Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 4/8 tsamba 4-5
  • Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Odzaza ndi Chiyembekezo
  • Kodi Ziri Kathu?
  • Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?
    Galamukani!—1990
  • Zamoyo Zakuthambo—Kupeza Yankho
    Galamukani!—1990
  • Ma UFO—Kodi Ali Amithenga Ochokera kwa Mulungu?
    Galamukani!—1996
  • Zimene Zinthu Zakuthambo Zimatiuza
    Galamukani!—2021
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 4/8 tsamba 4-5

Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale

OLEMBA nkhani zasayansi zopeka amakono sanayambitse lingaliro la zamoyo zakuthambo. Zaka mazana 23 apitawo, wanthanthi Wachigriki wotchedwa Metrodorus anaphunzitsa kuti chilengedwe chonse chokhala ndi dziko limodzi lokha lokhalidwa ndi anthu sichingakhale chotheka mofanana ndi munda waukulu wodzalidwa ndi chimanga chimodzi chokha. Lucretius, wolemba ndakatulo Wachiroma wa zaka za zana loyamba B.C.E., analemba kuti “m’mbali zina za thambo kuli maiko ena ndi mafuko osiyanasiyana a anthu.”

Chiphunzitso chimenechi, chotchedwa kuchuluka kwa maiko, sichinayanjidwe ndi Dziko Lachikristu kwa zaka mazana ambiri. Koma chiyambire chifupifupi 1700 mpaka kumayambiriro kwa zaka za zana lathu, anthu ophunzira ambiri, kuphatikizapo asayansi aakulu kwambiri m’mbiri, anakhulupirira mwamphamvu kuti moyo uliko ku maiko ena. Kwenikwenidi, mphunzitsi wina wa pakati pa ma 1800 anawukiridwa kwambiri pamene anayesera kulemba nkhani yokana chiphunzitsocho.

Anthu anawoneka kukhala ofunitsitsa kukhulupirira kukhalako kwa zamoyo zakuthambo, ngakhale popanda umboni wokwanira. Mu 1835 mtolankhani wa nyuzipepala analemba kuti akatswiri a zakuthambo anapeza moyo pa mwezi. Iye analemba kuti zinyama zachilendo, zomera zachilendo, ndiponso anthu okhala ndi mapiko, omayendayenda ndi kugwedezeka mowonekera, zinawonedwa pa chipangizo chowonera kutali! Nyuzipepala yake inafalikira mokulira. Ambiri anapitiriza kukhulupirira nthanoyo ngakhale pambuyo pakuti inavumbulidwa kukhala chinyengo.

Asayansi analinso ndi kawonedwe kotsimikiza. Kumapeto kwa ma 1800, katswiri wa zakuthambo Percival Lowell anakhutiritsidwa kuti angawone dongosolo locholoŵana la ngalande pamwamba pa pulaneti Mars. Anazilemba molongosoka ndi kulemba mabuku onena za anthu amene anazipanga. Mu France, Academy of Sciences inali yotsimikiza kuti kunali moyo ku Mars kotero kuti inalonjeza mphotho kwa munthu woyamba kulankhula ndi zamoyo zakuthambo kuchotsapo nzika za ku Mars.

Ena anapanga makonzedwe achilendo olankhulira ndi zolengedwa za ku maiko apafupi, kuyambira pa kuyatsa moto waukulu mu Chipululu cha Sahara ndi kubzala nkhalango zowongoka kudutsa Siberia. Mu 1899 wopanga wa ku America anaimika nsanamira yokutidwa ndi mkuwa ndi kutumiza zizindikiro zamphamvu zamagetsi kupyola mu iyo kuti ipatse chizindikiro kwa nzika za ku Mars. Tsitsi la anthu linaima, ndipo kuwala kunawunikira pa mtunda wa makilomita 50 mbali zonse, koma kunalibe yankho lochokera ku Mars.

Odzaza ndi Chiyembekezo

Pamene kuli kwakuti luso la zopangapanga limene likuchilikiza kufufuza kwa moyo kwamakono lingakhale latsopano, chinthu chimodzi sichinasinthe: Asayansi adakali ndi chidaliro chakuti mtundu wa anthu suli wokha pa chilengedwe. Monga mmene katswiri wa zakuthambo Otto Wöhrbach analembera m’nyuzipepala ya ku Germany Nürnberger Nachrichten kuti: “Mwachibadwa palibiretu wasayansi amene sanganene kuti inde atafunsidwa ngati kuli moyo wa zamoyo zakuthambo.” Gene Bylinsky, mkonzi wa bukhu lakuti Life in Darwin’s Universe, akuzilongosola motere: “Tsiku lirilonse kuyambira tsopano, ngati akatswiri a zakuthambo a wailesi ati akhulupiriridwe, chizindikiro chochokera ku nyenyezi chidzawala modutsa mpata wosayerekezeka wa thambo kudzathetsa kusungulumwa kwathu kwachilengedwe.”

Kodi nchifukwa ninji asayansi ali otsimikiza koposa kuti kuyenera kukhala moyo m’maiko ena? Kulingalira kwawo kotsimikiza kunayamba ndi nyenyezi. Ziripo zambirimbiri—zikwizikwi za mamiliyoni m’khamu lathu la nyenyezi. Ndiyeno ziyerekezo zinayamba. Motsimikizirika, zambiri za nyenyezi zimenezo ziyeneranso kukhala ndi mapulaneti amene amazizungulira, ndipo moyo uyenera kuyambika pa ena a maiko amenewo. Mogwirizana ndi kulingalira koteroko, akatswiri a zakuthambo alingalira kuti pali chifupifupi zikwi kufika ku mamiliyoni a anthu amene ali m’khamu lathu la nyenyezi!

Kodi Ziri Kathu?

Kodi zimapanga kusiyana kotani kaya ngati kuli moyo kunja kwa Dziko Lapansi kapena ayi? Ndithudi, asayansi amakhulupirira kuti yankho lirilonse lingakhale ndi chiyambukiro chachikulu pa banja la anthu. Iwo amati kudziŵa kuti tiri tokha m’chilengedwe kungaphunzitse mtundu wa anthu kuwona moyo kukhala wamtengo wapatali polingalira za kukhala kwake wapadera. Ku mbali ina, wasayansi wolemekezedwa wina akulingalira kuti anthu achilendo angakhale otsogola ndi zaka mamiliyoni ambiri kuposa ife ndipo angatipatseko nzeru zawo zambiri. Iwo angatiphunzitse mmene tingachiritsire matenda athu, kuthetsa kuipitsa, nkhondo, ndi njala. Iwo angatisonyezenso mmene tingalakire imfa yeniyeniyo!

Kopandiratu matenda, nkhondo, imfa—mtundu umenewo wa chiyembekezo umatanthauza zambiri kwa anthu m’nthaŵi zathu zovutitsa. Mosakaikira zimateronso kwa inu. Komabe, mwinamwake mungavomereze kuti nchabwino kukhala wopanda chiyembekezo koposa kuyedzamira pa chonyenga. Pamenepa, nchofunika kwa ife kupeza ngati asayansi ali ndi maziko olimba pamene akunena kuti chilengedwe chikuchuluka ndi maiko okhalidwa ndi anthu.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kodi asayansi ali ndi maziko olimba pamene akunena kuti chilengedwe chikuchuluka ndi maiko okhalidwa ndi anthu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena