Maphunziro a Gileadi m’Chikhulupiriro Choyeretsetsa
“OPHUNZIRA athu aphunzitsidwa bwino lomwe m’chikhulupiriro choyeretsetsa.” Mawu ameneŵa ndiwo anali oyambira programu yomaliza maphunziro a kalasi la 95 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, yomwe inachitidwa pa Sande, September 12, 1993. Mmaŵa umenewo alendo oitanidwa 4,614 ndi ziŵalo za banja la Beteli amene anasonkhana m’Nyumba Yosonkhanira ku Jersey City anatsogozedwa m’pemphero ndi George Gangas. Mbale Gangas wakhala chiŵalo cha banja la Beteli kwa zaka 65 ndipo pausinkhu wa zaka 97 ndiye wamkulu pa ziŵalo zonse za Bungwe Lolamulira.
Albert Schroeder, yemwenso ali wa Bungwe Lolamulira ndi tcheyamani wa programuyo, anafotokoza kuti: “Kwa miyezi isanu kosi ya Gileadi yazikidwa pa chikhulupiriro choyeretsetsa.” Koma kodi “chikhulupiriro choyeretsetsa” nchiyani? Iye anafotokoza kuti “chikhulupiriro choyeretsetsa” chimenechi, chotchulidwa pa Yuda 20, ndicho mpambo wonse wa chowonadi cha Baibulo. Chotero kosi ya Gileadi njozikidwa pa Mawu a Yehova, Baibulo, limene lili buku lalikulu lophunziridwa.
Ophunzira Alandira Malangizo Owonjezereka
Wokamba nkhani woyamba anali John Stuefloten wa Komiti ya Watchtower Farms, amene anakamba nkhani ya mutu wakuti “Kupindula ndi Chisonkhezero cha Anthu Anzeru.” Baibulo limanena kuti awo ‘oyenda ndi anzeru adzakhala anzeru.’ (Miyambo 13:20) Mkati mwa kosi ya Gileadi, ophunzirawo anathera maola oposa 900 akumaphunzira Baibulo. Mbale Stuefloten anafunsa ophunzirawo kuti: “Kodi chisonkhezero cha Yehova chidzakuyambukirani motani mtsogolo? Mukupita kumaiko 18 okhala ndi chiŵerengero chophatikizidwa pamodzi cha anthu mamiliyoni 170. Chotero kodi ndimotani mmene mudzasonkhezerera anthu amenewo?” Mwa kusonyeza nzeru ya Yehova, amishonale atsopanowo adzakhoza kuthandiza ena kukhala olambira a Yehova, Magwero a nzeru zosatha.
Nkhani yotsatira, yokambidwa ndi Lloyd Barry wa Bungwe Lolamulira, inali ndi mutu wakuti “Kukhala Zonse kwa Anthu Onse.” (1 Akorinto 9:22) Pafupifupi zaka 45 zapitazo, Mbale Barry mwiniyo anali wophunzira m’kalasi la 11 la Gileadi. Tsopano kalasi la 95 linayamikira kulandira uphungu wothandiza woperekedwa ndi munthu yemwe kale anali mmishonale amene ali ndi chidziŵitso cha zaka zambiri za kutumikira m’dziko lachilendo. Iye analimbikitsa ophunzirawo kugwirizana mosataya nthaŵi ndi anthu a m’magawo awo achilendo mwa kuphunzira kakhalidwe ka m’malowo ndi chinenero cha kumaloko. Iye ananena kuti zimenezi zingachitidwe bwino lomwe mwa kuyanjana ndi kugwira ntchito ndi anthu a kumaloko limodzinso ndi kuphunzira miyambo yawo ndi kuitsatira pamene kuli koyenera.
Wotsatira, Dean Songer wa Komiti ya Fakitale anakamba nkhani ya mutu wosangalatsa wakuti “Omasulidwa ku Ntchito.” Pambuyo pa zaka zoposa 35 za utumiki wanthaŵi yonse, Mbale Songer amamvetsetsa zimene kukhala ndi moyo wa cholinga, wosacholoŵana kumatanthauza, kusumika maganizo pantchito yoyenera kuchitidwa, popanda nkhaŵa za zinthu zakuthupi. Ndipo imeneyo ndiyo inali mfundo yaikulu ya uphungu wake kwa ophunzira. Oimba nyimbo pakachisi wa Yehova anamasulidwa ku ntchito zimene Alevi ena anali kuchita kotero kuti adzipereke kotheratu pantchito yawo yapadera. (1 Mbiri 9:33) Mofananamo, amishonale a Gileadi amasulidwa ku zinthu wamba zonga ntchito yakuthupi kotero kuti asumike maganizo awo pa utumiki wawo wapadera. Mbale Songer anamaliza ndi chenjezo ili: “Khalani ndi kapenyedwe ka moyo kabwino ndi moyo wosacholoŵana. Thayo lanu monga awo omasulidwa ku ntchito zina ndilo la kugwira ntchito usana ndi usiku, kutamanda Yehova.”
Daniel Sydlik, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anatsatira ndi nkhani ya mutu wakuti “Kuphunzitsa Ena Mmene Angapezere Zabwino Koposa m’Moyo.” Iye analimbikitsa ophunzira “osati kungophunzitsa chikhulupiriro chokha komanso kukhala olimba mtima kwambiri mokhoza kusonyeza anthuwo zimene ayenera kuchita kuti agwirizanitse miyoyo yawo ndi chifuniro cha Mulungu.” Aphunzitsi abwino ayenera kukhala ogwira mtima ndi osonkhezera. “Zindikirani kufunika kwa kuphunzitsa makhalidwe Achikristu mmalo mwa kungophunzitsa malamulo ndi malangizo okha,” iye anatero ndipo pomaliza anawonjezera kuti: “Koposa zonse, abale okondedwa, dziphunzitseni inu eni ndipo phunzitsani ena mmene angasonyezere chikondi, pakuti ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—1 Akorinto 13:1-3; Akolose 3:14.
Pambuyo pa miyezi ya kuphunzira, ophunzirawo anafikira pa kukonda kwambiri alangizi awo aŵiri a Gileadi. Jack Redford, yemwe kale anali mmishonale, analankhula choyamba, pankhani ya mutu wakuti “Mwapanga Chosankha Chabwino.” M’dongosolo lakale Lachiyuda, asanakhale mtumwi Wachikristu, Paulo anali ndi malo apamwamba, anali wotchuka, waulamuliro, ndi wosungika m’zandalama. Koma pa Afilipi 3:8, Paulo anafotokoza zonsezi kukhala “zapadzala,” kapena “zinyansi,” malinga ndi matembenuzidwe a Phillips. Mtima wake unali pa utumiki, ndipo anapanga chosankha chabwino. Mosiyana naye, unyinji wa anthu lerolino amasonyeza mwa zosankha zawo m’moyo kuti amaona chuma chakuthupi kukhala chamtengo wapatali koposa moyo wosatha. Amishonale a Gileadi apanga chosankha chabwino. Jack Redford anamaliza mwa kunena kuti: “Palibe chilichonse chimene dziko la Mdyerekezi lingakupatseni chimene chingalingane ndi utumiki waumishonale. Samalirani mwaŵi wosayerekezereka umenewo, ndipo lekani dziko lisamalire zinyansi zake!”
Ulysses Glass wakhala mlangizi wa Gileadi kwa zaka 32 zapitazo. Iye anapatsa ophunzirawo uphungu wotsazikira m’nkhani ya mutu wakuti “Mulungu Yekha Ndiye Angapange Mtengo,” akumazika nkhani yake pa Salmo 1:3. Luso la zopangapanga lamakono silinathe mpang’ono pomwe kuyerekezera kupanga mtengo, wolinganizidwa ndi Mulungu. M’lingaliro lina, Akristu owona ali ngati mitengo, yodzalidwa ndi kuthiriridwa ndi Yehova. Mbale Glass ananena kuti kwa miyezi isanu, ophunzirawo anali “kuthiriridwa nthaŵi zonse ndi kasupe wa madzi opatsa moyo wa m’Mawu a Mulungu,” monga mitengo m’munda kapena m’paradaiso wauzimu. Komabe, monga amishonale, iwo ayenera kutetezera “mizu yawo yauzimu ku zowononga zilizonse.” Iwo analimbikitsidwa ‘kupitiriza kumwa madzi a moyo ochokera kwa Yehova chifukwa ndi Mulungu yekha amene angapange mtengo.’
Nkhani yomalizira inakambidwa ndi Carey Barber, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira. Pokhala muutumiki wa nthaŵi yonse kwa zaka 70, Mbale Barber anakhoza kulankhula mwachidaliro nkhani ya mutu wakuti “Khalani Odzipereka Kotheratu kwa Yehova.” Unyinji wa anthu sanadzipereke kotheratu kwa Yehova. (Deuteronomo 5:9) Komabe, monga momwe Mbale Barber anasonyezera, mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwathu, “kuli kotheka ndithu kukhala wodzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu.” Iye anawonjezera kuti: “Palibe aliyense amene anganenedi kuti: ‘Mdyerekezi ndiye wandichititsa zimenezi.’” Koma Mdyerekezi angatigonjetse ngati tilephera kumkaniza. (Yakobo 4:7) Kukhala otanganitsidwa m’ntchito ya Yehova ndiko njira yaikulu yokanizira Satana ndi dziko lake ndi kukhala odzipereka kotheratu kwa Yehova.
Aikidwa Kukhala Amishonale
Programu ya mmaŵa inatha ndi kuikidwa mwalamulo kwa ophunzira 46 onsewo kukhala amishonale. Mabanja 23 amenewo analandira madiploma amene mbali yake imafotokozera kuti omaliza maphunzirowo ali “oyeneretsedwa mwapadera kuchita ntchito yophunzitsa, kuchirikiza ubwenzi ndi kugwirira ntchito mtendere wokhalitsa ndi ulamuliro wabwino ndi chilungamo pakati pa anthu onse.” Ndithudi kalasi la 95 la Gileadi lidzayesayesa kukwaniritsa ntchito yofunika kwambiri imeneyi m’maiko 18 kumene agaŵiridwa. Magawo amenewo ngapadziko lonse ndipo aphatikizapo maiko a ku Asia, Afirika, Ulaya, Latin America, ndi Caribbean.
Masana, pambuyo pa Phunziro la Nsanja ya Olonda lachidule lochititsidwa ndi Charles Woody wa Komiti ya Dipatimenti Yautumiki, omaliza maphunziro a Gileadi atsopanowo anasonyeza programu yawo, ya mutu wakuti “Gileadi Yatikonzekeretsa Kuphunzitsa Monga Amishonale.” Mbaliyo inatha ndi drama lakuti “Zosankha Zomwe Tikuyang’anizana Nazo.”
Programu yosangalatsa imeneyi itatha, amishonale atsopanowo tsopano anali okonzekera kutumizidwa kungodya zinayi za dziko lapansi kukauzako ena za “chikhulupiriro choyeretsetsa.”
[Bokosi patsamba 26]
Ziŵerengero za Kalasi
Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 7
Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 18
Chiŵerengero cha ophunzira: 46
Chiŵerengero cha mabanja: 23
Avareji ya zaka zakubadwa: 30.06
Avareji ya zaka m’chowonadi: 12.92
Avareji ya zaka muutumiki wanthaŵi yonse: 9.4
[Chithunzi patsamba 26]
Kalasi la 95 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ya pamwambayo ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Buelow, D.; Donzé, V.; Innes, S.; Fulk, N.; Billingsby, M.; Hoddinott, L.; Nygren, B.; Eriksson, L. (2) Boker, J.; Thomas, M.; Stedman, S.; Billingsby, D.; Waugh, I.; Purves, M.; Luttrell, M. (3) Jacobsen, T.; Boker, J.; Martínez, L.; Nilsson, E.; Purves, P.; Holt, L.; Larsen, M.; Jones, L. (4) Numminen, P.; Numminen, H.; Buelow, M.; Olson, W.; Holt, S.; Donzé, G.; DesJardins, C.; DesJardins, D. (5) Larsen, K.; Martínez, D.; Nygren, P.; Waugh, P.; Jones, D.; Hoddinott, J.; Thomas, G. (6) Innes, B.; Fulk, R.; Eriksson, A.; Nilsson, S.; Stedman, J.; Olson, K.; Jacobsen, F.; Luttrell, J.