December
Lolemba, December 1
Akufa amaukitsidwa.—Luka 20:37.
Kodi Yehova ali ndi mphamvu zotha kuukitsa akufa? Inde. Iye ndi “Wamphamvuyonse.” (Chiv. 1:8) Choncho ali ndi mphamvu zotha kugonjetsa mdani aliyense ngakhalenso imfa. (1 Akor. 15:26) Chifukwa china chomwe chingatichititse kukhulupirira kuti Mulungu angathe kuukitsa anthu omwe anamwalira n’chakuti amakumbukira zinthu kuposa wina aliyense. Iye amatchula dzina la nyenyezi iliyonse. (Yes. 40:26) Amakumbukiranso anthu amene anamwalira. (Yobu 14:13; Luka 20:38) Iye amakumbukiranso tinthu ting’onoting’ono tokhudza anthu omwe adzawaukitse kuphatikizapo makhalidwe ndi maonekedwe awo, zimene zinawachitikira pa moyo komanso zimene ankadziwa. Ndi zomveka kukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzaukitsa akufa chifukwa tikudziwa kuti amafunitsitsa komanso ali ndi mphamvu zokwaniritsira lonjezoli. Taganizirani chifukwa china chotichititsa kukhulupirira lonjezoli. Yehova anachitapo kale zimenezi. Kale, iye anapatsa amuna angapo okhulupirika kuphatikizapo Yesu, mphamvu zoukitsa akufa. w23.04 9-10 ¶7-9
Lachiwiri, December 2
Nthawi zonse mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima ndipo azikhala okoma ngati kuti mwawathira mchere.—Akol. 4:6.
Tikamafotokoza zimene timakhulupirira mwaluso komanso mofatsa, anthu angafune kumvetsera ndipo tingapitirize kukambirana nawo. N’zoona kuti munthu akafuna kuti tizitsutsana kapena kunyoza zimene timakhulupirira sitiyenera kupitiriza kukambirana naye. (Miy. 26:4) Komabe si onse amene amachita zimenezi, ambiri angamvetsere. Kunena zoona, timapindula kwambiri tikamayesetsa kuti tikhale ofatsa. Muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu zimene zimafunikira kuti mupitirize kukhala ofatsa mukamayankha mafunso ovuta kapena ena akamakutsutsani. Kumbukirani kuti kukhala ofatsa kungathandize kuti kusiyana maganizo pa nkhani inayake kusafike mpaka pokhala mkangano waukulu. Ndipo kuyankha mofatsa komanso mwaulemu kungachititse kuti anthu asinthe mmene amationera ndiponso mmene amaonera mfundo za m’Baibulo. Tiyeni ‘tizikhala okonzeka nthawi zonse’ kuyankha aliyense amene akufuna kudziwa zomwe timakhulupirira, ndipo tizichita zimenezo “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (1 Pet. 3:15) Pajatu kufatsa sikutanthauza kufooka. w23.09 19 ¶18-19
Lachitatu, December 3
Valani . . . kuleza mtima.—Akol. 3:12.
Taganizirani njira 4 zomwe tingasonyezere kuleza mtima. Choyamba, munthu woleza mtima sakwiya msanga. Iye amayesetsa kukhala wodekha akakhala ndi nkhawa kapenanso ena akamukhumudwitsa. (Eks. 34:6.) Chachiwiri, munthu woleza mtima amadikira modekha. Ngati zinazake zikuchedwa kuposa mmene amayembekezerera, munthu wotereyu amapewa kukwiya. (Mat. 18:26, 27) Chachitatu, munthu woleza mtima sachita zinthu mwaphuma. Komabe munthu woleza mtima akamafuna kuchita zinazake zofunika, samangofulumira kuzichita kapenanso kumazichita mothamanga. M’malomwake amakhala ndi nthawi yokwanira yokonzekera zimene akufuna kuchitazo, kenako amachita zinthuzo mogwirizana ndi kuchuluka kwa nthawi yomwe zikufunika kuti zichitike. Cha 4, munthu woleza mtima amapirira mayesero popanda kudandaula. Amachita zonse zomwe angathe kuti apitirizebe kupirira n’kumaona zabwino zimene zikuchitika. (Akol. 1:11) Choncho monga Akhristu, tiyenera kukhala oleza mtima m’mbali zonsezi za moyo wathu. w23.08 20-21 ¶3-6
Lachinayi, December 4
Yehova ndi amene amayesa mitima.—Miy. 17:3.
Chifukwa chachikulu chotichititsa kuti tiziteteza mtima wathu ndi chakuti Yehova amafufuza mtima. Zimenezi zikutanthauza kuti iye samangoona mmene timaonekera kwa anthu ena, koma amaonanso zimene zili mumtima mwathu. Iye adzapitiriza kutikonda ngati timaganizira nzeru zake, zomwe zingatithandize kuti tikhale ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 4:14) Tikatero, sitidzasokonezedwa ngakhale pang’ono ndi makhalidwe omwe Satana ndi dziko loipali amalimbikitsa. (1 Yoh. 5:18, 19) Pamene tikuyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, tidzayamba kumukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Chifukwa choti sitifuna kukhumudwitsa Atate wathu, tidzadana ngakhale ndi maganizo oti tichite zoipa. Mlongo wina wa ku Croatia dzina lake Marta, yemwe anayesedwa kuti achite makhalidwe oipa, analemba kuti: “Ndinaona kuti zinkandivuta kukhala ndi maganizo oyenera komanso kulimbana ndi mtima wolakalaka kuchita zoipa, zomwe ndikanangosangalala nazo kwa nthawi yochepa. Koma kuopa Yehova kunanditeteza.” Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Marta? Iye anaganizira zomwe zikanachitika ngati akanasankha zinthu molakwika. Ifenso tingachite chimodzimodzi. w23.06 20-21 ¶3-4
Lachisanu, December 5
“Anthu a mitundu inawo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, akadzaona zimene ndakuchitirani komanso adzadziwa kuti ndine Mulungu woyera,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.—Ezek. 36:23.
Yesu ankadziwa kuti cholinga cha Yehova ndi kuyeretsa dzina lake komanso kutsutsa mabodza onse amene ananenedwa okhudza iye. N’chifukwa chake Mbuye wathu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu ankamvetsa kuti kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, ndi nkhani yaikulu yokhudza zolengedwa zonse. Palibe aliyense, kumwamba kapena padziko lapansi, amene anayeretsa kwambiri dzina la Yehova kuposa Yesu. Koma kodi pamene Yesu ankamangidwa, adani ake ankamuimba mlandu wotani? Ankanena kuti ankanyoza Mulungu. Mosakayikira, Yesu ankadziwa kuti kunyoza dzina loyera la Atate wake ndi tchimo lalikulu kwambiri. Choncho anakhumudwa kwambiri poona kuti akuimbidwa mlandu umenewu. N’kutheka kuti zimenezi ndi zomwe zinachititsa Yesu kuti ‘azunzike koopsa mumtima mwake,’ kutatsala maola ochepa kuti agwidwe.—Luka 22:41-44. w24.02 11 ¶11
Loweruka, December 6
Nzeru zimamanga nyumba ya munthu.—Miy. 24:3.
Pampikisano wathu wokalandira moyo, tiyenera kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu kuposa mmene timakondera achibale athu. (Mat. 10:37) Komabe zimenezi sizitanthauza kuti tizinyalanyaza maudindo athu m’banja ngati kuti ndi amene akutichititsa kuti tisamasangalatse Mulungu ndi Khristu. M’malomwake, kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu ndi Khristu, tiyenera kukwaniritsa udindo wathu m’banja. (1 Tim. 5:4, 8) Tikamachita zimenezi tidzakhala osangalala. Ndipotu Yehova anakonza zoti banja lizikhala losangalala ngati mwamuna ndi mkazi wake amakondana komanso kulemekezana, ngati makolo amakonda ana awo komanso kuwaphunzitsa ndiponso ngati ana amamvera makolo awo. (Aef. 5:33; 6:1, 4) Kaya udindo wanu ndi wotani m’banja, muzidalira nzeru zopezeka m’Baibulo m’malo mochita zinthu pongotengera mmene mukumvera, chikhalidwe kapena zimene anthu omwe amati ndi akatswiri amanena. Muzigwiritsanso ntchito bwino mabuku athu. Mabukuwa amafotokoza zomwe mungachite kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo. w23.08 28 ¶6-7
Lamlungu, December 7
Uziliwerenga ndi kuganizira mozama masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo. Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.—Yos. 1:8.
Mkazi wa Chikhristu amafunika kuphunzira maluso osiyanasiyana. Maluso ena amene mtsikana amaphunzira ali wamng’ono amamuthandiza kwa moyo wake wonse. Mwachitsanzo, kuphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. M’zikhalidwe zina, anthu amaona kuti akazi sayenera kuphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. Komatu luso limeneli ndi lofunika kwa Mkhristu aliyense. (1 Tim. 4:13) Choncho musalole chilichonse kukulepheretsani kuwerenga ndi kulemba bwino. Kodi maluso amenewa angakuthandizeni bwanji? Malusowa angakuthandizeni kuti mulembedwe ntchito n’kumapeza ndalama. Angakuthandizeni kuti muziphunzira Mawu a Mulungu n’kumaphunzitsanso anthu ena. Koposa zonse, lusoli limakuthandizani kuti mukhale pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova chifukwa chakuti mumawerenga Mawu ake n’kumawaganizira mozama.—1 Tim. 4:15. w23.12 20 ¶10-11
Lolemba, December 8
Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.—2 Pet. 2:9.
Tizipempha Yehova kuti atithandize kupewa mayesero. Popeza kuti si ife angwiro, nthawi zambiri timalimbana ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Satana amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe potichititsa kuti tizivutika kuchita zoyenera. Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kusokoneza maganizo athu pogwiritsa ntchito zosangalatsa zoipa. Zikatere, tingayambe kumaganizira zinthu zoipa zomwe zingachititse kuti tisakhale oyera pamaso pa Yehova komanso tichite tchimo lalikulu. (Maliko 7:21-23; Yak. 1:14, 15) Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tithe kulimbana ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. M’pemphero lake la chitsanzo, Yesu anatchulamonso mfundo yakuti: “Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa, koma mutiteteze kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Yehova amafuna kutithandiza, koma tiyenera kumupempha kuti atithandize. Tiyeneranso kumachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athu. w23.05 6-7 ¶15-17
Lachiwiri, December 9
Chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga.—Mlal. 4:12.
Anthu okwatirana akamaona kuti ubwenzi wawo ndi Atate wawo wakumwamba ndi wofunika kwambiri, amakhala okonzeka kutsatira malangizo ake, zimene zimawathandiza kupewa komanso kulimbana ndi mavuto omwe angachititse kuti chikondi chawo chichepe. Anthu omwe ali pa ubwenzi ndi Yehova amayesetsa kumutsanzira ndipo amakhala ndi makhalidwe monga kukoma mtima, kuleza mtima komanso kukhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Anthu okwatirana omwe amasonyeza makhalidwewa siziwavuta kuti azikondana kwambiri. Mlongo wina dzina lake Lena, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 25, anati: “Zimakhala zosavuta kukonda komanso kulemekeza munthu yemwe amakonda Yehova.” Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo. Pa anthu ambirimbiri a m’banja la Davide, Yehova anasankha Yosefe ndi Mariya kuti adzakhale makolo a Mesiya. Chifukwa chiyani? Awiri onsewa anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, ndipo iye ankadziwa kuti iwo adzakhala ndi banja labwino chifukwa chomukonda. w23.05 21 ¶3-4
Lachitatu, December 10
Muzimvera amene akukutsogolerani.—Aheb. 13:17.
Ngakhale kuti Mtsogoleri wathu Yesu ndi wangwiro, anthu amene amawagwiritsa ntchito kuti azititsogolera, si angwiro. Choncho zingamativute kuwamvera, makamaka ngati atiuza kuti tichite zinthu zimene sitikufuna. Pa nthawi ina, mtumwi Petulo sankafuna kumvera malangizo amene anapatsidwa. Mngelo atamuuza kuti adye nyama zimene zinali zodetsedwa mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, iye anakana, osati kamodzi kokha koma katatu. (Mac. 10:9-16) N’chifukwa chiyani anakana? Iye ankaona kuti malangizo atsopanowo anali osamveka. Koma pa nthawi ina mtumwi Paulo anamvera pamene akulu a ku Yerusalemu anamulangiza kuti apite kukachisi ndi amuna 4 ndipo akadziyeretse posonyeza kuti amatsatira Chilamulo. Iye ankadziwa kuti Akhristu sankatsatiranso Chilamulo ndipo sanalakwitse chilichonse, komabe anamvera. Iye “anatenga amunawo n’kukachita nawo mwambo wa kudziyeretsa.” (Mac. 21:23, 24, 26) Zimene anachitazi zinathandiza kuti pakhale mgwirizano.—Aroma 14:19, 21. w23.10 10 ¶15-16
Lachinayi, December 11
Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba.—Sal. 25:14.
N’kutheka kuti simunaganizirepo kuti mantha ndi khalidwe lofunika kuti anthu akhale mabwenzi abwino. Komabe, anthu amene amafuna kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ayenera ‘kumamuopa.’ Kaya takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kumuopa kwambiri. Koma kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani? Munthu amene amaopa Mulungu moyenera amamukonda ndipo safuna kuchita chilichonse chomwe chingasokoneze ubwenzi wake ndi iye. Yesu ‘ankaopa Mulungu’ mwa njira imeneyi. (Aheb. 5:7) Iye sankaona Yehova ngati winawake woopsa. (Yes. 11:2, 3) M’malomwake, ankamukonda kwambiri ndipo ankafuna kumumvera. (Yoh. 14:21, 31) Mofanana ndi Yesu, ifenso timalemekeza kwambiri Yehova chifukwa ndi wachikondi, wanzeru, wachilungamo komanso wamphamvu. Timadziwanso kuti Yehova amatikonda ndipo amakhudzidwa ndi zimene timachita akatipatsa malangizo. Tikhoza kumuchititsa kuti amve kupweteka mumtima kapenanso kusangalatsa mtima wake.—Sal. 78:41; Miy. 27:11. w23.06 14 ¶1-2; 15 ¶5
Lachisanu, December 12
Atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pomʼpweteketsa. Iye anachita zosakhulupirika kwa Yehova.—2 Mbiri 26:16.
