Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 128
  • Yesu Ngwamoyo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Ngwamoyo!
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Ngwamoyo!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Ali Moyo
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yesu Anaukitsidwa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 128

Mutu 128

Yesu Ngwamoyo!

PAMENE akaziwo akupeza manda a Yesu ali pululu, Mariya wa Magadala akuthamanga kukauza Petro ndi Yohane. Komabe, mwachiwonekere akazi ena atsala pamandapo. Mwamsanga, mngelo akuwonekera nawaitanira kuloŵa mkati.

Munomo akaziwo akuwonanso mngelo wina, ndipo mmodzi wa angelowo akuti kwa iwo: “Musawope inu; pakuti ndidziŵa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iyayi; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzawone malo mmene anagonamo Ambuye. Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa.” Chotero mwa mantha ndi kukondwera kwakukulu, akazi amenewa nawonso akuchoka mothamanga.

Panthaŵi ino, Mariya wapeza Petro ndi Yohane, ndipo akuwasimbira kuti: “Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziŵa kumene anamuika iye.” Pomwepo atumwi aŵiriwo akuyamba kuthamanga. Yohane ngwopepuka miyendo—mwachiwonekere pokhala wachichepere—ndipo akuyambirira kufika kumandako. Panthaŵi ino akaziwo achokako, chotero palibe aliyense amene ali pafupi. Posuzumira m’mandamo, Yohane akuwona nsalu zokulungira, koma iye sakuloŵamo.

Pamene Petro akufika, sakudodomadodoma koma akuloŵa mkati mwenimwenimo. Akuwona nsaluzo ziri zounjikika pamenepo ndiponso nsalu yogwiritsiridwa ntchito kukulungira mutu wa Yesu. Iyo yapindidwa ndi kuikidwa pamalo amodzi. Tsopano Yohane nayenso akuloŵa m’mandamo, ndipo akukhulupirira lipoti la Mariya. Koma Petro kapena Yohane sakuzindikira kuti Yesu waukitsidwa, ngakhale kuli kwakuti kaŵirikaŵiri iye anali atawauza kuti Akatero. Atachita kakasi, aŵiriwo akubwerera kunyumba, koma Mariya, amene wabwereranso kumandako, akutsalira.

Zidakali choncho, akazi enawo akufulumira kukauza ophunzira kuti Yesu waukitsidwa, monga momwe angelo anawauzira kuchita. Pamene iwo akuthamanga mofulumira monga momwe angathere, Yesu akukumana nawo nanena kuti: “Tikuwoneni.” Pogwera pa mapazi ake, iwo akumgwadira. Kenako Yesu akuti: “Musawope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiwona ine kumeneko.”

Poyambilirapo, pamene chivomezi chinachitika ndipo angelo nawonekera, asilikali olonda anachita kakasi nakhala ngati anthu akufa. Atatsitsimuka, iwo analoŵa mumzinda panthaŵi yomweyo nauza akulu ansembe zimene zidachitika. Atakambitsirana ndi “akulu” a Ayuda, chosankha chinapangidwa cha kuyesa kutontholetsa nkhaniyo mwa kupatsa asilikaliwo chiphuphu. Iwo analangizidwa kuti: “Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba uja mmene ife tinali m’tulo.”

Popeza kuti asilikali Achiroma angalandire chilango cha imfa kaamba ka kugona tulo pamalo awo, ansembewo analonjeza kuti: “Ndipo ngati ichi [nkhani ya kugona kwanu tulo] chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhaŵa.” Popeza mlingo wa chiphuphucho unali waukulu mokwanira, asilikaliwo anachita monga momwe analangizidwira. Monga chotulukapo, lipoti lonama lonena za kubedwa kwa mtembo wa Yesu linafikira kukhala lofalikira pakati pa Ayuda.

Mariya wa Magadala, amene akutsalira m’mbuyo kumandako, wadzazidwa ndi chisoni. Kodi Yesu angakhale ali kuti? Poŵeramira kutsogolo kuti awone m’mandamo, iye akuwona angelo aŵiri ovala zoyera, amene awonekeranso! Mmodzi wakhala chakumutu ndipo winayo chakumiyendo kwa malo amene mtembo wa Yesu unali utagona. “Mkazi, uliranji?” iwo akufunsa motero.

“Chifukwa anachotsa Ambuye wanga,” Mariya akuyankha motero, “ndipo sindidziŵa kumene anamuika.” Pamenepo iye akupotoloka nawona munthu wina amene akubwereza funsolo: “Mkazi, uliranji?” Ndipo ameneyu akufunsanso kuti: “Ufuna yani?”

Poyerekezera munthuyu kukhala wosamalira munda mmene muli mandawo, iyeyo akuti kwa iye: “Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamchotsa.”

“Mariya,” munthuyo akutero. Ndipo pomwepo iye wadziŵa, mwa njira yozoloŵereka imene iye amalankhulira naye, kuti ndiye Yesu. “Raboni;” (kutanthauza “Mphunzitsi”) iye akudzuma. Ndipo ndi chikondwerero chachikulu, iye amkupatira. Koma Yesu akuti: “Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kumka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.”

Tsopano Mariya akuthamangira kumene atumwi ndi ophunzira ena asonkhana. Iye akuwonjezera chochitika chake kulipoti limene akazi ena apereka kale lonena za kuwona Yesu woukitsidwayo. Komabe, amunaŵa, amene sanakhulupirire akazi oyamba, mwachiwonekere sakukhulupiriranso Mariya. Mateyu 28:3-15; Marko 16:5-8; Luka 24:4-12; Yohane 20:2-18.

▪ Atapeza manda apululu, kodi nchiyani chimene Mariya wa Magadala akuchita, ndipo kodi ndichokumana nacho chotani chimene akazi enawo akukhala nacho?

▪ Kodi Petro ndi Yohane akuchitanji atapeza manda apululu?

▪ Kodi akazi enawo akukumana ndichiyani popita kukasimba za chiukiriro cha Yesu kwa ophunzira?

▪ Kodi chinachitika nchiyani kwa asilikali olondawo, ndipo kodi lipoti lawo kwa ansembe linalabadiridwa motani?

▪ Kodi chikuchitika nchiyani pamene Mariya wa Magadala ali yekha kumandako, ndipo kodi ophunzira akulabadira motani malipoti a akaziwo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena