Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 7/8 tsamba 28-30
  • Kodi Ndingatani Akamanditonza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Akamanditonza?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Amanyodolera
  • Kupanga Chodzikanira
  • Kulankhula Mosaopa
  • Chikhulupiriro Choyesedwa Ndicho Chikhulupiriro Cholimba
  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Achinyamatanu—Yehova Sadzaiŵala Ntchto Yanu!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Ndingalalikire Bwanji Anzanga a Kusukulu?
    Galamukani!—2002
  • N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kuuza Anzanga Akusukulu Zimene Ndimakhu Lupirira?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 7/8 tsamba 28-30

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingatani Akamanditonza?

ACHINYAMATA amene amachita zinthu kapena kuvala mosiyana ndi anzawo angatonzedwe mwankhalwe. Zimenezi zimachitika makamaka kwa achinyamata achikristu amene makhalidwe awo kaŵirikaŵiri amakhala osiyana kwambiri ndi achinyamata anzawo. Kodi Kristu sananene za otsatira ake oona kuti: “Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso”?—Yohane 15:20.

Kodi zimenezi zimakhudza motani achinyamata amene ndi Mboni za Yehova? Ena a iwo amanyodoledwa chifukwa chosakondwerera nawo maholide ena; ena amatsutsidwa chifukwa chosachitira nawo suluti mbendera. Ambiri azunzidwa chifukwa chokana kumwa mankhwala ozunguza bongo, chifukwa cha kukhala kwawo okhulupirika, ndiponso chifukwa cha kumamatira kwawo miyezo ya Baibulo ya makhalidwe abwino.

Zinthu ngati zimenezi sizachilendo. Inde, mtumwi Petro anauza Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti: “M’menemo ayesa n’chachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano.” (1 Petro 4:4) Matembenuzidwe ena amanena kuti, “nakutchulani mayina amwano” (Knox) kapenanso, “nakunyozani.”—Today’s English Version.

Kodi mudanyodoledwapo chifukwa cha chipembedzo chanu? Ngati inde, limbikani mtima. Simuli nokha! Ndiponso mudzakhala wokondwa kudziŵa kuti mungaphunzire momwe mungachitire ndi chipsinjo cha kunyodoledwa chifukwa cha chikhulupiriro chanu.

Chimene Amanyodolera

N’chifukwa chiyani anthu ena amaseka anzawo amene ali ndi chikhulupiriro kapena makhalidwe osiyana ndi awo? Nthaŵi zina onyodola ameneŵa—mofanana ndi ozunza anzawo—amakhala ndi mantha ena ake. Angakunyazitseni pagulu kuti aoneke kukhala ochangamuka kwa anzawo. Mwachiwonekere, pamene ali okha ndi ochepa chabe amene angafune kuchita zimenezo—kapena amene angalimbe mtima kuti akunyozeni pamaso ndi pamaso.

Komanso, onyodola ena satha kumvetsa, monga momwe Petro analembera, chimakhala, “chachilendo.” Inde, iwo amadabwadi poona makhalidwe anu. Mwachitsanzo, ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, iwo angaganizedi moona mtima kuti n’zachilendo ndiponso zodabwitsa pamene aona kuti inu simuchita nawo kapena kutenga mbali pa zochitika za maholide ena. Mwina otsutsa angakhale atawauza zabodza ponena za Mboni.

Mulimonse mmene zingakhalire, pamene wina akulankhulani mawu achipongwe, mungavomereze zimene mwambi wa Baibulo umanena: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” (Miyambo 12:18) Koma kumbukirani kuti amene akulankhulani motere, sikuti amatero chifukwa amakudani. Kwenikweni, iwo amachita zimenezi mogwirizana ndi zimene mwambi wa Baibulo umanena—“wonena mwansontho.”

Komabe, kunyodoledwa kungakhale kopweteka monga ngati chilonda cha kubaidwa. Pamenepo mungalakelake kuika pambali chikhulupiriro chanu kuti muthane ndi chipongwecho. Koma kodi mungatani pamene mutonzedwa chifukwa cha chikhulupiriro chanu?

Kupanga Chodzikanira

Mtumwi Petro analangiza Akristu: Kukhala okonzeka nthaŵi zonse “kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Kupanga chodzikanira chotere kumafunikira chidziŵitso cholongosoka ndiponso kuzindikira zifukwa zokhalira ndi chikhulupiriro chanucho.

Komanso, muyenera kudziŵa mmene mungalankhulire kwa ena ndi “mantha” kapenanso monga momwe The Bible in Basic English imanenera, “mosadzitukumula.” Chidziŵitso chanu cha Baibulo ndi ziphunzitso zake siziyenera kukupangitsani kukhala odzikweza kwa ena. Mosiyanako, muyenera kuyesetsa kukhala ndi maganizo monga a mtumwi Paulo amene analemba ponena za utumiki wake kuti: “Ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.”—1 Akorinto 9:19.

Ngati mukuona kuti mukuchita mantha kupanga chodzikanira pa chikhulupiriro chanu, musataye mtima. Mboni zachinyamata zambiri zamva mofananamo. “Pamene ndinali pa sukulu ya pulayimale,” akutero Jamal, “sindimadziŵa kufotokozera ena za zifukwa zimene sindikondwerera nawo maholide ena kapenanso kuchitira suluti mbendera ngakhalenso chifukwa chimene ndimachitira ulaliki wa khomo ndi khomo.” Kodi chinam’thandiza n’chiyani? “Abambo anga anapitiriza kundithandiza mpaka ndinadziŵa kulongosola zinthu zimenezi, ndipo izi zinapangitsa kusintha kwakukulu m’moyo wanga.” Choncho ngati zimakuvutani kufotokozera ena za chikhulupiriro chanu, mwinamwake mungapemphe chithandizo cha makolo kapena cha abale ena achidziŵitso mumpingo wachikristu kuti akuthandizeni kuzindikira bwino lomwe chidziŵitso cha Mulungu.—Aefeso 3:17-19.

Mboni yachinyamata ya zaka 16 zakubadwa inanena kuti pologalamu ya phunziro laumwini la Baibulo inam’thandiza kulimba mtima polankhula mosaopa kusukulu. “Kale, pamene anzanga a m’kalasi ankandinyazitsa chifukwa choti ndine Mboni, ndimasoŵa choti ndinene,” iye akuvomereza motero. “Tsopano, monga mlaliki wa nthaŵi zonse, ndimaphunzira Baibulo kwambiri, ndipo ndimatha kuyankha ondinyodolawo. Kuŵerenga mosaphonya nkhani zatsopano za m’makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimandithandiza kulankhula za chikhulupiriro changa kwa anzanga a kusukulu.”

Zoonadi, mikhalidwe singafanane. Zochitika zosiyanasiyana mwachiwonekere zidzafunanso mayankho osiyanasiyananso. Komabe, pamene mwaputidwa ndi mawu onyoza sibwino kubwezera “choipa chosinthana ndi choipa.” (Aroma 12:17-21) Kubwezera mawu achipongwe, ngakhale kungaoneke kukhala kwanzeru, kumangowonjezera mkwiyo ndi kuti mwinamwake kuchita motero kungalimbikitsenso chitonzo chowonjezereka. Choncho, ena aona kukhala kwanzeru kungonyalanyaza chitonzocho.

Nthaŵi zina, mawuwo angamveke ngati nthabwala chabe, kungakhale kwanzeru kungoseka naye kusiyana ndi kukwiya ndi mawuwo. (Mlaliki 7:9) Ngati wotonzayo aona kuti mawu ake sakukukhudzani kwenikweni angaganize zongosiya chitonzocho.—Yerekezani ndi Miyambo 24:29; 1 Petro 2:23.

Kulankhula Mosaopa

Komabe, nthaŵi zina, pamene kuli kofunika, tingapereke mafotokozedwe achidule ndi aluso pa za chikhulupiriro chathu. Mtsikana wina wa zaka 13 zakubadwa anayesa zimenezi ndipo zinali ndi zotulukapo zabwino. “Panali pamene ndinali kuyenda kupita ku kalasi yanga,” iye anatero, “pamene ophunzira ambirimbiri anayamba kunyodola Mboni za Yehova. Ndinalakalaka kuti ndiyankhe, koma iwo anangodutsa ndi kupitiriza kundiseka—m’modzi wa iwo sanachite nawo zachipongwezo.” Wophunzira yemwe ndi Mboni ameneyu akulongosola kuti: “Mtsikanayo yemwe dzina lake ndi Jaimee anandicheukira nandiuza kuti iye ali ndi buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.a Iye anapitiriza kuti waŵerenga kale mbali yaikulu ya bukuli ndipo kuti amafuna kudziŵa zochuluka ponena za chikhulupiriro chathu. Ndinayambitsa phunziro la Baibulo kwa Jaimee.” Polimbikitsidwa ndi chokumana nacho chakechi, Mboni yachinyamatayi inayamba kulankhula ndi achinyamata anzake za chikhulupiriro chake. “Ndinali kuchezera nthaŵi zonse ophunzira anzanga anayi amene anasonyeza chidwi ndiponso amene ndili otsimikiza kuti posachedwapa ndidzayamba kuphunzira nawo,” Iye anatero.

Zaka zingapo zapitazo wophunzira wa ku Liberia, dziko la mu Africa, anali ndi chokumana nacho chofananacho. Panthaŵi ya phunziro la sociology, iye anafotokoza modzichepetsa kuti monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iye amakhulupirira chilengedwe osati chisinthiko. Poyamba, ophunzira ambiri anatsutsa kwambiri za lingaliro limeneli. Koma mphunzitsi wawo anam’lola kuti afotokoze za chikhulupiriro chake kwa kalasi yonse, pambuyo pake mphunzitsiyo anawombola buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?b

Pambuyo pa kuŵerenga bukulo, mphunzitsiyo anauza ophunzira a m’kalasimo kuti: “Buku ili lilibe lolingana nalo. Ndi limodzi mwa mabuku abwino koposa asayansi onena za chilengedwe amene ndaŵerengapo.” Ndiyeno mphunzitsiyo anafotokoza kuti ali kukonzekera kugwiritsa ntchito bukulo pamodzi ndi mabuku ena kwa matemu ena aŵiri, ndipo analimbikitsa wophunzira aliyense kupeza makope a bukulo kwa ophunzira wa Mboni uja. Mabuku ambiri anagaŵiridwa, ndipo ophunzira ambiri anasintha kaonedwe kawo ponena za Mboni za Yehova!

Chikhulupiriro Choyesedwa Ndicho Chikhulupiriro Cholimba

N’zoona kuti nthaŵi zina mungachite mantha poona unyinji wa awo amene sagwirizana nanu pa chikhulupiriro chanu chochokera m’Baibulo. (Yerekezani ndi Salmo 3:1, 2.) Choncho, ndichanzeru kufunafuna mabwenzi pakati pa awo amene mumagwirizana m’chikhulupiriro. (Miyambo 27:17) Komabe bwanji ngati pasukulu yanu kapena kumalo amene mukukhalapo kulibe achinyamata a chikhulupiriro chanu?

Ngati umu ndi mmene zinthu ziliri, kumbukirani kuti Bwenzi lanu lalikulu koposa ndi Yehova Mulungu, ndipo iye adzakuchirikizani. Iye wapirira chitonzo chachikulu cha Satana Mdyerekezi kwa zaka zikwi zambiri. Chotero, tingatsimikize kuti Yehova amakhala wokondwa m’mtima mwake pamene aona ife tikuima chilili pa chikhulupiriro chathu. Kachitidwe koteroko kamapatsa mwayi iye ‘kuyankha Satana, amene amam’tonza.’—Miyambo 27:11.

N’chinthu choyembekezeka kuti nthaŵi ndi nthaŵi chikhulupiriro chanu chidzayesedwa. (2 Timoteo 3:12) Komabe, mtumwi Petro akutitsimikizira kuti mayesedwe a chikhulupiriro chathu ndiwo “amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto.” (1 Petro 1:7) Choncho, pamene munyozedwa chifukwa cha chikhulupiriro chanu, onani kuti umenewo ndi mwayi wanu wa kulimbitsa chikhulupiriro chanucho ndinso kusonyeza chipiriro chanu. Mtumwi Paulo analemba kuti chipiriro chichita “chizoloŵezi.” (Aroma 5:3-5) Inde, chifuno cha kupeza chiyanjo cha Yehova chimapereka chisonkhezero champhamvu kwa inu kuti mupirire pamene mutonzedwa chifukwa cha chikhulupiriro chanu!

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 29]

Kodi mungapange chodzikanira pa chikhulupiriro chanu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena