Mutu 8
Kodi Ndani Amene Adzakhala Opulumuka?
1. (a) Kodi kupulumuka kulowa m’Dongosolo Latsopano lamtendere la Mulungu kudzadalira pa chiyani? (b) Kodi ndimotani mmene Chivumbulutso 7 chimalongosolera awo amene adzapulumuka kukhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi?
KUPULUMUKA chiwonongeko cha dziko chikudzacho sikudzakhala kongochitika mwamwaŵi, monga momwe zimachitikira kaŵirikaŵiri m’nkhondo za anthu. Sikudzatsimikiziridwa ndi kumene munthu akukhala, ndiponso sikudzachitika mwa kupita kwake msanga kumalo ena obisalira bomba kapena malo ena othawirako belo lachenjezo litamveka. Kupulumuka kudzadalira pa chifundo cha Mulungu limodzi ndi chosankha chimene munthu aliyense apanga “chisautso chachikulu” chisanayambe. Kodi ndimotani mmene mumapangira chosankha chimene chidzakuikani pakati pa opulumuka kukhala pa dziko lapansi m’Dongosolo Latsopano la paradaiso, lamtendere la Mulungu?—Chivumbulutso 7:9, 10, 14, 15.
2. Kodi ndani amene amakhazikitsa miyezo yopulumukira, ndipo kodi imeneyi ikupezeka kuti?
2 Baibulo silimaneneratu kokha kuti padzakhala opulumuka chiwonongeko cha dziko chirinkudza. Limaperekanso chitsanzo chotithandiza kudziwa mtundu wa anthu amene iwo adzakhala. Popeza kuti Mulungu akupangitsa kupulumuka kukhala kothekera, ali iye amene moyenerera amapereka miyezo.
3. Kuti pakhale mtendere ndi chisungiko, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti ochita zoipa adulidwe?
3 Mulungu mwanzeru ndi molungama adzatsimikizira kuti opulumuka ali anthu amene adzakhala ochita bwino m’Dongosolo lake Latsopano, osati awo amene adzagwirira ntchito kuliipitsa. Ngati iye alola anthu osalungama kupulumuka, sikukanakhala mtendere ndi chisungiko kwa olungama. Nyumba zawo ndi chisungiko chawo zikanakhalabe paupandu. Koma Baibulo limalonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwoŵa adzalandira dziko lapansi.” Kokha mwa kugwiritsira ntchito kwa Mulungu muyezo umenewo, monga momwe waperekedwera pa Salmo 37:9-11, ndipamene opulumuka adzakhala okhoza ‘kukondwera nawo mtendere wochuluka.’ Mmene Mulungu adzachitira chimenechi kukuwonedwa m’zochitika zakale pamene anthu oipa anachititsa Mulungu kudzetsa chiwonongeko.
Zitsanzo Zakale za Kupulumuka
4-6. (a) Kodi nchiyani chimene chimachitira umboni kuti chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chiri chenicheni chotsimikizirika? (b) Kodi nchifukwa ninji chiwonongekocho chinadza? (c) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kukhala kothekera kwa ophunzira a Yesu kupulumuka?
4 M’mzinda wa Roma lerolino mukali chipata cha chikumbukiro cha m’zaka za zana loyamba za Nyengo Ino, chotchedwa Chipata cha Tito. Pa chimenechi pajambulidwa kutengedwa kwa zinthu m’kachisi m’Yerusalemu pambuyo pa kuwonongedwa kwa mu 70 C.E. Chifukwa chake chiwonongekocho chiri chenicheni ndi chotsimikizirika. Chotsimikizirika mofananamo ndicho chenicheni chakuti zaka makumi angapo chiwonongekocho chisanachitike, Yesu anali ataneneratu ponse paŵiri kudza kwake ndi mmene anthu akapulumukira.
5 Anthu Achiyuda anali atabwevukira Mulungu kutsatira anthu ndi miyambo ya chipembedzo yopangidwa ndi anthu. (Mateyu 15:3-9) Iwo anaika chidaliro chawo mwa olamulira andale za dziko aumunthu mmalo mwa Ufumu wolonjezedwa wa Mulungu. (Yohane 19:15) Iwo anapita patali kwambiri kufikira pamfundo ya kukana ndi kutsutsa chowonadi cholengezedwa ndi Mwana wa Mulungu ndi atumwi ake. Yesu anachenjeza zotulukapo zimene njira yotero ikabweretsa.—Mateyu 23:37, 38; 24:1, 2.
6 Zotulukapo zake zinali ndendende monga momwe zinanenedweratu. M’chaka cha 66 C.E., Ayuda anapandukira Roma. Chiukiro choyambirira pa Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma chinatsatiridwa ndi kubwerera kwawo m’mbuyo kosayembekezereka. Kumeneku kunali chizindikiro ndi mwaŵi kwa awo okhulupirira Yesu kuchita zimene anali atanena: Thawani—tulukani m’mzinda woyembekezera kuwonongedwawo ndi m’chigawo chonse cha Yudeya, mosasamala kanthu za zimene zingasiyidwe m’mbuyo. Ophunzira owona a Yesu anachita zimenezo kumene. Pamenepo, m’chaka cha 70 C.E., Aroma anabwerera ndipo, pambuyo pa kuzinga, anawononga Yerusalemu ndi awo amene analephera kumvetsera. Mboni yowona ndi maso, wolemba mbiri Wachiyuda Josephus, akunena kuti anthu 1 100 000 m’Yerusalemu anafa ndi njala, nthenda, kumenyana kwa chiweniweni, kapena lupanga la Aroma. Komabe Akristu amene anachitapo kanthu motsimikizira anathawa.—Luka 19:28, 41-44; 21:20-24; Mateyu 24:15-18.
7. Kodi anthu anafunikira kuchitanji kuti apulumuke pamene Babulo anawonga mtundu wa Israyeli?
7 Mkhalidwe wofanana unafunga pafupifupi zaka mazana asanu ndi awiri ichi chisanachitike pamene Mulungu analola magulu ankhondo a Babulo motsogozedwa ndi Mfumu Nebukadinezara (II) kuwononga mtundu wa Israyeli. Chiwonongeko chimenecho, nachonso, chiri mbiri yotsimikizirika. Chifukwa chakuti zaka zambiri icho chisanachitike, Mulungu kupyolera mwa aneneri ake anali atachenjeza anthu akugwa pachikhulupiriro kuti njira yawo inali kutsogolera kuchiwonongeko. “Bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferanji?” chinali chiitano cha Mulungu kwa iwo. (Ezekieli 33:11) Unyinji sunakhulupirire chenjezolo, ndipo ngakhale pamene magulu ankhondo a Babulo anazinga Yerusalemu, Aisrayeli amenewo anapitirizabe kuyembekezera kuti palibe chiwonongeko chimene chikadza. Komabe chinachitika monga momwedi kunanenedweratu. Komabe Mulungu anatsimikizira kuti awo amene anasonyeza chikhulupiriro chawo mwa kumvera anapulumuka.—Yeremiya 39:15-18; Zefaniya 2:2, 3.
8-10. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova anadzetsa chiwonongeko cha dziko lonse m’masiku a Nowa? (b) Kodi nchifukwa ninji Nowa ndi banja lake anapulumutsidwa?
8 Kalekale m’mbiri ya anthu, tikupeza kusonyezedwa koyambirira kwambiri kwa chitsanzo chaumulungu cha kupulumuka. Chikulowetsamo, osati chiwonongeko cha mtundu umodzi, koma chiwonongeko cha dziko lonse. Ndipo chimenecho nachonso chiri chenicheni cham’mbiri, chophatikizapo Chigumula cha dziko lonse mkati mwa zakazo 2370/2369 B.C.E., m’masiku a Nowa. Ponena za mikhalidwe imene inalipo chiwonongeko cha dziko lonse chimenecho chisanachitike, Baibulo limati: “Ndipo anawona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse zamaganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.”—Genesis 6:5, 11.
9 Kuipa ndi chiwawa zinachititsa Mulungu kuchitapo kanthu. Nowa yekha ndi banja lake anasonyeza chikhulupiriro ndi kumvera. Mwachifundo kwa iwo, ndi kusungabe chiweruzo cholungama ndi chilungamo padziko lapansi, Yehova Mulungu “sanalekerera [osalanga] dziko lapansi lakale . . . la osapembedza.” Chotulukapo chinali chakuti “dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.”—2 Petro 2:5; 3:5-7.
10 Komabe Nowa ndi banja lake anapulumuka. Chifukwa ninji? Choyamba, iwo sanagwirizane ndi ‘dziko la anthu osapembedza’ limenelo m’kuipa kwawo. Iwo sanadzichititse kukhala otanganitsidwa kwambiri ndi zinthu wamba za moyo, kudya, kumwa ndi ukwati, kwakuti anakhala osazindikira chifuniro cha Mulungu kapena osamva chenjezo lake. Nowa ‘anayenda ndi Mulungu’ m’chilungamo. Chimenechi sichinatanthauze kuti iye ndi banja lake anangopewa kuchita machitidwe oipa. Mmalo mwake, iwo anachitapo kanthu motsimikizirika kuchita cholungama. Iwo anakhulupiriradi zimene Mulungu ananena, ndipo anakusonyeza mwa kukhoma chingalawa chachikulu chautali woposa mapazi 400. Nowa anachitanso motsimikizirika m’kukhala “mlaliki wa chilungamo,” akumauza ena za zifuno za Mulungu, kuchirikiza njira ya chilungamo.—Genesis 6:9, 13-16; Mateyu 24:37-39; Ahebri 11:7.
11. Monga momwe kwasonyezedwera ndi zitsanzo zochenjeza zimenezi, kodi tiyenera kuchitanji ngati titi tipulumuke chiwonongeko cha dziko lonse chikudzacho?
11 Anthu asanu ndi atatu amenewa anapulumuka chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndi ntchito zochokera m’chikhulupiriro. Yesu ndi atumwi ake anasonya ku chiwonongeko cha dziko chimenecho kukhala cholosera cha chimene chikuyang’anizana ndi anthu mu “nthawi ya mapeto” ino. Chotero kuli kowonekera bwino kuti nafenso tiyenera kudzilekanitsa ndi dziko lomka ku chiwonongeko, monga momwedi Nowa ndi banja lake analiri. Nafenso tiyenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Sitingatsogozedwe ndi miyezo yathu chabe ndi kuyembekezera kupulumuka. Mawu a Mulungu amati: “Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yowongoka, koma matsiriziro ake ndinjira ya imfa.” (Miyambo 16:25) Ndiponso kawonekedwe ka chilungamo cha kunja kokha sikadzadzetsa chipulumutso. Pakuti Yehova Mulungu amawona chimene chiri m’mtima.—Miyambo 24:12; Luka 16:15.
Chimene Yehova Akufuna m’Mitima ya Anthu
12, 13. (a) Kodi ndimikhalidwe yotani imene imachititsa anthu kufuna kusintha? (b) Kodi nchifukwa ninji kumeneku sikuli kokwanira kutsimikiziritsa kupulumuka kwawo kulowa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu? (c) Kuti tikhale pakati pa opulumuka, kodi nchiyani chimene chiyenera kusonkhezera kumva kwathu chisoni ndi mikhalidwe yoipa imene iripoyi?
12 Ambiri ali osakondwera ndi mikhalidwe iripoyi, ndipo amasonyeza kumeneko mwa madandaulo, ziwonetsero zosonyeza kusakondwa, ndipo m’maiko ena mwa chipanduko cha chiwawa. Ambiri amaipidwa ndi kukwera kwa misonkho ndi kukwerakwera kwa mitengo ya zakudya. Iwo amadandaula ndi ngozi yaupandu. Mantha amawachititsa kufuna kusintha. Koma, kodi izi nzokwanira kutsimikizira kupulumuka kwawo kulowa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu? Ayi, siziri. Chifukwa ninji siziri choncho?
13 Chifukwa chakuti munthu angakhale wosakondwera ndi mikhalidwe imeneyi ndi kukhalabe wadyera. Iye angavomerezedi mipangidwe ina ya kusawona mtima ndi chisembwere—malinga ngati iyemwini sakuvutika. Komabe, anthu owongoka mtima amawona zinthu mosiyana. Pamene aphunzira Baibulo amawona kuti mikhalidwe yoipa iri kokha umboni wakunja wautenda weniweni wa dzikoli. Iwo amazindikira kuti kutseri kwa zizindikiro zimenezi kuli kusadera nkhawa za kudziŵa ndi kuchita chifuniro cha Yehova ndi kusakhala ndi moyo mwa miyezo yake yolungama. Chifukwa chake, iwo saali kwakukulukulu achisoni ndi chisalungamo, upandu, kuipitsidwa kwa malo, kapena chiwopsezo cha nkhondo. Mmalo mwake, anthu owona mtima amenewo amamva chisoni kwakukulukulu powona dzina la Mulungu likuchitiridwa mwano ndi njira yoipa ya anthu. Ndipo iwo akumva chisoni kuti ena, osati kokha iwo okha, akuvutika kwambiri monga chotulukapo.
14. Kodi ndani amene ‘anaikidwa chizindikiro’ cha kupulumuka panthawi ya chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Babulo?
14 Kuti tipulumuke chiwonongeko cha dziko chimene chirinkudza, tiyenera kukhala ofanana ndi awo amene anapulumutsidwa pamene Babulo anawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., anthu olongosoledwa kukhala “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa” zimene zinali kuchitidwa mu mzindawu. (Ezekieli 9:4) Mikhalidwe inali “yonyansa” m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, osauka anali kutsenderezedwa, ena anali kuikidwa mu ukapolo ndi anthu anzawo mosagwirizana ndi lamulo. (Yeremiya 34:13-16) Mkhalidwe wa makhalidwe abwino wa ufumu wa Yuda unali utafikira pa kuipa kwambiri kuposa ufumu wakumpoto wa Israyeli, umene poyambirira unalongosoledwa ndi mneneri Hoseya kuti: “[Pali] kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba . . . ndi mwazi kukhudzana nawo mwazi.” (Hoseya 4:2; Ezekieli 16:2, 51) Awo okha amene anamva chisoni m’mtima chifukwa cha chisalungamo chotero ndi kupanda ulemu kumeneko zosonyezedwa kwa Mulungu ‘anaikidwa chizindikiro’ cha kupulumuka.—Ezekieli 9:3-6.
15. Kodi nchiyani chimene chimalepheretsa anthu ena kupanga masinthidwe ofunikawo kuti apulumuke chiwonongeko cha dziko chimene chirinkudza?
15 Ngakhale kuli kwakuti ambiri lerolino angafune kusangalala ndi moyo padziko lapansi kosatha m’mtendere, molemerera ndi muubwino, iwo samafuna kupanga masinthidwe m’njira yawo ya moyo imene kuphunzira ndi kutsatira chitsanzo Chabaibulo kaamba ka moyo wolungama zingabweretse. Pansi pa mtima wawo, samakondadi chilungamo kapena kudera nkhawa kowona mtima ndi anthu anzawo. Popeza kuti Dongosolo Latsopano la Mulungu lidzatulutsa chitaganya chatsopano m’chimene ‘mudzakhala chilungamo,’ mbiri yabwino yonena za dongosolo idzakondweretsa kokha awo amene amakonda chilungamo. Ena amawona kukhala kutsutsidwa nayo.—2 Petro 3:13; 2 Akorinto 2:14-17.
Chimene Mungachite Tsopano
16-18. (a) Kodi ndimotani mmene munthu amakhalira ‘wolembedwa chizindikiro’ cha kupulumuka? (b) Ponena za kulambira konyenga, kodi ndi kachitidwe kotani kamene ayenera kuchita ponena za kulambira konyenga, ndiyeno ponena za kulambira kowona? (c) Kodi ndimotani mmene ayenera kuwonera magulu andale zadziko monga ngati UN?
16 Yehova adzapulumutsa awo okha amene mowona mtima akufuna kukhala ndi moyo mu ulamuliro wake wolungama. Iye sadzaumiriza aliyense kukhala ndi moyo panthawiyo m’mikhalidwe imene iwo eni sakuifuna. Chifukwa chake, opulumutsidwawo adzafunikira kutsimikizira kuvomereza kwawo kowona ulamuliro wake waumulungu tsopano. Amafikira kukhala ‘olembedwa chizindikiro’ cha kupulumuka mwa kuvala “umunthu watsopano” Wachikristu, kugwirizanitsa miyoyo yawo ndi njira za Mulungu ndi kupereka umboni wakuti ali ophunzira a Mwana wa Mulungu. Mwakutero iwo “amasankha moyo” ndi madalitso, osati imfa. (Akolose 3:5-10, NW; Deuteronomo 30:15, 16, 19) Kodi inu mudzasankha chiyani?
17 Chosankha chanu chimalowetsamo kugonjera kwa Mulungu m’kulambira. Yesu anati: “Ora lirinkudza, ndipo liripo tsopano pamene olambira owona adzalambira Atate ndi mzimu ndi chowonadi, pakuti, ndithudi, Atate ali kufunafuna anthu otero kumlambira.” (Yohane 4:23, NW) Chifukwa cha chimenecho kupulumuka chiwonongeko cha dziko lonse chikudzacho kumafunikiritsa kuti munthuyo asiye kulambira konse konyenga ndi kukhala ndi phande m’kulambira kowona. Ndiponso, opulumuka sadzapezeka pakati pa awo oika chidaliro chawo m’Mitundu Yogwirizana kapena m’magulu alionse andale zadziko, popeza amenewa ali mbali ya dziko limene lidzawonongedwa.—Chivumbulutso 17:11; 18:17-21.
18 Madalitso osatha akuyembekezera awo amene atenga njira imene imatsogolera ku kupulumuka. Talingalirani tsopano zina za zinthu zokondweretsa kwambiri zimene Mulungu akulonjeza awo okhulupirira m’Mawu ake ndi kutsimikizira chikhulupiriro chimenecho mwa kachitidwe kotsimikizirika.
[Chithunzi patsamba 87]
“Khamu lalikulu” lidzapulumuka chiwonongeko cha dziko nkukhala padziko lapansi m’Dongosolo Latsopano la Mulungu