NYIMBO 12
Yehova Mulungu Wamkulu
Losindikizidwa
1. Inu Yehova M’lungu Wamkulu,
Wabwino m’zinthu zonse,
Tizikutamandani.
Muli ndi mphamvu, chikondi, nzeru.
Mulungu wathu ndinu.
2. Tikumaona chifundo chanu.
Ngakhale ndife fumbi
Tikapempha mumamva.
Mumatidyetsa, kutiphunzitsa,
Mumatithandizadi.
3. Tikutamanda inu Yehova.
Tikukuimbirani
Mosangalala ndithu.
Muyeneradi kutamandidwa
Kuchokera mumtima.
(Onaninso Deut. 32:4; Miy. 16:12; Mat. 6:10; Chiv. 4:11.)