Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es25 tsamba 47-57
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Lachinayi, May 1
  • Lachisanu, May 2
  • Loweruka, May 3
  • Lamlungu, May 4
  • Lolemba, May 5
  • Lachiwiri, May 6
  • Lachitatu, May 7
  • Lachinayi, May 8
  • Lachisanu, May 9
  • Loweruka, May 10
  • Lamlungu, May 11
  • Lolemba, May 12
  • Lachiwiri, May 13
  • Lachitatu, May 14
  • Lachinayi, May 15
  • Lachisanu, May 16
  • Loweruka, May 17
  • Lamlungu, May 18
  • Lolemba, May 19
  • Lachiwiri, May 20
  • Lachitatu, May 21
  • Lachinayi, May 22
  • Lachisanu, May 23
  • Loweruka, May 24
  • Lamlungu, May 25
  • Lolemba, May 26
  • Lachiwiri, May 27
  • Lachitatu, May 28
  • Lachinayi, May 29
  • Lachisanu, May 30
  • Loweruka, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25 tsamba 47-57

May

Lachinayi, May 1

Padziko lonse lapansi padzagwa njala yaikulu.​—Mac. 11:28.

Akhristu oyambirira anakhudzidwanso pamene kunagwa njala yaikulu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” N’zosakayikitsa kuti mitu ya mabanja inkadera nkhawa kuti izipezera bwanji zofunika mabanja awo. Nanga bwanji za achinyamata omwe anali ndi zolinga zofuna kuwonjezera utumiki wawo? Kodi mwina iwo anayamba kuona kuti aimitse kaye zolinga zawo? Ngakhale kuti panali mavutowa, Akhristuwo anasintha zinthu mogwirizana ndi mmene zinalili pa moyo wawo. Iwo anapitiriza kulalikira mmene akanathera ndipo anasangalala kugawira Akhristu anzawo a ku Yudeya zinthu zomwe anali nazo. (Mac. 11:29, 30) Omwe anapatsidwa zinthu zofunika anaona kuti Yehova akuwathandiza. (Mat. 6:31-33) Iwo ayenera kuti anayamba kugwirizana kwambiri ndi Akhristu omwe anawathandizawo. Ndipo amene anapereka zinthu zawo kapena kugwira nawo ntchito yothandizayo, anapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa cha kupatsa.—Mac. 20:35. w23.04 16 ¶12-13

Lachisanu, May 2

Timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.​—1 Yoh. 5:15.

Nthawi zina Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake polimbikitsa anthu omwe samutumikira kuti awathandize. Mwachitsanzo, iye analimbikitsa Mfumu Aritasasita kuti avomere zimene Nehemiya anapempha, zoti abwerere ku Yerusalemu kukathandiza pa ntchito yomanganso mzindawo. (Neh. 2:3-6) Masiku anonso Yehova angachititse anthu omwe samutumikira kuti atithandize. Si nthawi zonse pamene mapemphero athu amayankhidwa m’njira yodabwitsa. Koma mayankho amene Yehova amapereka amatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwambayu. Choncho muzikhala tcheru kuti muone mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu. Nthawi ndi nthawi muziima kaye n’kuganizira mmene Yehova akuyankhira mapemphero anu. (Sal. 66:19, 20) Tiyenera kumasonyeza chikhulupiriro, osati popemphera kwa Yehova pokha, koma povomerezanso yankho la pemphero lathu, kaya yankholo likhale lotani.—Aheb. 11:6. w23.05 11 ¶13; 12 ¶15-16

Loweruka, May 3

Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga.​—Sal. 40:8.

Pamene tinadzipereka kwa Yehova, tinalonjeza kuti tizidzamulambira komanso kuchita chifuniro chake. Tiyenera kumakwaniritsa lonjezo lathuli. Kuchita zinthu mogwirizana ndi zomwe tinalonjeza kuti tidzatumikira Yehova, si kolemetsa. Ndipotu Yehova anatilenga kuti tizichita chifuniro chake. (Chiv. 4:11) Iye anatilenga m’chifaniziro chake komanso ndi mtima woti tizifuna kumulambira. Zotsatira zake n’zakuti timakhala naye pa ubwenzi komanso timasangalala kuchita chifuniro chake. Koposa zonse, tikamachita chifuniro cha Mulungu komanso kutsanzira Mwana wake, ‘timatsitsimulidwa.’ (Mat. 11:28-30) Choncho muzikonda kwambiri Yehova poganizira zabwino zimene wakhala akukuchitirani komanso madalitso omwe adzakupatseni m’tsogolo. Mukamakonda kwambiri Mulungu, m’pamenenso zimakhala zosavuta kuti muzimumvera. (1 Yoh. 5:3) Yesu anakwanitsa kuchita chifuniro cha Mulungu chifukwa ankapempha Yehova kuti amuthandize komanso ankaganizira kwambiri madalitso omwe adzapeze m’tsogolo. (Aheb. 5:7; 12:2) Mofanana ndi Yesu, muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu ndipo nthawi zonse muziganizira chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. w23.08 27-28 ¶4-5

Lamlungu, May 4

Kodi sukudziwa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, kusakwiya msanga komanso kuleza mtima n’cholinga choti ulape?​—Aroma 2:4.

Tonsefe timasangalala ndi anthu omwe ndi oleza mtima. N’chifukwa chiyani? Chifukwa timalemekeza anthu amene amayembekezera kapena kudikirira chinachake popanda kukhumudwa. Timayamikira anthu ena akatilezera mtima pamene talakwitsa zinazake. Timayamikiranso kuti amene ankatiphunzitsa Baibulo ankaleza nafe mtima pamene tinkavutika kuphunzira, kuvomereza kapenanso kugwiritsa ntchito mfundo inayake ya m’Baibulo. Koposa zonse, timathokoza kwambiri kuti Yehova Mulungu amatilezera mtima. Ngakhale kuti timasangalala ena akamaleza mtima, si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuti ifeyo tisonyeze khalidweli. Mwachitsanzo, tingalephere kukhala oleza mtima ngati mumsewu muli magalimoto ambiri, makamaka pamene tachedwa. Nthawi zina tingalephere kuugwira mtima ena akatikhumudwitsa. Ndipo nthawi zinanso tingamavutike kuyembekezera dziko latsopano limene Yehova anatilonjeza. Komabe, pa zochitika zonsezi tiyenera kukhala oleza mtima kwambiri. w23.08 20 ¶1-2

Lolemba, May 5

Iye anabweza amuna ena onse a Isiraeli n’kutsala ndi amuna 300.​—Ower. 7:8.

Yehova analamula Gidiyoni kuti achepetse kwambiri chiwerengero cha asilikali ake. Iye akanatha kuganiza kuti, ‘Koma kodi ndikufunikadi kuchita zimenezi? Kodi n’zothandiza?’ Ngakhale zinali choncho, Gidiyoni anamvera. Masiku anonso, akulu amatsanzira Gidiyoni potsatira malangizo a gulu la Yehova amene asintha. (Aheb. 13:17) Gidiyoni anamvera ngakhale kuti ankachita mantha komanso zimene ankafunika kuchitazo zinali zoopsa. (Ower. 9:17) Yehova atamutsimikizira, Gidiyoni sankakayikira kuti Mulungu adzamuthandiza akamadzamenya nkhondo yoteteza anthu a Yehova. Akulu amene amakhala m’madera omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa amatsanzira Gidiyoni. Molimba mtima, iwo amatsogolera pamisonkhano komanso pa ntchito yolalikira ngakhale kuti akhoza kumangidwa, kufunsidwa mafunso, kuchitiridwa zachiwawa kapenanso kuchotsedwa ntchito. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, akulu adzafunika kulimba mtima kuti adzatsatire malangizo omwe adzapatsidwe posatengera kuti akumana ndi zoopsa zotani. w23.06 5-6 ¶12-13

Lachiwiri, May 6

Amene akundilemekeza ndidzawalemekeza.—1 Sam. 2:30.

Yehova analola kuti zabwino zimene Mkulu wa Ansembe Yehoyada anachita zilembedwe m’Mawu ake kuti zizitilangiza. (Aroma 15:4) Komanso Yehoyada atamwalira, anapatsidwa ulemu wapadera poikidwa m’manda “mu Mzinda wa Davide, chifukwa anachita zinthu zabwino mu Isiraeli zokhudza Mulungu woona ndi nyumba ya Mulungu woonayo.” (2 Mbiri 24:15, 16) Nkhani ya Yehoyada ingatithandize tonsefe kuti tiziopa Mulungu. Akulu angatsanzire Yehoyada pokhala tcheru n’kumateteza nkhosa za Mulungu mokhulupirika. (Mac. 20:28) Achikulire angaphunzireponso kanthu kwa Yehoyada kuti ngati atamaopa Yehova n’kukhalabe okhulupirika, iye angawagwiritse ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Achinyamata angaphunzirepo kanthu poona mmene Yehova anachitira zinthu ndi Yehoyada n’kumamutsanzira polemekeza achikulire, makamaka amene atumikira Mulungu mokhulupirika kwa nthawi yaitali. (Miy. 16:31) Tiyeni tizithandiza mokhulupirika ‘amene akutsogolera’ pomawamvera.—Aheb. 13:17. w23.06 17 ¶14-15

Lachitatu, May 7

Milomo ya wolungama imathandiza anthu ambiri.​—Miy. 10:21.

Pamisonkhano, muzichita zinthu mozindikira pofuna kusankha kuti muyankhe pafupipafupi motani. Ngati titamakweza dzanja lathu pafupipafupi, wochititsayo angamakakamizike kuti atitchule mobwerezabwereza ngakhale kuti ena sanayankhe. Zimenezi zingachititse kuti anthu ena asiye kuimika manja. (Mlal. 3:7) Ofalitsa ambiri akakweza manja kuti ayankhe pa phunziro, sitingamakhale ndi mwayi woti tiziyankha pafupipafupi ngati mmene timafunira. Ndipotu nthawi zina wochititsa sangatiloze. Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa komabe sitiyenera kukhumudwa tikapanda kutchulidwa. (Mlal. 7:9) Ngati simunakwanitse kupereka ndemanga maulendo angapo ngati mmene mumafunira, bwanji osamvetsera mwatcheru ena akamayankha n’cholinga choti muwayamikire pambuyo pamisonkhano? Abale ndi alongo anu angalimbikitsidwe mukawayamikira ngati mmene akanalimbikitsidwira ndi ndemanga zanu. w23.04 23-24 ¶14-16

Lachinayi, May 8

Ndatsimikiza mtima, inu Mulungu.​—Sal. 57:7.

Muziphunzira Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama. Mofanana ndi mtengo umene umakhala wolimba chifukwa chakuti uli ndi mizu yozama, ifenso tingakhale olimba ngati tili ndi chikhulupiriro chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu. Mtengo ukamakula, mizu yake imazama komanso kuchuluka. Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira Mawu a Mulungu komanso kuwaganizira mozama, timakhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso otsimikiza kuti mfundo zake n’zabwino kwambiri. (Akol. 2:6, 7) Muziganizira mmene malangizo a Yehova anathandizira komanso kutetezera atumiki ake m’mbuyomu. Mwachitsanzo, Ezekieli ankachita chidwi pamene mngelo ankayeza kachisi amene mneneriyu anaona m’masomphenya. Masomphenyawa analimbikitsa Ezekieli ndipo timaphunziraponso mfundo zofunika zokhudza zimene tingachite kuti tizitsatira mfundo za Yehova zokhudza kulambira koona. (Ezek. 40:1-4; 43:10-12) Timapindulanso kwambiri tikamapeza nthawi yophunzira komanso kuganizira zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu. Tikamachita zimenezi, tingakhale ndi mtima wokhazikika, kapena kuti wosasunthika, n’kumakhulupirira kwambiri Yehova.—Sal. 112:7. w23.07 18 ¶15-16

Lachisanu, May 9

Uteteze . . . kuganiza bwino.—Miy. 3:21.

M’Baibulo muli zitsanzo zabwino zambiri zimene achinyamata angatengere. Anthu akalewa ankakonda Mulungu ndipo anali ndi maudindo osiyanasiyana posamalira anthu ake. Mukhozanso kupeza zitsanzo zabwino za Akhristu olimba mwauzimu m’banja lanu ndiponso mumpingo. (Aheb. 13:7) Komanso muli ndi chitsanzo changwiro cha Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Mukamaphunzira mosamala za anthu amenewa, muziganiziranso makhalidwe abwino amene anali nawo. (Aheb. 12:1, 2) Kenako muziona zomwe mungachite kuti muwatsanzire. Munthu woganiza bwino amaganizira kaye asanasankhe zochita. Choncho yesetsani kuti mukhale ndi luso limeneli. Choyamba, muyenera kuphunzira mfundo za m’Baibulo ndi kumaganizira ubwino wake. Ndiyeno muzigwiritsa ntchito mfundo zimenezo posankha kuchita zinthu zimene zingasangalatse Yehova. (Sal. 119:9) Izi zidzakuthandizani kwambiri kuti mukule mwauzimu.—Miy. 2:11, 12; Aheb. 5:14. w23.12 24-25 ¶4-5

Loweruka, May 10

Muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.​—1 Pet. 3:15.

Makolo angaphunzitse ana awo mmene angayankhire mofatsa ena akamatsutsa zimene amakhulupirira. (Yak. 3:13) Makolo ena amayeserera zimenezi pa nthawi ya kulambira kwa pabanja. Amaganizira nkhani zimene anawo akhoza kukumana nazo kusukulu. Kenako amakambirana nawo ndi kuwasonyeza mmene angayankhire, n’kuwaphunzitsa mmene angachitire zimenezo mofatsa ndiponso m’njira yabwino kwambiri. Kukonzekera kungathandize Akhristu kudziwa mmene angafotokozere mogwira mtima zimene amakhulupirira. Kungathandizenso achinyamata kutsimikizira kuti ali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira mfundo za m’Baibulo. Pa jw.org pa gawo lakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,” pali zoti achinyamata achite. Zimenezi zinakonzedwa kuti zizithandiza achinyamata kulimbitsa chikhulupiriro chawo komanso kuwakonzekeretsa kuti azitha kuyankha m’mawu awoawo ena akamawafunsa. Kuphunzira nkhani zimenezi monga banja kungatithandize tonsefe kuti tizitha kufotokoza zimene timakhulupirira mofatsa komanso m’njira yabwino kwambiri. w23.09 17 ¶10; 18 ¶15-16

Lamlungu, May 11

Tisasiye kuchita zabwino, chifukwa pa nthawi yake tidzakolola tikapanda kutopa.—Agal. 6:9.

Kodi munayamba mwadziikirapo cholinga chinachake chauzimu koma n’kumalephera kuchikwaniritsa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Mwachitsanzo, Philip ankafuna kuti azipemphera pafupipafupi komanso mapemphero ake azikhala abwino, koma zinkamuvuta kupeza nthawi yopemphera. Erika anali ndi cholinga chakuti asamachedwe kufika pamisonkhano yokonzekera utumiki koma ankachedwa pafupifupi msonkhano uliwonse. Ngati panopa muli ndi cholinga china chomwe simunachikwaniritse, dziwani kuti si inu olephera. Kuti munthu akwaniritse ngakhale cholinga chaching’ono amafunika nthawi komanso khama. Mukamafunitsitsa kukwaniritsa cholinga chinachake mumasonyeza kuti mumaona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wamtengo wapatali komanso mukufunitsitsa kumupatsa zinthu zabwino kwambiri. Yehova amayamikira khama lanu. N’zoona kuti sayembekezera zambiri kuposa zimene mungakwanitse. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Choncho muzikhala ndi zolinga zimene mungazikwaniritse malinga ndi mmene zilili pa moyo wanu. w23.05 26 ¶1-2

Lolemba, May 12

Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?​—Aroma 8:31.

Anthu olimba mtima angathe kuchita mantha koma samalola kuti manthawo awalepheretse kuchita zoyenera. Danieli anali mnyamata wolimba mtima kwambiri. Iye ankaphunzira zolemba za aneneri a Mulungu kuphatikizapo maulosi a mneneri Yeremiya. Chifukwa cha zimenezi, iye anadzazindikira kuti ukapolo wa Ayuda ku Babulo unali utatsala pang’ono kutha. (Dan. 9:2) Mosakayikira, kuona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa kunathandiza Danieli kuti azikhulupirira Yehova, ndipo anthu amene amakhulupirira kwambiri Yehova angathe kukhala olimba mtima kwambiri. (Yerekezerani ndi Aroma 8:32, 37-39.) Chofunika kwambiri n’chakuti Danieli ankapemphera kwa Atate wake wakumwamba pafupipafupi. (Dan. 6:10) Iye anavomereza kuti anali atachimwira Yehova ndipo ankamufotokozera mmene ankamvera. Danieli anapemphanso Yehova kuti amuthandize. (Danieli 9:4, 5, 19) Iye anali munthu ngati ife tomwe, choncho sanabadwe ndi khalidwe la kulimba mtima. M’malomwake anakhala ndi khalidweli chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu, kupemphera komanso kudalira Yehova. w23.08 3 ¶4; 4 ¶7

Lachiwiri, May 13

Muzionetsa kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino n’kulemekeza Atate wanu wakumwamba.​—Mat. 5:16.

Tikamamvera olamulira akuluakulu, zimathandiza kuti zinthu zitiyendere bwino ifeyo komanso anthu ena. N’chifukwa chiyani tikutero? Mwa zina, timapewa chilango chimene chimaperekedwa kwa anthu osamvera malamulo. (Aroma 13:1, 4) Tikamamvera olamulira, iwo amaona kuti a Mboni za Yehova onse ndi anthu omvera. Mwachitsanzo, zaka zambiri m’mbuyomo, asilikali analowa m’Nyumba ya Ufumu ku Nigeria misonkhano ili m’kati. Iwo ankafufuza anthu amene ankachita zionetsero posafuna kupereka misonkho. Koma mkulu wa asilikaliwo anawauza kuti achoke ndipo ananena kuti: “A Mboni za Yehova nthawi zonse amapereka misonkho.” Nthawi iliyonse imene mwamvera lamulo, mumathandiza kuti anthu a Yehova akhale ndi mbiri yabwino ndipo zimenezi zikhoza kudzateteza Akhristu anzanu m’tsogolo. w23.10 9 ¶13

Lachitatu, May 14

Mukufunika kukhala opirira komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza.—Aheb. 10:36.

Atumiki ena a Yehova akhala akuyembekezera mapeto a dzikoli kwa nthawi yaitali. Kwa anthu, lonjezo la Mulunguli lingaoneke ngati likuchedwa kukwaniritsidwa. Yehova amadziwa mmene atumiki ake amamvera. Ndipotu anatsimikizira Habakuku kuti: “Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.” (Hab. 2:3) Kodi Mulungu ananena mawuwa pongofuna kulimbikitsa Habakuku yekha? Kapena kodi angatilimbikitsenso ifeyo masiku ano? Mouziridwa, mtumwi Paulo anafotokoza mawu omwewa kwa Akhristu omwe akuyembekezera dziko latsopano. (Aheb. 10:36, 37) Choncho ngakhale kuti lonjezo la Mulungu loti adzatipulumutsa lingaoneke ngati likuchedwa, sitingakayikire kuti ‘lidzakwaniritsidwa ndithu, silidzachedwa.’ w23.04 30 ¶16

Lachinayi, May 15

Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzira Mose.​—Num. 14:2.

Aisiraeli sanavomereze umboni woti Yehova ankagwiritsa ntchito Mose ngati womuimira wake. (Num. 14:10, 11) Mobwerezabwereza, iwo ankakana zoti Mose anatumidwa ndi Yehova. Pa chifukwa chimenechi, Yehova sanalole kuti Aisiraeli amenewa akalowe m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:30) Komabe, panali Aisiraeli ena omwe ankatsatira malangizo a Yehova. Mwachitsanzo, nthawi ina Yehova anati: “Kalebe . . . wakhala akunditsatira ndi mtima wonse.” (Num. 14:24) Mulungu anadalitsa Kalebe ndipo atafika m’dziko la Kanani, amamulola kusankha dera lomwe ankafuna kukhala. (Yos. 14:12-14) Aisiraeli amene analoledwa kulowa m’Dziko Lolonjezedwalo, anaperekanso chitsanzo chabwino potsatira malangizo a Yehova. Pamene Yoswa anasankhidwa kuti alowe m’malo mwa Mose, kuti aziwatsogolera, iwo ‘ankamulemekeza kwambiri masiku onse a moyo wake.’ (Yos. 4:14) Zotsatira zake n’zakuti, Yehova anawadalitsa powapatsa dziko limene anawalonjeza.—Yos. 21:43, 44. w24.02 21 ¶6-7

Lachisanu, May 16

Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.​—1 Yoh. 4:21.

Mofanana ndi dokotala, yemwe amatha kudziwa zokhudza mtima wathu poona kagundidwe kake pamkono, ifenso tikhoza kudziwa ngati timakonda kwambiri Mulungu poona mmene timakondera anzathu. Ngati titaona kuti chikondi chathu kwa Akhristu anzathu chayamba kuchepa, chimenechi chingakhale chizindikiro chakuti chikondi chathu kwa Mulungu chayambanso kuchepa. Koma ngati nthawi zonse timawasonyeza chikondi, chingakhale chizindikiro chakuti timakondanso kwambiri Mulungu. Ngati sitikukonda kwambiri abale ndi alongo athu ndiye kuti pali vuto lalikulu. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa zingasonyeze kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu suli bwino. Mtumwi Yohane anafotokoza mfundo imeneyi pomwe ananena kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Yehova amasangalala nafe pokhapokha ngati ‘timakondana.’—1 Yoh. 4:7-9, 11. w23.11 8 ¶3; 9 ¶5-6

Loweruka, May 17

Bambo ako ndi mayi ako adzasangalala.​—Miy. 23:25.

Ali mwana, Mfumu Yehoasi anasankha zinthu mwanzeru. Iye analibe bambo ndipo anatsatira malangizo a Mkulu wa Ansembe Yehoyada amene anali wokhulupirika. Mkulu wa ansembeyo ankalangiza Yehoasi ngati mwana wake. Potengera chitsanzo cha Yehoyada, Yehoasi anasankha kuti azitumikira Yehova komanso kuthandiza anthu ena kuti azimutumikira. Yehoasi anakonzanso zoti kachisi wa Yehova akonzedwe. (2 Mbiri 24:1, 2, 4, 13, 14) Ngati mukuphunzitsidwa kuti muzikonda Yehova komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wanu, dziwani kuti mukupatsidwa mphatso yapadera. (Miy. 2:1, 10-12) Makolo anu angakuphunzitseni m’njira zambiri. Iwo adzasangalala ngati mutamatsatira malangizo a m’Malemba amene amakupatsani. Chofunika kwambiri n’chakuti mudzasangalatsa Mulungu ndipo mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba. (Miy. 22:6; 23:15, 24) Zimenezitu ndi zifukwa zabwino zokuchititsani kutsanzira zimene Yehoasi anachita ali mwana. w23.09 8-9 ¶3-5

Lamlungu, May 18

Ine ndidzakumvetserani.​—Yer. 29:12.

Yehova analonjeza kuti aziyankha mapemphero athu. Mulungu wathu amakonda atumiki ake okhulupirika choncho sanganyalanyaze mapemphero awo. (Sal. 10:17; 37:28) Koma izi sizikutanthauza kuti azitipatsa chilichonse chomwe tingamupemphe. Tiyenera kudikira mpaka m’dziko latsopano kuti tidzalandire zinthu zina zimene timapempha. Yehova amayankha mapemphero athu mogwirizana ndi cholinga chake. (Yes. 55:8, 9) Mbali ina ya cholingacho ndi yakuti padzikoli padzakhale anthu osangalala, ogwirizana komanso omvera ulamuliro wake. Koma Satana amanena kuti anthu angamasangalale ngati atamadzilamulira okha. (Gen. 3:1-5) Pofuna kusonyeza kuti zimene Satana amanena ndi zabodza, Yehova walola kuti anthu azidzilamulira. Koma ulamuliro wa anthu wayambitsa mavuto ambiri amene tikukumana nawo masiku ano. (Mlal. 8:9) Timadziwanso kuti Yehova sangathetse mavuto onse panopa. w23.11 21 ¶4-5

Lolemba, May 19

Ndakusankha kuti ukhale bambo wa mitundu yambiri.—Aroma 4:17.

Ngakhale kuti Abulahamu anali ndi zaka 100 komanso Sara anali ndi zaka 90, mwana amene Mulungu anawalonjeza anali asanabadwe. Kwa anthu, zinali zosatheka kuti Abulahamu ndi Sara akhale ndi mwana. Apatu Abulahamu anayesedwa kwambiri. Komabe “[iye] anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri.” (Aroma 4:18, 19) Ndipotu zimene ankayembekezerazi zinachitikadi. Iye anabereka Isaki, mwana amene ankamuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Aroma 4:20-22) Mulungu angamasangalale nafe n’kumationa kuti ndife olungama komanso anzake ngati mmene zinalili ndi Abulahamu. Ndipotu Paulo anafotokoza zimenezi pomwe analemba kuti: “Mawu akuti ‘Mulungu anamuona [Abulahamu] kuti ndi wolungama’ sanalembere iye yekha. Analemberanso ifeyo. Nafenso timaonedwa kuti ndife olungama chifukwa timakhulupirira Mulungu amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 4:23, 24) Mofanana ndi Abulahamu, tiyenera kumakhulupirira Yehova, kumachita zabwino komanso kukhala ndi chiyembekezo. w23.12 7 ¶16-17

Lachiwiri, May 20

Mwaona kusautsika kwanga. Mukudziwa mavuto aakulu amene ndili nawo.​—Sal. 31:7.

Mukamakumana ndi mayesero omwe akukuchititsani mantha, muzikumbukira kuti Yehova amaona zomwe zikukuchitikirani ndipo amadziwa mmene mukumvera. Mwachitsanzo, sikuti Yehova ankangoona nkhanza zomwe Aisiraeli ankachitiridwa ku Iguputo koma ankadziwanso ‘ululu umene ankamva.’ (Eks. 3:7) Koma mwina simungadziwe mmene Yehova akukuthandizirani mukamachita mantha chifukwa cha mayesero enaake. Choncho muzimupempha kuti akuthandizeni kuona mmene akukuthandizirani. (2 Maf. 6:15-17) Kenako muziganizira izi: Kodi munamvetsera nkhani kapena ndemanga inayake pamisonkhano yomwe yakulimbikitsani? Kodi pali buku, vidiyo kapena nyimbo ya broadcasting yomwe yakulimbikitsani? Kodi pali wina yemwe wakulimbikitsani ndi mfundo inayake kapena lemba? Zingakhale zosavuta kuiwala mmene abale ndi alongo athu amatisonyezera chikondi komanso mmene zinthu zomwe Yehova amatipatsa zimatilimbikitsira. Komatu zimenezi ndi mphatso zapadera zochokera kwa Yehova. (Yes. 65:13; Maliko 10:29, 30) Mphatsozi zimasonyeza kuti Mulungu amatikonda. (Yes. 49:14-16) Zimasonyezanso kuti ndi woyenera kuti tizimudalira. w24.01 4-5 ¶9-10

Lachitatu, May 21

Tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.​—Mac. 4:29.

Asanabwerere kumwamba, Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti ayenera kuchitira umboni za iye “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Luka 24:46-48) Pasanapite nthawi yaitali, atsogoleri a Chiyuda anagwira mtumwi Petulo ndi Yohane n’kupita nawo kukhoti lalikulu la Ayuda ndipo anawalamula kuti asiye kulalikira ndiponso anawaopseza. (Mac. 4:18, 21) Petulo ndi Yohane anati: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:19, 20) Petulo ndi Yohane atamasulidwa, ophunzirawo anapemphera kwa Yehova mokweza mawu kuti awathandize kukwaniritsa chifuniro chake. Yehova anayankha pemphero lochokera pansi pa mtimali.—Mac. 4:31. w23.05 5 ¶11-12

Lachinayi, May 22

Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.​—Mat. 17:5.

Yehova ndi Mwana wake akhala ali limodzi kwa zaka zambirimbiri ndipo izi zachititsa kuti azikondananso kwambiri. Ubwenzi wawowu ndi wakale kwambiri kuposa ubwenzi wina uliwonse. Palemba laleroli, Yehova anafotokoza mmene amakondera Yesu. Yehova akanatha kungonena kuti, ‘Uyu ndi amene amandisangalatsa.’ Koma pofuna kutisonyeza mmene amakondera Yesu, ananena kuti “uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.” Yehova ankasangalala kwambiri ndi Yesu komanso ndi zimene Yesuyo anali atatsala pang’ono kuchita (Aef. 1:7) Ndipo Yesu sankakayikira kuti Atate wake amamukonda. Ankaona kuti chikondi cha Yehova ndi chenicheni ndipo ankachimva mumtima mwake. Iye anafotokoza mobwerezabwereza kuchokera pansi pa mtima kuti Atate wake amamukonda.—Yoh. 3:35; 10:17; 17:24. w24.01 28 ¶8

Lachisanu, May 23

Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.​—Miy. 22:1.

Tayerekezerani kuti mnzanu akukunenerani zoipa. Mukudziwa kuti ndi zabodza, koma anthu ena akukhulupirira zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, anthu akupitiriza kunenabe zabodzazo ndipo anthu enanso ambiri akukhulupirira. Kodi mungamve bwanji? N’zosachita kufunsa kuti bodza limeneli lingakupwetekeni kwambiri. Chitsanzo chimenechi chingatithandize kumvetsa mmene Yehova anamvera mbiri yake itaipitsidwa. Mmodzi wa ana ake auzimu ananena bodza lokhudza iyeyo kwa Hava, ndipo Hava anakhulupirira bodzalo. Bodzalo linachititsa kuti makolo athu oyambawo asamvere Yehova. Zotsatira zake n’zakuti anthu onse anachimwa ndipo amafa. (Gen. 3:1-6; Aroma 5:12) Mavuto onse omwe timaona m’dzikoli monga imfa, nkhondo ndi zinthu zina zomvetsa chisoni, zinayamba chifukwa cha bodza lomwe Satana anafalitsa. Kodi Yehova anamva kupweteka chifukwa cha bodzali ndi zotsatirapo zake? Mosakayikira zinamupweteka. Komabe Yehova sanapse mtima kapena kusunga chakukhosi. Ndipotu iye nthawi zonse ndi “Mulungu wachimwemwe.”—1 Tim. 1:11. w24.02 8 ¶1-2

Loweruka, May 24

Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?—Gen. 39:9.

Kodi mungatani kuti mukhalebe okhulupirika ngati Yosefe? Muzisankhiratu panopa zimene mungachite mutakumana ndi mayesero. Muziphunzira kukana mwamsanga zinthu zimene Yehova amadana nazo ndipo musamaziganizire n’komwe. (Sal. 97:10; 119:165) Zimenezi zidzakuthandizani kuti musachite tchimo. N’kutheka kuti inuyo mumadziwa kuti munapeza choonadi ndipo mukufuna kutumikira Yehova ndi mtima wanu wonse koma mukuzengereza kuti mudzipereke komanso kubatizidwa. Ngati ndi choncho, mungachite zimene Mfumu Davide anachita. Mungapemphe Yehova kuti: “Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga. Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa. Muone ngati mwa ine muli chilichonse choipa, ndipo munditsogolere mʼnjira yamuyaya.” (Sal. 139:23, 24) Yehova amadalitsa anthu omwe “amamufunafuna ndi mtima wonse.” Mukamayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu choti mudzipereke ndiponso kubatizidwa, mumasonyeza kuti mumamufunafuna ndi mtima wonse.—Aheb. 11:6. w24.03 6 ¶13-15

Lamlungu, May 25

Iye safunikira kupereka [nsembe] tsiku ndi tsiku.​—Aheb. 7:27.

Mkulu wa ansembe anali ndi udindo woimira anthu kwa Mulungu. Mkulu wa ansembe woyamba wa Aisiraeli anali Aroni ndipo anasankhidwa ndi Yehova pamene chihema chinayamba kugwira ntchito. Koma mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo anafotokoza, “pankafunika ansembe ambiri olowa m’malo chifukwa imfa inkachititsa kuti munthu asapitirize kukhala wansembe.” (Aheb. 7:23-26) Popeza sanali angwiro, akulu a ansembewo ankafunikanso kumapereka nsembe za machimo awo. Apa m’pamene akulu a ansembe a Aisiraeli akusiyana kwambiri ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba, yemwe ndi Yesu Khristu. Monga Mkulu wa Ansembe, Yesu Khristu ndi “mtumiki wam’malo oyerawo komanso m’chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova osati munthu.” (Aheb. 8:1, 2) Paulo anafotokoza kuti “popeza iye adzakhala ndi moyo mpaka kalekale, palibe wansembe amene adzamulowe m’malo.” Anapitiriza kuti mosiyana ndi ansembe a Chiisiraeli, Yesu ndi “wosaipitsidwa, wosiyana ndi anthu ochimwa,” choncho “safunikira kupereka tsiku ndi tsiku nsembe” za machimo ake. w23.10 26 ¶8-9

Lolemba, May 26

Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka.—Chiv. 21:1.

“Kumwamba kwakale” kukuimira maboma a anthu omwe amachita zinthu motsogoleredwa ndi Satana ndi ziwanda zake. (Mat. 4:8, 9; 1 Yoh. 5:19) Ndipo Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko lapansi” ponena za anthu. (Gen. 11:1; Sal. 96:1) Choncho “dziko lapansi lakale” likuimira anthu oipa omwe ali padzikoli. Sikuti Yehova adzangokonza zina ndi zina zokhudza “kumwamba” ndi “dziko lapansi” zomwe zilipozi. M’malomwake adzasintha, kapena kuti kuzichotseratu n’kubweretsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zomwe zikuimira boma latsopano komanso anthu olungama. Yehova adzasintha dzikoli komanso adzachititsa kuti anthu akhale atsopano powathandiza kuti akhale angwiro. Mogwirizana ndi zimene Yesaya ananena, dziko lonse lidzakhala lokongola ngati munda wa Edeni. Munthu aliyense payekha adzathandizidwanso kuti akhale watsopano. Olumala, amene ali ndi vuto losaona komanso losamva adzachiritsidwa ndipo ngakhale amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.—Yes. 25:8; 35:1-7. w23.11 4 ¶9-10

Lachiwiri, May 27

Khalani okonzeka.​—Mat. 24:44.

“Chisautso chachikulu” chidzayamba modzidzimutsa. (Mat. 24:21) Komabe, mosiyana ndi ngozi zina zadzidzidzi, si anthu onse omwe adzadzidzimuke ndi kuyambika kwa chisautso chachikulu. Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anachenjeza otsatira ake kuti azikonzekera za nthawiyi. Tikakhala okonzeka, zidzakhala zosavuta kupirira pa nthawiyo komanso kuthandiza ena kuti azipirira. (Luka 21:36) Tidzafunika kupirira kuti timvere Yehova n’kumakhulupirira kuti atiteteza. Nanga tidzatani ngati abale athu atataya zinthu zina kapena katundu wawo yense? (Hab. 3:17, 18) Tidzafunika kukhala achifundo kuti tiwapatse zimene akufunikira. Kodi tidzatani ngati mgwirizano wa mayiko utatiukira ndipo tikufunika kukhala ndi abale ndi alongo athu m’kanyumba kakang’ono kwa kanthawi? (Ezek. 38:10-12) Tidzafunika kuwasonyeza chikondi chachikulu kuti tidzapirire pa nthawi yovutayo. w23.07 2 ¶2-3

Lachitatu, May 28

Samalani kwambiri kuti mukamayenda, musamayende ngati anthu opanda nzeru koma ngati anthu anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.​—Aef. 5:​15, 16.

Anthu okwatirana angaphunzire pa chitsanzo cha Akula ndi Purisika, limene ndi banja lomwe Akhristu ambiri oyambirira ankalilemekeza. (Aroma 16:3, 4) Iwo ankalalikira, kuthandiza ena komanso kugwira ntchito limodzi. (Mac. 18:2, 3, 24-26) Ndipotu nthawi zonse Baibulo likamanena za Akula ndi Purisika, limawatchulira limodzi. Kodi anthu okwatirana angawatsanzire bwanji? Taganizirani zinthu zambiri zimene inuyo monga mwamuna kapena mkazi, mumafunika kuchita. Kodi n’zotheka kuti muzichitira limodzi zina mwa zinthu zimenezi monga banja, osati aliyense payekha? Mwachitsanzo, Akula ndi Purisika ankalalikira limodzi. Kodi inunso nthawi zambiri mumakonza zoti muzilalikira limodzi? Akula ndi Purisika ankagwiranso ntchito limodzi. Mwina inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simugwira ntchito yofanana, koma kodi mungamagwire limodzi ntchito zapakhomo? (Mlal. 4:9) Mukamathandizana ntchito inayake, mumagwirizana kwambiri ndiponso mumapeza mpata wocheza. w23.05 22-23 ¶10-12

Lachinayi, May 29

Ndikamachita mantha, ndimadalira inu.​—Sal. 56:3.

Tonsefe nthawi zina timachita mantha. Mwachitsanzo, pamene Mfumu Sauli inkafuna kupha Davide, iye anathawira mumzinda wa Afilisiti wa Gati. Posakhalitsa, Akisi yemwe anali mfumu ya ku Gati anamva kuti Davide anali msilikali wamphamvu yemwe ankatchulidwa mu nyimbo kuti anapha “masauzande ambirimbiri” a Afilisiti. Davide “anachita mantha kwambiri.” (1 Sam. 21:10-12) Iye ankaopa zimene Akisi angamuchitire. Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti alimbe mtima? Mu Salimo 56, Davide anafotokoza mmene ankamvera pamene anali ku Gati. Salimoli limafotokoza bwino chimene chinamuchititsa mantha komanso zimene zinamuchititsa kuti asiye kuchita manthawo. Atayamba kuopa, Davide anadalira Yehova. (Sal. 56:1-3, 11) Iye anali ndi zifukwa zabwino zomuchititsa kudalira Yehova. Mothandizidwa ndi Yehova, Davide anaganiza zochita zinthu zina zachilendo. Iye anayerekezera kukhala wamisala ndipo zimenezi zinamuthandiza. Tsopano Akisi sanaonenso Davide ngati munthu woopsa ndipo anamulola kuti azipita.—1 Sam. 21:13–22:1. w24.01 2 ¶1-3

Lachisanu, May 30

Oitanidwa aja, omwe ndi osankhidwa mwapadera ndiponso okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.​—Chiv. 17:14.

Kodi anthu amene akutchulidwa mulemba lalerowa ndi ndani? Amenewa ndi odzozedwa onse, omwe adzakhale atapita kumwamba. Choncho wodzozedwa womaliza akadzatengedwa kupita kumwamba pambuyo pa chisautso chachikulu, imodzi mwa ntchito yawo yoyamba idzakhala kumenya nkhondo. Akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba, iwo adzagwira ntchito limodzi ndi Khristu ndi angelo ake oyera pomenya nkhondo yomaliza yolimbana ndi adani a Mulungu. Tangoganizani, ali padzikoli, Akhristu ena odzozedwa anali achikulire komanso opanda mphamvu. Koma iwo akadzangopita kumwamba adzakhala zolengedwa zauzimu zamphamvu zomwe sizingafe ndipo adzamenya nkhondo limodzi ndi Mfumu yankhondo Yesu Khristu. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, iwo adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu pothandiza anthu kuti akhale angwiro. Mosakayikira, iwo adzachitira zinthu zabwino kwambiri abale ndi alongo awo kuposa mmene akanachitira ali padzikoli. w24.02 6-7 ¶15-16

Loweruka, May 31

Pitirizani kuyenda motsogoleredwa ndi mzimu, ndipo simudzachita zimene thupi lomwe si langwiro likulakalaka ngakhale pangʼono.—Agal. 5:16.

Anthu ena ngakhale kuti amakhala atakonzeka, amazengereza kuti adzipereke komanso kubatizidwa. Iwo angamaganize kuti, ‘Bwanji ngati pambuyo pake nditachita tchimo lalikulu n’kuchotsedwa?’ Ngati muli ndi maganizo amenewa, dziwani kuti Yehova adzakupatsani chilichonse chomwe mukufunikira kuti “mukhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene [iye] amafuna, kuti muzimusangalatsa pa chilichonse.” (Akol. 1:10) Iye adzakupatsaninso mphamvu kuti muzichita zoyenera. Yehova wasonyeza kuti angachite zimenezi chifukwa wathandizapo kale anthu ambiri kuti azichita zoyenera. (1 Akor. 10:13) N’chifukwa chake pamakhala anthu ochepa kwambiri omwe amachotsedwa mumpingo. Yehova amathandiza anthu ake kuti akhalebe okhulupirika. Munthu aliyense yemwe si wangwiro amayesedwa kuti achite zinthu zoipa. (Yak. 1:14) Komabe, mungathe kusankha zomwe mungachite mukakumana ndi mayesero. Mfundo ndi yakuti inuyo ndi amene muli ndi udindo wosankha zimene mukufuna kuchita pa moyo wanu. Ngakhale kuti ena amatsutsa zimenezi, mungathe kudziphunzitsa kuti musamalakelake zinthu zoipa. w24.03 5 ¶11-12

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena