Galamukani! Ithandiza Kujambula Chikwangwani Choletsa Kusuta Fodya
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY
POSACHEDWAPA, mumzinda wa Mortara kumpoto kwa Italy, gulu lolimbana ndi matenda a kansa lotchedwa Italian Anticancer League pamodzi ndi a nyuzipepala inayake anakonza mpikisano wa ana akusekondale kuti ajambule chikwangwani choletsa kusuta fodya. Mtsikana wina wa Mboni za Yehova wazaka 14 wotchedwa Simona, anaŵerenga nkhani zosiyanasiyana za mu Galamukani! kuti apezemo chidziŵitso chokhudza kuopsa kwa fodya, kwenikweni anaŵerenga nkhani zopezeka m’magazini ya July 8, 1989 ndi June 8, 1995. Simona akulemba kuti: “Pamene ndinali kufunafuna nkhani zoterezi, ndinachita chidwi kwambiri nditaona zikuto za magazini ameneŵa. Ndinajambula chigaza cha mutu wa munthu chili ndi ndudu ya fodya pakamwa pake chonga chimene ndinaona mu Galamukani!, mawu amene anali pa chikuto pake anandithandiza kuganiza za mutu wa nkhani yanga.” Mutu wake unali wakuti, “Fodya—Amapha Mamiliyoni a Anthu kuti Apange Mamiliyoni” Chikwangwani chake chinali chimodzi mwa zikwangwani 250 zimene zinaloŵa nawo mu mpikisanowo.
Ngakhale kuti Simona anali wamng’ono kuyerekeza ndi ana asukulu anzake amene anachita nawo mpikisanawo, iye ndi amene anapatsidwa mphotho yoyamba, pamodzinso ndi ndalama zokwanira $300 zomulipirira sukulu. Simona analemba kalata ku nthambi ya Watch Tower Society kuti athokoze kaamba ka nkhani zofufuzidwa bwino za m’Galamukani! Iye amakonda kuŵerenga Galamukani! osati kokha chifukwa cha zikuto zake komanso chifukwa cha nkhani zake zokhudza thanzi, zinthu zimene zikuchitika, ndi mavuto amene achinyamata akupeza. Nkhani zimenezi zimabwera panthaŵi imene zikufunika komanso n’zothandiza. Iye anamaliza kalata yake motere: “Mawu omaliza: Pitirizani ntchito yanu yabwino!”
Ngati mungafune kumva zambiri pa nkhani zina zokhudza Akristu, chonde pezani Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena tumizani kabokosi aka mutalembamo zofunika.
□ Nditumizireni bolosha yakuti “Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?”
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.