November
Loweruka, November 1
Mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.—Mat. 21:16.
Ngati ndinu makolo, muzithandiza ana anu kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. Nthawi zina pamisonkhano timaphunzira nkhani zikuluzikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena makhalidwe. Komabe pangathe kukhala ndime imodzi kapena ziwiri zomwe mwana akhoza kuyankhapo. Komanso muzithandiza ana anu kumvetsa chifukwa chake sangalozedwe nthawi iliyonse yomwe akweza dzanja. Kuwafotokozera zimenezi kungawathandize kuti asamakhumudwe ena akalozedwa m’malo mwa iwowo. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekere ndemanga zomwe zingalemekeze Yehova komanso zingalimbikitse Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafotokoze mwachidule zimene zinatichitikirapo, tizipewa kulankhula kwambiri zokhudza ifeyo. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malomwake, tiziyesetsa kuganizira kwambiri zokhudza Yehova, Mawu ake komanso anthu ake monga gulu. w23.04 24-25 ¶17-18
Lamlungu, November 2
Choncho tisapitirize kugona ngati mmene ena onse akuchitira, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.—1 Ates. 5:6.
Chikondi n’chofunika kuti tikhalebe maso komanso tiziganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kuti tizipirira tikamagwira ntchito yolalikira ngakhale pamene kuchita zimenezi kungatibweretsere mavuto. (2 Tim. 1:7, 8) Chifukwa chokonda anthu omwe satumikira Yehova, timapitirizabe kulalikira ngakhalenso kudzera pafoni komanso polemba makalata. Sitifooka chifukwa timayembekezera kuti tsiku lina, anthu amenewa adzasintha n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Kukonda anthu kumaphatikizapo kukonda Akhristu anzathu. Timasonyeza chikondichi ‘potonthozana ndi kulimbikitsana.’ (1 Ates. 5:11) Mofanana ndi asilikali, omwe amathandizana pa nthawi ya nkhondo, ifenso timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse mwadala abale ndi alongo athu kapenanso kuwabwezera zoipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timasonyezanso chikondi polemekeza abale omwe amatsogolera mumpingo.—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11
Lolemba, November 3
[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephere kuchita?—Num. 23:19.
Njira imodzi yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mozama zokhudza dipo. Dipo ndi lomwe limatitsimikizira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Tikamaganizira mosamala chifukwa chake dipo linaperekedwa komanso zimene zinalowetsedwapo, timayamba kukhulupirira kwambiri kuti lonjezo la Mulungu loti tidzakhala ndi moyo wosatha m’dziko labwino lidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kodi panafunika chiyani kuti dipo liperekedwe? Yehova anatumiza Mwana wake wokondedwa woyamba kubadwa komanso mnzake wapamtima, kuti adzabadwe monga munthu wangwiro padzikoli. Ali padzikoli, Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana. Kenako anazunzidwa komanso kufa imfa yowawa. Apatu Yehova analipira mtengo wokwera kwambiri. Mulungu wathu wachikondi sakanalola kuti Mwana wake avutike n’kufa pongofuna kuti tidzakhale ndi moyo wabwino koma waufupi. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Chifukwa choti anapereka mtengo wokwera chonchi, Yehova adzaonetsetsa kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. w23.04 27 ¶8-9
Lachiwiri, November 4
Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?—Hos. 13:14.
Kodi Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa akufa? N’zosachita kufunsa. Iye anauzira anthu angapo kuti alembe m’Baibulo lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Chiv. 20:11-13) Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwaniritsa zomwe walonjezazo. (Yos. 23:14) Ndipotu iye ndi wofunitsitsa kudzaukitsa anthu amene anamwalira. Taganizirani zomwe Yobu analankhula. Iye sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Yehova adzalakalaka kumuonanso ali ndi moyo. (Yobu 14:14, 15) Yehova amafunitsitsanso kudzaukitsa atumiki ake onse amene anamwalira, kuti akhale athanzi komanso osangalala. Nanga bwanji za anthu mabiliyoni omwe anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yehova? Mulungu wathu wachikondi amafunanso kudzawaukitsa. (Mac. 24:15) Iye amafuna kuti iwo akhale ndi mwayi wokhala anzake komanso kuti adzakhale ndi mwayi wokhala padzikoli mpaka kalekale.—Yoh. 3:16. w23.04 9 ¶5-6
Lachitatu, November 5
Mulungu adzatipatsa mphamvu.—Sal. 108:13.
Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero. Iye wapereka kale zinthu zomwe zingatithandize kuti tipeze mphamvu. Choncho ngati tikufuna kuti atithandize kuti tichite bwino utumiki wathu, tipirire mayesero kapena tikhalebe osangalala, tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima ndiponso kufufuza malangizo ake pophunzira Baibulo patokha. Tizilolanso kuti abale ndi alongo atilimbikitse. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chathu. Tikatero tidzalandira ‘mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha, n’cholinga choti tithe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.’—Akol. 1:11. w23.10 17 ¶19-20
Lachinayi, November 6
Muzithokoza pa chilichonse.—1 Ates. 5:18.
Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova m’mapemphero athu. Tingamuyamikire chifukwa cha zabwino zimene tili nazo. Ndipotu mphatso iliyonse yabwino imachokera kwa iye. (Yak. 1:17) Mwachitsanzo, tingamuthokoze chifukwa cha dziko lokongolali komanso zinthu zochititsa chidwi zam’chilengedwe. Tingamuthokozenso chifukwa chotipatsa moyo, banja, anzathu komanso chiyembekezo. Timafunanso kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kusangalala ndi ubwenzi wamtengo wapatali womwe tili nawo ndi iye. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tiziganizira zifukwa zomwe zimatichititsa kuti tiziyamikira Yehova. Anthu ambiri m’dzikoli ndi osayamika. Nthawi zambiri iwo amangoganizira zimene akufuna, osati zimene angachite kuti asonyeze kuyamikira zimene ali nazo. Ngati titatengera maganizo amenewa, ndiye kuti mapemphero athu akhoza kukhala omangopempha. Kuti zimenezi zisatichitikire, tiyenera kumayesetsa kukhala ndi mtima woyamikira zonse zimene Yehova amatichitira.—Luka 6:45. w23.05 4 ¶8-9
Lachisanu, November 7
Azipempha ndi chikhulupiriro, asamakayikire ngakhale pang’ono.—Yak. 1:6.
Yehova ndi Bambo wathu wachikondi ndipo sasangalala kutiona tikuvutika. (Yes. 63:9) Komabe iye satiteteza ku mavuto onse amene timakumana nawo, omwe ali ngati mitsinje kapena malawi a moto. (Yes. 43:2) Ngakhale zili choncho, iye amatilonjeza kuti angatithandize ‘kudutsa,’ kapena kuti kupirira zinthu ngati zimenezi. Iye sadzalola kuti mavuto atilepheretse kukhalabe okhulupirika kwa iye. Yehova amatipatsanso mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu kuti utithandize kupirira. (Luka 11:13; Afil. 4:13) Choncho sitikayikira kuti tidzakhala ndi zonse zomwe timafunikira kuti tipirire komanso tikhalebe okhulupirika kwa iye. Yehova amayembekezera kuti tizimudalira. (Aheb. 11:6) Nthawi zina mavuto athu angaoneke aakulu moti sitingathe kuwapirira. Mwinanso tingakayikire ngati Yehova angatithandize. Koma Baibulo limatitsimikizira kuti ndi mphamvu za Mulungu, ‘tingakwere khoma.’ (Sal. 18:29) Choncho m’malo mokayikira, tiyenera kupemphera ndi chikhulupiriro chonse kuti ayankha mapemphero athu.—Yak. 1:6, 7. w23.11 22 ¶8-9
Loweruka, November 8
Madzi osefukira sangazimitse chikondi, ndipo mitsinje singachikokolole.—Nyimbo 8:6, 7.
Mawu amenewa akufotokozatu bwino kwambiri zokhudza chikondi chenicheni. Akufotokoza mfundo yolimbikitsa kwa anthu okwatirana, yakuti angathe kumakondana kwambiri. Anthu okwatirana amafunika kuchita khama kuti azikondana kwa moyo wawo wonse. Mwachitsanzo, moto ukhoza kuyaka mpaka kalekale ngati ukusonkhezeredwa. Kupanda kutero ukhoza kuzima. Mofanana ndi zimenezi, chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi chingakhalebe cholimba ngati akuyesetsa kuchilimbitsa. Nthawi zina anthu okwatirana angamaone kuti chikondi chawo chikuchepa, makamaka pamene akulimbana ndi mavuto a zachuma, matenda kapenanso udindo wolera ana. Kuti asazimitse “lawi la Ya,” onse, mwamuna ndi mkazi ayenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. w23.05 20-21 ¶1-3
Lamlungu, November 9
Usachite mantha.—Dan. 10:19.
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olimba mtima? Makolo athu angatilimbikitse kuti tikhale olimba mtima koma limeneli si khalidwe lomwe timatengera pobadwa. Kuphunzira kulimba mtima kuli ngati kuphunzira luso linalake. Njira imodzi imene imatithandiza kuphunzira luso linalake ndi kuonetsetsa zimene mphunzitsi wathu akuchita, n’kumamutsanzira. Mofanana ndi zimenezi, timaphunzira kukhala olimba mtima poonetsetsa mmene ena akusonyezera khalidweli n’kumawatsanzira. Mofanana ndi Danieli, tiyenera kuwadziwa bwino Mawu a Mulungu. Tiziyesetsa kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova popemphera kwa iye momasuka komanso nthawi zonse. Tiyeneranso kumakhulupirira kwambiri Yehova ndipo tisamakayikire kuti ali kumbali yathu. Kenako pamene chikhulupiriro chathu chayesedwa, tidzakhala olimba mtima. Kulimba mtima kumachititsa kuti anthu ena azikulemekeza. Kungathandizenso anthu a maganizo abwino kuti aphunzire za Yehova. Kunena zoona, tili ndi zifukwa zomveka zokhalira olimba mtima. w23.08 2 ¶2; 4 ¶8-9
Lolemba, November 10
Muzifufuza zinthu zonse n’kutsimikizira zimene zili zabwino.—1 Ates. 5:21.
Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “muzifufuza zinthu zonse n’kutsimikizira,” ankagwiritsidwa ntchito pofotokoza njira yomwe anthu ankagwiritsa ntchito poyesa zitsulo zamtengo wapatali. Choncho, tiyenera kuyesa zimene timamva kapena kuwerenga kuti titsimikizire ngati zili zoona. Kuchita zimenezi kudzakhala kofunika kwambiri kwa ife pamene chisautso chachikulu chikuyandikira. M’malo momangokhulupirira zilizonse, timagwiritsa ntchito luso lathu loganiza kuti tiziyerekezera zimene tawerenga kapena kumva ndi zomwe Baibulo komanso gulu la Yehova limanena. Tikamachita zimenezi, sitidzapusitsidwa ndi mabodza a ziwanda. (Miy. 14:15; 1 Tim. 4:1) Monga gulu, atumiki a Mulungu adzapulumuka pa chisautso chachikulu. Komabe, aliyense payekha sadziwa zamawa. (Yak. 4:14) Ndiponso kaya tidzakhala tili ndi moyo pa nthawiyo kapena tidzakhala titamwalira, tidzapatsidwa mphoto ya moyo wosatha ngati titakhalabe okhulupirika. Tiyeni tonsefe tiziganizira kwambiri za chiyembekezo chathu chosangalatsachi ndiponso kupitiriza kukonzekera tsiku la Yehova. w23.06 13 ¶15-16
Lachiwiri, November 11
[Amaulula] chinsinsi chake kwa atumiki ake.—Amosi 3:7.
Sitikudziwa mmene maulosi ena a m’Baibulo adzakwaniritsidwire. (Dan. 12:8, 9) Koma ngati sitikumvetsa bwino mmene ulosi winawake udzakwaniritsidwire sizitanthauza kuti sudzakwaniritsidwa. Tizikhulupirira kuti Yehova adzatiululira mmene udzakwaniritsidwire pa nthawi yoyenera monga wakhala akuchitira m’mbuyomu. Anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:3) Kenako maboma a dzikoli adzaukira zipembedzo zonyenga n’kuziwonongeratu. (Chiv. 17:16, 17) Pambuyo pake adzaukira anthu a Mulungu. (Ezek. 38:18, 19) Zimenezi zidzachititsa kuti nkhondo ya Aramagedo iyambike. (Chiv. 16:14, 16) Sitimakayikira kuti zimenezi zichitika posachedwapa. Choncho panopa tiyeni tipitirize kuyamikira Atate wathu wakumwamba pochita chidwi ndi maulosi a m’Baibulo komanso kuthandiza ena kuti azichita zomwezo. w23.08 13 ¶19-20
Lachitatu, November 12
Tiyeni tipitirize kukondana, chifukwa chikondi chimachokera kwa Mulungu.—1 Yoh. 4:7.
Pamene mtumwi Paulo ankafotokoza za chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi, anamaliza ndi mawu akuti “chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.” (1 Akor. 13:13) N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chifukwa m’tsogolomu sitidzafunikanso kukhulupirira malonjezo a Mulungu okhudza dziko lapansi latsopano, kapenanso kukhala ndi chiyembekezo chakuti malonjezowo adzakwaniritsidwa, chifukwa zidzakhala zitakwaniritsidwa kale. Koma nthawi zonse tidzafunika kukonda Yehova ndiponso anthu. Ndipotu chikondichi chidzapitiriza kukula mpaka kalekale. Komanso chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu enieni. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Chikondi chimathandizanso kuti tizigwirizana. Paulo ananena kuti chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akol. 3:14) Mtumwi Yohane anauza Akhristu anzake kuti: “Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.” (1 Yoh. 4:21) Tikamakondana timasonyeza kuti timakondanso Mulungu. w23.11 8 ¶1, 3
Lachinayi, November 13
Titaye cholemera chilichonse.—Aheb. 12:1.
Baibulo limayerekezera moyo wa Akhristu ndi mpikisano wothamanga. Amene apambana amapatsidwa mphoto ya moyo wosatha. (2 Tim. 4:7, 8) Tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tipitirize kuthamanga chifukwa kuposa ndi kale lonse, panopa tili kumapeto kwa mpikisanowu. Mtumwi Paulo, anafotokoza chomwe chingatithandize kuti tipambane. Iye anatiuza kuti “tivule cholemera chilichonse . . . ndipo tithamange mopirira mpikisano umene atiikirawu.” Kodi Paulo ankatanthauza kuti palibe chilichonse chimene Mkhristu ayenera kunyamula? Ayi, sankatanthauza zimenezo. M’malomwake ankatanthauza kuti tiyenera kutaya chilichonse chosafunika. Zinthu zimenezi zingatilepheretse kuthamanga bwino komanso kutichititsa kuti titope. Kuti tipirire, tiyenera kumazindikira komanso kutaya mwamsanga chilichonse chomwe chingachititse kuti tilemedwe. Koma pamene tikuchita zimenezo, sitiyenera kutaya zinthu zomwe timafunika kunyamula chifukwa ngati titatero tikhoza kukhala osayenera mpikisanowu.—2 Tim. 2:5. w23.08 26 ¶1-2
Lachisanu, November 14
Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa kunja.—1 Pet. 3:3.
Kukhala ololera kumatithandiza kuti tizilemekeza maganizo a anthu ena. Mwachitsanzo, alongo athu ena amakonda kuphoda, pomwe ena ayi. Akhristu ena amasangalala kumwako mowa pang’ono, pomwe ena amasankha kuti asamamwe n’komwe. Akhristu onse amafuna kukhala ndi thanzi labwino koma amasankha zinthu mosiyana pa nkhani yosamalira thanzi lawo. Ngati timaona kuti zimene timasankha pa nkhani inayake ndiye zabwino kwambiri n’kumalimbikitsa Akhristu anzathu kuti azichita zomwezo, tikhoza kukhumudwitsa ena komanso kugawanitsa mpingo. (1 Akor. 8:9; 10:23, 24) Mwachitsanzo, m’malo motiikira malamulo pa nkhani ya zimene tiyenera kuvala, Yehova anatipatsa mfundo zoti tizitsatira. Tiyenera kuvala moyenera monga atumiki a Mulungu, n’kumasonyeza kuti ndife oganiza bwino, odzichepetsa komanso ‘anzeru.’ (1 Tim. 2:9, 10) Choncho sitichititsa anthu kuti azingoganizira za ifeyo chifukwa cha mmene tavalira. Mfundo za m’Baibulo zingathandizenso akulu kuti asamaike malamulo awoawo pa nkhani ya zovala komanso masitayilo a tsitsi. w23.07 23-24 ¶13-14
Loweruka, November 15
Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndipo mudzasangalala kwambiri ndi zakudya zabwino.—Yes. 55:2.
Yehova watithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi tsogolo labwino. Anthu amene amavomera kuitanidwa ndi “mkazi wopusa” amangoganizira za “kutsekemera,” kapena kuti chisangalalo chimene angapeze chifukwa chochita zachiwerewere. Zotsatira zake n’zakuti adzakathera “m’dzenje la Manda.” (Miy. 9:13, 17, 18) Izitu n’zosiyana kwambiri ndi zimene zimachitikira amene amavomera kuitana kwa “nzeru yeniyeni.” Panopa tikuphunzira kukonda zimene Yehova amakonda komanso kudana ndi zimene amadana nazo. (Sal. 97:10) Timasangalalanso kuuza ena kuti adzasangalale ndi “nzeru yeniyeni.” Zimakhala ngati ‘tapita pamalo okwera amumzinda kukaitana anthu kuti: “Aliyense wosadziwa zinthu abwere kuno.”’ Sikuti ifeyo komanso anthu amene avomera kuitanidwa timangopeza madalitso panopa, koma tidzapezanso madalitso m’tsogolo ndipo ‘tidzakhala ndi moyo’ mpaka kalekale, pamene ‘kumvetsa zinthu kudzatitsogolera.’—Miy. 9:3, 4, 6. w23.06 24 ¶17-18
Lamlungu, November 16
Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu, ndipo munthu amene amalamulira mkwiyo wake amaposa munthu amene wagonjetsa mzinda.—Miy. 16:32.
