Dziko Labwinopo—Kodi Ndiloto Chabe?
MUKANAKHALA wotsatira wa chiphunzitso cha Mazdaism monga momwe chinalalikidwa ndi mneneri wa ku Iran wotchedwa Zoroaster, mukanayembekezera tsiku limene dziko lapansi likabwerera ku kukongola kwake koyambirira. Mukanakhalako m’Girisi wamakedzana, mwinamwake mukanalingalira za kufika ku Zisumbu Zamwaŵi zokondweretsa kapena za kuona kubweranso kwa Nyengo Yamtendere yolongosoledwa ndi wolemba ndakatulo Hesiod m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. Mmwenye wa fuko la Guaraní ku South America angakhale akufunafunabe Dziko Lopanda Zoipa. Pokhala m’nthaŵi yathu ino, mwinamwake mukuyembekezera kuti dziko lidzawongokera chifukwa cha ziphunzitso zandale kapena chifukwa cha nkhaŵa yamakono kaamba ka zamoyo ndi malo okhala.
Nyengo Yamtendere, Zisumbu Zamwaŵi, Dziko Lopanda Zoipa—ameneŵa ndi ena a maina ambiri agwiritsiridwa ntchito kulongosola chilakolako chimodzimodzicho, chiyembekezo cha dziko labwinopo.
Dzikoli, dziko lathuli, siliri konse malo abwino koposa. Maupandu ankhalwe omawonjezerekawonjezereka, nkhondo za pachibale za chiwawa chosalingana ndi china chilichonse, kuphana kwa mafuko, kusalingalira kuvutika kwa ena, umphaŵi ndi njala, ulova ndi kupanda umodzi, mavuto a zamoyo ndi malo okhala, matenda osachiritsika amene akukantha mamiliyoni—ndandanda ya mavuto atsopano ikuonekera kukhala yosatha. Polingalira za nkhondo zimene zikumenyedwa tsopano lino, mtolankhani wa ku Italy anati: “Funso limene limabuka mwachibadwa nlakuti kaya ngati udani suli mkhalidwe wamphamvu kwambiri m’nthaŵi yathu.” Polingalira za mkhalidwewo, kodi muganiza kuti nkoyenera kukhumba chinachake chosiyana, chinachake chabwinopo? Kapena kodi chikhumbo chimenecho chili kokha kulakalaka Utopia, loto limene silidzakwaniritsidwa konse? Kodi tikukhala m’dziko labwino koposa?
Ameneŵa sali mafunso atsopano. Kwa zaka mazana ambiri anthu akhala akulingalira za dziko mmene muli kugwirizana, chilungamo, kukhupuka, ndi chikondi. M’kupita kwa nthaŵi, anthanthi ambiri anafotokoza mwatsatanetsatane malingaliro awo a Maboma abwino kwambiri, maiko abwinopo. Koma mwachisoni, iwo sanakhoze konse kufotokoza mmene angawachititsire kukhala achipambano.
Kodi ndandanda yokhalako kwa zaka mazana ambiri imeneyi ya maloto, ma Utopia, ndi zikhumbo za anthu za chitaganya chabwinopo ingatiphunzitse kenakake?
[Chithunzi patsamba 3]
Kodi ili ndi dziko labwino koposa?