Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 8/8 tsamba 8-11
  • Thandizani Ana Anu Kukula Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ana Anu Kukula Bwino
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkhalidwe Woyenera
  • Kuyamikira
  • Kulankhulana
  • Kuletsa Mkwiyo
  • Kusunga Mwambo ndi Ulemu
  • Kusamalira Zosoŵa Zauzimu
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 8/8 tsamba 8-11

Thandizani Ana Anu Kukula Bwino

TIKAFIKA pa mfundo yolera ana, makolo ambiri amafufuza uku ndi uku kufuna mayankho amene kwenikweni amapezeka mosavuta m’nyumba mwawo mwenimwenimo. Mabanja osaŵerengeka ali ndi Baibulo, koma limangokhala pashelufu osaligwiritsira ntchito polera ana.

Ndithudi, ambiri masiku ano amakayikira kugwiritsira ntchito Baibulo monga chitsogozo pa moyo wa banja. Amalinena kuti lidatha ntchito, nlachikale, kapenanso kuti lili ndi malamulo okhwima. Koma kufufuza koona mtima kumasonyeza kuti Baibulo ndi buku loyenera m’mabanja. Tiyeni tione kuti izi ziri motani.

Mkhalidwe Woyenera

Baibulo limauza tate kuti ayenera kuona ana ake monga ‘timitengo ta azitona pozinga podyera pake.’ (Salmo 128:3, 4) Timitengo ting’onoting’ono sitingakule kufika pokhala mitengo yobala zipatso popanda kulimirira, popanda kuthiridwa manyowa, dothi labwino, ndiponso chinyezi. Mofananamo, kuti mulere bwino ana zimalira khama ndiponso kusamala. Ana amafunikira malo abwino kuti akule ndi kufikapo.

Chofunika choyamba pa mkhalidwe woyenera umenewo ndicho chikondi—pakati pa bambo ndi mayi ndiponso pakati pa ana ndi makolo. (Aefeso 5:33; Tito 2:4) Ambiri amakondana m’mabanja mwawo koma saona chifukwa chilichonse chonenera za chikondi chimenecho. Komabe, talingalirani: Kodi mukadati mwakambitsirana ndi bwenzi lanu ngati mukanamlembera kalata imene simunalembepo adiresi, simunamatepo sitampa, mwinanso simunatumize? Momwemonso, Baibulo limasonyeza kuti chikondi chenicheni sikumangodzimva nokha mumtima; chimaonekera mwa mawu ndiponso m’zochita. (Yerekezerani ndi Yohane 14:15 ndiponso 1 Yohane 5:3.) Mulungu anaika chitsanzo, ponena mawu osonyeza chikondi chake kwa Mwana wake: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 3:17.

Kuyamikira

Kodi makolo angasonyeze motani chikondi chimenecho kwa ana awo? Choyamba, yang’anani pa zabwino. Nkwapafupi kuti muone zolakwa kwa ana. Chibwana chawo, kuchepa kwawo chidziŵitso, ndiponso kudzikonda kudzaonekera mwanjira zambiri, tsiku ndi tsiku. (Miyambo 22:15) Komabe amachitanso zabwino zambiri tsiku lililonse. Kodi inu mudzaonapo ziti? Mulungu sakhalira kuona zolakwa zimene timachita koma m’malo mwake amakumbukira zabwino zimene timachita. (Salmo 130:3; Ahebri 6:10) Tiyenera kukhala mofananamo ndi ana athu.

Mwamuna wina wachinyamata anati: “Moyo wanga wonse panyumba pathu, sindikumbukirapo kuti ndinathokozedwapo—kaya ndichite zabwino zotani kunyumba kapena kusukulu. Makolo musamanyalanyaze chinthu chofunika chimenechi kwa ana anu! Ana onse ayenera kuthokozedwa kaŵirikaŵiri pa zinthu zabwino zimene achita. Izi zidzachepetsa mpata wakuti akule ali ‘otaya mtima,’ ndi chikhulupiriro chakuti palibe chilichonse chabwino chomwe angathe.—Akolose 3:21.

Kulankhulana

Njira ina yosonyezera chikondi kwa ana anu ndiyo kutsatira uphungu wa pa Yakobo 1:19: “Yense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” Kodi mumawapangitsa ana anu kunena zakukhosi ndipo inu nkumamvetseradi zimene akunenazo? Ngati ana anu azindikira kuti mudzayamba kuwapatsa malangizo asanathe nkomwe kunena kapena kuti mudzapsa mtima mukadziŵa mmene iwo akulingalirira, basi sadzakuuzani malingaliro awo. Koma akazindikira kuti mudzamvetsera, adzakhala olakalaka kulankhula.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:5.

Komabe, bwanji ngati asonyeza malingaliro amene mudziŵa kuti ali olakwa? Kodi ndiyo nthaŵi yoyankha mwaukali, kupereka malangizo, kapena kupereka chilango? Ndithudi, zonena zina zachibwana zingapangitse kukhala kovuta kuti ‘mudekhe polankhula, mudekhe pakupsa mtima.’ Komabe talingaliraninso za Mulungu ndi ana ake. Kodi amaopsa, kwakuti ana ake nkukhala ndi mantha kuti amuuze zakukhosi? Ayi! Salmo 62:8 limati: “Khulupirirani pa [Mulungu] nyengo zonse, anthu inu: tsanulirani mitima yanu pamaso pake: Mulungu ndiye pothawirapo ife.”

Motero pamene Abrahamu anali ndi nkhaŵa chifukwa cha ganizo la Mulungu lofuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, sanaope kunena kwa Atate wake wakumwamba kuti: “Musamatero ayi . . . kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?” Yehova sanamdzudzule Abrahamu; Anamvetsera ndipo anamtonthoza. (Genesis 18:20-33) Mulungu ndi wodekha kwambiri ndiponso woleza mtima, ngakhale pamene ana ake akunena za kukhosi kwawo zomwe sizili zoyenera ndipo zopanda pake.—Yona3:10–4:11.

Mofananamo makolo ayenera kupangitsa ana awo kusaopa kunena zakukhosi kwawo, mosasamala kanthu kuti nzokhumudwitsa chotani. Motero ngati mwana wanu wapsa mtima mwasontho, mvetserani. M’malo momdzudzula mwaukali, mvetsetsani momwe mwanayo akulingalirira ndipo mpangitseni kunena zifukwa zake. Mwachitsanzo, mukhoza kunena kuti: ‘Ukumveka ngati wamukwiyira uje. Kodi ungandiuze chomwe chinachitika?’

Kuletsa Mkwiyo

Ndithudi, palibe kholo loleza mtima ngati Yehova. Ndipo ana angayesedi kuleza mtima kwa makolo awo. Ngati ana anu amakukwiyitsani kaŵirikaŵiri, musakhumudwe ndi kuganiza kuti mukulephera kukhala kholo labwino. Nthaŵi zina, simudzakhala mukulakwa kukwiya. Mulungu mwiniyo amakwiyira ana ake ndi chifukwa chabwino, ngakhale ena okondedwa kwambiri ndi iye. (Eksodo 4:14; Deuteronomo 34:10) Komabe, Mawu ake amatiphunzitsa kuletsa mkwiyo wathu.—Aefeso 4:26.

Motani? Nthaŵi zina zimathandiza kukhala chete kwakanthaŵi motero kuti mkwiyo wanuwo uzizire. (Miyambo 17:14) Ndipo kumbukani kuti, Ameneyu ndi mwana! Musayembekezere kuti adzasonyeza khalidwe la munthu wamkulu kapena kulingalira mwauchikulire. (1 Akorinto 13:11) Kumvetsetsa kuti nchifukwa ninji mwana wanu wachita zotere kukhoza kuchepetsa mkwiyo wanu. (Miyambo 19:11) Musaiŵale kusiyana kwakukulu kumene kuli pakati pa kuchita chinthu choipa ndi kukhala woipa. Kuzazira mwana kuti ndi woipa kukhoza kupangitsa mwana kulingalira kuti, ‘Nanga nkuyeseranji nkomwe kukhala wabwino?’ Koma kuwongolera mwana mwachikondi kudzathandiza kuti adzachite bwino nthaŵi ina.

Kusunga Mwambo ndi Ulemu

Kuphunzitsa ana kusunga mwambo ndi ulemu ndilo vuto limodzi limene makolo amakumana nalo. M’tsiku lathu pamene dziko limangololera zilizonse, ambiri amadabwa ngati kuli koyenera nkomwe kuletsa mwana zinthu zina. Baibulo limayankha kuti: “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Ena amasonyeza kusakondwa ndi mawu akuti “nthyole” akumaganiza kuti zimenezo zimasonya kuchitira nkhanza mwana. Koma sichoncho ayi. Liwu lachihebri la “nthyole” linatanthauza tsatsa, monga lija mbusa amagwiritsira ntchito pokusa—osati kuzivulaza—nkhosa zake.a Motero nthyole imaimira chilango.

M’Baibulo, kulanga nthaŵi zambiri kumatanthauza kuphunzitsa. Nchifukwa chake buku la Miyambo limanena nthaŵi zinayi kuti, ‘imva mwambo.’ (Miyambo 1:8; 4:1; 8:33; 19:27) Ana ayenera kuphunzira kuti kuchita zabwino kumabweretsa mphotho ndi kuti kuchita zoipa kumabweretsa mavuto. Chilango chingathandize mwana kuona kuipa kwa khalidwe loipa, monga momwe mphotho—monga kuyamikira—ingamthandizire kuona ubwino wa khalidwe labwino. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 11:26-28.) Makolo angachite bwino kutengera chitsanzo cha Mulungu zikafika pa mfundo yopereka chilango, chifukwa anauza anthu ake kuti ndidzakukwapulani “pamlingo woyenera.” (Yeremiya 46:28, NW) Ana ena amangofuna kuwakalipira pang’ono kuti aongoke. Ena amafunikira chilango chokhwimirapo. Koma kukwapula “pamlingo woyenera” sikutanthauza kufika mpaka poti mwanayo mwamvulaza kaya mwakuthupi kapena mwamaganizo.

Chilango chachikatikati chiyenera kuphatikizapo kuphunzitsa ana malire amene sayenera kudumpha. Ambiri mwa ameneŵa ananenedwa momvekera bwino m’Mawu a Mulungu. Baibulo limaphunzitsa kusadumpha malire pa zinthu za mwini. (Deuteronomo 19:14) Limaika malire omvekera, likumanena kuti nkulakwa kuchita chiwawa kapena kuvulaza wina mwadala. (Salmo 11:5; Mateyu 7:12) Limapereka malire pa zakugonana, limaletsa kugonana kwapachibale. (Levitiko 18:6-18) Limalongosola ngakhalenso malire a munthu payekha, likumaletsa kutchula wina maina onyoza kapena kunena mawu otukwana. (Mateyu 5:22) Kuphunzitsa ana mfundozi ndiponso malire ameneŵa—ponseponse, mwamawu ndiponso mwakusonyeza chitsanzo—nzofunika kuti banja lizikhala bwino.

Njira ina yosungitsira mwambo ndi ulemu m’banja ndiyo kuzindikira udindo wa aliyense m’banja. M’mabanja ambiri masiku ano, maudindo amenewa amanyalanyazidwa kapena kusokonezedwa. M’mabanja ena, kholo limanena mavuto aakulu kwa mwana, zomwe mwanayo sanafike poti nkuzitha. Pamene m’mabanja ena, ana amaloledwa kukhala timafumu totsendereza, tikumapanga zosankha zoti banja lonselo litsatire. Kuteroko nkulakwa ndipo kumawononga mwana. Makolo ndiwo ayenera kupezera ana awo zofunika—kaya zakuthupi, zamaganizo, kapena zauzimu—osati ana kupezera makolo. (2 Akorinto 12:14; 1 Timoteo 5:8) Lingalirani za chitsanzo cha Yakobo, amene anasintha kayendedwe ka banja lake lonse ndiponso antchito ake kuti asavutitse ana ang’onoang’ono. Anazindikira kufooka kwawo ndipo anachitapo kanthu mwamsanga.—Genesis 33:13, 14.

Kusamalira Zosoŵa Zauzimu

Ngati tifuna kuti tikhale ndi banja lachimwemwe palibe chinthu chofunika kwambiri kuposa zauzimu. (Mateyu 5:3) Ana ali ndi kuthekera kwakukulu kwa kukonda zauzimu. Ali ndi mafunso ambiri: Kodi nchifukwa ninji tiriko? Ndani anapanga dziko ndiponso zinyama, mitengo, nyanja zake? Nchifukwa ninji anthu amafa? Kodi chimachitika nchiyani pambuyo pake? Nchifukwa ninji anthu abwino zoipa zimawachitikira? Ndandandayo ikuoneka kuti singathe. Kaŵirikaŵiri, ndi makolo amene amakonda kusalingalira zotero.b

Baibulo limalimbikitsa makolo kuti azikhala ndi nthaŵi kuphunzitsa ana awo zauzimu. Limanena za maphunziro amenewa monga kukambitsirana kwa nthaŵi zonse koma kwabwino pakati pa makolo ndi ana awo. Makolo angathe kuphunzitsa ana awo za Mulungu ndiponso Mawu ake pamene akuyendera pamodzi, pamene akhala m’nyumba, panthaŵi yogona—paliponse pomwe mpata wapezeka.—Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 6:4.

Baibulo limachita zambiri koposa kungoyamikira programu ya zauzimu imeneyi. Lilinso ndi nkhani zophunzira. Ndithudi, kodi inu mungayankhe bwanji mafunso a ana omwe tanena pamwambapa? Baibulo lili ndi mayankho ake. Ndi omveka bwino, osangalatsa, ndipo amapereka chiyembekezo chotsimikizirika m’dziko lino lopanda chiyembekezo. Koma chabwino choposa apo, kumvetsetsa nzeru ya m’Baibulo kukhoza kulimbikitsa kwambiri ana anu m’masiku ano amene zinthu zonse nzosokonekera. Apatseni malangizo amenewo, ndipo ndithudi adzakhala osangalala—tsopano ndiponso m’tsogolo.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! yachingelezi ya September 8, 1992, masamba 26-7.

b Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha banja linapangidwa ncholinga choti lizigwiritsiridwa ntchito paphunziro labanja ndipo lili ndi malangizo othandiza ochokera m’Baibulo onena za ukwati ndi kulera ana. Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Funani njira zomwe mungayamikirire zochita za ana anu nthaŵi zonse

[Bokosi patsamba 9]

Mmene Mungathandizire Ana Kuti Akule Bwino

• Pangitsani panyumba kukhala pa chisungiko moti aziona kuti amakondedwa ndi kufunidwa

• Ayamikireni kaŵirikaŵiri. Tchulani zimene mukuwayamikirazo

• Muzimvetsera zonena zawo

• Pakakhala kukwiya muziyamba mwakhala chete

• Mosasinthasintha, ikani malire odziŵika bwino

• Perekani chilango molingana ndi mmene chikufunikira kwa mwana aliyense payekha

• Musayembekezere zimene mwana wanu sangathe kuchita

• Samalirani zosoŵa zauzimu mwakuphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse

[Bokosi patsamba 11]

Kuneneratu Pasadakhale

MALAMULO a m’Baibulo anathandiza anthu m’dziko la Israyeli wakale kusangalala ndi moyo wabanja womwe unali wapamwamba kuposa wa mitundu yowazinga. Wolemba mbiri yakale Alfred Edersheim akuthirira ndemanga kuti: “Kungodumpha malire a Israyeli, nkosayenera kuti tizinena kuti kunali moyo wabanja, kapena kunena za banja chabe, monga momwe timalidziŵira.” Mwachitsanzo, pakati pa Aroma akale, lamulo linapatsa mwamuna mphamvu zonse m’banja. Ankatha kugulitsa ana ake monga akapolo, kuwagwiritsa ntchito monga antchito, mwina ngakhale kuwanyonga—popanda chilango kwa iye.

Aroma ena amaona Ayuda monga odabwitsa chifukwa chochita ndi ana awo mwaulemu. Ndipo wolemba mbiri yakale wachiroma wa m’zaka za zana loyamba Tacitus analemba nkhani yosonyeza mmene ankadera Ayuda, akumanena kuti miyambo yawo inali “yoluluzika ndi yonyansa.” Komabe, anatsimikizira kuti: “Kwa iwo ndi mlandu kupha mwana wakhanda aliyense wobadwa kumene.”

Baibulo linapereka malamulo apamwamba. Linaphunzitsa Ayuda kuti ana ngofunika—ndipo ayenera kuonedwa monga mphatso yochokera kwa Mulungu mwini—ndipo anayenera kusamaliridwa bwino. (Salmo 127:3) Mwachionekere ambiri amakhala mogwirizana ndi uphungu umenewo. Ngakhale chilankhulo chawo chimasonyeza zimenezi. Edersheim analemba kuti Kuwonjezera pa liwu lotchulira mwana wamwamuna ndi wamkazi, Chihebri chakale chinali ndi mawu asanu ndi anayi otchulira ana, lililonse losonyeza msinkhu wake wa mwanayo. Mwachitsanzo, panali liwu lotchulira mwana amene akali kuyamwa ndipo lina lotchulira amene waleka. Kwa okulirapo pang’ono, panali lina losonyeza kuti ana amenewa tsopano alimba ndi kukhala amphamvu. Ndipo kwa achinyamata, panali liwu limene kwenikweni limatanthauza kuti ‘wamasuka.’ Edersheim akuthirira ndemanga kuti: “Ndithudi, amene amaonetsetsa moyo wa mwana kufikira popereka maina onena msinkhu uliwonse wa mwana, ayenera kuti amazoloŵerana ndi ana awo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena