Chikristu Chifalikira Kumayiko Ena
YESU pa Phiri la Azitona pafupi ndi Betaniya, analamula zogwira ntchito yolalikira yomwe ikasintha mbiri ya dziko lonse. Ntchito imeneyi ikayambira ku Yerusalemu, pafupifupi makilomita atatu kumadzulo. Uthengawo ukafalikira kumadera apafupi a Yudeya ndi Samariya, mpaka “kufikira ku malekezero ake a dziko.”—Mac. 1:4, 8, 12.
Patangopita nthaŵi yochepa Yesu atanena mawu ameneŵa, Phwando la Pentekoste linasonkhanitsa Ayuda ndi anthu oloŵa Chiyuda ochokera m’madera onse a Ufumu wa Roma, osonyezedwa pamapu ali m’munsiŵa. Chikristu chinafalikira kwambiri pamene mtumwi Petro analalikira kwa anthuwo tsiku limenelo.—Mac. 2:9-11.
Posapita nthaŵi, chizunzo chinabalalitsa otsatira a Kristu kuchoka m’Yerusalemu. Petro ndi Yohane anathandiza Asamariya kumvetsa komanso kulandira uthenga wabwino. (Mac. 8:1, 4, 14-16) Chikristu chinafalikira ku Africa pamene Filipo analalikira Mwaitiopiya m’njira ya m’chipululu ‘yochokera ku Yerusalemu kumka ku Gaza.’ (Mac. 8:26-39) Inali nthaŵi yomweyo pamene uthenga wabwino unabala zipatso m’dera la Luda, lomwe lili ku Chigwa cha Saroni, ku doko la Yopa. (Mac. 9:35, 42) Kenako Petro anapita ku Kaisareya kumene anathandiza Korneliyo, yemwe anali ofesala wa Roma, ndi abale ake, ndiponso anzake kukhala Akristu odzozedwa ndi mzimu.—Mac. 10:1-48.
Paulo, yemwe poyamba anali kuzunza Akristu, anadzakhala mtumwi wa kwa anthu amitundu. Pamaulendo ake onse atatu aumishonale, ndi ulendo wake womaliza wopita ku Roma, Paulo anayenda pamtunda ndi pasitima za pamadzi. Mtumwiyu ndi anthu ena anafalitsa uthenga wabwino ku mizinda yambiri ya Ufumu wa Roma. Paulo anafunitsitsa kukafika ku Spanya (Onani patsamba 2.), ndipo Petro anakatumikira mpaka kum’maŵa kwenikweni, ku Babulo. (1 Pet. 5:13) Inde, chifukwa cha utsogoleri wamphamvu wa Kristu, otsatira ake anafalitsa Chikristu kumayiko ena. Cha m’ma 60 ndi 61 C.E., ‘uthenga wabwino unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akol. 1:6, 23) Kuyambira pamenepo, uthenga wabwino umenewuwafikadi ku “malekezero ake a dziko.”
[Bokosi patsamba 32]
ANACHOKERA KU . . .
Ayuda ndi oloŵa Chiyuda omwe anamva uthenga wabwino pa Pentekoste 33 C.E. anachokera ku Aparti, Mediya, Elamu, Mesopotamiya, Yudeya, Kapadokiya, Ponto, Asiya, Frugiya, Pamfuliya, Igupto, Libiya, Roma, Kurene, ndi Arabiya. Ambiri anabatizidwa. Kodi mukuganiza kuti anakachita chiyani atabwerera kwawo?
[Bokosi patsamba 33]
MIPINGO ISANU NDI IŴIRI
Yesu anatumiza uthenga ku mipingo isanu ndi iŵiri ku Asiya Mina. Onani malo amene mipingoyo inali: kunyanja ku Efeso ndi Smurna; kumtunda ku Pergamo, Filadelfeya, ndi Laodikaya; Tiyatira umene unali m’mphepete mwa mtsinje; ndi Sarde umene unali panjira yamalonda. Zotsalira za mizinda imeneyi zimene zafukulidwa zimasonyeza kuti Baibulo limanena za malo enieni.
[Mapu patsamba 32]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Spread of Christianity
Madera Amene Uthenga Wabwino Unafika Msanga
B1 ILURIKO
B1 ITALIYA
B1 Roma
C1 MAKEDONIYA
C2 GIRISI
C2 Atene
C2 KRETE
C3 Kurene
C3 LIBIYA
D1 BITUNIYA
D2 GALATIYA
D2 ASIYA
D2 FRUGIYA
D2 PAMFULIYA
D2 KUPRO
D3 IGUPTO
D4 ITIOPIYA
E1 PONTO
E2 KAPADOKIYA
E2 KILIKIYA
E2 MESOPOTAMIYA
E2 SURIYA
E3 SAMARIYA
E3 Yerusalemu
E3 YUDEYA
F2 MEDIYA
F3 Babulo
F3 ELAMU
F4 ARABIYA
G2 PARTHIA
[Nyanja]
C2 Nyanja ya Mediterranean
D1 Nyanja Yakuda
E4 Nyanja Yofiira
F3 Nyanja Ya Perisiya
[Mapu patsamba 32, 33]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Maulendo a Paulo
Ulendo Woyamba Waumishonale (Mac. 13:1–14:28)
H3 Antiokeya (wa Suriya)
H3 Selukeya
G4 KUPRO
G3 Salami
G4 Pafo
G3 PAMFULIYA
F3 Perge
F3 PISIDIYA
F2 Antiokeya (wa Pisidiya)
G2 Ikoniyo
G2 LUKAONIYA
G2 Lustra
G3 Derbe
G2 Lustra
G2 Ikoniyo
F2 Antiokeya (wa Pisidiya)
F3 PISIDIYA
G3 PAMFULIYA
F3 Perge
F3 Ataliya
H3 Antiokeya (wa Suriya)
Ulendo Wachiŵiri Waumishonale (Mac. 15:36–18:22)
H3 Antiokeya (wa Suriya)
H3 SURIYA
H3 KILIKIYA
H3 Tariso
G3 Derbe
G2 Lystra
G2 Ikoniyo
F2 Antiokeya (wa Pisidiya)
F2 FRUGIYA
G2 GALATIYA
E2 MUSIYA
E2 Trowa
E1 SAMATRAKE
D1 Neapoli
D1 Filipi
C1 MAKEDONIYA
D1 Amfipoli
D1 Tesalonika
D1 Bereya
C2 GIRISI
D2 Atene
D2 Korinto
D3 AKAYA
E2 Efeso
G4 Kaisareya
H5 Yerusalemu
H3 Antiokeya (wa Suriya)
Ulendo Wachitatu Waumishonale (Mac. 18:22–21:19)
H3 SURIYA
H3 Antiokeya (wa Suriya)
G2 GALATIYA
F2 FRUGIYA
H3 KILIKIYA
H3 Tariso
G3 Derbe
G2 Lystra
G2 Ikoniya
F2 Antiokeya (wa Pisidiya)
E2 Efeso
E2 ASIYA
E2 Troas
D1 Filipi
C1 MAKEDONIYA
D1 Amfipoli
D1 Tesalonika
D1 Bereya
C2 GIRISI
D2 Atene
D2 Korinto
D1 Bereya
D1 Tesalonika
D1 Amfipoli
D1 Filipi
E2 Troas
E2 Aso
E2 Mitilene
E2 KIYO
E2 SAMO
E3 Mileto
E3 Ko
E3 RODE
F3 Patara
H4 Turo
H4 Ptolemayi
G4 Kaisareya
H5 Yerusalemu
Ulendo wa ku Roma (Mac. 23:11–28:31)
H5 Yerusalemu
G4 Kaisareya
H4 Sidoni
F3 Mura
F3 LUKIYA
E3 Knido
D3 KRETE
D4 KAUDA
A3 MELITA
A3 SICILY
A3 Surakusa
A1 ITALIYA
B2 Regio
A1 Potiyolo
A1 Roma
Njira Zazikulu (Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
[Mipingo isanu ndi iŵiri]
E2 Pergamo
E2 Tiyatira
E2 Sarde
E2 Smurna
E2 Efeso
F2 Filadelfeya
F2 Laodikaya
[Malo Ena]
E3 PATMO
F2 Kolose
F5 Alesandriya
F5 IGUPTO
G1 BITUNIYA
G5 Yopa
G5 Luda
G5 Gaza
H1 PONTO
H2 KAPADOKIYA
H4 Damasiko
H4 Pella
[Nyanja]
Nyanja ya Mediterranean
[Chithunzi patsamba 33]
Bwalo la ku Mileto, mzinda umene Paulo anakumanako ndi akulu ochokera ku Efeso
[Chithunzi patsamba 33]
Guwa la nsembe la Zeu ku Pergamo. Akristu a mu mzinda umenewu ankakhala kumene ‘kunali mpando wachifumu wa Satana’—Chiv. 2:13