Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 2/15 tsamba 3-4
  • Paradaiso Kapena Dzala—Kodi Musankhapo Chiti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paradaiso Kapena Dzala—Kodi Musankhapo Chiti?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Osati Kokha mu “Paradaiso”
  • Nkwaupandu Wocheperapo koma Kovutitsa Maganizo Kwambiri
  • Ndintchito Yaikulu Chotani Nanga!
  • Sangalalani ndi Dziko Lapansi Loyeretsedwa Mtsogolomo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuzulamo Kuipitsa Malo Mumtima ndi m’Maganizo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kodi Ukhondo Ndi Wofunika Motani?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 2/15 tsamba 3-4

Paradaiso Kapena Dzala​—Kodi Musankhapo Chiti?

PALIBE amene akanamuyesa kukhala munthu wina wosiyana: mlendo wa ku Yuropu wofuna kupuma ndi wofunitsitsa kusangalala kuŵala kwa dzuŵa pachilumba chaparadaiso. Akudutsa miyulu yaikulu yamchenga yokhala m’mphepete mwa gombe lanyanja, iye analondola mosamalitsa njirayo yodzera m’zinyalala za mabotolo otaidwa, zitini, matumba a pulasitiki, chingamu ndi zipepala za maswiti, manyuzipepala, ndi magazini. Mwachiwonekere atakhumudwa, anadabwa ngati ameneyu anali paradaiso amene iye anayendera ulendo kudzawona.

Kodi inu munayamba mwakhalapo ndi chochitika chofanana? Kodi chifukwa ninji anthu amalakalaka kupita kutchuti kumalo a paradaiso, koma atafika konko, mwachiwonekere samazengereza kuipitsa malowo kukhala dzala lenileni?

Osati Kokha mu “Paradaiso”

Kunyalanyaza kwachiwonekere kumeneku kwa kukongola, udongo, ndi ukhondo sikuli kokha m’malo a “paradaiso” kumene ocheza ambiri amapitako. Chitaganya chamakono nchokanthidwa kwambiri ndi kuipitsidwa kwa malo pafupifupi kulikonse. Mabizinesi ambirimbiri amaipitsa pamlingo waukulu mwakutulutsa matani ambirimbiri azinyalala zochokera m’zinthu zopangidwa. Zinyalala zapaizoni zosataidwa bwino ndi kutaika mwangozi kwa mafuta zikuwopseza kuipsa zigawo zazikulu za dziko lathu lapansili, kuzipangitsa kukhala zosayenerera moyo.

Nkhondo nazonso zimaipitsa malo. Pamene dziko linayang’ana ndi mantha aakulu, nkhondo ya ku Persian Gulf ya 1991 inawonjezera mlingo watsopano. Magulu ankhondo a Iraq anakoleza moto dala pafupifupi zitsime zamafuta 600, akumasanduliza Kuwait “kukhala masomphenya a helo wa m’chivumbulutso,” monga momwe nyuzipepala ina ya ku Yuropu inafotokozera mkhalidwewo. Magazini aku Jeremani otchedwa Geo anatcha ng’anjoyo kuti “chowononga malo okhala choipitsitsa koposa ndi kalelonse chochitidwa ndi anthu.”

Pamapeto ankhondoyo, ntchito yakuyeretsa inayambidwa mwamsanga. Kuzimitsa chabe zitsime zamafuta zonyekukazo kunatha miyezi yambiri ya ntchito yakalavulagaga. World Health Organization inachitira lipoti kuti kuipitsidwa kwa malo kowonjezereka mu Kuwait kungachititse chiŵerengero cha akufa kumeneko kuwonjezereka ndi 10 peresenti.

Nkwaupandu Wocheperapo koma Kovutitsa Maganizo Kwambiri

Pachitsanzo chotchuka ndi choluluza chirichonse cha kuipitsa malo okhala pamlingo waukulu, pali zitsanzo zoipitsa pamlingo wochepa zikwi zambiri. Anthu otaya zinyalala ndi “akatswiri” olembalemba pamakoma ndi m’malo ena angakhale oipitsa mwaupandu pang’ono, komabe iwo amathandizira kuwonongera pulaneti Dziko lapansili kuthekera kwake kwa kukhala paradaiso.

M’malo ena zolembalemba pamakoma nzowanda kwambiri kotero kuti nzika zafikira kukhala “zakhungu kuzolembalembazo,” osazindikira konse. Zolembalembazo zimapezeka pamatiroko asitima zapansi panthaka, pamakoma azinyumba, ndi patinyumba tatelefoni. Zolembalembazo sizimapezeka pamakoma a zimbudzi za anthu onse zokha.

Mizinda ina njodzala ndi zinyumba zogumukagumuka ndi zosakhalidwa ndi anthu. Zigawo zokhala anthu zimaipitsidwa ndi nyumba zauve ndi mabwalo osasamaliridwa. Magalimoto owonongeka, makina otaidwa, ndi zinyalala zotaidwa zimakhala mbwee pamabwalo apafamu amene akanakhala malo okongola kwambiri.

M’madera ena anthu amawonekera kukhala osadera nkhaŵa ndi matupi awo alitsiro ndi auve. Kuyendayenda atavala nyankhalala ndi osapesa kungakhale osati kokha kovomerezedwa komanso fashoni. Anthu amene amakonda ukhondo ndi udongo amawonedwa kukhala achikale ndi opanda pake.

Ndintchito Yaikulu Chotani Nanga!

Ndimkupiti woyeretsa waukulu chotani nanga umene ukakhala wofunika kusanduliza magombe, nkhalango, ndi mapiri amalo athuŵa dziko lapansi kukhala malo a paradaiso osonyezedwa pazithunzithunzi za pazikuto za magazini onyezimira a alendo​—ndiponso zimene zikafunikira kuchitidwa kumizinda, matauni, mafamu ndi anthu enieniwo!

Wocheza wotchulidwa kuchiyambi anakondwera kuwona kagulu ka antchito oyeretsa akupita m’chigawocho pambuyo pake m’tsikulo kuchotsa mbali zazikulu zazinyalala. Komabe, iwo sanachotse, magalasi osweka, zivundikiro zamabotolo, zotsegulira zitini, ndi zidutswa zosaŵerengeka zandudu. Chotero ngakhale pambuyo pakuyeretsa, panali umboni waukulu wakuti malowo anali okhoza kutchedwabe dzala mmalo mwa paradaiso.

Kuyeretsa kwa padziko lonse kopulumutsa pulaneti iri Dziko lapansi kuti lisakhale dzala kukafunikira kuchotsa zotsalirira zazing’ono zonse zamalo auve ameneŵa. Kodi pali ziyembekezo zirizonse zakuti kuyeretsa kotero kudzachitika? Ngati ziri choncho, motani? Kodi adzakuchita ndani? Liti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena