Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 30 tsamba 250-255
  • Chimene Muyenera Kuchita Kuchita kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimene Muyenera Kuchita Kuchita kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUDZIPATULIRA NDI UBATIZO
  • CHIFUNIRO CHA MULUNGU KWA INU LEROLINO
  • SANKHANI MOYO WAMUYAYA M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI
  • Cosankha Canu ca Kumtumikira Mulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 30 tsamba 250-255

Mutu 30

Chimene Muyenera Kuchita Kuchita kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha

1. (a) Kodi ndinjira ziwiri zotani zimene ziri zokutsegukirani? (b) Kodi mungasankhe motani njira yabwino?

YEHOVA MULUNGU akukulonjezani kanthu kena kabwino kwambiri—moyo wosatha m’dongosolo lake la zinthu latsopano lolungama. (2 Petro 3:13) Koma kukhala ndi moyo pa nthawi imeneyo kumadalira pa kuchita kwanu chifuniro cha Mulungu tsopano. Dziko loipa liripoli, kuphatikizapo onse amene akukhalabe mbali yake, liri pafupi kuchoka, “koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2:17) Motero muyenera kusankha pakati pa njira ziwiri. Ina njopita ku imfa ndipo inayo ku moyo wamuyaya. (Deuteronomo 30:19, 20) Kodi mudzatsatira iti?

2. (a) Ngati muli ndi chikhulupiriro chenicheni, kodi mudzakhutiritsidwa maganizo za chiyani? (b) Kodi kukhulupirira Mulungu monga momwe mwana amakhulupiririra atate wachikondi kudzakuthandizani motani kumtumikira?

2 Kodi mumasonyeza motani kuti mukusankha moyo? Choyambirira, muyenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova ndi m’malonjezo ake. Kodi mwakhutiritsidwa maganizo mwamphamvu kuti Mulungu aliko “ndi kuti iye amakhala wofupa awo omfunafuna mwaphamphu”? (Ahebri 11:6, NW) Mufunikira kudalira Mulungu monga momwe mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi amadalirira atate wachikondi ndi wachifundo. (Salmo 103:13, 14; Miyambo 3:11, 12) Pokhala ndi chikhulupiriro choterocho, simudzakayikira kuti uphungu wake ngwanzeru kapena kuti njira zake nzoyenera, ngakhale ngati nthawi zina simukumvetsetsa zinthu mokwanira.

3. (a) Kuphatikiza pa chikhulupiriro, kodi nchiyaninso chikufunika? (b) Kodi ndi ntchito zotani zimene zikufunika kuti musonyeze kuti mukusankha moyo?

3 Komabe, choposa chikhulupiriro chikufunika. Payeneranso kukhala ntchito kuti zisonyeze chimene malingaliro anu enieni ali ponena za Yehova. (Yakobo 2:20, 26) Kodi mwachita zinthu kusonyeza kuti muli ndi chisoni chifukwa cha kulephera kulikonse papitapo kuchita chimene chiri choyenera? Kodi mwasonkhezereka kulapa kapena kupanga masinthidwe kugwirizanitsa njira yamoyo wanu ndi chifuniro cha Yehova? Kodi mwatembenuka, ndiko, kuti, mwakana njira iriyonse, yoipa imene mungakhale munali kutsatira, ndipo kodi mwayamba kuchita zinthu zimene Mulungu amafuna? (Machitidwe 3:19; 17:30) Ntchito zoterozo zidzasonyeza kuti mukusankha moyo.

KUDZIPATULIRA NDI UBATIZO

4. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukusonkhezerani kuchita chifuniro cha Mulungu? (b) Pamene musankha kuti mukufuna kutumikira Mulungu, kodi choyenera kuchita nchiyani?

4 Kodi nchiyani chimene chiyenera kukusonkhezerani kusankha moyo mwa kuchita chifuniro cha Mulungu? Chiyamikiro chiyenera. Tangoganizirani: Yehova wakutheketserani chimasuko ku matenda onse, kuvutika, ndipo ngakhale imfa! Mwa mphatso yamtengo wapatali ya Mwana wake iye wakutsegulirani njira ya ku moyo wosatha m’dziko lapansi laparadaiso. (1 Akorinto 6:19, 20; 7:23; Yohane 3:16) Pamene chikondi cha Yehova chikusonkhezerani kumkondanso, kodi muyenera kuchitanji? (1 Yohane 4:9, 10; 5:2, 3) Muyenera kufikira Mulungu m’dzina la Yesu ndi kumuuza m’pemphero kuti mukufuna kukhala mtumiki wake, kuti mukufuna kukhala wake. M’njira imeneyi mukudzipatulira nokha kwa Mulungu. Imeneyi ndinkhani yaumwini ndi yamtseri. Palibe aliyense angakuchitireni.

5. (a) Mutapanga kudzipatulira kwanu kwa Mulungu, kodi iye amakuyembekezerani kuchitanji? (b) Kodi ndichithandizo chotani chimene chiri chopezeka kwa inu m’kukwaniritsa kudzipatulira kwanu?

5 Mutapanga kudzipatulira kwanu kwa Mulungu, iye adzakuyembekezerani kukukwaniritsa. Motero dzisonyezeni kuti ndinu munthu wosunga pangano mwa kumamatira ku chosankha chimenechi, kapena kudzipatulira, malinga ngati muli moyo. (Salmo 50:14) Ngati mukhalabe pafupi ndi gulu lowoneka la Mulungu, mungathandizidwe ndi Akristu anzanu amene mokondwa adzakupatsani chilimbikitso ndi chichirikizo chachikondi.—1 Atesalonika 5:11.

6. (a) Pamene mupatulira moyo wanu kwa Mulungu, Kodi ndisitepe lotani limene pa nthawi imeneyo liri lofunika? (b) Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la ubatizo?

6 Komabe, muyenera kuchita zambiri koposa kuuza Yehova mtseri kuti mukufuna kukhala wake. Mufunikira kusonyeza pamaso pa ena kuti mwapanga kudzipatulira kwa kutumikira Mulungu. Kodi mumachita zimenezi motani? Mwa kubatizidwa m’madzi. Ubatizo wam’madzi woterowo ndiwo chisonyezero chapoyera chakuti munthu wapatulira moyo wake kwa Yehova ndipo akudzipereka kuchita chifuniro Chake.

7. (a) Kodi Yesu anapatsa Akristu chitsanzo chotani? (b) Kodi nchifukwa ninji ubatizo wolamulidwa ndi Yesu suli wa makanda?

7 Chakuti ubatizo wam’madzi ndiwo chofunika chachikulu chikusonyezedwa ndi chitsanzo cha Yesu Kristu. Yesu sanangouza Atate wake kuti iye adadza kudzachita chifuniro Chake. (Ahebri 10:7) Pamene iye anali pafupi kuyamba utumiki wake monga wolalikira ufumu wa Mulungu, Yesu anadzipereka kwa Yehova ndipo anabatizidwa m’madzi. (Mateyu 3:13-17) Popeza kuti Yesu anapereka chitsanzo, awo lerolino amene akudzipatulira okha kwa Yehova kuchita chifuniro chake ayenera kubatizidwa. (1 Petro 2:21; 3:21) Kunena zowona, Yesu analamulira omtsatira kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse ndi kenako kubatiza ophunzira atsopano amenewa. Kumeneku sindiko kubatizidwa kwa makanda. Ndiko ubatizo wa anthu amene akhala okhulupirira, osankha kutumikira Yehova.—Mateyu 28:19; Machitidwe 8:12.

8. Ngati mukufuna kubatizidwa, kodi muyenera kuuza zimenezi yani mumpingo, ndipo kodi nchifukwa ninji?

8 Ngati mwasankha kutumikira Yehova ndipo mukufuna kubatizidwa, kodi muyenera kuchitanji? Muyenera kuuza chikhumbo chanu woyang’anira wotsogoza wa mpingo wa Mboni za Yehova umene inu mukusonkhana nawo. Iye, limodzi ndi akulu ena mu mpingowo, mokondwa adzapenda nanu chidziwitso chimene inu mufunikira kudziwa kuti mutumikire Mulungu m’njira yovomerezeka. Pamenepo kungalinganizidwe kuti inu mubatizidwe.

CHIFUNIRO CHA MULUNGU KWA INU LEROLINO

9. Kodi Nowa anachitanji chigumula chisanadze chimene chiri chifuniro cha Mulungu kwa inu kuti muchite tsopano?

9 Chisanadze chigumula, Yehova anagwiritsira ntchito Nowa, “mlaliki wa chilungamo,” kuchenjeza za chiwonongeko chirinkudza ndi kusonyeza kumalo okha a chisungiko, chingalawa. (Mateyu 24:37-39; 2 Petro 2:5; Ahebri 11:7) Chifuniro cha Mulungu nchakuti inu tsopano muchite ntchito yolalikira imodzimodziyo. Yesu ananeneratu ponena za nthawi yathu: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Ena ayenera kudziwa zinthu zimene mwaphunzira ponena za zifuno za Mulungu ngati iwo ati apulumuke mapeto a dongosolo lino ndi kukhala ndi moyo kosatha. (Yohane 17:3) Kodi mtima wanu sukosonkhezereka kukhala ndi mbali m’kuuza ena chidziwitso chopatsa moyo chimenechi?

10. (a) Kodi kukonda anthu kuyenera kutisonkhezera kutsatira chitsanzo cha Yesu chotani? (b) Kodi yochuluka ya ntchito yolalikira ikuchitidwa motani?

10 Tsatirani chitsanzo cha Kristu. Iye sanayembekezere anthu kudza kwa iye, koma iye anamka nafunafuna awo amene akamvetsera uthenga Waufumu. Ndipo iye analangiza atsatiri ake—iwo onse—kuchita chimodzimodzi. (Mateyu 28:19; Machitidwe 4:13; Aroma 10:10-15) Potsatira chilangizo ndi chitsanzo cha Kristu, Akristu oyambirira anafikira anthu m’nyumba zawo. Iwo anapita “kunyumba ndi nyumba” ndi uthenga Waufumu. (Luka 10:1-6; Machitidwe 20:20, NW) Imeneyi idakali njira yaikulu imene Akristu owona akuchitira nayo uminisitala wawo m’nthawi yathu.

11. (a) Kodi nchifukwa ninji kumafunikira kulimba mtima kulalikira ponena za ufumu wa Mulungu, koma kodi nchifukwa ninji sitifunikira kuchita mantha? (b) Kodi Yehova amawona motani ntchito imene timachita?

11 Kumafuna kulimba mtima kuchita ntchito imeneyi. Satana ndi dziko lake ngotsimikizira kuyesa kukuletsani, monga momwedi iwo anayesera kuletsa kulalikira atsatiri oyambirira a Kristu. (Machitidwe 4:17-21; 5:27-29, 40-42) Koma simufunikira kuchita mantha. Monga momwedi Yehova anachirikizira ndi kulimbikitsira Akristu oyambirira amenewo, adzachita zomwezo kwa inu lerolino. (2 Timoteo 4:17) Motero limbani mtima! Sonyezani kuti mukukondadi Yehova ndi anthu anzanu mwa kukhala ndi phande lokwanira m’ntchito yopulumutsa moyo yolalikira ndi kuphunzitsa. (1 Akorinto 9:16; 1 Timoteo 4:16) Yehova sadzaiwala ntchito yanu, koma adzakufupani kwambiri.—Ahebri 6:10-12; Tito 1:2.

12. Kodi tingaphunzirenji m’chitsanzo cha mkazi wa Loti?

12 Palibe chirichonse cha phindu lenileni chimene dongosolo lakale lino lingapereke, motero musaganize kuti mukuperewedwa mwa kulifulatira. “Kumbukirani mkazi wa Loti,” Yesu anatero. (Luka 17:32) Iye ndi banja lake atapululuka m’Sodomu, anayang’ana mokhumbira zinthu zimene adzasiya mmbuyo. Mulungu anawona kumene mtima wake unali, ndipo iye anasanduka chulu chamchere. (Genesi 19:26) Musakhale ngati mkazi wa Loti! Yang’anitsitsani pa zimene ziri mtsogolo, pa “moyo weniweni” m’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu.—1 Timoteo 6:19.

SANKHANI MOYO WAMUYAYA M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI

13. Kodi Yesu anapereka motani chosankha chimene tonsefe tifunikira kupanga?

13 Ndithudi, pali zosankha ziwiri zokha. Kristu anaziyerekezera ndi chosankha cha imodzi ya njira ziwiri. Njira imodzi, iya anati, ‘njaikulu ndi yotakata.’ Pa iyo apaulendo akuloledwa ufulu wa kudzikondweretsa. Komabe, njira inayo, ‘njopapatiza.’ Inde, awo okhala panjira imeneyo amafunidwa kumvera malangizo ndi malamulo a Mulungu. Unyinji, Yesu anatero, ukutsatira njira yaikuluyo, owerengeka okha yopapatizayo. Kodi mudzasankha njiri iti? M’kupanga chosankha chanu, kumbukirani izi: Njira yaikuluyo idzafika kumagomero mwadzidzidzi—chiwonongeko! Ndiponso, njira yopapatizayo idzakufikitsani m’dongosolo latsopano la Mulungu. M’memeno mungakhale ndi phande m’kupangitsa dziko lapansi kukhala paradaiso waulemerero, m’mene mungakhale kosatha m’chimwemwe.—Mateyu 7:13, 14.

14. Kodi muyenera kukhala mbali ya chiyani kuti mulowe m’dongosolo latsopano la Mulungu?

14 Musanene kuti pali njira zosiyanasiyana, kapena misewu, zimene mungatsatire kuti mupeze moyo m’dongosolo latsopano la Mulungu. Pali imodzi yokha. Panali chingalawa chimodzi chokha chimene chinapyola Chigumula, osati ngalawa zambiri. Ndipo kudzakhala gulu limodzi lokha—gulu lowoneka la Mulungu—limene lidzapyola “chisautso chachikulu” choyandikira mofulumiracho. Sizowona konse kuti zipembedzo zonse zimatsogolera ku cholinga chimodzi. (Mateyu 7:21-23; 24:21) Muyenera kukhala mbali ya gulu la Yehova, mukumachita chifuniro cha Mulungu, kuti mulandire dalitso lake la moyo wosatha.—Salmo 133:1-3.

15. (a) Kodi tifunikira kuchitanji tsiku lirilonse? (b) Kodi ndichiyembekezo chotani chimene chiri choposa kwambiri loto?

15 Motero chititsani chithunzithunzi cha dongosolo la zinthu latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu kukhala chowala m’maganizo ndi mumtima mwanu. Tsiku lirilonse ganizirani mphatso yabwino kwambiri imene Yehova Mulungu akukulonjezani—kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Limeneli siloto. Ndizenizeni! Pakuti lonjezo Labaibulo nlotsimikizirika kukwaniritsidwa: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha . . . Pakudulidwa oipa udzapenya.”—Salmo 37:29, 34.

[Chithunzi patsamba 251]

Dzipatulireni nokha kwa Yehova . . . ndi kubatizidwa

[Chithunzi patsamba 253]

“Kumbukirani mkazi wa Loti”

[Zithunzi patsamba 254]

Chititsani dongosolo latsopano la Mulungi kukhala lowala m’maganizo ndi mumtima mwanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena