Kusungirira Umodzi Wathu Wachikristu
“TANGOLINGALIRANI mukutchedwa mbale kapena mlongo,” analemba tero mlembi wa Chikatolika, Domenico Mosso, “osati ndi wansembe, koma ndi mwamuna wa m’zaka zapakati pafupi ndi inu kapena ndi mkazi wachichepere wokongola yemwe wangofika kumene kulamanja kwanu. ‘Mwati bwanji?’ ‘Ndanena kuti, mwauka bwanji mbale.’ ‘Munganene bwanji tero . . . sindikudziŵani nkomwe, chotero nchifukwa ninji kuzoloŵerana koteroko? Ndiko nkomwe, tiri m’tchalitchi.’”
Lingaliro lenileni la ubale ndithudi likusowa mkati mwa matchalitchi a Chikristu cha Dziko. Ichi chimasonyeza kusoweka kwawo kwa umodzi Wachikristu. Ngakhale kuli tero, siziri tero ndi Mboni za Yehova. Mofanana ndi atsatiri oyambirira a Yesu, ife mwaufulu timatcha wina ndi mnzake mbale ndi mlongo. (2 Petro 3:15) Mosasamala kanthu za kumene tingapite m’dziko, kulandiridwa kotentha, kwa ubale kuli kwapafupi motero monga Nyumba ya Ufumu yapafupi koposa. Umodzi umasonyezedwanso m’chenicheni chakuti mipingo yonse imatsatira dongosolo limodzimodzi la malangizo ndipo kuti Mboni zonse zimadzilowetsa m’kulalikira “mbiri yabwino ya ufumu.”—Mateyu 24:14.
Pa usiku iye asanafe, Yesu Kristu anapemphera kuti: “Ndipempherera . . . iwo akukhulupirira ine chifukwa cha mawu awo; kuti onse akakhale amodzi, monga inu, Atate, mwa ine ndi ine mwa inu.” (Yohane 17:20, 21) Mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti Yehova Mulungu anayankha pemphero la Yesu. Pakati pa Akristu oyambirira, udani wa nthaŵi yaitali pakati pa Ayuda ndi Akunja unatha kupyolera mu mphamvu yogwirizanitsa ya ziphunzitso za Kristu.—Agalatiya 3:28.
Ngakhale kuli tero, chinatenga kuyesetsa kusungirira umodzi umenewu. Mtumwi Paulo anachonderera ogwira ntchito anzake “kuyenda koyenera m’maitanidwe [a a kumwamba] . . . kusamalitsa kusunga umodzi wa mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.” Iwo sanayenera kugawanikana m’mipatuko yosiyanasiyana. Ayi, “thupi limodzi, ndi mzimu umodzi, monganso anakuitanani m’chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu; Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse.” Atumwi, abusa, ndi aphunzitsi mu mpingo anapatsidwa kuti athandize “onse kufikira umodzi m’chikhulupiriro.”—Aefeso 4:1-6, 11-14.
Mboni za Yehova m’nthaŵi zamakono zasungirira mwachipambano “umodzi” umenewu. Ngakhale kuli tero, nsonga zosiyanasiyana—mzimu wa kudzidalira, kusiyana kwa makhalidwe a moyo ndi fuko, zophophonya zosiyanasiyana ndi kupanda ungwiro pakati pa Akristu anzawo—zingawopsyeze “umodzi wathu m’chikhulupiriro.” Ndimotani mmene iwo ungasungidwire?
Kudyera pa Gome Limodzimodzilo
Yehova samawunikira Mkristu aliyense payekha. M’malomwake, Kristu anaika gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti lipereke zinthu zophunzirira za m’Malemba ndi uphungu wa pa nthaŵi yake kwa Akristu kuzungulira dziko lonse. (Mateyu 24:45-47) Nsanja ya Olonda mwakutero imafalitsidwa m’zinenero 103 kuti ithandize kufikira chifuno cha dziko lonse chimenecho.
Kudyera pa gome limodzimodzilo lauzimu kwachita zokulira kutulutsa ndi kusungirira umodzi wa chikhulupiriro. Nthaŵi zina, ngakhale kuli tero, uphungu wina ungawoneke kukhala wosagwira ntchito m’maiko ena. Kodi tiyenera kudzimva kuti sitifunikira chidziŵitso chimenechi? Kutalitali. Ena a machenjezo a Paulo kwa Akristu okhala mu mzinda wa makhalidwe oipa, wolambira mafano wa Korinto ungakhale unawonekera kukhala wosagwira ntchito mokwanira kwa Akristu okhala m’midzi. (1 Akorinto 6:15, 16; 10:14) Komabe, Akristu kulikonse anawona zolemba za Paulo monga mbali ya “Malemba.”—2 Petro 3:16.
Mofananamo lerolino, nkhani zina sizingawoneke kukhala zikugwira ntchito ku mikhalidwe ya kumaloko monga mmene zimachitira zina. Koma tiyenerabe kulandira chenjezo la pasadakhale, tikumadziŵa kuti mu mbadwo wathu wa kulankhuzana kofulumira, zikhoterero zoipa zomwe zayambika mu mbali imodzi ya dziko zingafalikire mofulumira!
Kupanda Ungwiro ndi Kukhala ndi Malingaliro Onkitsa
Ananena tero wophunzira Yakobo: Timakhumudwa tonse m’zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Chifukwa cha kupanda ungwiro, anthu alinso okhoterera ku kukhala onkitsa. Ichi sichingawoneke kukhala vuto ngati anthu amagawana malingaliro amodzimodziwo. Mwachitsanzo, anthu aŵiri onkitsa osakondweretsedwa mwamsanga angakhale pamodzi bwino lomwe. Koma ngati wina ali wa uve ndipo winayo ali wosakondweretsedwa msanga, sipangakhale mapeto ku kukangana!
Mboni za Yehova zatuluka “kuchokera kwa mtundu uliwonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Monga chotulukapo, aliyense payekha pakati pathu angakhale ndi malingaliro osiyana kotheratu ponena za zinthu zoterozo zonga kadyedwe, zovala, chisamaliro cha za umoyo, ndi po ngakhale malamulo a makhalidwe abwino m’mayanjano. Malingaliro osiyana oterowo safunikira kuika kukangana pakati pathu. Baibulo limachenjeza motsutsana ndi kukhala wonkitsa ndipo limatilimbikitsa ife kugwirira ntchito kulinga ku kulinganizika ndi kulingalira. “Nzeru yochokera kumwamba iri . . . ya mtendere, yaulere,” limatero Baibulo.—Yakobo 3:17.
Zowona, Baibulo limatsutsa mwachindunji kwambiri machitachita ena. Koma kaŵirikawiri limatilimbikitsa ife kokha kutenga njira ya pakati pa kunkitsa kuŵiri. Lingalirani chomwe Baibulo limanena pa nkhani zotsatirazi:
Ntchito ya Kuthupi: “Ulesi ugonetsa tulo tofa nato, ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.” (Miyambo 19:15) “Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.”—Mateyu 6:24.
Kulankhula: Wokhala chete achita mwanzeru.” (Miyambo 10:19) “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake . . . mphindi ya kutonthola ndi mphindi ya kulankhula.”—Mlaliki 3:1, 7.
Kuyanjana: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) “Phazi lako lilowe m’nyumba ya mnzako kamodzi kamodzi, kuti angatope nawe ndi kukuda.”—Miyambo 25:17.
Kulera Ana: “Wolekerera mwanake osammenya amuda, koma womkonda amyambize kumlanga.” (Miyambo 13:24) “Musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”—Akolose 3:21.
Ku ukulu umene malingaliro athu amakhalira olinganizika koposa kukhala onkitsa, kudzakhalanso kuchepera kwa kuwombana ndi Akristu ena kumene tidzakumana nako. Koma bwanji ngati kusamvana kuwonekerabe chifukwa cha kupanda ungwiro? Kumbukirani mawu a Paulo pa Akolose 3:13: “Kulolerana wina ndi mnzake ndi kukhululukirana eni okha ngati wina ali nacho chifukwa cha pa mnzake.”
‘Iye Anandikhumudwitsa Ine’
Ena mu mpingo, ngakhale kuli tero, angayedzamire ku kukhala ozindikira monkitsa, kuŵerenga zisonkhezero zoipa kukhala mawu opanda liwongo ndi magesicha. Mwinamwake ichi chiri chifukwa cha chiyambi chawo. Mosasamala kathu ndi chimene chiri nkhaniyo, chimakhala chomvetsa chisoni chotani nanga pamene ozindikira mopambanitsa amenewo adzilola iwo eni kulakwiridwa ndi chinthu chaching’ono kapena, moipirakobe, kuvutitsa ena ponena za nkhani mwa kufesa mbewu za kusagwirizana!
Zowona, Baibulo limatsutsa mkhalidwe womwe ungakhumudwitse ophunzira ena. (Luka 17:1, 2) Ndipo achikulire ayenera kukhala ozindikira ku malingaliro a Akristu anzawo. Pa nthaŵi imodzimodziyo, Baibulo limatilangiza ife mwamphamvu molimbana ndi kukhala ozindikira monkitsa ndi kukulitsa zolakwa m’maganizo athu. (Mlaliki 7:9) M’kuwonjezerapo, kufalitsa kusakhutiritsidwa pakati pa abala athu mwa kubukitsa zophophonya za wina wake chiri chimodzi cha zinthu zimene “Yehova amada.”—Miyambo 6:16-19.
Mzimu wa Mulungu ungatithandize ife kulaka kukhala ozindikira mopambanitsa. M’malo mwa kukhalirira pa zophophonya za abale athu, ife, ndi thandizo la mzimu, tingalingalire bwino, malingaliro omangirira. (Afilipi 4:8) Ichi chimapititsa patsogolo umodzi.
Umodzi Si Kufanana
Umodzi wa dziko lonse, ngakhale kuli tero, siumatanthauza kutsendereza kwa umunthu kapena kuphwanya chiyambi. Kumene maprinsipulo a Baibulo amagwira ntchito, tiri achimwemwe kusiya kulingalira kodziimira pa tokha kwa madongosolo a dziko iri ndi kulandira kutsogoza kwa mzimu wa Yehova. Komabe, m’kuchita ntchito yathu monga olalikira, pali malo okulira kaamba ka umunthu ndipo, inde, kulingalira. Ndithudi, abale athu kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito luso lokulira m’kusinthira njira zawo za kuchitira umboni ku mikhalidwe ya kumaloko.
Kenaka pali malo okulira a machitachita pamene maprinsipulo a Malemba sakukhudzidwa mwachindunji, kuphatikizapo miyambo ina ya kumaloko. Mu kontinenti ya Europe, anthu kaŵirikaŵiri amagwirana m’manja. M’mbali za ku Far East, iwo amawerama. Uliwonse wa miyamboyi uli wolandirika kwa Akristu. Kapena lingalirani kavalidwe ndi kapesedwe. Baibulo limapereka kokha zitsogozo zokulira za kudekha ndi kulinganizika. Mkati mwa zimenezo, tingatsatire zokonda zanthu, pamene tikusonyeza “malingaliro owongoka.”—1 Timoteo 2:9, 10.
Chotero, akulu mwakutero nthaŵi zonse ali osamalitsa kupereka uphungu pa maziko olimba a maprinsipulo a Baibulo m’malo mwa zokonda za umwini. Ndithudi, pamene chibwera ku nkhani zauzimu, iwo adzakhala patsogolo m’kupititsa patsogolo umodzi weniweni. Tingachite mbali yathunso. Ife ‘tingapitirize kuwona ngati tiri m’chikhulupiriro’ mwa kuphunzira mokhazikika Baibulo ndi zofalitsidwa za ‘kapolo wokhulupirika.’ (2 Akorinto 13:5) Tingasungirire umodzi mu zintchito mwa kupanga molimba mtima “chilengezo chapoyera” cha chikhulupiriro chathu.—Ahebri 13:15.
M’njira imeneyi tidzalabadira uphungu wowuziridwa: “Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu, koma mumangike mu mtima womwewo ndi chiŵeruziro chomwecho.”—1 Akorinto 1:10.
[Chithunzi patsamba 30]
Kusungilira maunansi abwino, ngakhale pamene wina ali ndi maziko kaamba ka kupatsira mlandu, kuli koyenerera kaamba ka umodzi