Malikulu a Maphunziro a Watchtower Atumiza Amishonale
MAKALASI a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower achitikira m’malo osiyanasiyana. Pakati pa 1943 ndi 1960, makalasi 35 opangidwa ndi ophunzira ochokera ku maiko 95, analandira maphunziro apadera ku South Lansing, New York, U.S.A. Ndiyeno sukuluyo inasamutsidwira ku malikulu a padziko lonse ku Brooklyn, New York, kumene inakhala kwa zaka pafupifupi 28. Kuyambira mu 1988 mpaka kuchiyambi kwa 1995, Sukulu ya Gileadi inachitira maphunziro ku Wallkill, New York.
Pazaka zimenezi sukuluyo inafutukuka. Mwa chitsogozo chake maphunziro a milungu khumi anaperekedwa ku makalasi atatu ku Mexico; makalasi asanu otero anachitidwa ku Germany; aŵiri ku India. Chiyambire 1987 sukulu yake yaing’ono yotchedwa Sukulu Yophunzitsa Utumiki yakhala ndi makalasi ake m’maiko 34, ikumapereka maphunziro apadera a milungu isanu ndi itatu kwa anyamata oyeneretsedwa. Komabe, maphunziro operekedwa kwa kalasi la 99 la Gileadi, pa Malikulu a Maphunziro a Watchtower omangidwa chatsopano ku Patterson, New York, anali a milungu 20, omwe anaphatikizapo kuphunzira Baibulo lonse mozama, kupenda mbiri yamakono ndi gulu la Mboni za Yehova, limodzi ndi uphungu wochuluka ponena za ntchito ya umishonale ku maiko akutali.
Pa September 2, kalasi la 99 limenelo linamaliza maphunziro. Programu yomaliza maphunziro ya maola atatu inachitikira m’holo yatsopano pa Malikulu a Maphunziro a Watchtower. Inadzala yonse. Magulu ena omvetsera pa nyumba za Beteli ku Patterson, Wallkill, ndi Brooklyn analunzanitsidwa pa wailesi yakanema. Tsiku limeneli silinali losangalatsa kwa kalasi lomaliza maphunziro lokha ndi achibale awo ndi mabwenzi komanso kwa anthu mazana amene anagwira ntchito yodzifunira yomanga nyumba zatsopano za sukuluzo.
M’mawu ake otsegulira, Carey Barber wa Bungwe Lolamulira anafotokoza kwambiri chifuno cha zimene zinali kuchitika. Iye anati: “Ano adzakhala malikulu a ntchito yaikulu koposa ya maphunziro aumulungu imene yakhala ikupitabe patsogolo pa dziko lino lapansi.” Anafotokoza kuti tikuyandikira chimake cha nkhondo ya mbewu ya mkazi ndi mbewu ya njoka. (Genesis 3:15) Anasonyeza kuti amene adzapulumuka nkhondo yowopsayo pa chisautso chachikulu chikudzacho ndi aja okha amene ali ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu ndipo amawamvera.
“Programu yathu yamakono ya maphunziro,” iye anatero, “yakonzedwa kuthandiza anthu a Yehova kulikonse kufika pa kukula msinkhu kofotokozedwa pa Miyambo 1:1-4—kwa kudziŵa nzeru ndi mwambo, kuzindikira mawu ozindikiritsa, kulandira mwambo wopatsa chidziŵitso, chilungamo, chiweruzo, zolunjika, ndi kulingalira.” Kuli koteteza chotani nanga kukhala ndi nzeru yauzimu yotero!
Uphungu wa Kalasi Lomaliza Maphunziro
Mawu otsegulira amenewo anatsatiridwa ndi nkhani zachidule zisanu zokambidwa kwa kalasi lomaliza maphunziro. Harold Jackson, amene kale anali mlangizi wa Gileadi ndipo tsopano amagwira ntchito pamalikulu ku Brooklyn, analimbikitsa kalasilo kuti, “Gwiritsani Chikhutiro Chanu Chaumulungu.” Lloyd Barry, yemwe anali mmishonale kwa nthaŵi yaitali ndipo tsopano ali m’Bungwe Lolamulira, analankhula nkhani yakuti “Kutumikira Yehova Modzichepetsa.” Iye anafotokoza kuti mkhalidwe umenewu udzafunika kwambiri kwa omaliza maphunziro pakuzoloŵerana kwawo ndi mikhalidwe yatsopano limodzinso ndi pamaunansi awo ndi amishonale anzawo, mipingo imene adzatumikiramo, ndi anthu akomweko.
Karl Adams, amene pakali pano ali m’gulu la alangizi a Gileadi, anakamba ndi kalasilo pafunso lakuti “Kodi Chikhulupiriro Chidzakutsogolerani Kuchita Chiyani?” Anawalimbikitsa kusakhala ngati Aisrayeli aja amene anadandaula ndi mikhalidwe ya m’chipululu nalakalaka kubwerera ku Igupto, koma m’malo mwake, kukhala ngati Abrahamu, amene anayembekeza Ufumu wa Mulungu m’malo mobwerera ku Uri wa Akaldayo monga njira yothetsera mavuto ake. (Eksodo 16:2, 3; Ahebri 11:10, 15, 16) Ulysses Glass, wosunga kaundula wa sukulu, anagwiritsira ntchito nkhani ya Asafu yolembedwa pa Salmo 73 polangiza kalasi lomaliza maphunzirolo kuti, “Simbani Madalitso Anu.” Ndipo Albert Schroeder, wa Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yamutu wakuti “Yehova Amagaŵira.” Posonyeza umboni wa chogaŵira chotero, anatchula Sukulu ya Gileadi imeneyo ndi mbali yake pakukwaniritsa ntchito yaikulu yolalikira ndi kupanga ophunzira.
Pambuyo pake omvetserawo anatchera khutu kwambiri pamene Milton Henschel, pulezidenti wa Watch Tower Society, analankhula za “Kukhala Ziŵalo za Wina ndi Mnzake.” Anaŵerenga ndi kukambapo kwambiri pa Aroma chaputala 12. Zina zimene ananena zinali zakuti: “Tiyenera kukumbukira kuti tili paunansi wolimba kwambiri ndi atumiki anzathu mumpingo.” Anawonjezera kuti: “Ndi bwino nthaŵi zonse kumaonana wina ndi mnzake monga chuma cha Yehova, ndipo m’malo mosulizana, m’malo mopezana zifukwa, tiyeni tikhale othandizana nthaŵi zonse. Timadzithandiza tokha pamene tisunga umodzi wauzimu mumpingo Wachikristu.” Iye anasonyeza mmene kuthandizana kotero kungasonyezedwere pokonza chakudya m’nyumba za amishonale, mwa kumakumbukira kuti onse sangadye chinthu chimodzimodzi. Anawalimbikitsanso kuthandizana pamene ali mu utumiki wakumunda ndi Akristu anzawo osaukira m’malo mwa kuwasuliza. Ngati timathandizanadi, kumangirirana, ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake, anatero Mbale Henschel, “Yehova adzatikonda chifukwa cha zimenezi.” Ha, ndi chilangizo chabwino chotani nanga kwa amishonale amene adzakhala akutumikira m’maiko amene ali osiyana kwenikweni ndi aja kumene akuchoka!
Kulidziŵa Bwino Kalasilo
Ophunzira 48 a kalasi la 99 anali ndi avareji ya zaka 32 zakubadwa ndipo anali atathera zaka zoposa 11 mu utumiki wanthaŵi yonse.
Kufunsa kumene kunali mbali ya programu yomaliza maphunziro kunapatsa omvetsera mwaŵi wa kuwadziŵa bwino ena a iwo. Nikki Liebl, wa ku United States, ndi Simon Bolton, wa ku England, anasimba zochitika zimene zinayesa chikhulupiriro chawo chakuti Yehova adzagaŵira zosoŵa zawo zakuthupi. Anaona chisamaliro cha Yehova pamene anaika patsogolo utumiki wanthaŵi yonse.
Isabelle Kazan, amene chilankhulidwe chake chobadwa nacho ndi Chifrenchi, anati anaphunzira Chiarabu kuti azilalikira anthu olankhula Chiarabu kwawo ku France. Pamene anayamba mu 1987, kagulu kokha kamene kanali m’Paris kanali chabe ndi abale anayi olankhula Chiarabu, kuwonjezera pa iye ndi mlongo wina amene anali kuphunzira chinenerocho. (Zinali zovuta. Anali kutaya maola asanu ndi atatu pokonzekera phunziro lawo la Nsanja ya Olonda mlungu uliwonse kuti aziyankhapo.) Kodi khama lawolo linakhala ndi zotulukapo zabwino? Eya, lerolino pali Mboni zolankhula Chiarabu zimene zalinganizidwa kupanga madera asanu m’France yense. Wophunzira wina, Miko Puro, anasimba mmene Chifrenchi chomwe anaphunzira kusukulu chinamthandizira kulalikira kwa othaŵa kwawo Achiafirika kwawoko ku Finland, ndipo chidzamthandizanso m’gawo lake ku Benin. Bonny Bowes anasimba za nkhondo yake ya kulankhula Chifrenchi bwino kuti akhoze kutumikira mogwira mtima ku Quebec, Canada. Ndipo Bjarki Rasmussen, wa ku Denmark, anasimba zokumana nazo zimene iye ndi mkazi wake anakhala nazo m’zaka za utumiki wawo ku Faeroe Islands. Inde, amishonale atsopano ameneŵa ali atumiki anthaŵi yonse ozoloŵera.
Omaliza maphunzirowo anagaŵidwa ku maiko 19—m’Afirika, Central ndi South America, Eastern Europe, ndi Kummaŵa. Omaliza maphunziro a makalasi oyambirira atumikira kale m’maiko oposa 200. Ambiri a omaliza maphunzirowo akali okangalika m’magawo awo. Amishonale atsopano ameneŵa akugwirizana nawo tsopano pakufutukula kwina umboni wa Ufumu kufikira malekezero ake a dziko lapansi.—Machitidwe 1:8.
[Zithunzi patsamba 25]
Zochitika m’kalasi ku Malikulu a Maphunziro a Watchtower
[Chithunzi patsamba 26]
Kalasi la 99 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Heffey, S.; Riley, E.; Mortensen, D.; Honable, A.; Bolton, J.; Poole, J.; Siimes, G.; Sousa, L. (2) Pashnitski, B.; Shepherd, D.; Pashnitski, W.; Järvinen, J.; Paulsen, K.; Rasmussen, E.; Schewe, C.; Olsson, L. (3) Paulsen, E.; Samsel, T.; Bowes, B.; Harris, E.; Kazan, I.; Liebl, N.; Sousa, P.; Puro, J. (4) Lager, K.; Lager, V.; Golden, K.; Bolton, S.; Johnson, M.; Johnson, S.; Liebl, A.; Rasmussen, B. (5) Harris, D.; Samsel, W.; Schewe, O.; Heffey, R.; Kazan, L.; Riley, T.; Järvinen, O.; Puro, M. (6) Mortensen, D.; Golden, R.; Honable, L.; Shepherd, M.; Bowes, R.; Siimes, T.; Poole, E.; Olsson, J.
[Zithunzi patsamba 27]
Akali m’magawo awo: (kulamanzere) Charles Leathco ndi mkazi wake, Fern, ku Brazil, omaliza maphunziro m’kalasi loyamba ndi lachisanu ndi chimodzi la Gileadi; (pansipa) Martha Hess, ku Japan, womaliza maphunziro m’kalasi lachisanu ndi chiŵiri la Gileadi