Chidziŵitso pa Nyuzi
Ngachikale?
Malinga nkunena kwa wansembe Waangilikani mu Adelaide, Australia, machenjezo otsutsa kudzutsa chilakolako chathupi cha kugonana chimene chingatsogolere kukuchita chisembwere ndi chigololo ngachikale ndipo osakhala a m’magwero Achikristu. M’kupenda kwake kwaposachedwapa pa zakugonana, iye akusimba kuti anthu aŵiri otomerana kudzakwatirana saanali kwenikweni kuchimwa ngati iwo anagonana asanakwatirane. Ndiponso kupendako kukuchirikiza kuti kugonana kwa aziŵalo zofanana kungakhale kovomerezeka m’zochitika zina. Malinga nkunena kwa Courier Mail ya ku Brisbane, mneneri wa wa Uniting Church mu Australia “anagwirizana ndi miyezo yaikulu ya kusimbidwako.”
Komabe, Baibulo limafotokoza kuti ndicho chifuniro cha Mulungu kwa onse ‘kudzipatula kudama’ ndi kuti “adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (1 Atesalonika 4:3, 4; 1 Akorinto 6:9, 10) Ndithudi, awo amene amavomereza Baibulo kukhala Mawu a Mulungu ouziridwa amazindikira kuti lingaliro lake la kugonana limachokera kwa Mlengi wa nzeru zonse. Chiyambukiro chake pa awo amene amakhalira moyo miyezo ya Baibulo chimapereka umboni wakuti zotchedwa chotero kuti zitsogozo zachikale zamakhalidwe abwino zimachirikizabe kukukhazikika kwa banja ndi kugaŵira tchinjirizo kuzipsera zazikulu zamalingaliro ndi nthenda zonyansa zimene zimakhala zotulukapo m’khalidwe losadzisungira.
Chitetezero Chabwino Koposa
Kugwiritsiridwa ntchito kolakwa kwa mankhwala oledzeretsa kudakali vuto lodetsa nkhaŵa. Motero, kodi ndiiti imene iri njira yabwino koposa ya kutetezera achichepere kukugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa? M’kupendedwa kofalitsidwa m’nyuzipepala ya ku Brazil O Estado de S.Paulo, pulofesala wa French ndi dokotala wa nthenda zamaganizo Claude Olievenstein anagogomezera kufunika kwa zitsogozo ndi chichirikizo zachikondi. Iye anati: “Pamene anthu amalankhula za mankhwala lerolino, ntchito ya apolisi, dongosolo la chiweruzo, ndi sukulu zimagogomezeredwa. Komabe, chofunika chachikulu ndicho chija cha chitetezero cha [kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala oledzeretsa] kwa banja. . . . Ana ambiri samadziŵa chimene chiri ulamuliro wa atate. Atate amakhala kulibe; mwachiwonekere iye wasiya.”
Polongosola chifukwa chake chitetezero cha kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa mankhwala oledzeretsa chiri chofunika kwenikweni pamlingo wa banja, Dr. Olievenstein anawonjezera kuti: “Tikukhala ndi moyo m’chitaganya chofuna phindu kumene anthu ali amanyazi ndi makhalidwe abwino. Pamene ana athu, chifukwa cha mankhwala oledzeretsa, ayamba kusonyeza kakhalidwe kenakake, chiri chifukwa chakuti sitimapanganso makhalidwe abwino kuti adziŵidwe. Chitaganya chathu chakhala chopimbidzala, chosalingalira, chotanganitsidwa. Anthu amaganiza za nkhondo ya kukhala ndi moyo chabe.”
Malinga nkunena kwa magazini otchedwa Superinteressante, kufufuza kwa ku U.S. kukutsimikiziritsa kufunika kwa ulamuliro wakholo. Magazinowo akufotokoza kuti: “Achichepere ochita bwino koposa m’mayeso a sukulu ndi okhazikika kwambiri mwamalingaliro amachokera m’mabanja amene makolo anagwiritsira ntchito ulamuliro wokhazikitsira malamulo enieni a kakhalidwe ndi kupereka ufulu mkati mwake wokhala ndi malire otsimikizirika. Mofananamo, chiŵerengero cha achichepere omwerekera kumankhwala ndi zakumwa zoledzeretsa nchovomerezeka kukhala chapansi m’mabanja oterowo.”
Pokhala ndi chifukwa chabwino, Baibulo limalangiza makolo kuti: “Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.” (Miyambo 29:17) Inde, chikonzero chozikidwa pa Baibulo chingathe kuthandiza makolo kutetezera kugwiritsira ntchito molakwa kwa mankhwala oledzeretsa ndi kuwongolera mkhalidwe wa moyo kaamba ka banja lonse.