Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/15 tsamba 21
  • Chidziwitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziwitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndani Amene Ali Atsutsi?
  • Mzinda wa “Malinga”
  • Kupotoza Koipa Kosakaza
  • Kodi Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana Ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Gawo 1—Kodi Yesu ndi Ophunzira Ake Anaphunzitsa Chiphunzitso cha Utatu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Utatu Wodalitsidwa”—Kodi Uli mu Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Gawo 4—Kodi chiphunzitso cha Utatu chinayamba liti ndipo motani?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/15 tsamba 21

Chidziwitso pa Nyuzi

Kodi Ndani Amene Ali Atsutsi?

“Mu Baibulo timawerenga kuti Mulungu ali Utatu,” analemba motero Profesa Johan Heyns, mtsogoleri wauzimu wa Tchalitchi cha Dutch Reformed cha ku South Africa, mu nyuzipepala ya ku South Africa Naweek-Volksblad mu kope la November 15, 1986. Kwa awo amene analingalira kuti Mulungu sangakhale atatu koma m’modzi, akupitiriza profesayo, “Tchalitchi cha Chikristu chinanena kuti anthu amenewa akulalikira chiphunzitso chonyenga, ndipo chotero tchalitchi chinawakananso iwo monga atsutsi.”

Koma kodi ndi kuti kumene liwu lakuti Utatu limapezeka mu Baibulo? Profesa Heyns sananene chirichonse. Ichi nchosadabwitsa chifukwa chakuti, monga mmene The New Encyclopaedia Britannica imalongosolera, “palibe ngakhale liwu lakuti Utatu osatinso kulongosoledwa komveka kwa chiphunzitsocho kumene kumawoneka mu Chipangano Chatsopano, ndipo Yesu ndi otsatira ake sanayesere kusokoneza Shema [Kulongosoledwa kwa chikhulupiriro cha Chiyuda] mu Chipangano Chakale: ‘Imvani Israyell: Ambuye Mulungu wathu ali Ambuye mmodzi’ (Deut. 6:4).” Ngati sichinaphunzitsidwe ndi Yesu ndi ophunzira ake ndiponso osalongosoledwa mwachindunji mu Baibulo, kodi ndimotani mmene chiphunzitso cha Utatu chinakhalira chotchuka? Ngakhale kuti Britannica ikunena kuti choyambitsa chiphunzitsocho chiri mu “Chipangano Chatsopano,” iyo imavomereza kuti “chiphunzitsocho chinayamba kukula mwapang’onopang’ono mkati mwa zaka mazana angapo ndi kupyolera mu kutsutsana kochuluka” ndikuti kufika ku mapeto kwa zana la chinayi “chiphunzitso cha Utatu chinatenga mtundu wa kaimidwe womwe chasungirira kuyambira nthawi imeneyo.”

Ngati awo amene amakana kukhulupirira kuti Mulungu ali atatu mu mmodzi ali atsutsi, nanga bwanji ponena za Yesu Kristu iyemwini? lye anabwereza mawu apamwambapowo apa Deutronomo 6:4: “Ambuye Mulungu wathu ali Ambuye mmodzi.” (Marko 12:29, King James Version) Yesu ananenanso kuti: “Atate ali wamkulu pa ine.” (Yohane 14:28 NW) Chotero kodi ndani amene ali atsutsi? Awo amene amamamatira ku zimene Yesu anaphunzitsa kapena awo amene amaumirira ku chiphunzitso chomwe chinakula mazana pambuyo pa imfa yake?​—Yerekezani 1 Akorinto 4:6 ndi 2 Yohane 9.

Mzinda wa “Malinga”

“Sydney lerolino uli mzinda umene uli pans) pa chiwopsyezo,” inayamba motero ndemanga ya mkonzi mu The Sun-Herald, nyuzipepala ya mu Sydney, Australia. “Matauni ake a ang’ono okhalamo ali ochingidwa, okhomedwa ndi maloko awiri ndiponso ndi malinga ochinjiriza amagetsi. Masitima ake oyenda utsiku amasakazidwa, kulembedwa ndi mawu otukwana ndipo simukhala anthu. Makwalala ake pambuyo pa mdima akukhala mowonjezereka owopsya.

Ngakhale kuti zapamwambazo zingakhale chithunzi chodetsa nkhawa cha mizinda yaikuluikulu yambiri kuzungulira dziko lapansi, zimaika chenjezo la kudera nkhaWa kwapadera kwa anthu a ku Australia. Komabe, ophunzira Baibulo sali odabwltsidwa kuwona kufallkira kwa kusayeruzika. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti amakumbukira mawu a ulosi a Yesu ponena za mikhalidwe mu tslku lathu. Yesu ananena kuti “chifukwa cha kuchuruka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.” (Mateyu 24:12) Ndipo pamene ndemanga ya mkonzi wa The Sun-Herald ikudandaulira kuwonjezereka kwa mantha okhudza womwe unatchedwa Mzinda Wamwawi kwambiri wa dziko la mwawi, “mwawi” sudzabweretsa ku mapeto kuipa. Yehova yekha, kupyolera mwa boma lake la kumwamba, adzatero. Masalmo 5:4 akutitsimikizira ife kuti Yehova “sali Mulungu wakukondwera nacho choipa; mphulupulu slikhala ndi inu.”

Kupotoza Koipa Kosakaza

Baibulo limalamula Akristu ‘kusala mwazi.’ (Machitidwe 15:29) Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti lamulo la m’Malemba limeneli limagwiritsidwa ntchito ku kudya kwa mwazi limodzinso ndi kulandira mwazi. AIDS, nthenda yakupha yomwe imayambukira dongosolo la chitetezero chathupi ingatengedwe kuchokera ku kulandira mwazi. Mkupotoza komvetsa chisoni koma koipa, mwana wobadwa ndi nthenda yosawonekawoneka ndi yakupha nthenda ya kuperewera kwa chitetezero yotchedwa reticular dysgenesis anapatsidwa kuwokedwa kwa nkolopfupa pa msinkhu wa miyezi isanu ndi umodzi. Njirayo inaphatikizapo kuthiridwa mwazi. Kuwokako kunawoneka kukhala kwa chipambano kufikira pamene madokotala anazindikira kuti kuthiridwa kwa mwaziko kunapatsa khandalo nthenda ina yakupha. “Pa msinkhu wa zaka 2 1/2 wodwalayo akuchita bwino kupatulapo kokha chinthu chimodzi,” ikusimba motero Physician’s Weekly. “Mwanayo anapatsidwa maplateleti pambuyo pa kuwokedwako pamene kufufuza kaamba ka (kachirombo ka AIDS) kunali kusanakhale kwa lamulo ndipo tsopano ali ndi AIDS.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena