Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es25 tsamba 7-17
  • January

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Lachitatu, January 1
  • Lachinayi, January 2
  • Lachisanu, January 3
  • Loweruka, January 4
  • Lamlungu, January 5
  • Lolemba, January 6
  • Lachiwiri, January 7
  • Lachitatu, January 8
  • Lachinayi, January 9
  • Lachisanu, January 10
  • Loweruka, January 11
  • Lamlungu, January 12
  • Lolemba, January 13
  • Lachiwiri, January 14
  • Lachitatu, January 15
  • Lachinayi, January 16
  • Lachisanu, January 17
  • Loweruka, January 18
  • Lamlungu, January 19
  • Lolemba, January 20
  • Lachiwiri, January 21
  • Lachitatu, January 22
  • Lachinayi, January 23
  • Lachisanu, January 24
  • Loweruka, January 25
  • Lamlungu, January 26
  • Lolemba, January 27
  • Lachiwiri, January 28
  • Lachitatu, January 29
  • Lachinayi, January 30
  • Lachisanu, January 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25 tsamba 7-17

January

Lachitatu, January 1

Munthu amene anamwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi ake. Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye.​—Luka 7:12.

Yesu “anaona” mayi oferedwa ndipo kenako “anawamvera chifundo.” (Luka 7:13) Sikuti Yesu anangowamvera chisoni, koma anawasonyezanso chifundo. Iye analankhula ndi mayiwo, mosakayikira ndi mawu olimbikitsa, kuti: “Tontholani mayi.” Kenako anachitapo kanthu kuti awathandize. Anaukitsa mnyamatayo ndipo “anam’pereka kwa mayi ake.” (Luka 7:14, 15) Kodi tingaphunzire chiyani pa chozizwitsa chomwe Yesu anachita poukitsa mwana wa mayi wamasiye? Tikuphunzirapo kuti tizichitira chifundo anthu omwe aferedwa. N’zoona kuti sitingaukitse anthu akufa ngati mmene Yesu anachitira. Koma mofanana ndi iye tikhoza kuchitira chifundo anthu omwe aferedwa ngati titamachita nawo chidwi. Tingawasonyeze chifundo polankhula komanso kuchita zomwe tingathe kuti tiwathandize ndiponso kuwatonthoza. (Miy. 17:17; 2 Akor. 1:3, 4; 1 Pet. 3:8) Ngakhale mawu ochepa kapena zinthu zing’onozing’ono zosonyeza kukoma mtima zingawalimbikitse kwambiri. w23.04 5-6 ¶13-15

Lachinayi, January 2

Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma nʼkoti Mulungu alandire ulemerero.​—Yoh. 11:4.

Ngakhale kuti Yesu anadziwa kuti mnzake Lazaro wamwalira, iye anakhalabe komwe analiko kwa masiku ena awiri ndipo kenako anapita ku Betaniya. Choncho pamene ankafika m’mudzimo, panali patapita masiku 4 kuchokera pamene Lazaro anamwalira. Yesu ankafuna kuchita chinthu chomwe chikanathandiza anzakewo komanso kulemekeza Mulungu. (Yoh. 11:6, 11, 17) Nkhaniyi ikutiphunzitsa mmene tiyenera kumachitira zinthu ndi anzathu. Taganizirani izi: Pamene Mariya ndi Marita ankatumiza uthenga kwa Yesu sikuti ankamupempha kuti abwere ku Betaniya. Iwo anangomuuza kuti mnzake wapamtima akudwala. (Yoh. 11:3) Lazaro atamwalira, Yesu akanatha kumuukitsa ali kutali. Komabe anasankha kuti apite ku Betaniya kuti akakhale ndi anzake, Mariya ndi Marita. Kodi muli ndi mnzanu yemwe amakuthandizani popanda kumupempha? Ndiye kuti mumadziwa kuti mukhoza kumudalira kuti akuthandizani “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Mofanana ndi Yesu, tiyeni tizikhala odalirika kwa anzathu. w23.04 10 ¶10-11

Lachisanu, January 3

Amene watilonjeza ndi wokhulupirika.​—Aheb. 10:23.

Tikamakumana ndi mayesero, mwina tingayambe kuona kuti dziko latsopano la Yehova silidzabwera. Koma kodi zimenezi zingatanthauze kuti chikhulupiriro chathu chafooka? Osati kwenikweni. Taganizirani chitsanzo ichi: Ngati tili m’nyengo yozizira kwambiri, mwina tingamaone ngati nyengo yotentha siibwera. Koma kenako nyengo yotenthayo imabwera. Mofanana ndi zimenezi, ngati tafooka kwambiri mwina tingamaone kuti dziko latsopano silidzabwera. Koma ngati chikhulupiriro chathu ndi cholimba timadziwa kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. (Sal. 94:3, 14, 15; Aheb. 6:17-19) Chikhulupirirocho chingatithandize kuti tizipitiriza kuika kulambira Yehova pamalo oyamba pa moyo wathu. Timafunikanso chikhulupiriro cholimba kuti tizigwira ntchito yathu yolalikira. Anthu ambiri omwe timawalalikira amaona kuti “uthenga wabwino” wokhudza dziko latsopano la Mulungu, umanena za zinthu zomwe ndi zosatheka. (Mat. 24:14; Ezek. 33:32) Sitiyenera kutengera maganizo awo okayikirawa. Choncho tiyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. w23.04 27 ¶6-7; 28 ¶14

Loweruka, January 4

Timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse, timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.—1 Yoh. 5:15.

Kodi munadzifunsapo ngati Yehova amayankha mapemphero anu? Ngati ndi choncho dziwani kuti si inu nokha. Abale ndi alongo enanso anadzifunsapo zimenezi, makamaka pa nthawi yomwe ankakumana ndi mavuto. Ngati ifenso tikukumana ndi mavuto, zingakhale zovuta kuzindikira mmene Yehova akuyankhira mapemphero athu. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amayankha mapemphero a atumiki ake? Malemba amatitsimikizira kuti Yehova amatikonda kwambiri komanso ndife a mtengo wapatali kwa iye. (Hag. 2:7; 1 Yoh. 4:10) N’chifukwa chake amatiuza kuti tizimupempha kuti azitithandiza. (1 Pet. 5:6, 7) Iye amafuna kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba komanso tizipirira mavuto amene tikukumana nawo. Nthawi zambiri timawerenga m’Baibulo kuti Yehova anayankha mapemphero a atumiki ake. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe mukuchiganizira? w23.05 8 ¶1-4

Lamlungu, January 5

Mariya ananena kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova.”​—Luka 1:46.

Payekha, Mariya anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ndipo chikhulupiriro chake sichinkadalira pa zimene Yosefe ankachita. Iye ankadziwa bwino Malemba. Ankapezanso nthawi yoganizira zimene ankaphunzira. (Luka 2:19, 51) Mosakayikira, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kunachititsa Mariya kukhala mkazi wabwino kwambiri. Masiku anonso akazi ambiri amayesetsa kutsanzira Mariya. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Emiko ananena kuti: “Ndisanakwatiwe, nthawi zonse ndinkachita zinthu zokhudza kulambira. Koma nditakwatiwa, ndinazindikira kuti chikhulupiriro changa chinkangodalira pa zimene mwamuna wanga ankachita, chifukwa iye ndi amene ankapemphera komanso kutsogolera pa zinthu zokhudza kulambira. Ndinaona kuti ndiyenera kumayesetsa pandekha kuti ndizilimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova. Choncho panopa ndimapeza nthawi kuti ndizikhala pandekha ndi Mulungu wanga, kupemphera, kuwerenga Malemba komanso kuganizira zomwe ndawerengazo.” (Agal. 6:5) Akazinu, mukamapitiriza kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, amuna anu adzakhala ndi zifukwa zambiri zokutamandani ndiponso kukukondani.—Miy. 31:30. w23.05 22 ¶6

Lolemba, January 6

Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.​—Sal. 34:11.

Tonsefe sitimabadwa ndi mtima woopa Yehova, m’malomwake timafunika kuyesetsa kuti tikhale nawo. Njira imodzi yomwe tingachitire zimenezi ndi kuganizira zomwe iye analenga. Tikamaona nzeru, mphamvu komanso chikondi cha Mulungu kwa anthufe, zomwe zimaonekera “m’zinthu zimene anapanga,” timayamba kumulemekeza komanso kumukonda kwambiri. (Aroma 1:20) Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tiziopa Mulungu ndi kupemphera nthawi zonse. Tikamapemphera kwambiri, m’pamenenso Yehova amakhala weniweni kwa ife. Nthawi iliyonse imene tamupempha kuti atipatse mphamvu kuti tipirire mayesero enaake, timakumbukira kuti iye ali ndi mphamvu zodabwitsa. Tikamayamikira Yehova chifukwa cha mphatso ya Mwana wake, zimatikumbutsa kuti iye amatikonda kwambiri. Ndipo tikamapemphera mapemphero opembedzera kuti atithandize pa vuto linalake, timakumbukira kuti iye ndi wanzeru kwambiri. Mapemphero oterewa amatichititsa kuti tizimulemekeza kwambiri. Ndipo amatipangitsa kukhala otsimikiza kuti tisachite chilichonse chomwe chingawononge ubwenzi wathu ndi iye. w23.06 15 ¶6-7

Lachiwiri, January 7

Yehova ndi Wotipatsa Malamulo.​—Yes. 33:22.

Nthawi zonse Yehova wakhala akupereka malamulo omveka bwino kwa anthu ake. Mwachitsanzo, bungwe lolamulira la mu nthawi ya atumwi linafotokoza kuti Akhristu ayenera kukhala olimba m’njira zitatu izi: (1) kupewa kulambira mafano koma n’kumalambira Yehova yekha, (2) kulemekeza kupatulika kwa magazi komanso (3) kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino. (Mac. 15:28, 29) Kodi Akhristu masiku ano angapitirize bwanji kukhala osasunthika pa zinthu zitatu zimenezi? Angatero polambira komanso kumvera Yehova. Iye analamula Aisiraeli kuti azidzipereka kwa iye yekha. (Deut. 5:6-10) Pamene ankayesedwa ndi Mdyerekezi, Yesu anafotokoza momveka bwino kuti tiyenera kumalambira Yehova yekha. (Mat. 4:8-10) Choncho sitimagwiritsa ntchito mafano polambira. Sitimalemekezanso kwambiri anthu mpaka kumakhala ngati tikuwalambira, kaya ndi atsogoleri a zipembedzo, andale kapenanso akatswiri a masewera ndi anthu ena otchuka. Timalambira Yehova yekha chifukwa ndi amene ‘analenga zinthu zonse.’—Chiv. 4:11. w23.07 14-15 ¶3-4

Lachitatu, January 8

Chifukwa choopa Yehova, munthu amapewa kuchita zoipa.​—Miy. 16:6.

Dziko lolamuliridwa ndi Satanali ndi lodzadza ndi zachiwerewere komanso zolaula. (Aef. 4:19) Choncho tiyenera kuopa Mulungu komanso kumapewa zoipa. Pa Miyambo chaputala 9, nzeru ndi kupusa aziyerekezera ndi akazi awiri. Mkazi aliyense akufotokozedwa ngati kuti akuitana munthu “wosadziwa zinthu,” kapena kuti wopanda nzeru. Zili ngati aliyense akuitana kuti, ‘Bwera kunyumba kwanga udzadye chakudya.’ (Miy. 9:1, 4-6) Koma pali kusiyana kwakukulu pa zimene zikuchitikira aliyense woitanidwa ndi akaziwa. Taganizirani zimene timawerenga zokhudza “mkazi wopusa.” (Miy. 9:13-18) Mopanda manyazi, iye amaitanira wopanda nzeru kuti akadye kunyumba yake ponena kuti, ‘bwera kuno’. Kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Baibulo limati “kumeneko kuli akufa.” Timachenjezedwa za “mkazi wamakhalidwe oipa” ndiponso “mkazi wachiwerewere.” Ponena za iye, timauzidwa kuti: “Kupita kunyumba yake kuli ngati kupita kokafa.” (Miy. 2:11-19) Pa Miyambo 5:3-10, timachenjezedwa za “mkazi wamakhalidwe oipa” winanso yemwe “mapazi ake amatsikira ku imfa.” w23.06 21-22 ¶6-7

Lachinayi, January 9

Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.​—Afil. 4:5.

Akulu ayenera kukhala chitsanzo chabwino pa nkhani yololera. (1 Tim. 3:2, 3) Mwachitsanzo, mkulu sayenera kuyembekezera kuti maganizo ake azitsatiridwa nthawi zonse, chabe chifukwa chakuti iyeyo ndi wamkulu kuposa akulu ena. Iye amadziwa kuti mzimu wa Yehova ungachititse mkulu aliyense pabungwe lawo kunena zinthu zomwe zingathandize bungwelo kusankha zochita mwanzeru. Ndipo ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo, akulu ololera amavomereza mofunitsitsa zimene akulu ambiri pabungwe lawo asankha, ngakhale kuti si zimene iwowo akanasankha. Akhristu amapeza madalitso ambiri chifukwa chokhala ololera. Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo athu ndipo mumpingo mumakhala mtendere. M’banja la Yehova, lomwe ndi logwirizana, muli anthu osiyana zochita ndi zikhalidwe ndipo izi zimatisangalatsa. Koposa zonse, timasangalala kudziwa kuti tikutsanzira Mulungu wathu Yehova, yemwe ndi wololera. w23.07 25 ¶16-17

Lachisanu, January 10

Anthu ozindikira adzawamvetsetsa.​—Dan. 12:10.

Danieli ankaphunzira maulosi ali ndi cholinga chabwino kuti adziwe choonadi. Iye analinso wodzichepetsa ndipo anazindikira kuti Yehova amathandiza anthu amene amamudziwa komanso kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino kuti amvetse bwino zinthu. (Dan. 2:27, 28) Iye anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa podalira Yehova kuti amuthandize. (Dan. 2:18) Danieli ankaphunziranso maulosi mosamala. Ankafufuzanso m’Malemba ouziridwa omwe analipo pa nthawiyo. (Yer. 25:11, 12; Dan. 9:2) Kodi mungatsanzire bwanji Danieli? Muzifufuza zolinga zanu. Kodi mumaphunzira maulosi a m’Baibulo chifukwa chofunitsitsa kudziwa choonadi? Ngati ndi choncho, Yehova adzakuthandizani. (Yoh. 4:23, 24; 14:16, 17) Ena angachite zimenezi pofuna kupeza umboni wakuti Baibulo silinauziridwe ndi Mulungu. Pochita zimenezi, angamaone kuti si vuto kudziikira mfundo zokhudza chabwino ndi choipa n’kumazitsatira. Komabe, tiyenera kuphunzira maulosi tili ndi cholinga chabwino. w23.08 9 ¶7-8

Loweruka, January 11

Ukafooka . . . , mphamvu zako zidzachepa.—Miy. 24:10.

Tikamayembekezera zosatheka, podziyerekezera ndi ena tikhoza kudzilemetsa. (Agal. 6:4) Ngati timadziyerekezera ndi ena, tikhoza kuyamba mtima wansanje komanso wampikisano. (Agal. 5:26) Poyesetsa kuti tikwanitse zomwe ena achita, tikhoza kumadzikakamiza kuti tichite zimene sitingathe potengera luso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Komanso “chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.” Ndiye tingamve bwanji ngati titamafuna kuchita zinthu zomwe sitingazikwanitse n’komwe? (Miy. 13:12) Kuchita zimenezo kungatiwonongere mphamvu zathu komanso kungachititse kuti tizivutika kuthamanga pampikisano wokalandira moyo. Musamayembekezere kuti muchita zoposa zimene Yehova amayembekezera kuti mungachite. Iye sayembekezera kuti muzimupatsa zimene mulibe. (2 Akor. 8:12) Dziwani kuti Yehova sayerekezera zomwe mumachita ndi zimene ena amachita. (Mat. 25:20-23) Zimene iye amaona kuti ndi zamtengo wapatali ndi zoti mumamutumikira ndi mtima wonse, ndinu wokhulupirika komanso ndinu wopirira. w23.08 29 ¶10-11

Lamlungu, January 12

Kodi ndife ndi ludzu?​—Ower. 15:18.

Yehova anayankha pempho la Samisoni pochititsa kuti nthaka itulutse madzi. Samisoni atamwa madziwo, “anapezanso mphamvu ndi kutsitsimulidwa.” (Ower. 15:19) N’kutheka kuti madzi ankatulukabe pamalowa kwa zaka zambiri, mpaka pa nthawi imene mneneri Samueli anauziridwa kulemba buku la Oweruza. Aisiraeli amene anaona madziwa ankakumbukira kuti Yehova ndi wodalirika ndipo amathandiza atumiki ake okhulupirika pa nthawi yomwe avutika. Kaya tili ndi luso lotani kapena tachita zambiri potumikira Yehova, ifenso tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza. Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumavomereza kuti zinthu zikhoza kutiyendera bwino pokhapokha ngati tikudalira Yehova. Mofanana ndi Samisoni yemwe anapeza mphamvu atamwa madzi omwe Yehova anamupatsa, nafenso tikhoza kupeza mphamvu mwauzimu tikamadalira zinthu zonse zomwe Yehova amatipatsa.—Mat. 11:28. w23.09 4 ¶8-10

Lolemba, January 13

Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.​—Miy. 15:1.

Kodi tingatani ngati ena atikhumudwitsa, mwachitsanzo ngati anena zoipa zokhudza Mulungu wathu kapena kunyoza Baibulo? Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake komanso nzeru kuti tichite zinthu mofatsa. Bwanji ngati pambuyo pake tazindikira kuti sitinayankhe bwino? Tiyenera kuipemphereranso nkhaniyo komanso kuganizira zimene tingadzachite kuti tiyankhe bwino nthawi ina. Tikatero, Yehova adzatipatsa mzimu wake womwe ungatithandize kuugwira mtima komanso kukhala ofatsa. Mavesi ena a m’Baibulo angatithandize kuti tilankhule modekha pa nthawi imene zili zovuta kuti tichite zinthu mofatsa. Mzimu wa Mulungu ungatithandize kukumbukira mavesi amenewo. (Yoh. 14:26) Mwachitsanzo, mfundo zimene timapeza m’buku la Miyambo zingatithandize kukhala ofatsa. (Miy. 15:18) Buku la m’Baibuloli limasonyezanso ubwino wodziletsa ngakhale pa nthawi imene n’zovuta kuchita zimenezo.—Miy. 10:19; 17:27; 21:23; 25:15. w23.09 15 ¶6-7

Lachiwiri, January 14

Ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse.​—2 Pet. 1:12.

Mtumwi Petulo anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Pa nthawiyi, iye anayenda ndi Yesu, analalikira kwa anthu a mitundu ina komanso anatumikira m’bungwe lolamulira. Komabe atatsala pang’ono kufa, Yehova anamupatsa ntchito ina yoti agwire. Cha m’ma 62 mpaka 64 C.E., anauziridwa kulemba makalata awiri a m’Baibulo, omwe ndi buku la 1 Petulo ndi 2 Petulo. Iye ankakhulupirira kuti makalatawa adzathandiza Akhristu pambuyo pa imfa yake. (2 Pet. 1:13-15) Petulo analemba makalata ake ouziridwawa pa nthawi imene Akhristu anzake ankavutika ndi “mayesero osiyanasiyana.” (1 Pet. 1:6) Anthu oipa ankayambitsa ziphunzitso zabodza komanso makhalidwe oipa mumpingo. (2 Pet. 2:1, 2, 14) Akhristu omwe ankakhala ku Yerusalemu anali atatsala pang’ono kuona “mapeto a zinthu zonse.” Asilikali a Aroma anali atatsala pang’ono kuwononga mzindawo komanso kachisi wake. (1 Pet. 4:7) Mosakayikira, makalata a Petulo anathandiza Akhristuwo kudziwa zimene angachite kuti azipirira mayesero omwe ankakumana nawo komanso kukonzekera zimene akanakumana nazo m’tsogolo. w23.09 26 ¶1-2

Lachitatu, January 15

[Khristu] anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.​—Aheb. 5:8.

Mofanana ndi Yesu, ifenso tingaphunzire kukhala omvera pamene takumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, chakumayambiriro kwa mliri wa COVID-19, tinalangizidwa kuti tisiye kupita ku Nyumba za Ufumu komanso kulalikira kunyumba ndi nyumba. Kodi inuyo zinakuvutani kumvera? Komatu kumvera kwanu kunakutetezani, kunathandiza kuti muzigwirizana ndi abale ndi alongo ndiponso kunasangalatsa Yehova. Panopa, tonsefe ndife okonzeka kudzamvera malangizo alionse amene tingadzalandire pa chisautso chachikulu. Kumvera kungadzathandize kuti tipulumuke. (Yobu 36:11) Chifukwa chachikulu chimene chimatichititsa kumvera Yehova ndi chakuti timamukonda komanso timafuna kumusangalatsa. (1 Yoh. 5:3) Sitingathe kubwezera Yehova pa zabwino zonse zimene watichitira. (Sal. 116:12) Koma tingathe kumumvera komanso kumvera anthu amene wawalola kuti azititsogolera. Tikamamvera timasonyeza kuti ndife anzeru ndipo anthu anzeru amakondweretsa mtima wa Yehova.—Miy. 27:11. w23.10 11 ¶18-19

Lachinayi, January 16

Lambirani iye amene anapanga kumwamba, [ndi] dziko lapansi.​—Chiv. 14:7.

Kodi mngelo akanabwera kudzalankhula nanu, mukanamvetsera zimene akanakuuzani? Masiku ano mngelo akulankhula “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” Kodi iye akunena kuti chiyani? Akuti, “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero . . . lambirani iye amene anapanga kumwamba [ndi] dziko lapansi.” (Chiv. 14:6, 7) Yehova ndi Mulungu woona amene aliyense ayenera kumulambira. Timayamikira kuti watipatsa mwayi wamtengo wapatali womulambira m’kachisi wake wamkulu wauzimu. Kodi kachisi wauzimu ndi chiyani, nanga tingapeze kuti mfundo zofotokoza kachisiyu? Kachisi wauzimu si nyumba yeniyeni koma ndi njira yolambirira Yehova movomerezeka kudzera mu nsembe ya Yesu. Mtumwi Paulo anafotokoza za kachisiyu m’kalata imene analembera Akhristu a Chiheberi omwe ankakhala ku Yudeya. w23.10 24 ¶1-2

Lachisanu, January 17

“Sipakufunika gulu lankhondo kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watero Yehova.—Zek. 4:​6, 7.

Mu 522 B.C.E., adani a Ayuda anakwanitsa kuletsa ntchito yomanganso kachisi. Koma Zekariya anawatsimikizira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito mzimu wake wamphamvu powathandiza kuti apitirizebe ntchito yawo ngakhale kuti panali mavuto. Mu 520 B.C.E., Mfumu Dariyo analamula kuti kachisiyo apitirize kumangidwa ndipo anapereka ndalama komanso anthu oti athandize pa ntchitoyo. (Ezara 6:1, 6-10) Yehova analonjeza anthu akewo kuti adzawathandiza ngati ataika ntchito yomanga kachisi pamalo oyamba. (Hag. 1:8, 13, 14; Zek. 1:3, 16) Atalimbikitsidwa ndi aneneriwo, Ayudawo anayambiranso kumanga kachisi mu 520 B.C.E. ndipo anamaliza pasanathe zaka 5. Popeza kuti Ayudawo ankaika zimene Mulungu ankafuna pamalo oyamba ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, iye anawathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi komanso kuwapatsa zimene ankafunikira. Zotsatira zake n’zakuti iwo anayamba kulambira Yehova mosangalala.—Ezara 6:14-16, 22. w23.11 15 ¶6-7

Loweruka, January 18

Tiziyenda moyenera potsatira chikhulupiriro chimene bambo wathu Abulahamu anali nacho.—Aroma 4:12.

Ngakhale kuti anthu ambiri anamvapo zokhudza Abulahamu, amadziwa zochepa zokhudza iye. Komabe inu mumadziwa zambiri zokhudza Abulahamu. Mwachitsanzo, mumadziwa kuti iye amatchedwa “bambo wa onse . . . amene ali ndi chikhulupiriro.” (Aroma 4:11) Ndiye mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi inenso ndingamakhulupirire kwambiri Yehova ngati mmene Abulahamu anachitira?’ Inde n’zotheka. Njira imodzi yomwe tingakhalire ndi chikhulupiriro ngati Abulahamu, ndi kuphunzira pa chitsanzo chake. Mulungu atamulamula, Abulahamu anasamukira kutali ndi dziko lakwawo, ankakhala m’matenti komanso anali wofunitsitsa kupereka mwana wake Isaki ngati nsembe. Zimene anachitazo zinasonyeza kuti iye ankakhulupirira kwambiri Yehova. Chikhulupiriro komanso ntchito zake zinachititsa kuti Yehova azisangalala naye komanso akhale mnzake. (Yak. 2:22, 23) Yehova amafuna kuti tonsefe, kuphatikizapo inuyo, tikhale naye pa ubwenzi. Choncho iye anauzira Paulo ndi Yakobo kuti alembe m’Baibulo chitsanzo cha Abulahamu. w23.12 2 ¶1-2

Lamlungu, January 19

Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule.—Yak. 1:19.

Alongo, muziphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Akhristu amafunika kulankhula bwino ndi anthu. Pa nkhani imeneyi, Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anapereka malangizo amene ali mulemba lalero. Mukamamvetsera mosamala pamene ena akulankhula, mumasonyeza kuti mumaganizira anthu ena ndiponso kuwamvera chisoni. (1 Pet. 3:8) Ngati mukukayikira zoti mwamvetsa zimene munthu wina akunena kapena mmene akumvera mungachite bwino kumufunsa mafunso oyenera. Kenako muziganiza kaye musanalankhule. (Miy. 15:28) Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikufuna kulankhula ndi zoona komanso zolimbikitsa? Kodi zisonyeza ulemu komanso kukoma mtima? Muziphunzira kwa alongo olimba mwauzimu amene amalankhula bwino ndi anthu. (Miy. 31:26) Muziona mmene amalankhulira. Mukaphunzira kulankhula bwino ndi anthu, m’pamenenso muzigwirizana nawo kwambiri. w23.12 21 ¶12

Lolemba, January 20

Munthu aliyense amene amadzipatula . . . amakana nzeru zonse zopindulitsa.​—Miy. 18:1.

Masiku ano, Yehova angagwiritse ntchito anthu a m’banja lathu, anzathu kapenanso akulu kuti atithandize. Komabe zinazake zikatipweteka simatimafuna kucheza ndi anthu, timangofuna kukhala patokha. Zimenezi sizachilendo. Koma kodi tingatani kuti Yehova atithandize? Muzipewa mtima wosafuna kucheza ndi anthu. Nthawi zambiri munthu akakhala payekha saganiza bwino chifukwa amangoganizira za iyeyo ndi mavuto amene akukumana nawo. Kaganizidwe kameneka kangachititse kuti asasankhe bwino zochita. N’zoona tonsefe timafunika kukhala patokha makamaka tikakumana ndi mavuto aakulu. Komabe tikakhala kwatokha kwa nthawi yaitali, timatalikirana ndi anthu amene Yehova angawagwiritse ntchito kuti atithandize. Choncho muzilola kuti anthu a m’banja lanu, anzanu komanso akulu akuthandizeni. Muziona kuti anthu amenewa ndi njira imene Yehova angagwiritse ntchito kuti akuthandizeni.—Miy. 17:17; Yes. 32:1, 2. w24.01 24 ¶12-13

Lachiwiri, January 21

Lezala lisamadutse mʼmutu wake.​—Num. 6:5.

Anaziri ankalonjeza kuti sadzameta tsitsi lawo. Imeneyi inali njira yosonyezera kuti adzipereka kotheratu kwa Yehova. N’zomvetsa chisoni kuti pa nthawi ina Aisiraeli sankalemekeza kapena kuthandiza Anaziri. Nthawi zina Mnaziri ankafunika kulimba mtima kwambiri kuti akwaniritse lonjezo lake n’kukhalabe wosiyana ndi ena. (Amosi 2:12) Chifukwa chakuti timasankha kuchita chifuniro cha Yehova, ifenso timakhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli. Timafunika kulimba mtima kuti tizidziwikitse kuti ndife a Mboni za Yehova tikakhala kuntchito kapena kusukulu. Komanso pamene zochitika ndi makhalidwe a m’dzikoli zikuipiraipira, nthawi zina zingakhale zovuta kuti tizitsatira mfundo za m’Baibulo komanso kuuza ena uthenga wabwino. (2 Tim. 1:8; 3:13) Komabe tingachite bwino kumakumbukira kuti ‘timasangalatsa mtima wa [Yehova]’ tikapitiriza kukhala olimba mtima n’kumasonyeza kuti ndife osiyana ndi anthu omwe samutumikira.—Miy. 27:11; Mal. 3:18. w24.02 16 ¶7; 17 ¶9

Lachitatu, January 22

Muzilandirana.​—Aroma 15:7.

Taganizirani za anthu osiyanasiyana omwe anali mumpingo wa ku Roma. Sikuti mumpingowu munali Ayuda okhaokha, omwe makolo awo anawaphunzitsa kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. Koma munalinso anthu amitundu ina omwe anali osiyana kwambiri ndi Ayuda. N’kutheka kuti ena anali akapolo pomwe ena ayi, ndipo mwina enanso anali ndi akapolo. Ndiye kodi Akhristuwo akanatani kuti azikondana kwambiri ngakhale kuti anali osiyana chonchi? Mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti ‘azilandirana.’ Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa? Mawu amene anawamasulira kuti “kulandira,” amatanthauza kuchitira winawake zinthu mokoma mtima kapena kumuchereza, monga kumuitanira kunyumba kapena pakati pa anzathu. Mwachitsanzo, Paulo anauza Filimoni kuti alandire kapolo wake Onesimo yemwe anathawa, ndipo anati: “Umulandire ndi manja awiri.” (Filim. 17) Komanso Purisikila ndi Akula analandira Apolo yemwe ankadziwa mfundo zochepa zokhudza Chikhristu poyerekeza ndi iwowo ndipo “anamutenga.” (Mac. 18:26) Choncho Akhristuwa sanalole kuti kusiyana pa zinthu zina kuwagawanitse ndipo ankalandirana. w23.07 6 ¶13

Lachinayi, January 23

Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova.​—Sal. 116:14.

Chifukwa chachikulu chomwe chimatichititsa kuti tidzipereke kwa Yehova ndi choti timamukonda. Sikuti chikondichi chimangotengera mmene tikumvera. M’malomwake, chimabwera chifukwa ‘chodziwa zinthu molondola’ komanso ‘kumvetsetsa zinthu zauzimu’ zomwe zachititsa kuti muzikonda kwambiri Mulungu. (Akol. 1:9) Kuphunzira Malemba kwakuthandizani kutsimikizira kuti (1) Yehova ndi weniweni, (2) Baibulo ndi Mawu ake ouziridwa, ndiponso (3) iye amagwiritsa ntchito gulu lake pokwaniritsa cholinga chake. Anthu amene amadzipereka kwa Yehova amadziwa mfundo zoyambirira zopezeka m’Mawu a Mulungu ndipo amazitsatira pa moyo wawo. Amayesetsa mmene angathere kuuza ena zimene amakhulupirira. (Mat. 28:19, 20) Amakonda kwambiri Yehova ndipo amafunitsitsa kulambira iye yekha. Kodi izi ndi zimene inunso mukuchita? w24.03 4-5 ¶6-8

Lachisanu, January 24

Iwo adzakhala thupi limodzi.​—Gen. 2:24.

Abigayeli anakwatiwa ndi Nabala yemwe Baibulo limanena kuti anali wouma mtima komanso wopanda khalidwe. (1 Sam. 25:3) Ziyenera kuti zinali zovuta kwa Abigayeli kukhala ndi mwamuna ngati ameneyu. Kodi Abigayeli anali ndi njira yachidule yothetsera banja lake? Inde. Iye akanatha kuchita zimenezi pamene Davide, amene anali mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anabwera kuti adzaphe mwamuna wake chifukwa chonyoza Davideyo ndi anyamata ake. (1 Sam. 25:9-13) Abigayeli akanatha kuthawa n’kusiya Davide kuti apange zomwe ankafuna. M’malomwake anapita kukalankhula ndi Davide kuti asaphe Nabala. (1 Sam. 25:23-27) N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Abigayeli ankakonda Yehova ndipo ankalemekeza mfundo zake zokhudza ukwati. Iye ankadziwa kuti Yehova amaona kuti ukwati ndi wopatulika. Iye ankafuna kusangalatsa Mulungu ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kuti achite zonse zimene akanatha kuti ateteze banja lake ndiponso mwamuna wake. Anachita zinthu mwamsanga kuti Davide asaphe Nabala. w24.03 16-17 ¶9-10

Loweruka, January 25

Ndikanakulimbikitsani ndi mawu amʼkamwa mwanga.​—Yobu 16:5.

Kodi pali ena mumpingo mwanu omwe asiya zinthu zina n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova? Kodi mukudziwa achinyamata ena omwe molimba mtima akuyesetsa kuti akhale osiyana ndi anzawo kusukulu, ngakhale kuti kuchita zimenezo n’kovuta? Kodi pali ena omwe akuyesetsa kukhalabe okhulupirika ngakhale kuti akutsutsidwa ndi achibale awo? Tiyenera kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kulimbikitsa Akhristu anzathu okondedwawa powayamikira chifukwa choyesetsa kukhala odzimana komanso olimba mtima. (Filim. 4, 5, 7) Yehova amadziwa kuti timafuna ndi mtima wonse kumusangalatsa, komanso kuti timafunitsitsa kudzimana zinthu zina n’cholinga choti tikwaniritse lonjezo lathu lomwe tinapanga podzipereka. Iye anatilemekeza potipatsa mwayi woti tizisonyeza patokha kuti timamukonda. (Miy. 23:15, 16) Choncho tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitirizabe kutumikira Yehova komanso kuyesetsa kuchita zomwe tingathe pomupatsa zinthu zabwino kwambiri. w24.02 18 ¶14; 19 ¶16

Lamlungu, January 26

Anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu.​—Mac. 10:38.

Tayerekezerani kuti mukuona zimene zinachitika kumapeto kwa chaka cha 29 C.E., chakumayambiriro kwa utumiki wa Yesu. Yesu ndi mayi ake Mariya komanso ena mwa ophunzira ake, aitanidwa ku ukwati ku Kana. Mariya ndi mnzawo wa eni ukwatiwo ndipo akuthandizira kulandira alendo. Koma phwandolo lili mkati, pachitika vuto lina. Vinyo waathera. Mwamsanga, Mariya akuuza mwana wake kuti: “Vinyo waathera.” (Yoh. 2:1-3) Ndiye kodi Yesu akuchita chiyani? Iye akuchita chozizwitsa posandutsa madzi kukhala “vinyo wabwino.” (Yoh. 2:9, 10.) Yesu anachitanso zozizwitsa zina zambiri pa utumiki wake. Iye anagwiritsa ntchito mphamvu zomwe anali nazo zochitira zozizwitsa pothandiza anthu masauzande ambiri. Mwachitsanzo, taganizirani kuchuluka kwa anthu omwe anawathandiza pa zozizwitsa ziwiri zokha. Pamene anadyetsa amuna 5,000 komanso pa nthawi ina amuna 4,000. Ngati titaphatikizapo akazi ndi ana omwe analiponso pa nthawiyi, n’kutheka kuti anadyetsa anthu 27,000. (Mat. 14:15-21; 15:32-38) Pa zochitika ziwiri zonsezi, Yesu anachiritsanso anthu ambiri odwala.—Mat. 14:14; 15:30, 31. w23.04 2 ¶1-2.

Lolemba, January 27

Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja, ine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”​—Yes. 41:13.

Pakachitika vuto linalake lalikulu, masiku ena mukhoza kumakhala wofooka komanso ndi nkhawa. Mofanana ndi Eliya, mungamafune kuti muzingogona osadzuka. (1 Maf. 19:5-7) Tingafunike kuthandizidwa kuti tipitirize kutumikira Yehova. Pa nthawi ngati imeneyi, Yehova amatitsimikizira kuti adzatithandiza monga mmene lemba laleroli likusonyezera. Mfumu Davide anaona Yehova akumuthandiza mwa njira imeneyi. Iye atakumana ndi mavuto komanso kuopsezedwa ndi adani, anauza Yehova kuti: “Dzanja lanu lamanja limandithandiza.” (Sal. 18:35) Nthawi zambiri Yehova amatithandiza polimbikitsa anthu ena kuti atithandize. Mwachitsanzo, Davide atafooka, Yonatani yemwe anali mnzake anabwera kudzamuthandiza komanso kumuuza mawu olimbikitsa. (1 Sam. 23:16, 17) Yehova anasankhanso Elisa kuti akalimbikitse Eliya.—1 Maf. 19:16, 21; 2 Maf. 2:2. w24.01 23-24 ¶10-12

Lachiwiri, January 28

Yehova ndi amene amapereka nzeru. Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka m’kamwa mwake.—Miy. 2:6.

Yehova amapereka zinthu mowolowa manja. Timaona zimenezi tikaganizira za “nzeru yeniyeni” yomwe pa Miyambo chaputala 9, ikufotokozedwa ngati mkazi. Nkhaniyi imasonyeza kuti mkazi wophiphiritsayu wapha nyama yake, wasakaniza vinyo komanso wayala patebulo pake. (Miy. 9:2) Kuwonjezera pamenepo, mogwirizana ndi vesi 4 ndi 5, “nzeru [mkazi wophiphiritsayu] ikunena kuti, ‘Bwerani mudzadye chakudya changa.’” N’chifukwa chiyani tiyenera kupita kunyumba ya nzeru yeniyeni komanso kukadya chakudya chake? Yehova amafuna kuti ana ake akhale anzeru ndiponso otetezeka. Iye safuna kuti tiziphunzira m’njira yowawa kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake tingadzanong’oneze nazo bondo. N’chifukwa chake “anthu owongoka mtima, amawasungira nzeru zopindulitsa.” (Miy. 2:7) Ngati timalemekeza kwambiri Yehova, tidzafuna kuti tizichita zimene zimamusangalatsa. Timamvetsera malangizo ake anzeru ndipo timasangalala kuwatsatira.—Yak. 1:25. w23.06 23 ¶14-15

Lachitatu, January 29

Mulungu si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu.​—Aheb. 6:10.

Ngakhale kuti sitingathe kuchita zambiri potumikira Mulungu tisamakayikire kuti iye amayamikira zimene timakwanitsa kuchita kuti timusangalatse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? M’nthawi ya Zekariya, Yehova anauza mneneriyu kuti apange chisoti chachifumu pogwiritsa ntchito golide ndi siliva yemwe Ayuda omwe anatsala ku Babulo anatumiza. (Zek. 6:11) “Chisoti chachifumucho” chinali choti ‘chizidzawakumbutsa’ za zinthu zimene anapereka mowolowa manja. (Zek. 6:14, mawu a m’munsi.) Tingakhale otsimikiza kuti Yehova sadzaiwala zimene timachita mwakhama pomutumikira ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. N’zosachita kufunsa kuti tipitiriza kukumana ndi mavuto m’masiku otsirizawa ndipo mwina zinthu ziziipiraipira. (2 Tim. 3:1, 13) Koma sitiyenera kuda nkhawa kwambiri. Kumbukirani zimene Yehova anauza anthu ake m’masiku a Hagai. Iye anati: “Ine ndili ndi inu . . . musachite mantha.” (Hag. 2:4, 5) Ifenso tisamakayikire kuti Yehova adzakhala nafe tikamachita zimene amafuna. w23.11 19 ¶20-21

Lachinayi, January 30

Ndine munthu wochimwa.​—Luka 5:8.

Yehova akanatha kusankha kuti zimene mtumwi Petulo ankalakwitsa zisalembedwe m’Baibulo. Koma anauzira anthu kuti alembe zimenezo kuti tiziphunzirapo kanthu. (2 Tim. 3:16, 17) Kuphunzira za Petulo, yemwe ankalakwitsa zinthu komanso anali munthu ngati ifeyo, kumatithandiza kuona kuti Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu osalakwitsa kalikonse. Iye amafuna kuti tizipitiriza kumutumikira ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kuchita khama? Pambuyo poyesetsa kulimbana ndi vuto linalake, nthawi zina zingapezeke kuti talakwitsanso. Koma tiyenera kupitirizabe kuchita khama, osagwa ulesi. Tonsefe timalankhula kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake timadzimvera nazo chisoni. Komabe tikapanda kutaya mtima, Yehova amatithandiza kuti tikonze zomwe zalakwikazo. (1 Pet. 5:10) Chifundo chomwe Yesu ankamusonyeza Petulo ngakhale kuti ankalakwitsa zinthu, chingatilimbikitse kuti tipitirize kutumikira Yehova. w23.09 20-21 ¶2-3

Lachisanu, January 31

Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.​—Yoh. 11:21.

Yesu akanatha kuchiritsa Lazaro, mogwirizana ndi zimene Marita ananena, zomwe zili mulemba lalero. Koma Yesu anaganiza zochita chinthu china chapadera kwambiri. Analonjeza Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” Anamuuzanso kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yoh. 11:23, 25) Zimenezi ndi zoona chifukwa Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa akufa. M’mbuyomu iye anaukitsapo kamtsikana katangomwalira kumene komanso anaukitsapo mnyamata ndipo zikuonekanso kuti linali tsiku lomwe anamwaliralo. (Luka 7:11-15; 8:49-55) Koma kodi akanaukitsa munthu yemwe panali patapita masiku 4 kuchokera pamene anamwalira ndipo thupi lake linali litayamba kuwonongeka? Mariya yemwe ndi mchemwali wina wa Lazaro, anapita kukakumana ndi Yesu. Iye anabwerezanso zimene mchemwali wake ananena kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” (Yoh. 11:32) Poona komanso kumva Mariya ndi anthu ena akulira, zinamukhudza kwambiri Yesu. Chifukwa chokonda kwambiri anzakewo, iye anagwetsa misozi. Amadziwa mmene zimapwetekera munthu yemwe umamukonda akamwalira. N’zoonekeratu kuti iye ankafunitsitsa kuchotsa chomwe chinawachititsa kuti akhale ndi chisoni. w23.04 10-11 ¶12-13

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena