Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/15 tsamba 3-4
  • Timafuna Munthu Wina Kuti Amvetsere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timafuna Munthu Wina Kuti Amvetsere
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • “Zopempha Zanu Zidziwike kwa Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/15 tsamba 3-4

Timafuna Munthu Wina Kuti Amvetsere

MONGA anthu, timayesayesa kupeza chimwemwe ndi chikhutiro m’moyo. Koma patabuka mavuto aumwini, kumakhala kothandiza ndi kotonthoza chotani nanga kukhala ndi munthu wina amene tingakambitsirane naye mavuto athu!

Dr. George S. Stevenson akuti: “Kukambitsirana zinthu kumathandiza kuchepetsa nkhaŵa yanu, kumakuthandizani kuwona bwino koposa nkhaŵa yanu, kaŵirikaŵiri kumakuthandizani kuzindikira zimene mungachite.” Dr. Rose Hilferding anati: “Tonsefe tiyenera kufotokozerana mavuto athu. Tiyenera kufotokozerana nkhaŵa zathu. Tiyenera kuzindikira kuti pali munthu wina m’dziko amene ali wofunitsitsa kumvetsera ndi kuzindikira.”

Ndithudi, palibe munthu amene angakwaniritse kotheratu chosoŵa chimenechi. Chifukwa cha kuchepa kwa nthaŵi ndi zinthu zina, anthu amene timawadalira sangakhalepo pamene tiwafuna koposa, kapena tingazengereze kukambitsirana nkhani zina ndi mabwenzi athu apamtima.

Komabe, Akristu owona samakhala konse opanda munthu womvetsera, popeza kuti njira ya pemphero imakhalapo nthaŵi zonse. Mobwerezabwereza Baibulo limatilimbikitsa kupemphera kwa Mulungu, Mlengi wathu, amene dzina lake ndilo Yehova. Tikulamulidwa kupemphera mowona mtima, m’dzina la Yesu, ndi mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Ngakhale nkhani zaumwini ndi zamseri zingatchulidwe m’pemphero. ‘M’zonse . . . zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu,’ tikuuzidwa motero pa Afilipi 4:6. Ha, ndimphatso yabwino chotani nanga! Mfumu Yolamulira ya chilengedwe chathu nthaŵi zonse imakhala yokonzeka kulandira ndi kuvomereza mapemphero a atumiki ake odzichepetsa pamene akhumba kumfikira.​—Salmo 83:18; Mateyu 6:9-15; Yohane 14:13, 14; 1 Yohane 5:14.

Komabe, kodi Mulungu amamvetseradi? Ena amaganiza kuti kugwira ntchito kwa pemphero kumangodalira pa zoyesayesa za munthu: Munthu amapemphera, kukonza malingaliro ake ndi kuwafotokoza m’mawu. Atazindikira vuto lake, amafunafuna njira yolithetsera ndipo amakhala maso pa chirichonse chimene chingamthandize kupeza yankho lake. Vuto lakelo litathetsedwa, amathokoza Mulungu, koma kwenikweni anali maganizo ndi zoyesayesa zake zimene zinachititsa zotulukapo zokhumbidwa.

Lerolino ambiri amaganiza kuti zimenezo ndizo zimene pemphero liri. Kodi nanunso mumaganiza motero? Kodi mphamvu ya pemphero imangothera pamenepo? Kunena zowona, zoyesayesa zamaganizo ndi zakuthupi za munthuyo mogwirizana ndi mapemphero ake zimachita mbali yaikulu m’kulandira mayankho. Komabe, bwanji nanga za mbali ya Mulungu m’nkhaniyo? Kodi Mulungu amamvetsera pamene mupemphera kwa iye? Kodi amawalingalira mapemphero anu kukhala ofunika, kulingalira zimene mwanena ndi kuwayankha?

Mayankho a mafunso ameneŵa ngofunika. Ngati Mulungu sapereka chisamaliro chake ku mapemphero athu, pamenepo pemphero limapindulitsa maganizo okha. Kumbali ina, ngati Mulungu amalandira ndi kumvetsera pemphero lathu lirilonse mokondwa, tiyenera kukhala oyamikira motani nanga kaamba ka mphatso imeneyi! Tiyenera kusonkhezeredwa kuigwiritsira ntchito mphatso imeneyo tsiku lirilonse.

Pamenepo, tikupemphani kupitiriza kuŵerenga, pamene nkhanizi zikukambitsiridwa m’nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena