Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es25 tsamba 37-46
  • April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Lachiwiri, April 1
  • Lachitatu, April 2
  • Lachinayi, April 3
  • Lachisanu, April 4
  • Loweruka, April 5
  • Lamlungu, April 6
  • Lolemba, April 7
  • Lachiwiri, April 8
  • Lachitatu, April 9
  • Lachinayi, April 10
  • Lachisanu, April 11
  • TSIKU LA CHIKUMBUTSO
    Dzuwa Litalowa
    Loweruka, April 12
  • Lamlungu, April 13
  • Lolemba, April 14
  • Lachiwiri, April 15
  • Lachitatu, April 16
  • Lachinayi, April 17
  • Lachisanu, April 18
  • Loweruka, April 19
  • Lamlungu, April 20
  • Lolemba, April 21
  • Lachiwiri, April 22
  • Lachitatu, April 23
  • Lachinayi, April 24
  • Lachisanu, April 25
  • Loweruka, April 26
  • Lamlungu, April 27
  • Lolemba, April 28
  • Lachiwiri, April 29
  • Lachitatu, April 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25 tsamba 37-46

April

Lachiwiri, April 1

Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? . . . Nanga n’chifukwa chiyani mwandipusitsa chonchi?​—Gen. 29:25.

Atumiki a Yehova otchulidwa m’Baibulo ankakumana ndi mavuto omwe sankawayembekezera. Taganizirani chitsanzo cha Yakobo. Bambo ake anamulamula kuti akwatire mmodzi wa ana aakazi a Labani, wachibale wawo yemwe ankalambira Yehova ndipo iwo anamutsimikizira kuti Yehova adzamudalitsa kwambiri. (Gen. 28:1-4) Choncho Yakobo anachita zinthu zoyenera. Iye anachoka ku Kanani kupita kwawo kwa Labani, yemwe anali ndi ana aakazi awiri, Leya ndi Rakele. Yakobo anakonda Rakele mwana wamng’ono wa Labani ndipo anavomera kuti agwirira ntchito bambo akewo zaka 7 kuti amukwatire. (Gen. 29:18) Koma zinthu sizinachitike mmene Yakobo ankaganizira. Labani anamupusitsa pomupatsa mwana wake wamkulu Leya kuti amukwatire. Labani analola kuti Yakobo akwatire Rakele patatha mlungu umodzi koma ngati angamugwirirenso ntchito zaka zina 7. (Gen. 29:26, 27) Labani sankachitanso zinthu mwachilungamo ndi Yakobo. Iye anachitira Yakobo zinthu zopanda chilungamozi kwa zaka 20.—Gen. 31:41, 42. w23.04 15 ¶5

Lachitatu, April 2

Mukhuthulireni zonse zamumtima mwanu.​—Sal. 62:8.

Kodi tingapite kwa ndani tikamafuna malangizo komanso kulimbikitsidwa? Tikudziwa yankho la funso limeneli. Tikhoza kupemphera kwa Yehova. Ndipotu iye amatiuza kuti tizichita zimenezo. Amafuna kuti tizipemphera kwa iye nthawi zonse kapena kuti “mosalekeza.” (1 Ates. 5:17) Tingapemphere kwa iye momasuka komanso kumupempha kuti azititsogolera pa mbali iliyonse ya moyo wathu. (Miy. 3:5, 6) Popeza Yehova ndi Mulungu woolowa manja, satiikira malire a nthawi zomwe tingapemphere kwa iye. Yesu ankadziwa kuti Yehova amaona kuti kupemphera n’kofunika kwambiri. Asanabwere padziko lapansi, iye ankaona Atate wake akuyankha mapemphero a amuna ndi akazi okhulupirika. Mwachitsanzo, Yesu anali pambali pa Atate wake pomwe iwo ankayankha mapemphero ochokera pansi pa mtima a Hana, Davide, Eliya komanso anthu ena. (1 Sam. 1:10, 11, 20; 1 Maf. 19:4-6; Sal. 32:5) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera pafupipafupi komanso ndi chikhulupiriro.—Mat. 7:7-11. w23.05 2 ¶1, 3

Lachinayi, April 3

Kuopa anthu ndi msampha, koma amene amakhulupirira Yehova adzatetezedwa.—Miy. 29:25.

Mkulu wa Ansembe Yehoyada ankaopa Yehova. Umboni wa zimenezi unaonekera pamene Ataliya, mwana wa Yezebeli, analanda ufumu ku Yuda. Iye anali wankhanza ndipo chifukwa chofunitsitsa kukhala wolamulira, anafika mpaka poyesa kupha ana onse a mfumu, omwe anali zidzukulu zake. (2 Mbiri 22:10, 11) Yehoasi, yemwe anali mmodzi wa anawo, sanaphedwe chifukwa choti Yehosabati mkazi wa Yehoyada anamupulumutsa. Iye ndi mwamuna wake anamubisa n’kumamusamalira. Zimene Yehoyada ndi Yehosabati anachita zinathandiza kuteteza mzere wa mafumu wa Davide. Yehoyada anali wokhulupirika kwa Yehova ndipo sanachite mantha ndi Ataliya. Pamene Yehoasi anali ndi zaka 7, Yehoyada anasonyezanso kuti anali wokhulupirika kwa Yehova. Iye anakonza zoti Yehoasi akhale mfumu. Ngati izi zikanatheka ndiye kuti munthu woyenerera akanakhala pampando wachifumu wa Davide. N’zoonekeratunso kuti ngati zikanalephereka, Yehoyada akanaphedwa. Mothandizidwa ndi Yehova, zimene anakonzazi zinatheka. w23.06 17 ¶12-13

Lachisanu, April 4

Mpaka mutadziwa kuti Mulungu Wam’mwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.​—Dan. 4:25.

Zimene Danieli anauza Mfumu Nebukadinezara zikanachititsa kuti azimuona ngati woukira ndipo akanamupha. Koma iye analimbabe mtima ndipo anafotokoza tanthauzo la malotowo. Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza Danieli kuti akhale wolimba mtima kwa moyo wake wonse? Ayenera kuti ali mwana, anaphunzira pa chitsanzo cha mayi ake ndi bambo ake. (Deut. 6:6-9) Sikuti Danieli ankangodziwa malamulo akuluakulu a m’Chilamulo monga Malamulo Khumi. Koma ankadziwanso zambiri zokhudza zimene Aisiraeli ankayenera kudya ndi zimene sankayenera kudya. (Lev. 11:4-8; Dan. 1:8, 11-13) Danieli anaphunziranso mbiri ya anthu a Mulungu ndipo ankadziwa zomwe zinawachitikira chifukwa cholephera kutsatira mfundo za Yehova. (Dan. 9:10, 11) Zimene zinamuchitikira pa moyo wake zinamutsimikizira kuti Yehova komanso angelo ake amphamvu ankamuthandiza.—Dan. 2:19-24; 10:12, 18, 19. w23.08 3 ¶5-6

Loweruka, April 5

Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.—Miy. 11:2.

Rabeka anali mkazi wanzeru komanso wosazengereza pochita zinthu kwa moyo wake wonse. (Gen. 24:58; 27:5-17) Koma anali waulemu ndiponso wogonjera. (Gen. 24:17, 18, 65) Inunso mukakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo ngati Rabeka, mudzakhala chitsanzo chabwino m’banja lanu komanso mumpingo. Kudziwa malire athu ndi khalidwe lina lofunika kwambiri kuti Mkhristu akhale wolimba mwauzimu. Esitere anali mtumiki wa Mulungu wokhulupirika yemwe ankadziwa malire ake. Khalidwe limeneli linamuthandiza kuti asachite zinthu modzikuza. Iye anamvetsera komanso kutsatira malangizo ochokera kwa Moredikayi, yemwe anali wachibale wake wamkulu. (Esitere 2:10, 20, 22) Inunso mukhoza kusonyeza kuti mumadziwa malire anu mukamapempha malangizo ndiponso kuwatsatira. (Tito 2:3-5) Esitere anasonyezanso kuzindikira malire ake m’njira ina. Iye anali “wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri” koma sankachita zinthu modzionetsera.—Esitere 2:7, 15. w23.12 19 ¶6-8

Lamlungu, April 6

Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.​—1 Yoh. 3:20.

Kudziimba mlandu ndi cholemera chimene tiyenera kutaya. Ngati taulula tchimo lathu, kulapa komanso kuchita zonse zofunika kuti tisalibwerezenso, tingakhale otsimikiza kuti Yehova watikhululukira. (Mac. 3:19) Tikachita zimenezi, Yehova samafuna kuti tizipitiriza kudziimba mlandu. Iye amadziwa kuti kumangokhalira kudziimba mlandu n’koopsa. (Sal. 31:10) Ngati titakhala ndi chisoni chopitirira malire, tikhoza kusiya kuthamanga pampikisano wokalandira moyo. (2 Akor. 2:7) Mukamadziimba mlandu kwambiri, muziganizira mfundo yakuti Mulungu ‘amakhululukiradi.’ (Sal. 130:4) Iye akakhululukira amene alapa mochokera pansi pa mtima amalonjeza kuti: “Machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sangadzakuimbeninso mlandu chifukwa cha machimo omwe munachita m’mbuyomu. Choncho musamaganize kuti mavuto omwe mukukumana nawo chifukwa chakuti munachimwa, ndi umboni wakuti sanakukhululukireni. Ndipo musamadzikwiyire kapena kudzilanga chifukwa chakuti zimene munalakwitsa m’mbuyo mwina zikuchititsa kuti musamachite zambiri potumikira Yehova panopa. Yehova samangokhalira kuganizira machimo anu, ndipo inunso simuyenera kutero. w23.08 30-31 ¶14-15

Lolemba, April 7

Khalani olimba ndiponso osasunthika.​—1 Akor. 15:58.

Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, a Mboni za Yehova omwe ankamvera malangizo operekedwa ndi gulu lathu sankakhala ndi nkhawa ngati mmene zinalili ndi anthu omwe ankamvetsera mfundo zabodza. (Mat. 24:45) Tiyenera kupitiriza kuika maganizo athu pa “zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri.” (Afil. 1:9, 10) Zinthu zosokoneza zingatiwonongere nthawi komanso kutichititsa kuti tisamachite chidwi ndi zinthu zofunika kwambiri. Zinthu zomwe timachita nthawi zonse monga kudya, kumwa, zosangalatsa ndiponso ntchito zingatisokoneze ngati titayamba kuziika pamalo oyamba pa moyo wathu. (Luka 21:34, 35) Kuwonjezera pamenepo, tsiku lililonse timamva nkhani zokhudza mikangano ya anthu komanso zandale. Tisamalole kuti tizisokonezedwa ndi nkhani zimenezi. Ngati sitingatero, tikhoza kuyamba kulowerera mu zimenezi m’maganizo ndi mumtima mwathu. Satana amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pofuna kusokoneza cholinga chathu choti tizichita zoyenera. w23.07 16-17 ¶12-13

Lachiwiri, April 8

Muzichita zimenezi pondikumbukira.​—Luka 22:19.

Kwa anthu a Yehova, tsiku lokumbukira imfa ya Khristu ndi lofunika kwambiri pa chaka. Ndi mwambo wokhawo umene Yesu analamula otsatira ake kuti aziuchita. (Luka 22:19, 20) Umatikumbutsa zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira nsembe ya Yesu. (2 Akor. 5:14, 15) Timakhalanso ndi mwayi ‘wolimbikitsana’ ndi abale ndi alongo athu. (Aroma 1:12) Ndipo anthu ambiri achidwi amayamba kuyenda pa njira yopita ku moyo chifukwa cha zimene aona komanso kumva pamwambowu. Ganiziraninso mmene mwambo wa Chikumbutso umathandizira abale ndi alongo kukhala ogwirizana padziko lonse. N’chifukwa chake timaona kuti mwambo wa Chikumbutso ndi wofunika kwambiri kwa ife. w24.01 8 ¶1-3

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Luka 19:​29-44

Lachitatu, April 9

Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.​—Yoh. 3:16.

Tikamaganizira kwambiri mtengo umene Yehova ndi Yesu anapereka m’pamene timamvetsa mmene iwo amakondera munthu aliyense payekha. (Agal. 2:20) Dipo ndi mphatso imene anapereka chifukwa cha chikondi chawo. Yehova wasonyeza kuti amatikonda popereka nsembe Yesu, yemwe ndi wamtengo wapatali kwambiri kwa iye. Iye analola kuti Mwana wake avutike komanso aphedwe chifukwa cha ifeyo. Yehova samangomva mumtima mwake kuti amatikonda koma amatiuzanso mmene amatikondera. (Yer. 31:3) Yehova anatikokera kwa iye chifukwa chakuti amatikonda. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 7:7, 8.) Palibe chinthu chilichonse kapena munthu aliyense amene angatisiyanitse ndi chikondi chake. (Aroma 8:38, 39) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za chikondichi? w24.01 28 ¶10-11

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Luka 19:​45-48; Mateyu 21:​18, 19; 21:​12, 13

Lachinayi, April 10

Ndipo anaperekanso chiyembekezo chakuti chilengedwecho chidzamasulidwa.—Aroma 8:​20, 21.

Akhristu odzozedwa amasangalala ndi chiyembekezo chawo chopita kumwamba. Mmodzi mwa iwo, yemwe ndi M’bale Frederick Franz, anafotokoza mmene ankamvera chifukwa cha chiyembekezochi, ndipo anati: “Chiyembekezo chathu n’chotsimikizirika ndipo chidzakwaniritsidwa kwa aliyense wa a 144,000, omwe ndi kagulu ka nkhosa. Zimene tikuyembekezerazi zidzakhala zabwino kwambiri kuposa mmene tikuganizira.” Mu 1991, M’bale Franz ananenanso kuti: “Sitinaleke kuona kufunika kwa chiyembekezo chimenechi. Timachiyamikira mowonjezeraka kwa nthawi yonse yomwe tiyenera kuyembekezera. Ndi chinthu choyenera kuchiyembekezera . . . ndimakonda kwambiri chiyembekezochi kuposa ndi kale lonse.” Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tili ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chomwe chimatichititsa kuti tizisangalala. Ndipotu tikhoza kumakhulupirira kwambiri zimene tikuyembekezera. w23.12 9 ¶6; 10 ¶8

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 20:​1-47

Lachisanu, April 11

N’zosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.​—Aheb. 10:4.

Pafupi ndi khomo la chihema panali guwa lamkuwa lomwe ankaperekerapo nsembe za nyama kwa Yehova. (Eks. 27:1, 2; 40:29) Koma nsembe zimenezi sizinkathandiza kuti machimo onse a anthu akhululukidwe. (Aheb. 10:1-3) Nsembe za nyama, zomwe zinkaperekedwa mobwerezabwereza pachihema zinkaimira nsembe imodzi imene idzayeretseretu machimo a anthu. Yesu ankadziwa kuti Yehova anamutumiza padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake ngati dipo n’cholinga choti awombole anthu. (Mat. 20:28) Choncho pa ubatizo wake, Yesu anadzipereka kuti azichita zimene Yehova amafuna. (Yoh. 6:38; Agal. 1:4) Moyo wa Yesu unaperekedwa “kamodzi kokha” kuti uphimbiretu machimo a munthu aliyense amene amakhulupirira Khristu.—Aheb. 10:5-7, 10. w23.10 26-27 ¶10-11

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Luka 22:​1-6; Maliko 14:​1, 2, 10, 11

TSIKU LA CHIKUMBUTSO
Dzuwa Litalowa
Loweruka, April 12

Mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.​—Aroma 6:23.

Patokha sitikanatha kudzipulumutsa ku uchimo ndi imfa. (Sal. 49:7, 8) Choncho pokonza zoti Yesu adzapereke moyo wake chifukwa cha ife, Yehova ndi Mwana wake wokondedwa anapereka mtengo wokwera kwambiri. Tikamaganizira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anatichitirazi, tingamayamikirenso kwambiri dipo. Adamu, atachimwa, anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Iye sanataye moyo wake wokha, koma anatayanso wa ana ake onse. Kuti abwezeretse zimene Adamu anataya, Yesu anapereka nsembe moyo wake wangwiro. Pa nthawi yonse yomwe anali padzikoli, iye “sanachite tchimo ndipo sananenepo mawu achinyengo.” (1 Pet. 2:22) Pa nthawi ya imfa yake, Yesu anali wangwiro ngati mmene Adamu analili asanachimwe, choncho zinali zotheka kubwezeretsa moyo umene Adamu anataya.—1 Akor. 15:45; 1 Tim. 2:6. w24.01 10 ¶5-6

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Luka 22:​7-13; Maliko 14:​12-16 (Zochitika pa Nisan 14 dzuwa litalowa) Luka 22:​14-65

Lamlungu, April 13

Iye analowa m’malo oyera ndi magazi ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.​—Aheb. 9:12.

Yesu ataukitsidwa analowa m’Malo Oyera Koposa a kachisi wauzimu. Apa titha kuona kuti njira imene Yehova anakonza yoti pakhale kulambira koyera kudzera mu nsembe ya dipo ndiponso udindo wa Yesu Khristu monga Mkulu wa Ansembe, ndi yapamwamba kwambiri. Mkulu wa ansembe ku Isiraeli ankalowa m’Malo Oyera Koposa opangidwa ndi anthu atatenga magazi a nyama koma Yesu “analowa kumwamba kwenikweniko,” komwe ndi malo oyera kuposa ena alionse, kukaonekera pamaso pa Yehova. Kumwambako anakapereka kwa Mulungu ufulu umene anali nawo wokhala ndi moyo monga munthu wangwiro padziko lapansi ndipo anachita zimenezi m’malo mwa ifeyo “kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.” (Aheb. 9:24-26) Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padzikoli, tonsefe tikhoza kulambira Yehova m’kachisi wake wauzimu. w23.10 28 ¶13-14

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Luka 22:​66-71

Lolemba, April 14

Tiyeni tizifika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo tizipemphera ndi ufulu wa kulankhula.—Aheb. 4:16.

Taganizirani za udindo wa Yesu monga Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wachifundo. Kudzera mwa iye tikhoza kufika ku “mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu” popemphera kwa Mulungu kuti atichitire chifundo komanso kuti atithandize pa nthawi yoyenera. (Aheb. 4:14-15) Choncho tisamalole kuti tsiku lidutse tisanaganizire zimene Yehova ndi Yesu atichitira komanso zimene akutichitira panopa. Chikondi chawo chizitifika pamtima ndipo chizitichititsa kukhala akhama potumikira Mulungu komanso kumulambira. (2 Akor. 5:14, 15) Njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti timayamikira kuthandiza ena kuti akhale a Mboni za Yehova komanso ophunzira a Yesu. (Mat. 28:19, 20) Izi ndi zimene mtumwi Paulo anachita. Iye ankadziwa kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu osiyanasiyana apulumuke n’kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4. w23.10 22-23 ¶13-14

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:​62-66

Lachiwiri, April 15

Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.​—Chiv. 21:4.

Ambirife tikamalalikira timakonda kuwerengera anthu lemba lolimbikitsali powafotokozera mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. Kodi tingatsimikizire bwanji kuti lonjezo la pa Chivumbulutso 21:3, 4 lidzakwaniritsidwadi? Yehova atapereka lonjezoli, anaperekanso zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizilikhulupirira. Kodi anapereka zifukwa ziti? M’mavesi otsatira muli zifukwa zotichititsa kukhulupirira lonjezo la Yehova lokhuza Paradaiso. M’mavesiwo timawerenga kuti: “Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.’ Iye anandiuza kuti: ‘Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.’”—Chiv. 21:5, 6a. w23.11 3 ¶3-5

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Luka 24:​1-12

Lachitatu, April 16

Upitirize kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.—Tito 2:6.

Njira ina imene wachinyamata angasonyezere kuti ndi woganiza bwino, ndi zimene amasankha pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa. Nthawi zambiri mafashoni amapangidwa kapena kulimbikitsidwa ndi anthu amene salemekeza Yehova kapena a makhalidwe oipa. Mafashoni omwe amapangawo, amakhala a zovala zothina kapena zochititsa amuna kuoneka ngati akazi. Koma Mkhristu amene akukula mwauzimu amasankha zovala motsatira mfundo za m’Baibulo komanso chitsanzo cha anthu abwino mumpingo. Iye angadzifunse kuti: ‘Kodi zovala zanga zimasonyeza kuti ndine woganiza bwino komanso woganizira ena? Kodi kavalidwe kanga kamathandiza anthu kuzindikira mosavuta kuti ndinadzipereka kuti ndizitumikira Mulungu?’ (1 Akor. 10:31-33) Wachinyamata woganiza bwino amakhala wolemekezeka pamaso pa abale ndi alongo komanso Mulungu. w23.12 26 ¶7

Lachinayi, April 17

Ufumu wanga si wam’dzikoli. Ufumu wanga ukanakhala wam’dzikoli, atumiki anga akanamenya nkhondo.​—Yoh. 18:36.

M’mbuyomu, “mfumu yakum’mwera” yakhala ikuzunza anthu a Yehova. (Dan. 11:40) Mwachitsanzo, zisanafike zaka za m’ma 1950, abale athu ambiri anamangidwa chifukwa chokana kutenga nawo mbali n’zochitika za m’dzikoli ndipo ana ena a Mboni ankachotsedwa sukulu pachifukwa chomwechi. Komabe m’zaka zaposachedwapa, atumiki a Yehova omwe akukhala m’madera olamuliridwa ndi mfumuyi akhala akuyesedwanso m’njira zina zosaonekera. Mwachitsanzo, pa nthawi ya zisankho Mkhristu angayesedwe kuti akhale kumbali inayake ya chipani chandale kapena munthu winawake yemwe akupikisana nawo. N’kutheka kuti sangafike pokavota, komabe mumtima ndi m’maganizo mwake angakhale kuti ali mbali inayake. Apatu n’zofunika kwambiri kuti tisamalowerere ndale, osati n’zochita zathu zokha koma ngakhalenso m’maganizo ndi mumtima mwathu.—Yoh. 15:18, 19. w23.08 12 ¶17

Lachisanu, April 18

Atamandike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.​—Sal. 68:19.

Pamene tikuthamanga pampikisano wokalandira moyo, tiyenera ‘kuthamanga m’njira yoti tikalandire mphotoyo.’ (1 Akor. 9:24). Yesu ananena kuti tikhoza ‘kulemedwa ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo.’ (Luka 21:34) Zimenezi komanso malemba ena zingakuthandizeni kudziwa zinthu zimene mungafunike kusintha pamene mukuthamanga pampikisano wokalandira moyo. Tingakhale otsimikiza kuti tidzapambana mpikisano wokalandira moyo, chifukwa Yehova adzatipatsa mphamvu zimene tikufunikira. (Yes. 40:29-31) Choncho musachepetse liwiro lanu. Muzitsanzira mtumwi Paulo, yemwe anathamanga mwakhama kuti akapeze mphoto yomwe anamuikira patsogolo pake. (Afil. 3:13, 14) Palibe yemwe angakuthamangireni mpikisanowu, komabe Yehova angakuthandizeni kuti mupambane. Iye angakuthandizeninso kunyamula katundu wanu komanso kutaya zolemera zosafunika. Popeza Yehova ali kumbali yanu, mungakwanitse kuthamanga mopirira komanso kupambana. w23.08 31 ¶16-17

Loweruka, April 19

Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.​—Eks. 20:12.

Yesu ali ndi zaka 12, makolo ake anamusiya ku Yerusalemu. (Luka 2:46-52) Yosefe ndi Mariya anali ndi udindo woonetsetsa kuti ana awo onse ali nawo limodzi pamene ankabwerera kunyumba kuchokera kuchikondwerero. Iwo atamupeza, Mariya anamuimba Yesu mlandu kuti anawavutitsa. Yesu akanatha kunena kuti iwo sanachite chilungamo. M’malomwake anayankha makolo akewo mwachidule komanso mwaulemu. Koma Yosefe ndi Mariya “sanamvetse zimene anali kuwauzazo.” Ngakhale zinali choncho, Yesu “anapitiriza kuwamvera.” Achinyamata,kodi zimakuvutani kumvera makolo anu chifukwa chakuti amalakwitsa zinthu zina kapena sakumvetsani? Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Muziganizira mmene Yehova amamvera. Baibulo limanena kuti mukamamvera makolo anu ‘mumakondweretsa Ambuye.’ (Akol. 3:20) Yehova amadziwa ngati makolo anu sakumvetsani kapenanso ngati amakupatsani malamulo ovuta kuwatsatira. Komabe mukasankha kuwamvera, iye amasangalala. w23.10 7 ¶5-6

Lamlungu, April 20

Akhale ololera ndipo azikhala ofatsa kwa anthu onse.​—Tito 3:2.

