Ulendo wa Papa ku UN Kodi Unakwaniritsanji?
PAULENDO wake wapandege wooloka Atlantic kukalankhula ku UN ku New York City, Papa John Paul II anapyola makilomita 1,000,000 a maulendo ake a padziko lonse. Panali pa October 4, 1995, ndipo uwu unali ulendo wake wa 68 wopita kunja monga papa. Mosakayikira, iye ndiye papa amene wayenda maulendo ambiri koposa m’mbiri ya Tchalitchi cha Roma Katolika.
Anafika pa Newark International Airport, New Jersey, pa Lachitatu lina lamvula, ali wotetezeredwa kwambiri mu imodzi ya njira zachitetezo imene siinachitidwepo kwa munthu aliyense wolemekezeka. Kwayerekezeredwa kuti panali akuluakulu a boma ndi a mumzinda okwanira 8,000 amene anapatsidwa ntchito yotetezera papa. Nkhani ina inatcha zimenezo kukhala “chikamba cholinganizidwa mosamalitsa cha chitetezo,” choloŵetsamo mahelikoputala ndi odziŵa kusambira pansi pa madzi.
Nchifukwa Ninji Panali Ulendowo?
M’nkhani yake ya pabwalo landege, papa anafotokoza kuti amene iye analoŵa m’malo, Papa Paulo VI, analankhula kwa General Assembly ya UN ndi chiitano chamtendere chakuti: “Pasakhalenso nkhondo, nkhondo zisadzakhaleponso!” John Paul II ananena kuti anali kubwererako “kukamveketsa chikhulupiriro [chake] chakuti malingaliro ndi zifuno zimene zinachititsa UN kukhalapo zaka makumi asanu kumbuyoku nzofunika kwambiri tsopano kuposa ndi kale lonse m’dziko limene likufunafuna chifuno.”
Pamapemphero amadzulo ku Sacred Heart Cathedral, Newark, papa anasonyezanso kuchirikiza kwake UN, akumati: “Gulu limenelo lilipo kuti litumikire zabwino za banja lonse la anthu, ndipo motero nkoyenerera kuti papa akalankhule kumeneko monga mboni ku chiyembekezo cha Uthenga Wabwino.” Anawonjezera kuti: “Chotero pemphero lathu la mtendere lilinso pemphero la United Nations Organization. Francis Woyera wa ku Assisi . . . akuŵala monga wokonda mtendere kwambiri ndi wougwirira ntchito. Tiyeni tichonderere thandizo lake pantchito ya United Nations ya chilungamo ndi mtendere padziko lonse lapansi.”
M’nkhani yake ku UN, anatamanda kusintha kwa ndale kopanda chiwawa ku Eastern Europe mu 1989, kumene maiko ambiri anali atakhalanso ndi ufulu. Iye analimbikitsa “kukonda dziko koona” mosiyana ndi “utundu watsankhu ndi wopanda ufulu.” Analankhula za zisalungamo za dongosolo lilipoli, akumati: “Pamene anthu mamiliyoni akuvutika ndi umphaŵi umene ukutanthauza njala, matenda a njala, matenda, kusaphunzira, ndi kululuzika, tiyenera . . . kudzikumbutsa kuti palibe ali woyenera kudyera mnzake masuku pamutu kaamba ka phindu la iye mwini.”
Ndiyeno anati: “Pamene tikuyang’anizana ndi mavuto aakulu ameneŵa, kodi tingalephere motani kuzindikira ntchito ya United Nations Organization?” Ananena kuti UN iyenera “kukhala malo apakati a makhalidwe abwino kumene mitundu yonse yapadziko lonse ingakhale yomasuka.” Iye anagogomezera kufunika kwa kuchirikiza “kugwirizana kwa banja lonse la anthu.”
Mtendere Weniweni—Kuchokera Kumagwero Ati?
Mosakayikira, iye anafotokoza malingaliro abwino ambiri. Komabe, m’nkhani yake yaitaliyo, kodi panthaŵi ina iliyonse anasonyeza atsogoleri a dziko chothetsera mavuto a anthu cha Mulungu—ulamuliro wake wa Ufumu mwa Kristu Yesu? (Mateyu 6:10) Ayi. Kwenikweni, sanagwirepo mawu a Baibulo m’nkhani yake ku UN. Mosiyana ndi zimenezo, ananena kuti “ndi thandizo la chisomo cha Mulungu, m’zaka za zana likudzali ndi m’zaka chikwi zotsatirapo tingapange makhalidwe apamwamba oyenerera munthu, makhalidwe enieni a ufulu.” Kwa ophunzira Baibulo, lingaliro limenelo lingamveke kukhala likufanana ndi lija lonenedwa ndi awo a pa Babele wakale zaka zoposa 4,000 zapitazo, amene anaganiza kuti angagwirizanitsebe anthu mwa njira za anthu: “Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire dzina.” (Genesis 11:4) Chotero, malinga ndi malingaliro ameneŵa, ali atsogoleri andale a anthu, oimiridwa ku UN, amene adzapanga makhalidwe apamwamba atsopano ozikidwa pa ufulu.
Koma kodi Baibulo limaloseranji ponena za mtsogolo mwa maboma andale a munthu ndi UN yeniyeniyo? Mabuku a Danieli ndi Chivumbulutso amapereka chithunzi choonekera bwino cha mtsogolo mwawo mmene mukuwayembekezera. Danieli analosera kuti m’masiku otsiriza, Mulungu adzaika ulamuliro wa Ufumu wake, monga mwala waukulu ‘wosemedwa popanda manja.’ Kodi udzachitanji? “Masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthaŵi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” Maboma a munthu adzaloŵedwa m’malo ndi ulamuliro umodzi wolungama kaamba ka anthu onse.—Danieli 2:44, 45.
Kodi nchiyani chidzachitikira UN? Chivumbulutso chaputala 17 chimasonyeza UN (ndi amene inaloŵa m’malo mwake, League of Nations yosakhalitsayo) monga chirombo chofiiritsa chimene ‘chidzamka kuchitayiko.’ (Chivumbulutso 17:8)a Yehova sadzabweretsa mtendere weniweni kudzera mwa chinthu chilichonse chaumunthu, ngakhale kuti atsatiri ake akhale oona mtima motani. Mtendere weniweni udzabwera kudzera mwa Ufumu wa Mulungu wolonjezedwawo, wokhala m’manja mwa Kristu Yesu woukitsidwayo kumwamba. Amenewo ndiwo maziko a kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu la pa Chivumbulutso 21:3, 4: “Taonani chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”
Ulendowo—Kodi Chisonkhezero Chake Chinali Chotani?
Pamene papa anakhudza Baibulo m’nkhani zake, kodi Akatolika okhulupirika analimbikitsidwa kutulutsa ma Baibulo awo ndi kuona mawuwo? Chenicheni ndicho chakuti ochuluka sananyamule Baibulo nkomwe. Papa sanasonye ku mawu a m’Baibulo enieni kaŵirikaŵiri kuti alimbikitse omvetsera kuliŵerenga.
Chitsanzo china chinali pamene analankhula kwa anthu 83,000 mu Giants Stadium ya ku New Jersey ndi kunena kuti: “Tikuyembekezera kubweranso kwa Ambuye monga woweruza wa amoyo ndi akufa. Tikuyembekezera kubweranso kwake muulemerero, kudza kwa ufumu wa Mulungu mu uchikwanekwane wonse. Chimenecho ndicho chiitano chosalekeza cha masalmo kuti: ‘Yembekeza Ambuye ndi kulimba mtima; limba mtima, ndi kuyembekezera Ambuye.’” Koma kodi anagwira mawu ati m’masalmowo? Ndipo ndi Ambuye uti amene anali kunena—Yesu kapena Mulungu? (Yerekezerani ndi Salmo 110:1.) Malinga ndi nyuzipepala ya ku Vatican ya L’Osservatore Romano, anali kugwira mawu a Salmo 27:14, amene momvekera bwino amati: “Ika chiyembekezo chako mwa Yahweh, khala wolimba, limba mtima, ika chiyembekezo chako mwa Yahweh.” (The Jerusalem Bible) Inde, tiyenera kuika chiyembekezo chathu mwa Yahweh, kapena Yehova, Mulungu wa Ambuye Yesu.—Yohane 20:17.
M’mbiri yonse, kodi atsogoleri achipembedzo ndi akuluakulu achikatolika alimbikitsa mtendere pakati pa mitundu? Kodi chiphunzitso chachikatolika chathetsa mikangano yautundu, yaufuko, ndi ya anthu a manenedwe osiyana? Kupululutsa kwa mu 1994 ku Rwanda, mu Afirika wakummaŵa koma chapakati ndi nkhondo zachiŵeniŵeni za m’zaka zingapo zapitazo mu amene kale anali Yugoslavia zonsezo zikusonyeza kuti zikhulupiriro zachipembedzo kwenikweni zimalephera kuthetsa udani waukulu ndi tsankhu zimene zili m’mitima ya anthu. Kuulula machimo kwachiphamaso kwa mlungu ndi mlungu kapena kupezeka pa Misa nthaŵi zonse sikudzasintha mmene anthu amaganizirira ndi kuchitira zinthu. Payenera kukhala chisonkhezero chakuya kwambiri, chija chimene chimadza kokha pamene Mawu a Mulungu aloledwa kuloŵa mumtima ndi m’maganizo a wokhulupirira.