Kodi mumamva bwanji mnzanu wakuntchito kapena kusukulu akakufunsani zimene mumakhulupirira? Kodi mumachita mantha? Ambirife timachita mantha. Komatu funso limene angatifunse lingatithandize kudziwa zimene amaganiza kapena kukhulupirira ndipo zingatipatse mpata woti timuuze uthenga wabwino. Komabe nthawi zina munthu angatifunse funso n’cholinga choti tikangane. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa ena anamva zolakwika zokhudza zimene timakhulupirira. (Mac. 28:22) Kuwonjezera pamenepo, tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ ndipo anthu ambiri ‘safuna kugwirizana ndi ena’ komanso ndi “oopsa.” (2 Tim. 3:1, 3) Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingakhale bwanji wodekha komanso wokoma mtima pamene munthu wina akufuna kukangana nane pa zimene ndimakhulupirira?’ Kukhala wofatsa n’kumene kungakuthandizeni. Munthu wofatsa samakwiya msanga koma amadziletsa ena akamuputa ndiponso akakhala kuti sakudziwa zoti ayankhe. w23.09 14 ¶1-2
Lolemba, November 17
Mudzawaika kuti akhale akalonga padziko lonse lapansi.—Sal. 45:16.
Nthawi zina timalandira malangizo omwe amatiteteza ku zinthu monga kukonda chuma komanso zinthu zina zomwe zingatichititse kuswa malamulo a Mulungu. Apanso zinthu zimatiyendera bwino chifukwa chotsatira malangizo omwe Yehova amatipatsa. (Yes. 48:17, 18; 1 Tim. 6:9, 10) Mosakayikira, Yehova apitiriza kugwiritsa ntchito anthu kuti adzatipatse malangizo pa chisautso chachikulu komanso mpaka mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Tiyeni tipitirize kutsatira malangizo. Zimenezi zidzakhala zosavuta ngati panopa timatsatira malangizo a Yehova. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizitsatira malangizo a Yehova kuphatikizapo omwe timapatsidwa kudzera mwa amuna amene asankhidwa kuti azititsogolera. (Yes. 32:1, 2; Aheb. 13:17) Tikamatero, tingakhale ndi zifukwa zabwino zokhulupirira Yehova, yemwe ndi Wotitsogolera. Iye amatithandiza kuti tipewe zinthu zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi iyeyo, mpaka tikafike m’dziko latsopano mmene tidzalandire moyo wosatha. w24.02 25 ¶17-18
Lachiwiri, November 18
Mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu.—Aef. 2:5.
Mtumwi Paulo ankasangalala potumikira Yehova, koma ankakumananso ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri iye ankayenda maulendo ataliatali ndipo nthawi imeneyo sizinali zophweka kuchita zimenezi. Pa maulendo akewa, nthawi zina ankakumana ndi “zoopsa m’mitsinje” komanso “achifwamba pamsewu.” Nthawi zinanso anthu otsutsa ankamuchitira zankhanza. (2 Akor. 11:23-27) Komanso si nthawi zonse pamene Akhristu anzake ankasonyeza kuti ankayamikira khama lake lofuna kuwathandiza. (2 Akor. 10:10; Afil. 4:15) N’chiyani chinathandiza Paulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova? Iye anaphunzira zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova m’Malemba komanso pa zimene zinamuchitikira. Paulo sankakayikira kuti Yehova Mulungu ankamukonda. (Aroma 8:38, 39; Aef. 2:4, 5) Ndipo nayenso anayamba kumukonda kwambiri. Paulo anasonyeza kuti ankakonda Yehova ‘potumikira oyera ndi kupitiriza kuwatumikira.’—Aheb. 6:10. w23.07 9 ¶5-6
Lachitatu, November 19
Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.—Aroma 13:1.
Anthu ambiri amavomereza kuti maboma ndi ofunika komanso kuti tiyenera kumvera ena mwa malamulo omwe “olamulira akuluakulu” amapereka. Koma anthu omwewo safuna kumvera lamulo limene sakulikonda kapenanso limene akuliona kuti si lachilungamo. Baibulo limanena kuti maboma a anthu amayambitsa mavuto komanso kuti ali m’manja mwa Satana ndipo awonongedwa posachedwapa. (Sal. 110:5, 6; Mlal. 8:9; Luka 4:5, 6) Limanenanso kuti “amene akutsutsana ndi ulamuliro, akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza.” Panopa Yehova walola kuti maboma azilamulira n’cholinga choti pasakhale chisokonezo. Choncho tiyenera ‘kupereka kwa onse zimene amafuna,’ zomwe zikuphatikizapo misonkho, ulemu komanso kumvera. (Aroma 13:1-7) Tikhoza kumaona lamulo linalake ngati losayenera, lopanda chilungamo kapenanso lovuta kulimvera. Koma timamvera olamulirawa chifukwa Yehova amatiuza kuti tizitero ngati malamulo awowo sakusemphana ndi zimene iye amafuna.—Mac. 5:29. w23.10 8 ¶9-10
Lachinayi, November 20
Mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu.—Ower. 15:14.
Samisoni anabadwa pa nthawi imene Afilisiti ankalamulira komanso kupondereza Aisiraeli. (Ower. 13:1) Ulamuliro wankhanzawu unachititsa kuti Aisiraeli azivutika kwambiri. Yehova anasankha Samisoni kuti ‘adzatsogolere populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.’ (Ower. 13:5) Kuti athe kugwira ntchitoyi, Samisoni ankafunika kudalira Yehova. Pa nthawi ina, gulu la asilikali la Afilisiti linabwera kuti lidzagwire Samisoni ku Lehi. N’kutheka kuti kumeneku kunali ku Yuda. Anthu a ku Yuda anachita mantha ndipo anaganiza zopereka Samisoni kwa adaniwo. Choncho anthu a mtundu wake anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano n’kukamupereka kwa Afilisiti. (Ower. 15:9-13) Koma “mzimu wa Yehova unamupatsa mphamvu” Samisoni ndipo iye anadula zingwezo. Kenako “anapeza fupa laliwisi la nsagwada za bulu wamphongo” ndipo analitola n’kuligwiritsa ntchito popha Afilisiti okwana 1,000.—Ower. 15:14-16. w23.09 2 ¶3-4
Lachisanu, November 21
Zimenezi n’zogwirizana ndi cholinga chamuyaya chimene iye anakhala nacho chokhudza Khristu, yemwe ndi Yesu Ambuye wathu.—Aef. 3:11.
Yehova wakhala akuulula za “cholinga [chake] chamuyaya” m’Baibulo. Yehova angagwiritse ntchito njira zosiyanasiyana pofuna kukwaniritsa cholinga chake ndipo nthawi zonse amapangitsa kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. (Miy. 16:4) Komanso zotsatira za zimene amachita zimakhalapo mpaka kalekale. Kodi cholinga cha Yehova n’chiyani, nanga wasintha zinthu ziti kuti achikwaniritse? Mulungu anauza anthu oyambirira za cholinga chomwe anali nacho. Iye ankafuna kuti iwo ‘aberekane, achuluke, adzaze dziko lapansi, ndipo aliyang’anire, ayang’anirenso . . . chamoyo chilichonse’ padziko lapansi.’ (Gen. 1:28) Adamu ndi Hava atachimwira Yehova komanso kuchititsa anthu onse kuti akhale ochimwa, cholinga chake sichinalephereke. Anangosintha njira yokwaniritsira cholingacho. Nthawi yomweyo, iye anakhazikitsa Ufumu kumwamba kuti ukwaniritse cholinga chake chokhudza dzikoli komanso anthu.—Mat. 25:34. w23.10 20 ¶6-7
Loweruka, November 22
Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditafa kalekale.—Sal. 94:17.
Yehova angatithandize kuti tipitirizebe kumutumikira. Zimenezi zingakhale zovuta makamaka ngati tikulimbana ndi vuto linalake kwa nthawi yaitali. Nthawi zina zinthu zimene timalimbana nazo zingakhale zovuta kuposa zimene mtumwi Petulo anakumana nazo. Komabe Yehova angatipatse mphamvu kuti tisafooke. (Sal. 94:18, 19) Mwachitsanzo, m’bale wina asanaphunzire choonadi anakhala akugonana ndi amuna anzake kwa zaka zambiri. Koma iye anasinthiratu n’kusiya khalidwe loipali. Ngakhale zili choncho, nthawi zina amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi n’chiyani chamuthandiza kuti asafooke? M’baleyu anati: “Yehova amatipatsa mphamvu.” Anawonjezera kuti: “Mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova . . . ndaphunzira kuti n’zotheka kupitirizabe kuyenda m’njira ya choonadi . . . Yehova wakhala akundigwiritsa ntchito. Ndipo ngakhale kuti ndimalakwitsa zinthu zina, iye akupitirizabe kundipatsa mphamvu.” w23.09 23 ¶12
Lamlungu, November 23
Zotsatira za kudzichepetsa komanso kuopa Yehova ndi chuma, ulemerero ndi moyo.—Miy. 22:4.
Abale achinyamata, dziwani kuti kukula mwauzimu sikumangochitika pakokha. Muyenera kusankha anthu abwino oti muziwatsanzira, kukhala oganiza bwino, kukhala odalirika, kuphunzira maluso amene angakuthandizeni komanso kukonzekera maudindo anu a m’tsogolo. Mwina nthawi zina mungamaone kuti ndi zovuta mukaganizira zonse zimene muyenera kuchita. Komatu mukhoza kukwanitsa. Kumbukirani kuti Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani. (Yes. 41:10, 13) Nawonso abale ndi alongo anu mumpingo, adzakuthandizani. Mukadzakula n’kukhala Mkhristu wolimba mwauzimu, moyo wanu udzakhala wabwino komanso wosangalatsa. Abale achinyamatanu, timakukondani kwambiri. Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukule mwauzimu. w23.12 29 ¶19-20
Lolemba, November 24
[Tizinyalanyaza] cholakwa.—Miy. 19:11.
Tiyerekeze kuti muli pagulu limodzi ndi abale ndi alongo. Mukucheza mosangalala ndipo mukujambulitsa chithunzi. Ndiye mukujambula zithunzi ziwiri kapena zitatu kuopera kuti mwina choyambacho sichinaoneke bwino. Apa tsopano muli ndi zithunzi zitatu. Ngati pachithunzi chimodzicho m’bale wina sakumwetulira bwino mumangochidilita chifukwa muli ndi zithunzi zina ziwiri pamene aliyense akumwetulira bwino. Pali zabwino zambiri zimene timakumbukira zomwe tinachita ndi abale ndi alongo athu. Koma bwanji ngati pa nthawi ina m’bale kapena mlongo analankhula kapena kuchita zinthu mosaganizira ena? Kodi tiyenera kutani? Ndi bwino kungozichotsa m’maganizo mwathu ngati mmene tingachitire ndi zithunzi zija. (Aef. 4:32) Tikhoza kuchotsa zimenezi m’maganizo mwathu chifukwa pali zabwino zambiri zokhudza m’bale wathuyo zomwe tingamazikumbukire. Zinthu zabwinozo ndi zimene tiyenera kuzisunga m’maganizo mwathu. w23.11 12-13 ¶16-17
Lachiwiri, November 25
Akazi ayenera kudzikongoletsa ndi zovala zoyenera . . . mogwirizana ndi mmene akazi odzipereka kwa Mulungu amayenera kudzikongoletsera.—1 Tim. 2:9, 10.
Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito palembali amasonyeza kuti zovala za mkazi wa Chikhristu ziyenera kukhala zaulemu, komanso zosonyeza kuti amaganizira anthu ena. Timayamikira kwambiri alongo athu a Chikhristu chifukwa amayesetsa kuvala mwaulemu. Kuzindikira ndi khalidwe linanso limene alongo olimba mwauzimu amasonyeza. Kodi kuzindikira n’kutani? Kuzindikira kumatanthauza kutha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi zolakwika ndiyeno n’kusankha zoyenerazo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Abigayeli. Mwamuna wake anasankha zinthu molakwika zomwe zikanachititsa kuti banja lawo lonse likumane ndi mavuto. Abigayeli anachitapo kanthu mwamsanga ndipo kuzindikira kwake kunapulumutsa anthu ambiri. (1 Sam. 25:14-23, 32-35) Kuzindikira kumatithandiza kudziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi nthawi yoyenera kukhala chete. Kuzindikira kumatithandizanso kuti tizisonyeza chidwi kwa anthu ena popanda kuwapatsa maganizo olakwika.—1 Ates. 4:11. w23.12 20 ¶8-9
Lachitatu, November 26
Tingathe kusangalala chifukwa tili ndi chiyembekezo cholandira ulemerero wa Mulungu.—Aroma 5:2.
Mtumwi Paulo analembera mawu amenewa Akhristu a ku Roma. Abale ndi alongo kumeneko anali ataphunzira za Yehova ndi Yesu, anali ndi chikhulupiriro komanso anali atakhala Akhristu. Choncho Mulungu ‘anawaona kuti ndi olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,’ ndipo anawadzoza ndi mzimu woyera. (Aroma 5:1) Iwo analidi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri. Pambuyo pake Paulo analembera Akhristu odzozedwa a ku Efeso za chiyembekezo chimene Mulungu anawapatsa. Chiyembekezo chimenecho chinkaphatikizapo “zinthu . . . zimene walonjeza kwa oyera.” (Aef. 1:18) Polembera Akhristu a ku Kolose, Paulo anasonyezanso kumene iwo adzalandirire zimene ankayembekezera. Iye anati iwo anali ndi ‘chiyembekezo chodzalandira zinthu zimene anawasungira kumwamba.’ (Akol. 1:4, 5) Choncho chiyembekezo cha Akhristu odzozedwa n’chakuti adzaukitsidwa n’kukakhala ndi moyo wosatha kumwamba, komwe akalamulire limodzi ndi Khristu.—1 Ates. 4:13-17; Chiv. 20:6. w23.12 9 ¶4-5
Lachinayi, November 27
Mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.—Afil. 4:7.
Mawu omwe anawamasulira kuti “udzateteza” amanena za asilikali omwe ankalondera mzinda kuti usaukiridwe ndi adani. Anthu a mumzindawo ankagona mwamtendere podziwa kuti asilikali akulondera pageti. Mtendere wa Mulungu ukamateteza mtima ndi maganizo athu, ifenso timakhala mosateseka podziwa kuti ndife otetezeka. (Sal. 4:8) Mofanana ndi Hana, timakhalabe ndi mtendere wa mumtima ngakhale zitakhala kuti zinthu sizinasinthe nthawi yomweyo. (1 Sam. 1:16-18) Ndipo tikakhala osatekeseka, nthawi zambiri zimakhala zosavuta kuti tiziganiza bwino komanso tizisankha zochita mwanzeru. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani? Mukapanikizika ndi mavuto muziitana asilikali, titero kunena kwake, kuti akutetezeni. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzipemphera mpaka mutamva kuti muli ndi mtendere wa Mulungu. (Luka 11:9; 1 Ates. 5:17) Mukakumana ndi mavuto muzilimbikira kupemphera ndipo mudzaona mtendere wa Yehova ukuteteza mtima ndi maganizo anu.—Aroma 12:12. w24.01 21 ¶5-6
Lachisanu, November 28
Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.—Mat. 6:9.
Kuti ayeretse dzina la Atate wake, Yesu anapirira kuzunzidwa, kunyozedwa komanso mabodza omwe ankanenedwa okhudza iye. Iye ankadziwa kuti anali atamvera Atate wake mu zonse ndipo panalibe chifukwa choti achitire manyazi. (Aheb. 12:2) Ankadziwanso kuti Satana ndi amene ankachititsa zonse zomwe ankakumana nazo pa nthawi yovutayi. (Luka 22:2-4; 23:33, 34) Satana ankafunitsitsa kuti amulepheretse Yesu kukhala wokhulupirika, koma analephera mochititsa manyazi. Apa Yesu anasonyeza kuti Satana ndi wabodza komanso kuti Yehova ali ndi atumiki ake okhulupirika omwe amapitirizabe kumutumikira mokhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu. Kodi inuyo mukufunitsitsa kusangalatsa Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yanu? Ngati ndi choncho, pitirizani kutamanda dzina la Yehova komanso kuthandiza anthu ena kuti adziwe makhalidwe amene ali nawo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukutsanzira Yesu. (1 Pet. 2:21) Mofanana ndi Yesu, mudzasangalatsa Yehova komanso kusonyeza kuti Satana yemwe ndi mdani wake, ndi wabodza lankunkhuniza. w24.02 11-12 ¶11-13
Loweruka, November 29
Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?—Sal. 116:12.
Pa zaka 5 zapitazi, anthu oposa 1 miliyoni abatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Munthu akadzipereka kwa Yehova, amasankha kukhala wophunzira wa Yesu Khristu ndipo amaona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu n’kofunika kwambiri pa moyo wake. Ndiye kodi kudzipereka kumaphatikizapo chiyani? Yesu anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha.” (Mat. 16:24) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kudzikana wekha” anganenedwenso kuti “kudziletsa kuchita chinachake.” Monga mtumiki wodzipereka wa Yehova, tiyenera kudziletsa kuti tisachite chilichonse chimene Yehova sasangalala nacho. (2 Akor. 5:14, 15) Zimenezi zikuphatikizapo kukana kuchita “ntchito za thupi” monga chiwerewere. (Agal. 5:19-21; 1 Akor. 6:18) Kodi kudziletsa pa zinthu ngati zimenezi kungakhale kovuta? Ayi, makamaka ngati timakonda Yehova ndipo sitikayikira kuti kumvera malamulo ake kumatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino.—Sal. 119:97; Yes. 48:17, 18. w24.03 2 ¶1; 3 ¶4
Lamlungu, November 30
Umandisangalatsa kwambiri.—Luka 3:22.
Yehova amapereka mzimu woyera kwa anthu omwe amasangalala nawo. (Mat. 12:18) Choncho tizidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndakhala ndikusonyeza makhalidwe omwe mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala nawo?’ Kodi panopa mukuona kuti ndinu woleza mtima kwambiri mukayerekezera ndi mmene munalili musanaphunzire za Yehova? Zoona n’zakuti mukamasonyeza kwambiri makhalidwe amene mzimu woyera wakuthandizani kukhala nawo, m’pamenenso mumaona umboni wambiri wosonyeza kuti Mulungu akusangalala nanu. Yehova amagwiritsa ntchito dipo kuti lithandize anthu amene amasangalala nawo. (1 Tim. 2:5, 6) Koma bwanji ngati mtima wathu umatsutsabe zoti Yehova amasangalala nafe ngakhale kuti timakhulupirira dipo ndiponso tinabatizidwa? Kumbukirani kuti mtima wathu sitingaukhulupirire nthawi zonse koma tingakhulupirire Yehova. Iye amaona kuti anthu amene amakhulupirira dipo ndi olungama ndipo amawalonjeza kuti adzawadalitsa.—Sal. 5:12; Aroma 3:26. w24.03 30 ¶15; 31 ¶17