Mnzanu wakusukulu anganene kuti a Mboni za Yehova ayenera kusintha maganizo awo pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Tiyenera kumutsimikizira kuti timadziwa kuti aliyense ali ndi ufulu, ndipo timalemekeza zimene ena asankha. (1 Pet. 2:17) Kenako tingakambirane naye mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira ifeyo kukhala osangalala. Mukakumana ndi munthu yemwe akukutsutsani kwambiri musamafulumire kuganiza kuti mukudziwa zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mnzanu wakusukulu wakuuzani kuti si nzeru kukhulupirira kuti kuli Mulungu. Kodi muyenera kuganiza kuti iye amakhulupirira kwambiri kuti zamoyo zinachita kusintha komanso kuti akudziwa zambiri pa nkhaniyo? Mwina zenizeni zingakhale zakuti iye anangomva kwa anthu ena ndipo sanafufuzepo. M’malo mokangana naye pa nkhaniyo, mukhoza kupeza njira yomufotokozera zinthu zina zoti akaziganizire. Mungamusonyeze nkhani zokhudza chilengedwe pa jw.org. Pambuyo pake mwina angakonde kuti mukambirane nkhani inayake kapenanso vidiyo yopezeka pawebusaitiyi. Kukambirana naye mwaulemu kungachititse kuti asinthe maganizo ake. w23.09 17 ¶12-13

Lolemba, April 21

Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka. Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.​—Sal. 86:5.

Tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa komanso kutigwiritsa ntchito ngakhale kuti tinalakwitsapo zinazake. Chongofunika ndi kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikonze zomwe tinalakwitsazo, n’kupitiriza kumudalira. (Miy. 28:13) Samisoni sanali wangwiro, komabe sanasiye kuchita zonse zomwe akanatha potumikira Yehova ngakhale kuti analakwitsa zinthu pa nkhani yokhudza Delila. Yehova sanasiye kumugwiritsa ntchito. Anamugwiritsanso ntchito pochita zinthu zina zamphamvu. Yehova ankamuonabe monga munthu wokhulupirika ndipo analola kuti dzina lake lilembedwe pagulu la anthu okhulupirika otchulidwa mu Aheberi chaputala 11. N’zosangalatsa kudziwa kuti timatumikira Atate wathu wachikondi, yemwe amafunitsitsa kutipatsa mphamvu makamaka tikafooka. Choncho mofanana ndi Samisoni, tiyeni tizipempha Yehova kuti: “Chonde ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu.”—Ower. 16:28. w23.09 7 ¶18-19

Lachiwiri, April 22

[Muzikumbukira] nthawi zonse kubwera kwa tsiku la Yehova.​—2 Pet. 3:12.

Tikamakumbukira kuti tsiku la Yehova lili pafupi, timafunitsitsa kuuza ena uthenga wabwino. Komabe nthawi zina timachita mantha kuti tilalikire. Chifukwa chiyani? Mwina tingamaope zimene anthu angaganize kapena kuchita. Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso Petulo. Pa usiku womwe Yesu ankaimbidwa mlandu, Petulo sankafuna kuti anthu ena adziwe kuti anali wophunzira wake ndipo mobwerezabwereza anakana kuti sankamudziwa. (Mat. 26:69-75) Koma pambuyo pake mtumwi yemweyu ndi amene analemba motsimikiza kuti: “Musaope zimene iwo amaopa, ndipo musade nazo nkhawa.” (1 Pet. 3:14) Mawu akewa akutilimbikitsa kuti ifenso tingathe kusiya kuopa anthu. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamaope anthu? Petulo anati: “Muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.” (1 Pet. 3:15) Zimenezi zikuphatikizapo kuganizira udindo komanso mphamvu zimene Ambuye ndi Mfumu yathu Khristu Yesu ali nazo. w23.09 27-28 ¶6-8

Lachitatu, April 23

Nkhani zachiwerewere komanso chonyansa chamtundu uliwonse . . . zisatchulidwe nʼkomwe pakati panu.—Aef. 5:3.

Tiyenera kukhala osamala kuti tisamachite zinthu zomwe ndi “ntchito zosapindulitsa zamumdima.” (Aef. 5:11) Zimene zachitikirapo anthu ena zikusonyeza kuti munthu amene amakonda kuona, kumvetsera kapena kulankhula za zinthu zodetsa kapena zachiwerewere, zimakhala zosavuta kuti achite zinthu zoipa. (Gen. 3:6; Yak. 1:14, 15) Dziko la Satanali limafuna kutipusitsa kuti tizikhulupirira kuti zimene Yehova amaona kuti ndi zoipa komanso zodetsa ndi zabwinobwino. (2 Pet. 2:19) Njira imodzi yomwe Mdyerekezi wakhala akugwiritsa ntchito ndi kusokoneza anthu akuti asamathe kuzindikira choyenera ndi chosayenera. (Yes. 5:20; 2 Akor. 4:4) Mpake kuti mafilimu ambiri, mapulogalamu a pa TV komanso pa intaneti amalimbikitsa mfundo zosemphana ndi mfundo zolungama za Yehova. Satana amafuna kutichititsa kuti tiziganiza kuti makhalidwe oipa komanso achiwerewere omwe ndi ofala m’dzikoli, ndi osaopsa.—Aef. 5:6. w24.03 22 ¶8-10

Lachinayi, April 24

Utumiki umene amuna amenewa akuchita uli ngati chifaniziro ndiponso chithunzi cha zinthu zakumwamba.​—Aheb. 8:5.

Chihema chinali chitenti chimene Aisiraeli ankanyamula akamachoka malo ena kupita ena. Iwo anachigwiritsa ntchito kwa zaka pafupifupi 500, mpaka pamene kachisi weniweni anamangidwa ku Yerusalemu. (Eks. 25:8, 9; Num. 9:22) Chihema ndi malo amene Aisiraeli ankakumana kuti akalambire komanso kupereka nsembe. (Eks. 29:43-46) Koma chihemacho chinkaimiranso zinthu zina zazikulu. Chinali “chithunzi cha zinthu zakumwamba” ndipo chinkaimira kachisi wamkulu wa Yehova. Mtumwi Paulo ananena kuti “chihema chimenecho chinali chifaniziro cha nthawi inoyo.” (Aheb. 9:9) Choncho pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a Chiheberiwa, kachisi wauzimuyu anali alipo kale. Kachisiyu anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E. M’chaka chimenechi Yesu anabatizidwa, anadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kutumikira ngati “mkulu wa ansembe wapamwamba” m’kachisi wauzimu wa Yehova.—Aheb. 4:14; Mac. 10:37, 38. w23.10 25-26 ¶6-7

Lachisanu, April 25

Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.​—Afil. 4:5.

Kuti tipitirize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, Akhristufe tiyenera kukhala ololera. Tingachite zimenezi povomereza zinthu zikasintha pa moyo wathu komanso kulemekeza maganizo a ena ndiponso zimene asankha. Monga atumiki a Yehova timafuna kukhala ololera. Timafunanso kukhala odzichepetsa komanso oona mtima. Yehova amatchulidwa kuti “Thanthwe” chifukwa choti ndi wosasunthika. (Deut. 32:4) Komabe iye ndi wololera. Pamene zinthu zikusintha m’dzikoli, Mulungu wathu nayenso akupitiriza kusintha mmene amachitira zinthu kuti akwaniritse cholinga chake. Yehova analenga anthu m’chifaniziro chake, choncho nawonso amatha kusintha zinthu zikasintha. Iye anatipatsa mfundo za m’Baibulo zomveka bwino zomwe zimatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru, kaya tikukumana ndi mavuto otani. Chitsanzo chimene Yehova amatipatsa komanso mfundo zake ndi umboni wakuti ngakhale kuti iye ndi “Thanthwe,” ndi wololera. w23.07 20 ¶1-3

Loweruka, April 26

Nkhawa zitandichulukira, munanditonthoza komanso kundisangalatsa.​—Sal. 94:19.

M’Baibulo, Yehova amadziyerekezera ndi mayi wachikondi. (Yes. 66:12, 13) Taganizirani za mayi yemwe amasamalira mwana wake mwachikondi komanso amaonetsetsa kuti wamupatsa zimene akufunikira. Ifenso tikamamva ululu sitikayikira kuti Yehova amatisonyeza chikondi. Iye sasiya kutikonda tikalakwitsa zinazake. (Sal. 103:8) Aisiraeli ankakhumudwitsa Yehova mobwerezabwereza. Koma iye anasonyeza kuti ankakonda kwambiri anthu osalapawa powauza kuti: “Ndinayamba kukuona kuti ndiwe wamtengo wapatali, unalemekezedwa ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4, 5) Chikondi cha Yehova sichinasinthe. Ngakhale tilakwitse kwambiri zinthu, tikalapa n’kubwerera kwa iye, tidzaona kuti amatikondabe. Iye amatilonjeza kuti ‘adzatikhululukira ndi mtima wonse.’ (Yes. 55:7) Baibulo limafotokoza kuti akakhululuka zimakhala kuti ‘nyengo zotsitsimutsa zabwera kuchokera kwa Yehova.’—Mac. 3:19. w24.01 27 ¶4-5

Lamlungu, April 27

Dzanja la Yehova Mulungu wanga linkandithandiza.​—Ezara 7:28.

Yehova akhoza kutithandiza tikakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, tikamapempha abwana athu kuti tikapezeke kumsonkhano wachigawo kapena tikamawapempha nthawi yoti tizikapezeka pamisonkhano yampingo, timam’patsa Yehova mpata woti atithandize ndipo tikhoza kudabwa ndi mmene zinthu zingayendere. Zikatero timayambanso kudalira kwambiri Yehova. Ezara anali wodzichepetsa ndipo ankapempha Yehova kuti amuthandize. Nthawi iliyonse yomwe wapanikizika kwambiri chifukwa cha maudindo ake, iye ankapemphera kwa Yehova modzichepetsa. (Ezara 8:21-23; 9:3-5) Chifukwa cha zimenezi anthu ena ankakhala ofunitsitsa kumuthandiza komanso kutsanzira chikhulupiriro chake. (Ezara 10:1-4) Tikaona kuti tikudera nkhawa za mmene tingapezere zinthu zofunika pa moyo kapena mmene tingatetezere banja lathu, tizipemphera kwa Yehova ndipo tisamakayikire kuti atiyankha. w23.11 18 ¶15-17

Lolemba, April 28

Abulamu anakhulupirira zimene Yehova anamuuza, ndipo Mulunguyo anamuona kuti ndi wolungama.​—Gen. 15:6.

Yehova satiuza kuti ngati tikufuna kukhala olungama, tizichita ndendende zimene Abulahamu anachita. Pali njira zambiri zomwe tingasonyezere chikhulupiriro mwa zochita zathu. Tingalandire ndi manja awiri anthu atsopano omwe abwera mumpingo wathu, kuthandiza abale ndi alongo omwe akumana ndi mavuto komanso kuchitira zabwino anthu a m’banja lathu, ndipo zonsezi zingachititse kuti Yehova azisangalala nafe ndiponso kutidalitsa. (Aroma 15:7; 1 Tim. 5:4, 8; 1 Yoh. 3:18) Njira ina yomwe tingasonyezere bwino kuti tili ndi chikhulupiriro ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira. (1 Tim. 4:16) Tonsefe tingasonyeze mwa zochita zathu kuti timakhulupirira kuti zimene Yehova analonjeza zidzachitika komanso kuti amachita zinthu m’njira yabwino kwambiri. Tikamachita zimenezi tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzationa kuti ndife olungama ndiponso tidzakhala anzake. w23.12 2 ¶3; 6 ¶15

Lachiwiri, April 29

Uchite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.—1 Maf. 2:2.

Atatsala pang’ono kufa, Mfumu Davide analangiza Solomo zimene zili mulemba lalero. (1 Maf. 2:3) Abale onse masiku ano, angachite bwino kutsatira malangizo amenewa. Kuti akwanitse kuchita zimenezi, ayenera kuphunzira kumvera malamulo a Mulungu komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo pa zochita zawo zonse. (Luka 2:52) N’chifukwa chiyani Akhristu achinyamata ayenera kuyesetsa kuti akule mwauzimu? Mwamuna wa Chikhristu amakhala ndi maudindo ofunika kwambiri m’banja ndiponso mumpingo. Mosakayikira, inu Akhristu achinyamata muyenera kuti munaganizirapo za maudindo omwe mudzakhale nawo m’tsogolo. Mwina muli ndi cholinga chochita utumiki wa nthawi zonse, kukhala mtumiki wothandiza ndipo kenako kudzakhala mkulu mumpingo. Mwinanso mukufuna kudzakwatira n’kudzakhala ndi ana. (Aef. 6:4; 1 Tim. 3:1) Kuti zimenezi zitheke komanso zinthu zizikuyenderani bwino, muyenera kukula mwauzimu. w23.12 24 ¶1-2

Lachitatu, April 30

Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni.​—Aheb. 11:32.

Akulu anapatsidwa udindo wosamalira nkhosa zamtengo wapatali za Yehova. Amuna odziperekawa amayamikira mwayi wotumikira abale ndi alongo awo ndipo amachita khama kuti akhale ‘abusa omwe . . . amaweta’ nkhosa za Mulungu. (Yer. 23:4; 1 Pet. 5:2) Timayamikira kwambiri kukhala ndi amuna ngati amenewa m’mipingo yathu. Akulu angaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Gidiyoni, yemwe anali woweruza. (Aheb. 6:12; 11:32) Iye ankateteza komanso kutsogolera anthu a Mulungu. (Ower. 2:16; 1 Mbiri 17:6) Mofanana ndi Gidiyoni, akulu apatsidwa udindo wosamalira anthu a Mulungu pa nthawi yovuta kwambiri. (Mac. 20:28; 2 Tim. 3:1) Tingaphunzire zambiri kwa Gidiyoni pa nkhani ya kudzichepetsa komanso kumvera. Kupirira kwake kunayesedwa pamene ankagwira ntchito yake. Choncho kaya ndife mkulu kapena ayi, tonsefe tingamayamikire kwambiri akulu. Tingathandize abale akhamawa, omwe amagwira ntchito yotisamalira mumpingo.—Aheb. 13:17. w23.06 2 ¶1; 3 ¶3

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena