Ngale za m’Miyamba ya Afirika
Yosimbidwa ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Kenya
DERA laudzu wokhawokha la m’Afirika nlouma ndi lakatondo, loumikidwa ndi dzuŵa lowotcha. Tikuvutikira kudutsa m’mitengo yoyanganayangana ndi minga.
Ndiyeno mwadzidzidzi, tinangoti chilili, kuima. Titaona kanthu kena kamitundu yoŵala. Kambalame kena kakudzatera panthambi ya mtengo wa acacia, kambalame kamitundu yoŵala zedi ngati kuti dzuŵa lenilenilo lili m’timapiko take. Ngale yamapiko imeneyo imatchedwa moyenerera kuti sunbird (mbalame yadzuŵa).
Magalasi Onyezimira
Pali mitundu yoposa 100 ya mbalame za sunbird. Zambiri za izo zimapezeka m’madera otentha a m’Afirika, ku Asia, ku Australia, ndipo ngakhale kuzilumba za Pacific. Mbalame za sunbird, poti nzokongola komanso zambiri, zimaŵala ndi dzuŵa ngati timagalasi tonyezimira, zimaoneka ngati utawaleza wamitundu yambiri yoŵala: yofiira mosinthasintha, yachikasu, yobiliŵira, ngakhalenso yonga katondo.
Nthaŵi zambiri anthu amakonda kuziyerekezera mbalame za sunbird ndi zina zotchedwa hummingbird, za ku America. Mbalame za sunbird nzofanana ndi za hummingbird, ndipo zimamwa madzi a m’maluŵa. Komabe, izo nzazikulupo kuposa hummingbird ndipo zimaposedwa kuuluka ndi zinzawo za ku North America.
Kaŵirikaŵiri sunbird imayamwa madzi a m’maluŵa itakhala paduŵa penipenipo, ndiye imaloŵetsa mlomo wake wautali koma wopindika, kuti ufike kukhosi kwa duŵalo. Koma ngati duŵalo lili lalitali kwambiri moti mbalameyo yalephera kufikira mkati mwake, imaboola kunsi kwa duŵalo nkuyamwa za mkati mwake zokomazo. Zimadyanso tizilombo timene zimatola m’maluŵa momwemo ndi pazitsamba zapafupi.
Zazimuna zimaimba bwino kwambiri. Zimaimba nyimbo zosiyanasiyana. Ma sunbird onyada a ku East Africa amati “tsip” pomwe ena obiliŵira amchira wofiira amati “tsik-tsik-tsik-tsit-trii-trii-tarrrrr.” Kaŵirikaŵiri, nyimbo zawo nzimene zimathandiza oyang’ana mbalame kuthengo kuzindikira kuti zili pafupi. Komabe, mutangozipeza, sizimasoŵa ngakhale zili m’maudzu akatondo m’dambo la m’Afirika.
Njazintchito Koma Yosachititsa Chidwi
Sunbird yaimuna njosangalatsa kuiona ndi kuimva, koma yaikazi njaing’onoko ndipo si yoŵala kwenikweni. Nchifukwa chake oyang’ana mbalame ndi ojambula zithunzi amainyalanyaza kaŵirikaŵiri. Tingonena kuti iyoyo mungaizindikire kokha ngati ili pafupi ndi yaimuna. Koma ngakhale maonekedwe a mbalame yaikaziyo si osangalatsadi, iyo njazintchito kwambiri.
Nthaŵi zonse yaikaziyo ndiyo imamanga chisa ndipo kwenikweni ndiyo imagwira ntchito yolera ana. Yaikaziyo potanganidwa ndi ntchito za pachisapo, yaimunayo imalonda, itakonzeka kuingitsa chilichonse chimene chingafune kusokoneza.
Zisa Zolenjekeka
Komabe, zisa za ma sunbird si zokongola kwenikweni. Nthaŵi zonse zimangooneka ngati zinyatsi zimene zauluzidwa ndi mphepo nkukaziunjika panthambi yaminga yamtengo wa acacia. Chisa cha sunbird chimakhala ngati sokosi yolenjekeka, chimapangidwa ndi zinyatsi za timitengo, ndiye chimalukidwa nkukulungidwa ndi ukonde wa kangaude. Chisacho, kunja kwake chimakongoletsedwa ndi tizitsotso ta mitengo, zitsamba, ndi ndere pang’ono, ndipo kaŵirikaŵiri pamakhalanso khokho kapena timakoko ta zipatso tiŵiri tosungiramo zakudya, kuwonjezera pazimene tatchulazi.
Chisacho, mkati mwake mumayalidwa masamba opyapyala, udzu wofeŵa, nthenga, ndi zinthu zina zofeŵa. Khomo lake nchiboo chaching’ono kumbali imodzi, chapamwamba pachisacho. Kaŵirikaŵiri yaikaziyo imakhalira yokha mazira. Ngati yakhala m’chisa chake chonga chipatso cha peyala, mlomo wake wautali ndi wopindika umaonekera kunja utatulukira pakhomo la chisacho. Imaikira dzira limodzi kapena aŵiri, ndipo imadzawaswa patatha masiku ngati 14. Pamene anawo akutuluka m’chisacho, amakhala amtundu wosaŵala wofanana ndi wa mayi wawo. Koma pamene ana aamuna akukula, nthenga zawo zimayamba kukongola, moti tsiku lina zimadzazipangitsa kudziŵika monga mbalame za dzuŵa.
Mbalame ya sunbird yangokhala chimodzi mwa zinthu zambiri ndi zosiyanasiyana zimene Mpangi wanzeru analenga. Kukongola kwake ndi nzeru yake yachibadwa zimatithandiza kumdziŵa bwino Mlengi wake. Choncho, mbalame za sunbird ndi zina mwa zimene Baibulo limalamula kuti: “Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, . . . zokwaŵa, ndi mbalame zakuuluka.” “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.” (Salmo 148:7, 10; 150:6) Ngale zimenezi za m’miyamba ya Afirika ziyenera kutisonkhezera kutamanda Mlengi wachikondi amene anazipangayo.