Mfumu Uziya atakhala wamphamvu anaiwala kuti Yehova ndi amene anamupatsa mphamvuzo komanso kumuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tizikumbukira kuti Yehova ndi amene amatipatsa zabwino zonse zimene timasangalala nazo pa moyo wathu komanso pomutumikira. M’malo modzitama chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita, tizipereka ulemerero wonse kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumazindikira kuti si ife angwiro ndipo timafunika kulangizidwa. M’bale wina yemwe ali ndi zaka za m’ma 60 analemba kuti: “Ndaphunzira kuti ndisamakhumudwe kapena kukwiya msanga ena akandiuza kuti ndalakwitsa penapake. Ena akandipatsa malangizo chifukwa chakuti ndachita zinthu mosaganiza bwino, ndimayesetsa kusintha n’kumachita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova.” Zoona n’zakuti tikamaopa Yehova n’kumapitirizabe kukhala odzichepetsa, zinthu zimatiyendera bwino pa moyo wathu.—Miy. 22:4. w23.09 10 ¶10-11
Loweruka, December 13
Mukufunika kukhala opirira komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza.—Aheb. 10:36.
Akhristu oyambirira ankafunika kuti azipirira. Kuwonjezera pa mavuto a tsiku ndi tsiku omwe anthu onse ankakumana nawo, iwo ankakumananso ndi mayesero. Ambiri mwa Akhristuwa ankazunzidwa, osati ndi atsogoleri a Chiyuda kapena olamulira a Chiroma okha, koma ankazunzidwanso ndi achibale awo. (Mat. 10:21) Komanso nthawi zina ankafunika kulimbana ndi ziphunzitso za anthu ampatuko omwe ankafuna kugawanitsa mpingo. (Mac. 20:29, 30) Komabe Akhristuwo anapirira. (Chiv. 2:3) Kodi n’chiyani chinawathandiza? Iwo ankaganizira zitsanzo zopezeka m’Malemba za anthu omwe anapirira, monga Yobu. (Yak. 5:10, 11) Ankapempha Yehova kuti awapatse mphamvu. (Mac. 4:29-31) Komanso ankaganizira zotsatirapo zabwino zomwe akanapeza chifukwa chopirira. (Mac. 5:41) Ifenso tingathe kupirira ngati nthawi zonse titamaphunzira komanso kuganizira zitsanzo za anthu omwe anapirira, zotchulidwa m’Mawu a Mulungu ndiponso m’mabuku athu. w23.07 3 ¶5-6
Lamlungu, December 14
Choncho nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.—Mat. 6:33.
Yehova ndi Yesu amatitsimikizira kuti sadzatisiya ngakhale pang’ono. Atakana Khristu, mtumwi Petulo ankafunika kusankha zochita pa nkhani yofunika. Ankafunika kusankha pakati posiya kutsatira Khristu ndi kupitiriza kukhala wophunzira wake. Yesu anali atapempherera Petulo kuti chikhulupiriro chake chisathe. Yesu anauza Petulo kuti anamupempherera ndipo anasonyeza kuti sankakayikira kuti adzatha kulimbikitsa abale ake. (Luka 22:31, 32) Petulo ayenera kuti ankalimbikitsidwa akakumbukira zimene Yesu anamuuzazi. Ifenso tikafunika kusankha pa nkhani yofunika kwambiri, Yehova angagwiritse ntchito abusa achikondi kuti atitsimikizire kuti tingathe kukhalabe okhulupirika. (Aef. 4:8, 11) Yehova anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kupeza zofunika pa moyo. Ifenso tikamaika utumiki pamalo oyamba pa moyo wathu, iye adzatithandiza kupeza zimene timafunikira. w23.09 24-25 ¶14-15
Lolemba, December 15
Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.—Miy. 19:17.
Yehova amadziwa ngakhale zinthu zing’onozing’ono zomwe timachita pokomera mtima ena. Iye amaona kuti zimenezi ndi nsembe yamtengo wapatali komanso ngongole yomwe adzabweze. Ngati m’mbuyomu munatumikirapo ngati mkulu kapena mtumiki wothandiza, Yehova amakumbukira zimene munkachita pomutumikira ndiponso kuti munkachita zimenezo chifukwa cha chikondi. (1 Akor. 15:58) Iye amaonanso chikondi chomwe mukupitiriza kusonyeza. Yehova amafuna kuti tizimukonda kwambiri komanso tizikonda ena. Tingamakonde kwambiri Yehova ngati timawerenga komanso kuganizira Mawu ake, ndiponso kupemphera kwa iye nthawi zonse. Tikhozanso kumakonda kwambiri abale ndi alongo athu powathandiza m’njira zosiyanasiyana. Pamene chikondi chathu chikukula, tidzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova komanso banja lathu lauzimu. Ndipo tidzasangalala ndi zimenezi mpaka kalekale. w23.07 10 ¶11; 11 ¶13; 13 ¶18
Lachiwiri, December 16
Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani yosamalira thanzi lake. Koma pa nkhaniyi, m’Baibulo muli malamulo ochepa achindunji, monga lamulo lokhudza kupewa magazi ndiponso zamizimu, ndipo izi zimakhudza thandizo lamankhwala lomwe Mkhristu angasankhe kulandira. (Mac. 15:20; Agal. 5:19, 20) Koma pa nkhani zina munthu amasankha yekha. Kaya timaona kuti njira inayake yosamalira thanzi lathu ndi yabwino kwambiri, tiyenera kulemekeza ufulu wa abale ndi alongo athu wosankha njira imene akuona kuti ndi yabwino kwa iwowo. Pa nkhaniyi, nthawi zonse tiyenera kumakumbukira mfundo zotsatirazi: (1) Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetseretu matenda onse. (Yes. 33:24) (2) Mkhristu aliyense “azitsimikiza” za chimene chingamuthandize kwambiri. (Aroma 14:5) (3) Sitiyenera kuweruza ena kapena kuwakhumudwitsa. (Aroma 14:13) (4) Akhristu amasonyeza chikondi ndipo amaona kuti kukhala ogwirizana mumpingo n’kofunika kwambiri kuposa ufulu wawo wosankha zochita.—Aroma 14:15, 19, 20. w23.07 24 ¶15
Lachitatu, December 17
Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake.—Num. 6:8.
Kodi mumakonda kwambiri Yehova? N’zosachita kufunsa. Kuyambira kale, anthu osawerengeka akhalanso akumukonda ngati mmene inuyo mumachitira. (Sal. 104:33, 34) Ambiri akhala akudzimana zinazake kuti azilambira Yehova. Izi ndi zimenenso Aisiraeli otchedwa Anaziri ankachita. Mawuwa amanena za Mwisiraeli wakhama amene ankadzimana zinthu zina n’cholinga choti azitumikira Yehova m’njira yapadera. Chilamulo cha Mose chinkalola kuti mwamuna kapena mkazi achite lonjezo lapadera kwa Yehova losankha kukhala Mnaziri kwa nthawi inayake. (Num. 6:1, 2) Munthu amene wapanga lonjezoli ankafunika kutsatira malamulo enaake mosiyana ndi Aisiraeli anzake. Ndiye kodi n’chiyani chinkachititsa kuti Mwisiraeli apange lonjezoli? Ayenera kuti ankapanga lonjezoli chifukwa chokonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira madalitso omwe ankamupatsa.—Deut. 6:5; 16:17. w24.02 14 ¶1-2
Lachinayi, December 18
Inu Yehova . . . mumasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.—Dan. 9:4.
M’Baibulo, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kukhulupirika” kapena chikondi “chokhulupirika,” nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito pofotokoza za chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa atumiki ake. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito pofuna kufotokoza chikondi chimene chimakhalapo pakati pa atumiki a Mulungu. (2 Sam. 9:6, 7) Kukhulupirika kwathu kumawonjezereka nthawi ikamadutsa. Mfundo imeneyi ndi yoona tikaganizira zimene zinachitika pa moyo wa Danieli. Kwa moyo wake wonse iye ankayesedwa pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Yehova. Koma ena mwa mayesero aakulu, anakumana nawo ali ndi zaka za m’ma 90. Anthu omwe ankatumikira m’nyumba yachifumu sankasangalala naye ndipo sankalemekeza Mulungu amene iye ankamulambira. Choncho anakonza chiwembu choti Danieli aphedwe. Iwo anakhazikitsa lamulo lomwe likanachititsa kuti Danieli asankhe kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kapena kumvera mfumu. Kuti asonyeze kuti anali wokhulupirika kwa mfumu, Danieli ankangofunika kusiya kupemphera kwa Yehova kwa masiku 30. Koma iye anasankha kuti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova.—Dan. 6:12-15, 20-22. w23.08 5 ¶10-12
Lachisanu, December 19
Tipitirize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Yehova amafuna kuti tisasiye kusonyeza chikondi kwa abale ndi alongo athu. Ngati Mkhristu wina walephera kusonyeza makhalidwe abwino, tizingoona kuti amafuna kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo wangochita zinthu mosaganiza bwino. (Miy. 12:18) Mulungu amakonda atumiki ake okhulupirika ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina. Samasiya kutikonda tikalakwitsa zinazake, ndipo samatisungira chakukhosi. (Sal. 103:9) Choncho tiyenera kumatsanzira Atate wathu yemwe amakhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Tizikumbukiranso kuti pamene mapeto akuyandikira tiyenera kumagwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tiziyembekezera kuti Akhristufe tikhoza kuzunzidwa kwambiri kapenanso kumangidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. Ngati zimenezi zitatichitikira, tingafune kwambiri kuti abale ndi alongo athu atithandize.—Miy. 17:17. w24.03 15-16 ¶6-7
Loweruka, December 20
Yehova ndi amene amatsogolera mapazi a munthu.—Miy. 20:24.
M’Baibulo muli nkhani za achinyamata enanso omwe anakhala pa ubwenzi ndi Yehova. Iye ankawakonda ndipo zinthu zinawayendera bwino pa moyo wawo. Davide anali mmodzi wa achinyamatawa. Iye anasankha kutumikira Mulungu ali wachinyamata ndipo kenako anadzakhala mfumu yokhulupirika. (1 Maf. 3:6; 9:4, 5; 14:8) Mukamaphunzira za Davide, chitsanzo chake chikhoza kukulimbikitsani kuti muzitumikira Yehova mokhulupirika. Mukhozanso kukonza zoti muphunzire zambiri zokhudza Maliko kapena Timoteyo. Mudzaona kuti iwo anayamba kutumikira Yehova ali achinyamata ndipo anapitiriza kumusangalatsa. Zimene mukuchita panopa ndi zomwe zingachititse kuti zinthu zidzakuyendereni bwino kapena ayi. Mukamakhulupirira Yehova osati kudalira luso lanu lomvetsa zinthu, iye adzakuthandizani kuti muzisankha zinthu mwanzeru. Mukatero, mudzakhala wosangalala ndipo moyo wanu udzakhala wabwino. Kumbukirani kuti Yehova amayamikira zonse zimene mumachita pomutumikira. Palibenso njira ina yabwino yogwiritsira ntchito moyo wanu imene ingapose kutumikira Atate wathu wachikondi Yehova. w23.09 13 ¶18-19
Lamlungu, December 21
Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse.—Akol. 3:13.
Mtumwi Paulo ankadziwa kuti abale ndi alongo ake si angwiro. Mwachitsanzo, ena anamuweruza molakwika atayamba kugwirizana ndi mpingo. (Mac. 9:26) Pambuyo pake, ena ankamunenera miseche pofuna kuwononga mbiri yake. (2 Akor. 10:10) Paulo anaonanso munthu wina waudindo akuchita zolakwika zomwe zikanakhumudwitsa anthu ena. (Agal. 2:11, 12) Komanso mnzake wina dzina lake Maliko anamukhumudwitsa kwambiri. (Mac. 15:37, 38) Paulo akanatha kusankha kuti asamagwirizane ndi anthu amene anamukhumudwitsawa. Koma iye anapitiriza kuona zabwino mwa abale ndi alongo akewa ndipo ankatumikirabe Yehova mwakhama. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova? Paulo ankakonda abale ndi alongo ake. Kukonda anthu ena kunamuthandiza kuti aziganizira makhalidwe awo abwino osati zimene amalakwitsa. Chikondi chinamuthandizanso kuti azichita zomwe zili mu lemba lalero. w24.03 15 ¶4-5
Lolemba, December 22
Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.—2 Tim. 2:24.
M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kufunika kokhala ofatsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Isaki. Iye atakakhala m’dera la Afilisiti la Gerari, anthu ansanje a kumeneko anakwirira zitsime zimene antchito a bambo ake anakumba. M’malo momenyana nawo kuti alanditse zitsimezo, Isaki ndi banja lake anangosamukira kutali ndipo anakumba zitsime zina. (Gen. 26:12-18) Koma Afilisiti anapitiriza kunena kuti madzi a m’deralo analinso awo. Ngakhale zinali choncho, Isaki anapitiriza kuchita zinthu mwamtendere. (Gen. 26:19-25) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupitirizabe kukhala wofatsa ngakhale kuti ena ankafuna kumakangana naye? Ayenera kuti ankatengera chitsanzo cha makolo ake ndipo anaphunzira mmene Abulahamu ankachitira zinthu mwamtendere komanso ankaona “mzimu wabata ndi wofatsa” wa Sara.—1 Pet. 3:4-6; Gen. 21:22-34. w23.09 15 ¶4
Lachiwiri, December 23
Ndakonza kuti zimenezi zichitike komanso ndidzazichita.—Yes. 46:11.
Yehova anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa padzikoli kuti adzaphunzitse anthu zokhudza Ufumu komanso kudzapereka moyo wake monga dipo kuti atiwombole ku uchimo ndi imfa. Kenako Yesu anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba kuti akakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Nkhani yaikulu m’Baibulo ndi yakuti dzina la Yehova lidzayeretsedwa akamadzakwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Cholinga cha Yehova sichingasinthidwe. Iye adzakwaniritsa chilichonse chomwe walonjeza ndipo sizidzalephereka. (Yes. 46:10; Aheb. 6:17, 18) Kenako dzikoli lidzasinthidwa kukhala Paradaiso ndipo ana a Adamu ndi Hava angwiro komanso olungama ‘adzasangalala ndi moyo mpaka kalekale.’ (Sal. 22:26) Kuwonjezera pamenepo, pali zinthu zinanso zimene Yehova akufuna kuchita. Cholinga chake chachikulu ndi chakuti onse kumwamba ndi padziko lapansi akhale ogwirizana. Ndipo onse omwe adzakhale ndi moyo azidzagonjera Mulungu monga Wolamulira wawo. (Aef. 1:8-11) Kunena zoona, Yehova akukwaniritsa cholinga chake m’njira yochititsa chidwi. w23.10 20 ¶7-8
Lachitatu, December 24
“Limbani mtima, . . . pakuti ine ndili ndi inu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.—Hag. 2:4.
Ayuda omwe anachoka ku Babulo atafika ku Yerusalemu, sipanatenge nthawi yaitali kuti ayambe kukumana ndi mavuto a zachuma, a zandale komanso kutsutsidwa. Choncho ambiri zinawavuta kuika maganizo pa ntchito yomanganso kachisi wa Yehova. Ndiye Yehova anatumiza aneneri awiri, Hagai ndi Zekariya, kuti akawalimbikitse. Komabe patapita zaka pafupifupi 50, Ayudawo anafookanso. Ezara, anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo kuti adzalimbikitse anthu a Mulunguwo kuti aziika patsogolo zinthu zokhudza kulambira koona. (Ezara 7:1, 6) Maulosi a Hagai ndi Zekariya anathandiza anthu a Mulungu kalelo kuti apitirize kukhulupirira Yehova pamene ankatsutsidwa. Maulosiwa angatithandizenso ifeyo masiku ano kuti tipitirize kukhulupirira kuti Yehova angatithandize pamene tikukumana ndi mavuto.—Miy. 22:19. w23.11 14-15 ¶2-3
Lachinayi, December 25
Valani chikondi, chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.—Akol. 3:14.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda abale ndi alongo athu? Njira imodzi ndi kuwalimbikitsa kapena kuwatonthoza. Chifundo ndi chimene chingatichititse kuti ‘tipitirize kulimbikitsana.’ (1 Ates. 4:18) Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri abale athu? Tingatero poyesetsa kuti tiziwakhululukira zimene amalakwitsa. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizikondana kwambiri masiku ano? Petulo anapereka chifukwa chake pomwe ananena kuti: “Mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho . . . muzikondana kwambiri.” (1 Pet. 4:7, 8) Kodi chichitike n’chiyani pamene mapeto akuyandikira kwambiri? Ponena za otsatira ake, Yesu ananena kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Kuti tithe kupirira tiyenera kumagwirizana kwambiri. Tikatero, Satana sadzatha kutigawanitsa chifukwa chakuti tili ndi chikondi chimene chimatigwirizanitsa pamodzi.—Afil. 2:1, 2. w23.11 13 ¶18-19
Lachisanu, December 26
Ndife antchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Choonadi cha Mawu a Mulungu ndi champhamvu kwambiri. Tikamaphunzitsa anthu zoona zokhudza Yehova komanso mmene alili, pamachitika chinthu china chodabwitsa. Khungu limene Satana amachititsa m’maganizo mwa anthu limayamba kuchoka ndipo amayamba kuona makhalidwe abwino a Atate athu okondedwa, ngati mmene ifeyo timachitira. Iwo amagoma ndi mphamvu zake zopanda malire. (Yes. 40:26) Amayamba kumukhulupirira chifukwa amaona kuti ndi wachilungamo. (Deut. 32:4) Amaphunzira zambiri zokhudza nzeru zake zapamwamba. (Yes. 55:9; Aroma 11:33) Amalimbikitsidwanso kudziwa kuti iyeyo ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Akayamba kukhala naye pa ubwenzi, chiyembekezo chawo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale monga ana ake, chimakhala chotsimikizika. Tilitu ndi mwayi waukulu kwambiri wothandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Atate wawo. Tikamachita zimenezi, Yehova amationa kuti ndife “antchito anzake.”—1 Akor. 3:5. w24.02 12 ¶15
Loweruka, December 27
Ndi bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.—Mlal. 5:5.
Ngati mukuphunzira Baibulo kapena makolo anu ndi a Mboni, n’kutheka kuti mukuganizira zobatizidwa. Chimenechitu ndi cholinga chabwino kwambiri. Komabe musanabatizidwe, muyenera kudzipereka kwa Yehova. Kodi munthu amadzipereka bwanji kwa Yehova? Amamulonjeza m’pemphero kuti azilambira iye yekha komanso kuti aziika zimene Yehovayo amafuna pamalo oyamba. Apa amakhala akulonjeza Yehova kuti adzapitiriza kumukonda ndi ‘mtima wake wonse, moyo wake wonse, maganizo ake onse ndi mphamvu zake zonse.’ (Maliko 12:30) Munthu amadzipereka ali kwayekha ndipo imakhala nkhani ya pakati pa iyeyo ndi Yehova. Koma kubatizidwa kumachitika pagulu ndipo kumatsimikizira ena kuti munthuyo anadzipereka. Kudzipereka ndi lonjezo lopatulika ndipo mumafunika kumalikwaniritsa. Nayenso Yehova amayembekezera kuti muzilikwaniritsa.—Mlal. 5:4. w24.03 2 ¶2; 3 ¶5
Lamlungu, December 28
Aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.—Aef. 5:33.
Mabanja onse amakumana ndi mavuto. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti amene ali m’banja amakumana ndi “mavuto pa moyo wawo.” (1 Akor. 7:28) Zili choncho chifukwa chakuti banja ndi mgwirizano wa anthu awiri omwe si angwiro. Ndipo anthuwo amakhala osiyana makhalidwe, zimene amakonda ndiponso zimene amadana nazo. Angakhalenso osiyana zikhalidwe ndi kumene anakulira. Nthawi zina angakhalenso ndi makhalidwe amene sankaonekera asanalowe m’banja. Zinthu ngati zimenezi zikhoza kuyambitsa mavuto. M’malo moti aliyense azizindikira vuto lake n’kumayesetsa kuti alikonze, angayambe kuimba mlandu mnzake. Ndipo akhoza kumaona kuti kupatukana kapena kuthetsa ukwatiwo ndiye njira yothetsera mavutowo. Koma kodi zimenezo ndi zoona? Ayi. Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azilemekeza banja ngakhale mwamuna kapena mkazi wawo atakhala wovuta. w24.03 16 ¶8; 17 ¶11
Lolemba, December 29
Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa.—Aroma 5:5.
Pamene munadzipereka komanso kubatizidwa, munapitiriza kuphunzira komanso kukula mwauzimu, ndipo chiyembekezo chanu choti mudzakhala m’Paradaiso padziko lapansi chinapitiriza kukula. (Aheb. 5:13–6:1) N’kutheka kuti zimene zili pa Aroma 5:2-4 zakhala zikukuchitikirani. Mwakhala mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana koma mwawapirira, ndipo mwaona Yehova akusangalala nanu. Popeza simukayikira kuti Mulungu amakukondani, panopa muli ndi chifukwa chachikulu choyembekezerera zimene walonjeza. Chiyembekezo chanu chakhala champhamvu kwambiri kuposa mmene zinalili poyamba. Mumaona kuti zimene mukuyembekezera ndi zenizeni ndipo zimakukhudzani kwambiri. Chiyembekezocho chimakuthandizani pa mbali iliyonse ya moyo wanu, ndipo chakuthandizani kusintha mmene mumachitira zinthu ndi anthu a m’banja lanu, zimene mumasankha komanso mmene mumagwiritsira ntchito nthawi yanu. Mtumwi Paulo anatchulanso mfundo ina yofunika kwambiri pa nkhani ya chiyembekezo chomwe timakhala nacho pambuyo pokhala ovomerezeka kwa Mulungu. Iye anatitsimikizira kuti zimene tikuyembekezera zidzakwaniritsidwa.—Aroma 15:13. w23.12 12-13 ¶16-19
Lachiwiri, December 30
[Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.—Yes. 33:6.
Tikakumana ndi mavuto aakulu timamva kupweteka mumtima, maganizo athu amasokonezeka ndipo sitingachite zinthu ngati mmene timachitira nthawi zonse. Tingakhale ngati sitima yomwe ikukankhidwira uku ndi uku ndi mphepo yamphamvu. Kodi Yehova amatithandiza bwanji tikamamva chonchi? Iye amatitsimikizira kuti adzatithandiza kuti tisagwedezeke. Sitima ikakumana ndi mphepo yamphamvu panyanja, imayamba kukankhidwira uku ndi uku ndipo zimakhala zoopsa. Koma sitima zina zimakhala ndi zinthu zina m’mbali mwake zomwe zimathandiza kuti sitima ikhazikike pamadzi. Zinthu zimenezi zimathandiza kuti sitimayo isamatengeketengeke, zomwe zimachititsa kuti anthu omwe akwera akhale otetezeka. Koma zinthu zambiri zomwe zimathandiza kuti sitima isamagwedezeke zimagwira bwino ntchito sitimayo ikamayenda. Mofanana ndi zimenezi, Yehova adzatithandiza kuti tisagwedezeke ngati tikupitirizabe kumutumikira mokhulupirika pamene tikukumana ndi mavuto. w24.01 22 ¶7-8
Lachitatu, December 31
Ine ndimadalira Mulungu, sindikuopa.—Sal. 56:4.
Mukamachita mantha muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova wachita kale? Muziganizira zimene iye analenga. Mwachitsanzo, ‘mukamayang’anitsitsa’ mmene amasamalirira mbalame komanso maluwa, zomwe sizinalengedwe m’chifaniziro chake komanso sizingathe kumulambira, mungayambe kumudalira kwambiri kuti inunso adzakusamalirani. (Mat. 6:25-32) Muziganiziranso zimene Yehova wachitira atumiki ake. Mungathe kuwerenga za munthu wina wotchulidwa m’Baibulo yemwe anasonyeza chikhulupiriro cholimba kapenanso mungawerenge zimene zinachitikira mtumiki wa Yehova wa m’nthawi yathu ino. Kuwonjezera apo, muziganiziranso zimene Yehova wachita kale pokusamalira inuyo. Kodi anakuthandizani bwanji kuti muphunzire choonadi? (Yoh. 6:44) Kodi wakhala akuyankha bwanji mapemphero anu? (1 Yoh. 5:14) Kodi nsembe ya Mwana wake wokondedwa imakuthandizani bwanji tsiku lililonse?—Aef. 1:7; Aheb. 4:14-16. w24.01 4 ¶6; 7 ¶17