“Kanthu Kena Kapadera”
Mayi wina wazaka 70 wa ku Moscow, ku Russia, ataŵerenga buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, buku limene limasimba chilichonse chimene chinachitika m’moyo wa Yesu padziko lapansi, anati: “Sindinaŵerengepo buku ngati limeneli. Ndikufuna kudziŵa zambiri zokhudza Mulungu ndi Yesu Kristu ndipo ndikufuna ngakhale kuphunzira Baibulo.”
Ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Russia kaŵirikaŵiri imalandira makalata oterowo onena za mabuku osimba za m’Baibulo. Mayi winanso analemba kalata ngati imeneyo, wa ku Chelyabinsk, mzinda wokhala ndi anthu oposa miliyoni imodzi, pamtunda wa pafupifupi makilomita 1,500 kummaŵa cha kummwera kwa Moscow.
Mayiyo, ponena za buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, anati: “Bukulo nkanthu kena kapadera. Limapatsa anthu chiyembekezo cha tsogolo lachimwemwe ndipo limawathandiza kudziŵa mbiri yakale. Ndisanaliŵerenge bukuli, sindinkaganizapo za Mulungu ndipo sindinkakonda chipembedzo, koma tsopano ndikufuna kubatizidwa. Ndikufuna kuwaphunzira mabuku anu kwambiri. Ndikufuna kuti zinthu zimene ndikuphunzirazo ndiziwauza mabwenzi anga, achinansi anga, ndi achibale anga.”
Nanunso mungalandire buku limene lingakuthandizeni kuphunzira zambiri ponena za Yesu ndi zokhudza chiyembekezo chimene Baibulo limanena za moyo m’dziko latsopano. Ngati mungafune kulandira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako kapena mungafune kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, lemberani ku Watch Tower, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena kulembera ku adresi ina yoyenera imene ili patsamba 5.