Kodi Maloto Angalosere Mtsogolo?
KUYAMBIRA kale, anthu achita chidwi kwambiri ndi maloto. Aaigupto anakonza mabuku ochuluka omasulira maloto, ndipo Ababulo anali ndi omasulira maloto awo. Agiriki anali ndi mwambo wakuti anthu odwala azigona mu akachisi a Asclepius kuti alandire malangizo a zaumoyo m’maloto awo. M’zaka za zana lachiŵiri za Nyengo Yathu, Artemidorus anatulutsa buku limene anamasuliramo zizindikiro za maloto. Mabuku ena ambiri onga amenewo otulutsidwa kuyambira nthaŵiyo azikidwa pa buku lake. Kufikira lero, pakhala kuyesayesa kumasulira maloto, koma kodi iwo amapereka chidziŵitso cha zochitika za mtsogolo?
Kuti iwo akhale ndi tanthauzo la mtsogolo, ayenera kusonkhezeredwa ndi mphamvu yoposa ya munthu. M’Baibulo timapezamo zochitika zambiri pamene Mulungu anapereka mphamvu imeneyoyo. Anapereka maloto aulosi kwa atumiki ake limodzi ndi ena amene sanamlambire. Kwenikweni, Yobu 33:14-16 amati: “Mulungu alankhula . . . m’kulota, m’masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama, pamenepo atsegula makutu a anthu.”
Mulungu anachita zimenezi kwa Farao wa Aigupto m’masiku a Yosefe, amene anakhalako zaka zoposa 1,700 Nyengo Yathu isanayambe. Loto la Farao limapezeka pa Genesis 41:1-7, ndipo m’mavesi 25 mpaka 32, Yosefe akulimasulira kuti likulosera zaka zisanu ndi ziŵiri “zakuchuluka chakudya m’dziko lonse la Aigupto,” zotsatiridwa ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. Yosefe anafotokozera Farao kuti: “Chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao.” (Genesis 41:28) Lotolo linalosera zimene zinachitikadi.
Zimene zinachitikira mfumu yotchuka ya Ababulo zinali zofanana. Nebukadinezara analota loto limene linamvutitsa maganizo kwambiri, koma sanathe kulikumbukira. Choncho anaitana amatsenga ake kuti amuuze lotolo ndi tanthauzo lake. Pempho limeneli linali losatheka kwa iwo kulikwaniritsa.—Danieli 2:1-11.
Popeza kuti Mulungu ndiye anapatsa mfumu lotolo, Iye anatheketsa mneneri Danieli kuvumbula lotolo ndi tanthauzo lake. Danieli 2:19 amati: “Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Danieli m’masomphenya a usiku.” Danieli anapereka thamo kwa Mulungu kaamba ka loto limeneli kuti: “Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuchiululira mfumu; koma kuli Mulungu kumwamba Wakuvumbulutsa zinsinsi; iye ndiye wadziŵitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza.”—Danieli 2:27, 28.
Nthaŵi zina Mulungu anapereka malangizo kwa anthu ake mwa maloto, ndipo nthaŵi zina anawatsimikiza za chiyanjo chaumulungu kapena kuwathandiza kumvetsa mmene anali kuwathandizira. Kwa Yakobo, Mulungu anavumbula chiyanjo chake kupyolera m’loto.—Genesis 48:3, 4.
Pamene Yosefe, atate wolera wa Yesu, anadziŵa kuti Mariya anali ndi pathupi, anaganiza zomsudzula. Ndiyeno analandira malangizo m’loto kuti asachite zimenezo. Mateyu 1:20 amati: “Pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha mzimu woyera.” Pambuyo pake analandira chenjezo m’kulota: “Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m’kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthaŵire ku Aigupto.”—Mateyu 2:13.
Maloto Amene Saali Ochokera kwa Mulungu
Choonadi chakuti kumasulira maloto kunali kofala pakati pa awo amene sanali anthu a Mulungu chimasonyeza kuti maloto mwachisawawa sangalingaliridwe kukhala mavumbulutso odalirika a mtsogolo. M’masiku a mneneri wa Mulungu Yeremiya, aneneri onyenga anali kunena kuti: “Ndalota, ndalota.” (Yeremiya 23:25) Cholinga chawo chinali kusokeretsa anthu kuti aganize kuti Mulungu anali kulankhula kupyolera mwa iwo. Ponena za olota ameneŵa, Yeremiya anauziridwa kunena kuti: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto [awo, NW] amene [akulota, NW]. Pakuti anenera kwa inu zonama m’dzina langa . . . , ati Yehova.”—Yeremiya 29:8, 9.
Popeza kuti aneneri onyenga ameneŵa anali “akuombeza,” maloto awo angakhale atasonkhezeredwa ndi mphamvu ya mizimu yoipa ndi cholinga cha kunyenga anthu. Zofananazo zikusonyezedwa ndi zonenedwa pa Zekariya 10:2: “Aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe.”
Mdyerekezi ndiye wonyenga wamkulu amene kwa zaka zikwi zambiri wagwiritsira ntchito atsogoleri achipembedzo kunena monama kuti Mulungu walankhula kwa iwo m’masomphenya ndi m’maloto, monga momwedi aneneri onyenga anachitira m’masiku a Yeremiya ndi Zekariya. Ponena za otero, wolemba Baibulo wouziridwa Yuda analembera Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti: “Anthu ena anakwaŵira m’tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina awo kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.” Anthu ameneŵa, iye anatero, anali ‘kulota,’ titero kunena kwake.—Yuda 4, 8.
Yesani Zonenedwazo
Munthu anganene kuti Mulungu analankhula naye m’maloto kapena kuti maloto ake a zochitika za mtsogolo anakhala oona, komabe chimenecho si chifukwa chokwanira chomkhulupirira ndi kungomtsatira. Onani malangizo olembedwa kwa Aisrayeli pa Deuteronomo 13:1-3, 5: “Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa; ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziŵa, ndi kuitumikira; musamamvera mawu a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu . . . Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe.” Mulungu analola oterowo kulankhula zonama kuti ayese kukhulupirika kwa anthu ake.
M’malo mwa kungokhulupirira zonena za olota maloto olosera mtsogolo, njira yanzeru imene tiyenera kutenga ndiyo kuyesa zonena zawo kuti tisanyengedwe ndi wonyenga wamkulu wosaonekayo, amene ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9) Koma kodi angayesedwe motani ndi chidaliro?
Mawu a Mulungu olembedwa ndiwo chitsogozo chathu chopatsidwa ndi iye kutisonyeza choonadi. Ponena za iwo, Yesu Kristu anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Chotero 1 Yohane 4:1, NW, akutilangiza kuti: “Okondedwa, musamakhulupirira mawu ouziridwa alionse, koma yesani mawu ouziridwawo kuona ngati achokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri ambiri onyenga aloŵa m’dziko.” Zitayerekezeredwa bwinobwino ndi Baibulo, zonena zawo, mafilosofi, ndi zochita zimawombana nalo. Mawu a Mulungu ndiwo maziko osonyeza choonadi.
Kodi wolotayo amene amati ali ndi chidziŵitso chapadera kwenikweni amaombeza ula kapena kuchita zinthu zina zamizimu? Ngati amatero, Mawu a Mulungu amamtsutsa. “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.
Ngati amati ali ndi sou yosafa, akutsutsa Mawu a Mulungu amene amanena bwino lomwe kuti: “Sou imene ichimwa—imeneyo ndiyo idzafa.” (Ezekieli 18:4, NW) Kodi akudzikweza ndipo ali ndi kagulu kakekake? Mateyu 23:12 amachenjeza kuti: “Aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa.” Ndipo Machitidwe 20:30 amachenjeza Akristu kuti: “Mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.”
Kodi amasonkhezera chiwawa? Yakobo 3:17, 18 amatsutsa kuti: “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.” Kodi amafuna ulamuliro wa ndale kapena udindo m’dziko? Mawu a Mulungu amamtsutsiratu, kuti: “Iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” Motero Baibulo limavumbula chinyengo.—Yakobo 4:4.
Ngati munthu walota za imfa ya wapabanja kapena bwenzi lake, mwinamwake nchifukwa chakuti wakhala akudera nkhaŵa munthuyo. Kufa kwa munthuyo mwinamwake panthaŵi yeniyeni ya kulota usiku kumeneko sikumatsimikizira kuti lotolo linali lolosera. Pa loto lililonse la mtundu umenewu limene limaoneka ngati lachitika, pamakhala ena mazana ambiri amene samachitika.
Ngakhale kuti Mulungu anagwiritsiradi ntchito maloto kale kuvumbula zochitika zaulosi ndi kupereka malangizo pamene Mawu ake olembedwa anali kupangidwa, iye safunikira kuchita zimenezo lerolino. Mawu olembedwa amenewo ali ndi malangizo onse ochokera kwa Mulungu ofunika kwa anthu nthaŵi ino, ndipo maulosi ake amanena za zochitika za mtsogolo zaka zoposa chikwi. (2 Timoteo 3:16, 17) Chotero tili ndi chidaliro chakuti maloto athu saali zizindikiro zochokera kwa Mulungu za zochitika za mtsogolo koma ndi mmene ubongo umagwirira ntchito yofunika kusamalira ubwino wa maganizo athu.
[Chithunzi patsamba 7]
Monga momwe loto la Farao linasonyezera zomwe zinalinkudza, Mawu a Mulungu amaunikira mtsogolo mwathu