Agogo “Atsopano”
“Takulandilani kuno kunyumba kwa agogo aamuna ndi aakazi kumene ana amaleredwa mwachisasati inu mukuchita zina.”
Pakhomo la Gene ndi Jane pali mawu amenewo. Koma mutalowa m’kati simupezamo nkhalamba ziŵiri zitakhala pamipando ya ndakhuta gona. Koma m’malo mwake mupezamo banja la anthu omwe adakali ndi mphamvu zawo a m’zaka za m’ma 40. Koma m’malo mwakuti iwo akane kuti si ‘nkhalamba,’ Gene ndi Jane akuvomera mwachimwemwe kuti ndi agogo. Gene anavomera kuti, “kukhala gogo ndi chizindikiro chimodzi m’moyo wa munthu chosonyeza kuti ukukalamba. Imeneyo ndi mphotho yakuti unalera bwino ana ako—adzukulu.”
Mwambi wakale umati: “Zidzukulu ndizo korona wa okalamba.” (Miyambo 17:6) Kaŵirikaŵiri agogo ndi adzukulu amakhala pa ubwenzi wapadera ndipo amakhala ogwirizana kwambiri. Ndipo malinga ndi magazini a Generation, “pali chiŵerengero chachikulu cha anthu omwe ndi agogo pakati pa anthu a ku America kuposa kale lonse.” Chifukwa? “Chifukwa chakuti anthu akukhala ndi moyo nthaŵi yaitali tsopano ndiponso makono kuli chikhalidwe chatsopano,” inatero nkhaniyo. “Chifukwa chakuti ambiri samwalira msanga ndiponso anthu amabalana kwambiri, zidzapangitsa kuti zigawo zitatu mwa zinayi za akuluakulu adzakula n’kukhala agogo . . . Anthu amakhala agogo ali ndi zaka pafupifupi 45.”
M’madera ena agogo akumakhala ndi ntchito ina. Zikunka n’ziwonjezereka kuti ambiri a iwo akugwira ntchito yolera adzukulu awo. Mwachitsanzo, mwana wamwamuna wa Gene ndi Jane ndi mpongozi wawo banja lawo linatha ndipo onse aŵiriwo ali ndi udindo wolera ana. Jane anati, “Timayesa kuthandiza kusamalira mdzukulu wathu pamene mwana wathu wamwamunayo amapita kuntchito.” Malinga ndi ochita kafukufuku, anati agogo mu United States amene amasamalira adzukulu awo pa avareji amagwira ntchito imeneyi maola 14 pamlungu. Pamodzi onse amagwira ntchito yandalama zokwana mabiliyoni 29 pachaka!
Kodi agogo amakono amenewa amakhala ndi chisangalalo chotani? Kodi amakumana ndi mavuto otani? Nkhani zotsatira zinena zimenezo.