Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 10/15 tsamba 21
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ogonana Ofanana Ziŵalo​—Kodi Ngofanana Pamaso pa Mulungu?
  • Maupandu a Mwazi Apita Patsogolo
  • Papa pa Utumiki Wankhondo
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Tiyenera Kuyamba Kuvomereza Khalidwe Logonana Amuna Kapena Akazi Okhaokha?
    Galamukani!—2012
  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Kodi Ndimphatso ya Moyo Kapena Mpsopsono wa Imfa?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 10/15 tsamba 21

Chidziŵitso pa Nyuzi

Ogonana Ofanana Ziŵalo​—Kodi Ngofanana Pamaso pa Mulungu?

M’boma la ku Australia la Queensland, machitidwe a kugonana kwa ofanana ziŵalo​—ngakhale kwamtseri mwakumvana ndi zitsamwali​—ngosaloledwa mwalamulo. Posachedwapa, gulu lalikulu latchalitchi m’boma limenelo linatsutsa mwamphamvu malamulo oterowo; iwo akufuna kuti kugonana kwa ofanana ziwalo kuloledwe mwalamulo.

Mogwirizana ndi nyuzipepala ya The Courier-Mail, Gulu Logwirizana Pachilungamo cha Tchalitchi ndi Zamayanjano limeneli nlopangidwa ndi ziŵalo za matchalitchi a Angilikani, Roma Katolika, Lutheran, Baptist, ndikuphatikizapo a United ndi cha Quakers (Society of Friends). M’kunena kwawo kuti malamulo okhalapowo otsutsa ogonana ofanana ziŵalo ngozikidwa pa umbuli ndi mzimu wosuliza ena, gululo linati: “Kuchilikiza kwathu kaimidweka nkozikidwa pa chikhulupiriro chakuti anthu onse ngofanana pamaso pa Mulungu ndipo ayenera kukhala ofanana pamaso pa lamulo. Timakhulupirira kuti munthu wogonana ndi wachiŵalo chofanana naye ali munthu mofanana ndi munthu wogonana ndi wachiŵalo chosiyana.”

Pamene kuli kowona kuti anthu onse amabadwa ofanana, kodi lingaliro la Mulungu la kugonana kwa ofanana ziŵalo nlotani? M’Baibulo, machitidwe onse akugonana kwa ofanana ziŵalo ngotsutsidwa kusakhala achibadwidwe ndipo samavomerezedwa ndi Mulungu, natsogolera ku imfa. Izi zinali choncho osati m’Israyeli wakale yekha komanso m’nthaŵi Zachikristu. (Levitiko 18:22; Aroma 1:26, 27) Chitsutsochi nchomvekera bwino ndipo sichimafunikira kuwonjezerapo mawu: “Adama, . . . kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, . . . sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10.

Mmalo mwakuphokosera kofuna kukhalitsa mwalamulo kugonana kwa ofanana ziŵalo, Akristu owona amalangiza omangidwa muukapolo ndi kachitidwe kotonza Mulungu kamemeka kumasukamo ndikutembenukira ku Mawu a Mulungu a chowonadi.

Maupandu a Mwazi Apita Patsogolo

Kufufuza kwaposachedwapa kunavumbula kuti zophophonya mazana ambiri zapangidwa ndi Red Cross ya ku Amerika posamalira mwazi woyambukiridwa ndi matenda. Pafupifupi theka la 12 miliyoni kufika ku 15 miliyoni ya mayuniti a mwazi wogwiritsiridwa ntchito mu United States pachaka amaperekedwa ndi Red Cross ya ku Amerika. Pamene mayuniti alionse a mwazi woyambukiridwa ndi matenda apezedwa, FDA, (Food and Drug Administration), bungwe lotumikira boma, liyenera kudziŵitsidwa. Komabe, The New York Times ikunena kuti insipekitala waboma akunenetsa kuti Red Cross kaŵirikaŵiri inalephera kuchita motero. Iye akuti kufufuza kwa zolembedwa zawo kunavumbula zochitika zokwanira 380 zophatikiza kusamalira moipa mwazi woyambukiridwa ndi matenda zimene sizinachitiridwe lipoti konse ku boma. Ndiponso, insipekitalayo anapeza kuti mwa matenda a AIDS 228 amene angakhale anachititsidwa ndi kupoperedwa mwazi, Red Cross inachitira lipoti 4 okha ku FDA.

Pamene kuli kwakuti ambiri akuwulingalirabe kukhala wopulumutsa moyo, mwazi wopoperedwa ndiumene umachititsa imfa za anthu zikwizikwi chaka chirichonse. Komabe, alambiri owona a Mulungu, polabadira malamulo ake onena za mwazi, amatetezeredwanso ku ngozi zopezeka ndikupoperedwa mwazi. Mulungu analamula kuti: “Musadye mwazi; muuthire pansi ngati madzi . . . kuti chikukomereni inu ndi ana anu akudza m’mbuyo mwanu, pakuti mudzakhala mukuchita zoyenera.”​—Deuteronomo 12:23-25, New International Version.

Papa pa Utumiki Wankhondo

Chaka chatha papa anakumana ndi asilikali akadeti oposa 7,000 pa msasa wa asilikali wa pa Cecchignola ku Roma. Panthaŵiyo maofisala anayi achichepere oimira msasa wa asilikaliwo anafunsa papayo kuti kaya ngati utumiki wankhondo unali wogwirizana ndi chikumbumtima Chachikristu. Mogwirizana ndi nyuzipepala ya Vatican City yotchedwa L’Osservatore Romano, iwo anafunsa mwachindunji kuti: “Kodi munthu angakhale Mkristu wokhulupirika ndipo, panthaŵi imodzimodziyo kukhalanso msilikali wokhulupirika?” Poyankha papayo anati: “Palibe vuto lalikulu kapena kusatheka m’kugwirizanitsa ntchito Yachikristu ndi ya utumiki wankhondo. Ngati yomwe ndaitchula pomalizirayi tiilingalira ndi maganizo abwino, ingawonedwe kukhala chinthu chokongola, choyenera ndi chabwino.”

Komabe, kodi lingaliro loterolo nlogwirizana ndi uchete wosungidwa ndi Akristu oyambirira? M’buku lake lakuti An Historian’s Approach to Religion, Arnold Toynbee akutchula nkhani ya Maximilianus, wophedwera chikhulupiriro wa m’zaka za zana lachitatu yemwe, pamene anawopsezedwa kuphedwa ndi khoti la Roma kaamba kokana kulembetsedwa muusilikali, ananena kuti: “Sindidzatumikira. Mungandidule mutu, komatu sindidzatumikira maulamuliro a Dziko Lino; Ndidzatumikira Mulungu wanga.” Kodi nchifukwa ninji iye anakana kukhalamo ndi phande muutumiki wankhondo, atayang’anizana ndi imfa yotsimikizirika? Chifukwa chakuti iye anawalingalira otsatira owona a Yesu kusakhala “mbali ya dziko” monga momwe Yesu sanaliridi mbali ya dziko. Kuwonjezera apa, nkhondo ya Akristu anailingaira kukhala yauzimu, mogwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo akuti: ‘Sitichita nkhondo monga mwa thupi, pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi.’​—Yohane 17:16, NW; 2 Akorinto 10:3, 4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena