhala m’nthaŵi zino, pamene anthu ali ‘aukali, osakonda ubwino, opanda chikondi chachibadwidwe’—ndi kuti tisakwiye ngakhale ndi pang’ono pomwe?
Lingaliro Lachikatikati
Lingaliro la Baibulo pankhaniyi silili loletseratu kapena lovomerezeratu. Mwachitsanzo, onani mawu a Paulo pa Aefeso 4:26: “Kwiyani, koma musachimwe.” Vesili likanakhala lodabwitsa kwambiri ngati mkwiyo unali “tchimo loipitsitsa,” lofunikira chilango chamuyaya.
Paulo anali kugwira mawu Salmo 4:4, limene limati: “Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe.” Malinga ndi Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words, liwu Lachihebri lotembenuzidwa “chinthenthe,” lakuti ra·ghazʹ, limatanthauza “kunthunthumira ndi lingaliro lamphamvu.” Koma kodi ndi lingaliro lamphamvu liti? Kodi linali mkwiyo? M’matembenuzidwe a Septuagint a Salmo 4:4, liwu lakuti ra·ghazʹ linatembenuzidwa m’Chigiriki monga “kukwiyitsidwa,” ndipo mwachionekere ndi zimene Paulo anatanthauza panopa.
Kodi nchifukwa ninji Baibulo lingalole mkwiyo? Chifukwa chakuti si mkwiyo wonse umene uli woipa. Lingaliro lakuti, monga momwe ananenera wothirira ndemanga pa Baibulo wina, “mkwiyo wa munthu mwa iwo wokha suli wolungama konse ndipo sungaloledwe” si la Malemba. Katswiri wa Baibulo R. C. H. Lenski anakamba zolondola ponena za Aefeso 4:26 kuti: “Miyezo imene imaletsa mkwiyo uliwonse ndi kufuna kudekha kosasintha mumkhalidwe uliwonse ili ya Chisitoiki ndipo osati ya Chikristu.” Profesa William Barclay ananena chimodzimodzi kuti: “Payenera kukhala mkwiyo m’moyo Wachikristu, koma uyenera kukhala mtundu woyenera wa mkwiyo.” Koma kodi “mtundu woyenera wa mkwiyo” ndi wotani?
Mkwiyo Wolungama
Ngakhale kuti mkwiyo suli umodzi wa mikhalidwe yaikulu ya Yehova, iye mobwerezabwereza amalongosoledwa m’Malemba kukhala atakwiya ndi kusonyeza mkwiyo wake. Komabe, pazifukwa ziŵiri, mkwiyo wake nthaŵi zonse umakhala wolungama. Chifukwa choyamba nchakuti, iye samakwiya konse popanda chifukwa choyenera. Ndipo chachiŵiri, amasonyeza mkwiyo wake m’njira yolungama, salephera konse kudziletsa.—Eksodo 34:6; Salmo 85:3.
Yehova amakwiyitsidwa ndi chisalungamo chadala. Mwachitsanzo, iye anauza Aisrayeli kuti ngati akazunza akazi ndi ana amasiye, ‘mosalephera akamva kulira kwa’ oterowo. Iye anachenjeza kuti: ‘Mkwiyo wanga udzayaka.’ (Eksodo 22:22-24; yerekezerani ndi Miyambo 21:13.) Mofanana ndi Atate wake, Yesu anali ndi mtima wokonda ana. Pamene otsatira ake okhala ndi cholinga chabwino anayesa kuletsa ana kuti asafike kwa iye, “Yesu . . . anakwiya” natengera anawo m’manja mwake. (Marko 10:14-16) Dziŵani kuti liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kukwiya” poyambirira linatanthauza “kupweteka kwakuthupi kapena kunyanyulidwa.” Malingaliro amphamvu ndithu!
Ukali wolungama woterowo unaputidwanso mumtima mwa Yesu pamene anaona kuti amalonda ndi osinthitsa ndalama anasandutsa nyumba yolambirira ya Atate wake kukhala “phanga la achifwamba.” Iye anagubuduza magome awo nawathamangitsira kunja! (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:15) Pamene Afarisi ndi alembi anasonyeza nkhaŵa yaikulu kaamba ka malamulo awo otopetsa a Sabata kuposa pa odwala omwe anafunikira chithandizo, Yesu “anapwetekedwa mtima kwambiri pamene anazindikira kupanda chifundo kwawo,” ndipo “anapotoloka mwaukali kuyang’ana nkhope zomzinga.”—Marko 3:5, Phillips.
Mofananamo, Mose wokhulupirika wakaleyo anadzazidwa ndi ukali chifukwa cha Aisrayeli osakhulupirika pamene anagwetsera pansi magome a Chilamulo cha Mose. (Eksodo 32:19) Ndipo mlembi wolungama Ezara anakwiya kwambiri chifukwa cha kusamvera kwa Aisrayeli lamulo la Mulungu la ukwati kwakuti anang’amba zovala zake ndipo ngakhale kuzula lina la tsitsi lake!—Ezara 9:3.
Awo onse ‘okonda chokoma’ amalimbikira ‘kudana nacho choipa.’ (Amosi 5:15) Motero, Akristu lerolino angamve mkwiyo wolungama ukutukusira m’mitima yawo pamene aona machitidwe adala osalapa a nkhalwe, chinyengo, kusaona mtima, kusakhulupirika, kapena chisalungamo.
Kuchita ndi Mkwiyo Moyenerera
Sizinangochitika mwamalunji kuti Baibulo kaŵirikaŵiri limafanizira mkwiyo ndi moto. Mofanana ndi moto, mkwiyo uli ndi malo ake. Koma ungakhalenso wosakaza mowopsa. Mosiyana ndi Yehova ndi Yesu, kaŵirikaŵiri anthu amakwiya popanda chifukwa choyenera kapena amasonyeza mkwiyo wawo mwanjira yosalungama.—Onani Genesis 4:4-8; 49:5-7; Yona 4:1, 4, 9.
Kumbali ina, kungotsekereza mkwiyo mkati ndi kuchita monga ngati palibe sikungakhalenso kolungama. Kumbukirani, Paulo analangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Pali njira za Malemba zosonyezera mkwiyo, monga ngati ‘kunena mumtima mwanu,’ kutulutsa malingaliro anu kwa woululira zakukhosi wokhwima, kapena ngakhale kukambitsirana ndi wolakwayo modekha.—Salmo 4:4; Miyambo 15:22; Mateyu 5:23, 24; Yakobo 5:14.
Chifukwa chake, sikumakhala kulakwa nthaŵi zonse kukwiya. Onse aŵiri Yehova ndi Yesu akhala akukwiya—ndipo adzateronso! (Chivumbulutso 19:15) Ngati tifuna kuwatsanzira, tingakumane ngakhale ndi mikhalidwe mu imene kumakhala kulakwa kusakwiya! Mfungulo yake idzakhala kutsatira uphungu wa Baibulo, tikumatsimikizira kuti tili ndi chifukwa choyenera chokhalira ndi malingaliro amphamvu ndi kuti tikuwasonyeza m’njira yolungama ndi Yachikristu.
[Chithunzi patsamba 27]
Kaini ndi Abele