Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 7/8 tsamba 31
  • Mbewu Zimene Zinabala Zipatso Patapita Zaka Zambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbewu Zimene Zinabala Zipatso Patapita Zaka Zambiri
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto ndi Madalitso a Kulera Ana Asanu ndi Aŵiri
    Galamukani!—1999
  • Kuyandikira kwa Mulungu Kunandithandiza Kulaka
    Galamukani!—1993
  • Ndikuthokoza Yehova Kaamba ka Ana Anga Aamuna Asanu
    Galamukani!—1999
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 7/8 tsamba 31

Mbewu Zimene Zinabala Zipatso Patapita Zaka Zambiri

Kalata yotsatirayi, inalandiridwa kuchokera kwa munthu wina chifukwa chakuti anaŵerenga nkhani yakuti “Mavuto ndi Madalitso a Kulera Ana Asanu ndi Aŵiri,” mu Galamukani! ya January 8, 1999.

Okondedwa Mbale ndi Mlongo Dickman,

Ndangotsiriza kumene kuŵerenga nkhani yanu, ndipo ndaganiza kuti ndikulembereni kalata. Banja lanu ndinali kulidziŵa zaka zambiri zapitazo ku Mississippi [1960-61]. Ndingoti ndinali kupita kusukulu ndi ana anu, ndipo ndinali kubwera kunyumba kwanu kudzacheza ndi anyamatawo kaŵirikaŵiri ndithu. Koma zimenezo sindizo zinthu zimene zinakhazikika kwambiri pamaganizo anga ndidakali wamng’ono ayi. Ngakhale ndinali wamng’ono choncho, chimene chinali kundichititsa chidwi chinali chakuti anyamatawo anali kukana kuchitira sawatcha mbendera kusukulu, chifukwa chikumbumtima chawo chachikristu chinali kuwaletsa zimenezo. Ngakhale kuti ndinali wa Tchalitchi cha Grandview Baptist, pamene mnyamata wanu wina anandifotokozera kaimidwe kake, ndinadziŵa kuti anali kunena zoona.

Wina anandipatsa buku lotchedwa Kuchokera ku Paradaiso Wotayika Kumka ku Paradaiso Wopezedwanso, a kapena mwina ndinaliba. Sindikukumbukira bwino kuti ndinalitenga bwanji, koma ndinaliŵerenga lonse. Nthaŵi imeneyo, ndimangoliona ngati buku lokongola wamba la nthano basi. Sindinadziŵe kuti mbewu za choonadi zinali zitadzalidwa zimene zidzakhala zaka zambiri zisanamere.

Banja lathu linasamukira Kumpoto mu 1964, ndipo ine ndinasiya kupita kutchalitchi. Chinyengo cha chipembedzo chinandikhumudwitsa, choncho kwa zaka zambiri sindinali kufunanso kumva za chipembedzo.

Patapita zaka, ndinayamba kuganiza kwambiri za cholinga cha moyo, mpamene ndinaona kuti ndinali kufuna kukhala ndi unansi ndi Mlengi. Ndinafuna unansi umenewo koma popanda chinyengo cha chipembedzo. Mbewu zija zimene zinadzalidwa zaka zambiri zapitazo zinayamba kumera; koma ndinali ndisanadziŵe zimenezo.

Ndinali kuganiza kwambiri za mfundo yakuti sindinali kufuna kukakhala kumwamba; ndinali kufuna kukhala pompano padziko lapansi. Ndinali kuona kuti pulaneti lino n’lokongola ndithu, ndiye Mulungu angaliwonongerenji? Sindinali kuganizanso zakuti Yesu ndiye Mulungu. Ngati anali Mulungu, ndiye kuti nsembe yake inali yachinyengo. Maganizo ndi zikhulupiriro zimenezi, ngati mungazitchedi zikhulupiriro, ndinaona kuti zinali zosiyana kotheratu ndi zimene ndinaphunzira ku Tchalitchi cha Baptist. Ndiyeno ndinayamba kupemphera, kupemphera kwenikweni ndithu, ndipo Yehova anachitapo kanthu msanga. Mboni zinafika pakhomo panga patangopita masiku oŵerengeka, ndipo anayamba nane phunziro la Baibulo nthaŵi yomweyo. Ngakhale kuti ndinali ndisanaonanepo ndi Mboni za Yehova kuyambira pamene ndinadziŵana ndi banja lanu kufikira pamene ndinayamba kuphunzira, sindinasiye kuwalemekeza ana anuwo chifukwa cha kulimba mtima kwawo polimbikira kuchita zabwino. Pamene ndinangoyamba kuphunzira n’kuyamba kupeza chidziŵitso, chilichonse chinayamba kumveka bwino tsopano. Zinanditengera chaka chimodzi ndi theka kuti ndiwongolere moyo wanga. Ndinadzabatizidwa mu 1975.

Nthaŵi zonse tikamaphunzira nkhani za mmene khalidwe lathu lingaperekere umboni ngakhale kuti eni akefe sitikudziŵa n’komwe, ndimakumbukira banja lanu. Tikamaphunzira za kufunika kwa kufesa mbewu zambiri za Ufumu chifukwa sitidziŵa kuti zimera kuti kapena liti, ndikudziŵa kuti n’zoona, chifukwa ineyo zandichitikira zimenezo.

Ndikukuyamikirani chifukwa ndinu anthu a Yehova ndiponso kuti munasungabe chikhulupiriro chanu masiku amene aja. Munathandiza wina kupeza choonadi eni akenu musakudziŵa. Khalidwe lanu ndi chikhulupiriro chanu, ndi khalidwe la ana anu, linali kuŵalitsa choonadi. Sindinali kuganiza kuti ndidzadziŵa kumene muli, kapena kuti ndidzakhoza kukuthokozani. Zikomo kwambiri kachiŵirinso.

Landirani moni wanga wachikristu,

L. O.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mu 1958; tsopano silikusindikizidwanso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena