“Muzindikire Otere”
ZINTHU sizinali bwino mumpingo wa Korinto. Munali nkhani yonyansa ya chisembwere, ndipo panali malekano pakati pa abale. Ena anali ndi zothetsa nzeru zazikulu zaumwini kapenanso mafunso omwe anafunikira kuyankhidwa. Abale ena anali kuperekana kumakhoti; enanso anali kukana chiukiriro.
Panabukanso mafunso ofunika kwambiri. Kodi aja okhala m’mabanja a zipembedzo zosiyana anayenera kukhalabe ndi anzawo osakhulupirira, kapena anayenera kupatukana? Kodi ntchito ya alongo inali yotani mumpingo? Kodi kunali koyenera kudya nyama yoperekedwa nsembe ku mafano? Kodi misonkhano—kuphatikizapo Chakudya Chamadzulo cha Ambuye—inayenera kuchitidwa motani?—1 Akorinto 1:12; 5:1; 6:1; 7:1-3, 12, 13; 8:1; 11:18, 23-26; 14:26-35.
Mosakayikira, pokhala odera nkhaŵa za abale awo mumkhalidwe wauzimu wovuta umenewo, Akayiko, Fortunato, ndi Stefana anapita paulendo kukaonana ndi mtumwi Paulo ku Efeso. Kuwonjezera pa uthenga wovutitsa maganizo umenewu, nkotheka kuti iwo anatenganso kalata ya Paulo yochokera ku mpingo yokhala ndi mafunso pankhani zimenezo. (1 Akorinto 7:1; 16:17) Malinga ndi umboni, abale atatu ameneŵa sindiwo okha amene anada nkhaŵa ndi mkhalidwewo. Ndipotu, Paulo anali atalandira kale uthenga kwa “iwo a kwa Kloe” wakuti panali makani pampingo. (1 Akorinto 1:11) Ndithudi, lipoti la amithengawo linathandiza Paulo kumvetsetsa mkhalidwewo, kudziŵa uphungu womwe akanapereka, ndi moyankhira mafunso odzutsidwawo. Zikuoneka kuti kalata yomwe tsopano timatcha Akorinto Woyamba ndiyo yankho la Paulo, limene linatsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Mwinamwake Akayiko, Fortunato, ndi Stefana ndiwo anabweretsa kalatayo.
Kodi Akayiko, Fortunato, ndi Stefana anali ayani? Kodi tingaphunzirenji mwa kupenda zimene Malemba amanena za iwo?
Banja la Stefana
Banja la Stefana linali “chipatso choundukula” cha utumiki wa Paulo m’chigawo cha Roma cha Akaya, Kummwera kwa Greece, pafupifupi chaka cha 50 C.E., ndipo anabatizidwa ndi Paulo iye mwini. Mwachionekere, Paulo anawayesa chitsanzo chabwino, chisonkhezero champhamvu cholimbitsa Akorinto. Iye anawathokoza kwambiri chifukwa cha ntchito yawo kulinga ku mpingo kuti: “Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziŵa banja la Stefana, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima), kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nawo, ndi kugwiritsa ntchito.” (1 Akorinto 1:16; 16:15, 16) Kwenikweni amene anali a “banja” la Stefana sakutchulidwa. Mawuwo angangotanthauza a m’banjalo komanso angaphatikizepo akapolo kapena antchito. Popeza Akayiko linali dzina lachilatini lodziŵika kukhala la kapolo, ndi Fortunato kukhala la mfulu, othirira ndemanga ena amati aŵiriwo mwina anali a m’banja limodzimodzilo.
Mulimonse mmene zinalili, Paulo anaona banja la Stefana kukhala chitsanzo chabwino. A m’banjalo “anadziika okha kutumikira oyera mtima.” Banja la Stefana liyenera kukhala litazindikira kuti panali ntchito imene inafunika kuchitidwa kuthandiza mpingo ndipo modzifunira analandira utumiki umenewu kukhala thayo lawolawo. Ndithudi ena anafunikira kuchirikiza ndi kuzindikira chikhumbo chawo cha kutumikira oyera mtima.
“Anatsitsimutsa Mzimu Wanga ndi Wanu”
Ngakhale kuti Paulo anali wodera nkhaŵa za mkhalidwe wa ku Korinto, kufika kwa amithenga atatu kunamlimbikitsa. Paulo akuti: “Ndikondwera pa kudza kwawo kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu. Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu.” (1 Akorinto 16:17, 18) Polingalira za mkhalidwe wa ku Korinto, kusakhala pamodzi ndi Akorinto m’thupi mwinamwake kunamdetsa nkhaŵa Paulo, koma tsopano kukhalapo kwa nthumwi zawo kunakwaniritsa kusakhalapo kwa mpingo wonse. Nzotheka kuti lipoti lawo linathandiza Paulo kukhala ndi chithunzi chonse cha mkhalidwewo ndi kuthetsa ena a mantha ake. Ndi iko komwe mwina zinthu sizinali zoipa kwambiri monga mmene anaganizira.
Malinga ndi kunena kwa Paulo, ulendo wa atatuwo sunangotsitsimutsa mzimu wake komanso unalimbitsa mzimu wa mpingo wa ku Korinto. Mosakayikira kunali kotonthoza kwa iwo kudziŵa kuti nthumwi zawozo zinafotokoza bwinobwino mbali zonse za mkhalidwewo kwa Paulo ndi kuti zidzabwera ndi uphungu wake.
Motero Stefana ndi anzake aŵiriwo anathokozedwa kwambiri pakutumikira kwawo Akorinto. Kuyamikira kwa Paulo amuna ameneŵa kunasonyezedwa m’njira yakuti atabwerako anayenera kukhala atsogoleri mumpingo wogaŵanika wa Korinto. Mtumwiyo akulimbikitsa abale kuti: “[Pitirizani kudzigonjetsera inu nokha kwa, NW] otere, ndi yense wakuchita nawo, ndi kugwiritsa ntchito. . . . Muzindikire otere.” (1 Akorinto 16:16, 18) Ziyamikiro zazikulu zotero zimasonyeza bwino lomwe kukhulupirika kokwanira kumene amuna aŵa anali nako ngakhale kuti mumpingo munali zovuta. Amuna otero ayenera kulemekezedwa.—Afilipi 2:29.
Kugwirizana Mokhulupirika Kumatulutsa Zabwino
Mosakayikira, kugwirizana kwambiri ndi gulu la Yehova ndi oimira ake kumatulutsa zabwino. Pamene Paulo analemba kalata imene tsopano imatchedwa Akorinto Wachiŵiri, atangomaliza kalata yoyamba, zinthu zinali zitayamba kale kuyenda bwino mumpingo. Kupitiriza kugwira ntchito moleza mtima kwa abale ngati Akayiko, Fortunato, ndi Stefana, ndiponso ulendo wa Tito, kunatulutsa zabwino.—2 Akorinto 7:8-15; yerekezerani ndi Machitidwe 16:4, 5.
A m’mipingo yamakono ya anthu a Yehova angapindule mwa kusinkhasinkha za kutchulidwa kwachidule kwa amuna okhulupirika ameneŵa m’Malemba. Mwachitsanzo, tinene kuti mkhalidwe wina womapitiriza mumpingo wakumaloko sungathetsedwe msanga pazifukwa zina ndipo ukudetsa nkhaŵa abale. Kodi nchiyani chimene muyenera kuchita? Tsanzirani Stefana, Fortunato, ndi Akayiko, amene sanapeŵe thayo lawo la kuuza Paulo za mkhalidwewo ndiyeno mwachidaliro siyani nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Sanalole konse changu chawo cha chilungamo kuwasonkhezera kuchitapo kanthu paokha kapena ‘kukwiyira Yehova.’—Miyambo 19:3, NW.
Mipingo nja Yesu Kristu, ndipo panthaŵi yake yoyenera, monga ku Korinto, adzachitapo kanthu kuthetsa zovuta zilizonse zimene zingaike pangozi ubwino wawo wauzimu ndi mtendere. (Aefeso 1:22; Chivumbulutso 1:12, 13, 20; 2:1-4) Pamene tikuyembekezera zimenezo, ngati titsatira chitsanzo chabwino choperekedwa ndi Stefana, Fortunato, ndi Akayiko ndi kupitiriza kugwiritsa ntchito kutumikira abale athu, ifenso tidzakhala tikuchirikiza kakonzedwe ka mpingo mokhulupirika, kumangirira abale athu, ndi ‘kuwafulumiza ku chikondano ndi ntchito zabwino.’—Ahebri 10:24, 25.