Khalidwe losinthidwa la Mkristu woona silimazikidwa pa kutengeka maganizo kochititsidwa ndi miyambo yachipembedzo koma kumazikidwa pa kumvetsetsa kwa nzeru chifuniro cha Mulungu kwa munthu aliyense. Mtumwi Paulo anati: “Musafanizidwe ndi khalidwe la dziko lokuzingani, koma sinthani khalidwe lanu, lofanizidwa ndi maganizo anu atsopano. Iyi ndiyo njira yokha yopezera chifuniro cha Mulungu ndi kudziŵa chimene chili chabwino, chimene Mulungu akufuna, chimene chili chinthu changwiro kuchichita.” (Aroma 12:1, 2, JB) Khalidwe latsopano limeneli limapezedwa mwa phunziro la Mawu a Mulungu amene amatsogolera ku chidziŵitso cholongosoka cha chifuniro chake. Amapanga mphamvu yauzimu imene imasonkhezera maganizo ndi kuchititsa khalidwe lachikristu.—Aefeso 4:23; Akolose 1:9, 10.
Kodi Tchalitchi Chili pa “Mphambano Yovuta”?
Nyuzipepala yachispanya El País inafotokoza Papa John Paul II kukhala ali ndi “chisonkhezero chapadera” monga mwamuna wazaka 75, ndipo nyuzipepala ya ku United States inamutcha kukhala “katswiri wa nyuzi.” Ngwaluso pochita ndi ofalitsa nkhani ndiponso poyanjana ndi anthu ndi ana awo. Pamaulendo ake iye amaimiradi Holy See imene ili ku Vatican City. Ngakhale kuti Vatican imadziŵika mwalamulo ku UN, dalitso la papa pa gulu limenelo silidzalitsimikizira dalitso la Yehova Mulungu.
Ulendo wa papa unaonedwa mosiyanasiyana. Ambiri a Akatolika amene anapeza matikiti oloŵera Misa yochitidwira poyera anamva kukhala otsitsimulidwa ndi chochitikacho. Komabe, atsogoleri ena achikatolika sanauone bwino ulendowo ndi zimene ukhoza kuchititsa. The New York Times inagwira mawu Timothy B. Ragan, pulezidenti wa Catholic National Center for Pastoral Leadership, akunena kuti “Papa sanagwiritsire ntchito bwino mwaŵi wa ulendowo. Ngakhale kuti ulendowo ‘unali wosonkhezera ndipo wapadera kwa anthu ambiri pokhala atachitira Misa poyera,’” kwa atsogoleri achikatolika ambiri sunapereke “nthaŵi yakuti iye amvetsere ndi mpata wa kukambitsirana.” Akatolika ambiri amalingalira kuti pankhani zonga kusakwatira, kubala ana, ndi chisudzulo amakakamizidwa kumvetsera kwa munthu mmodzi wolankhula.
Akuluakulu ena achikatolika akuvomereza, kuti “tchalitchi chili pa mphambano yovuta,” ndipo akuwopa kuti Akatolika ambiri, “makamaka achichepere, akutaya lingaliro lenileni la chimene kukhala Mkatolika kumatanthauza.” James Hitchcock, wosunga mwambo wachikatolika, “akuona vutolo monga kusamvana kowononga pakati pa akuluakulu osunga mwambo mowonjezereka ndi ‘akuluakulu apakati’ osasunga mwambo kwenikweni.”
Ponena za mmene ulendo wa papa udzayambukirira vuto la akuluakulu a tchalitchi, Hitchcock anati: “Iye amadza kuno, amamkhumbira, amamka kwawo—ndipo palibe chimene chichitika. Kwa ine zotulukapo nzogwiritsa mwala.” Mosakayikira papa anaphonyadi mpata wa kuuza atsogoleri achipembedzo ku UN kumene kuli magwero a mtendere weniweni.
Ngakhale kuti UN Charter ndi manenanena a anthu amagogomezera za chonulirapo cha “mtendere ndi chisungiko,” musanyengedwe. Baibulo limachenjeza kuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:3) Mtendere weniweni ndi chisungiko zidzabwera kokha mwa chifuniro cha Mulungu ndipo m’njira yake—kudzera mu ulamuliro wake wa Ufumu, osati kudzera mu UN.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zowonjezereka pa ulosi wa m’Chivumbulutso umenewu, onani buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, masamba 240-51, lofalitsidwa mu 1988 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu a Chithunzi patsamba 22]
Zithunzi za UN