Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kabukuka
M’kabukuka muona kuti tsiku lililonse lili ndi lemba lake komanso ndemanga yake. Ngakhale kuti mukhoza kupanga lemba la tsiku nthawi ina iliyonse, ena amaona kuti zimakhala zothandiza kwambiri kupanga m’mawa. Zimenezi zimawathandiza kuti aziganizira mfundo za mulembalo tsiku lonse. Kupanga lemba la tsiku ndi banja lanu n’kothandiza kwambiri. Anthu otumikira pa Beteli padziko lonse amakambirana lemba la tsiku pa nthawi ya chakudya cham’mawa.
Ndemangazi zachokera mu Nsanja ya Olonda (w) ya April 2023 mpaka ya March 2024. Manambala olembedwa kumapeto kwa deti la magazini ya a Nsanja Olonda ndi a tsamba limene pachokera ndemanga ndipo nambala yotsatira ndi ya ndime zimene pachokera ndemangayo. (Onani chitsanzo m’munsimu.) Mfundo zina zogwirizana ndi lembali mungazipeze munkhaniyo.