Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 20-23
  • Chidaliro Changa mwa Yehova Chinandichirikiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidaliro Changa mwa Yehova Chinandichirikiza
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupeza Chidaliro mwa Yehova
  • Kulimbitsidwa ndi Ntchito Yauzimu
  • Utumiki Wanthaŵi Zonse Wofutukuka
  • Ntchito Yanga pa Beteli
  • Beteli Yathu
  • Mwaŵi Wamtengo Wapatali
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kutumikira Yehova Monga Banja Logwirizana
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 20-23

Chidaliro Changa mwa Yehova Chinandichirikiza

YOSIMBIDWA NDI AGENOR DA PAIXÃO

Mwana wathu yekhayo, Paul, anamwalira ndi chifuŵa pamene anali chabe ndi miyezi 11. Patapita miyezi itatu, pa August 15, 1945, mkazi wanga wokondedwa anamwalira ndi chibayo. Ndinali ndi zaka 28, ndipo masoka ameneŵa anandisiya wachisoni ndi wopsinjika maganizo. Komabe chidaliro mwa Yehova ndi malonjezo ake chinandichirikiza. Tandilolani ndisimbe mmene ndinakhalira ndi chidaliro chimenechi.

KUCHOKERA pamene ndinabadwa ku Salvador, Bahia State, Brazil, pa January 5, 1917, Amayi anandiphunzitsa kulambira “oyera mtima” a Tchalitchi cha Katolika. Anali ngakhale kundidzutsa mmamaŵa limodzi ndi abale anga kuti tipemphere pamodzi. Komabe, makolo anga anali kupitanso kumisonkhano ya candomblé, madzoma achiafirika ndi achibrazilu olambira makolo. Ndinali kuzilemekeza kwambiri zikhulupiriro zimenezi, koma ndinalibe chidaliro mwa amene amati oyera mtima achikatolika kapena mwa candomblé. Chimene chinandikhumudwitsa kwambiri chinali ufuko umene unali m’zipembedzo zimenezi.

M’kupita kwa nthaŵi akulu anga aŵiri anachoka panyumba kukafuna ntchito. Pambuyo pake atate analithaŵa banja. Choncho pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi, ndinapeza ntchito kuti ndizithandiza amayi ndi mlongo wanga wamng’ono. Patapita zaka ngati 16, kukambitsirana ndi wogwira naye ntchito m’fakitale kunakhala posinthira zinthu m’moyo wanga.

Kupeza Chidaliro mwa Yehova

Ndinakumana ndi Fernando Teles mu 1942. Kaŵirikaŵiri anali kunena kuti kulambira “oyera mtima” kunali kolakwa. (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Poyamba sindinamvetsere. Koma kuona mtima kwake ndi kukonda kwake anthu, mosasamala kanthu za khungu lawo, zinandikopa, ndipo ndinayamba kukhumbira chidziŵitso chake cha Baibulo, makamaka zimene ankanena pa Ufumu wa Mulungu ndi dziko lapansi la paradaiso. (Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4) Ataona chidwi changa, anandipatsa Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo.

Patapita milungu ingapo, ndinavomera atandiitana kuphunziro la Baibulo la mpingo. Gululo linali kuphunzira buku lakuti Religion [Chipembedzo], lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Phunziro limenelo linandisangalatsa ndipo ndinayamba kupezeka pamisonkhano yonse yampingo ya Mboni za Yehova. Chimene chinandikondweretsa makamaka chinali kupanda kwawo tsankhu ndi mmene anandilandirira nthaŵi yomweyo. Chapanthaŵi imeneyo ndinatomera Lindaura. Pamene ndinalankhula naye za zimene ndinali kuphunzira, anayamba kupezeka pamisonkhano limodzi nane.

Chinanso chimene chinandikondweretsa pamisonkhano chinali kugogomezera kwawo ntchito yolalikira. (Mateyu 24:14; Machitidwe 20:20) Nditalimbikitsidwa ndi apainiya, monga momwe amatchera atumiki a nthaŵi zonse, ndinayamba kulankhula ndi ena mwamwaŵi m’sitima popita kuntchito ndi pobwerako. Nditapeza amene wachita chidwi, ndinali kutenga keyala yake ndi kumchezera kuti ndiyese kukulitsa chidwicho.

Zikali choncho, chidaliro changa mwa Yehova ndi gulu limene akugwiritsira ntchito chinapitirizabe kukula. Motero, nditamvetsera nkhani ya Baibulo yonena za kudzipatulira kwachikristu, ndinabatizidwa, m’Nyanja ya Atlantic, pa April 19, 1943. Tsiku limodzimodzilo, ndinakhala ndi phande nthaŵi yoyamba mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba.

Patapita milungu iŵiri, pa May 5, ineyo ndi Lindaura tinakwatirana. Ndiyeno, mu August 1943, iye anabatizidwa pamsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova woyamba mumzinda wa Salvador. Ponena za msonkhanowo, 1973 Yearbook of Jehovah’s Witnesses inati: “Atsogoleri achipembedzo anakwanitsa kuletsa nkhani yapoyera ku Salvador, koma osati kulengeza kwakukulu ndipo kwabwino . . . kusanachitike.” Umboni wa chitsogozo cha Yehova m’nthaŵi za chizunzo chachikulu unalimbitsa chidaliro changa mwa iye.

Monga ndasimbira pachiyambipo, zaka ziŵiri zokha Lindaura atabatizidwa​—ndi miyezi itatu pambuyo pa imfa ya mwana wathu​—mkazi wanga wokondedwa anamwalira. Anali ndi zaka 22 zokha. Koma chidaliro chimene ndinali nacho mwa Yehova chinandichirikiza m’miyezi yovuta imeneyo.

Kulimbitsidwa ndi Ntchito Yauzimu

Mu 1946, chaka chimodzi nditatayikidwa mkazi wanga ndi mwana wanga, ndinaikidwa kukhala mtumiki wa phunziro la Baibulo mumpingo wokhawo umene unali mu Salvador panthaŵiyo. Chaka chimenecho Sukulu la Utumiki Wateokratiki linayamba m’mipingo ya m’Brazil, ndipo ndinakhala wochititsa sukulu woyamba m’boma la Bahia. Ndiyeno mu October 1946, Msonkhano Wateokratiki wa “Mitundu Yokondwa” unachitika mumzinda wa São Paulo. Wondilemba ntchito kwa zaka khumi ananena kuti anali kundifuna nalimbikira kunena kuti ndisapite. Komabe, nditamfotokozera mmene kupezeka pamsonkhanowo kunalili kofunika kwa ine, anandipatsa mphatso ndi kundifunira ulendo wabwino.

Mbali za msonkhanowo mu Municipal Theater ya ku São Paulo zinachitidwa m’Chipwitikizi​—chinenero cha Brazil​—limodzinso ndi m’Chihangare, m’Chijeremani, m’Chingelezi, m’Chipolishi, ndi m’Chirasha. Pamsonkhanowo maganizi a Galamukani! anatulutsidwa m’Chipwitikizi. Ndinasonkhezeredwa kwambiri ndi msonkhanowo​—anthu ngati 1,700 anapezeka pankhani yapoyera​—kwakuti ndinadzaza fomu yofunsira upainiya kuti ndikauyambe pa November 1, 1946.

Nthaŵiyo tinkagwiritsira ntchito kwambiri galamafoni m’ntchito yathu yaupainiya. Nkhani yakuti “Protection” [Chitetezo] ndiyo imene tinali kulizira eni nyumba nthaŵi zambiri. Ndiyeno, tinkanena kuti: “Kuti tidzitetezere kwa mdani wathu wosaoneka, tiyeneranso kumamatira kwa bwenzi losaoneka. Yehova ndiye bwenzi lathu lopambana ndipo ngwamphamvu kwambiri kuposa mdani wathu, Satana. Choncho tiyenera kumamatira kwambiri kwa Yehova kuti tidzitetezere kwa iye.” Ndiyeno tinkagaŵira kabuku ka Protection, komwe kanali ndi chidziŵitso chowonjezera.

Ndinali nditachita upainiya nthaŵi yosakwanira chaka pamene ndinalandira pempho lokatumikira monga mpainiya wapadera mumpingo wa Carioca ku Rio de Janeiro. Kumeneko tinakumana ndi chitsutso cholimba nthaŵi zina. Mnzanga, Ivan Brenner, nthaŵi ina anamuukiradi mwini nyumba wina. Okhala pafupi anaitana polisi, ndipo tonsefe anatitengera ku polisi.

Potifunsa, mwini nyumba wokwiyayo anatiimba mlandu wa kusokoneza mtendere. Mkulu wa polisi anamuuza kukhala chete. Ndiyeno mkulu wa polisi anatembenukira kwa ife ndipo ndi mawu aubwenzi ananena kuti tili aufulu kupita. Anagwira wotiimba mlandu ndi kumpatsa mlandu wa ndewu. Mikhalidwe yonga imeneyo inachirikiza chidaliro changa mwa Yehova.

Utumiki Wanthaŵi Zonse Wofutukuka

Pa July 1, 1949, ndinakondwera kwambiri kuitanidwa kukatumikira pa Beteli, monga momwe maofesi aakulu a Mboni za Yehova amatchedwera m’dziko lililonse. Beteli ku Brazil nthaŵiyo inali pa 330 Licínio Cardoso Street ku Rio de Janeiro. Nthaŵiyo munali 17 okha m’banja lonse la Beteli. Ndinali kupita ku mpingo wakumeneko wa Engenho de Dentro kwa kanthaŵi, koma pambuyo pake ananditumiza monga woyang’anira wotsogoza ku mpingo wokhawo wa ku Belford Roxo, mzinda wokhala pamtunda wa makilomita angapo kuchokera ku Rio de Janeiro.

Pakutha kwa mlungu tinkakhala ndi zochita zambiri. Masiku a Loŵeruka ndinali kupita ku Belford Roxo ndi sitima, kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda masana, ndiyeno kupita ku Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki madzulo. Ndinali kugona kwa abale ndi kuchita nawo utumiki wakumunda m’maŵa mwake. Masanawo ndinali kupezeka pankhani ya Baibulo yapoyera ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi kubwerera ku Beteli cha ku ma 9:30 usiku. Lero muli mipingo 18 m’Belford Roxo.

Mu 1954, nditakhala ndi programu imeneyo zaka zitatu ndi theka, ananditumizanso ku Rio de Janeiro monga woyang’anira wotsogoza mumpingo wa São Cristóvão. Ndinatumikira mumpingowo zaka khumi zotsatira.

Ntchito Yanga pa Beteli

Ntchito yanga yoyamba pa Beteli inali kumanga galaja ya galimoto lokhalo la Sosaite, vaneti yotchedwa Dodge ya mu 1949 ya dzina losemerera lakuti Chocolate chifukwa cha maonekedwe ake akuda. Galajayo itamalizidwa, anandiika kugwira ntchito m’kitchini, mmene ndinakhala zaka zitatu. Ndiyeno anandisamutsira ku Dipatimenti ya Makina Osindikizira, kumene ndakhala zaka zoposa 40 tsopano.

Makina ambiri osindikizira amene tinali nawo anali atagwirapo kale ntchito. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri tinali ndi makina akale osindikizira othasalala amene mwachikondi tinawatcha dzina la mkazi wa Abrahamu, Sara. Anali atagwira ntchito zaka zambiri m’fakitale kumalikulu a Watch Tower Society ku Brooklyn, New York. Ndiyeno m’ma 1950, anawasamutsira ku Brazil. Kunoko, monga mkazi wa Abrahamu, mu ukalamba wake anabala zipatso​—magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Nthaŵi zonse ndimadabwa ndi kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha zofalitsa zimene zikutulutsidwa ndi fakitale yosindikiza ya Brazil. M’chaka chonse cha 1953, tinasindikiza magazini 324,400, koma tsopano timatulutsa mamiliyoni oposa atatu mwezi uliwonse!

Beteli Yathu

Ndasangalala kwambiri zaka zonsezi kuona kufutukuka kwa Beteli yathu ya Brazil. Mu 1952 tinamanga fakitale yosanja ya miyalo iŵiri kumbuyo kwa nyumba yathu ku Rio de Janeiro. Ndiyeno mu 1968, Beteli inasamukira kunyumba yatsopano mumzinda wa São Paulo. Pamene tinasamukira kumeneko, zonse zinaoneka zazikulu ndi zotakata kwa banja lathu la Beteli la anthu 42. Tinkaganizadi kuti nyumba imeneyi idzasamalira pachiwonjezeko chathu chonse chamtsogolo. Komabe, mu 1971 nyumba zinanso ziŵiri zosanja za miyalo isanu zinamangidwa, ndipo fakitale yogwirana ndi nyumba yathu inagulidwa, kukonzedwanso, ndi kuilunzanitsa ndi nyumba zonse zinazi. Koma m’zaka zochepa chabe, kuwonjezeka kopitirizabe kwa alengezi a Ufumu kunafuna malo aakulu popeza tinapyola chiŵerengero cha 100,000 mu 1975.

Choncho, nyumba zina zatsopano zinamangidwa makilomita pafupifupi 140 kuchokera ku São Paulo pafupi ndi tauni yaing’ono ya Cesário Lange. Mu 1980 banja lathu la Beteli la anthu 170 linasamukira kunyumba zatsopanozi. Chiyambire pamenepo ntchito ya Ufumu yakula kwambiri. Tili ndi anthu oposa 410,000 tsopano amene akukhala ndi phande mokhazikika m’ntchito yolalikira m’Brazil! Kuti tisamalire zosoŵa zauzimu za alengezi a Ufumu onsewa, tapitirizabe kumanga mafakitale atsopano osindikiza mabuku ofokoza Baibulo ndi nyumba zokhalamo za antchito odzifunira a pa Beteli. Panopo tili ndi anthu ngati 1,100 m’banja la Beteli!

Mwaŵi Wamtengo Wapatali

Ndikuona utumiki wa pa Beteli monga mwaŵi wamtengo wapatali. Choncho, ngakhale kuti kale ndinaganiza zokwatiranso, ndinasankha kusumika maganizo anga kwambiri pamwaŵi wanga wa pa Beteli ndi pantchito yolalikira. Pano ndasangalala kutumikira pamodzi ndi achichepere ambirimbiri m’nyumba yosindikizira ndi kuwaphunzitsa ntchito zawo. Ndayesa kukhala nawo monga ana anga. Changu chawo ndi kupanda kwawo dyera zandilimbikitsa kwambiri.

Zaka zonsezi ndakhalanso ndi mwaŵi wa kukhala ndi anzanga abwino kwambiri m’chipinda chimodzi. Zoona, kusiyana maumunthu nthaŵi zina kunapereka vuto. Komabe ndinaphunzira kusayembekezera ena kukhala angwiro. Ndayesetsa kusakulitsa mavuto aang’ono kapena kudziyesa wofunika kwambiri. Kudziseka zophophonya zanga kwandithandiza kunyalanyaza za ena.

Mwaŵi wina wamtengo wapatali umene ndinakhala nawo unali uja wa kupezeka pamisonkhano yaikulu ya mitundu ku United States. Umodzi wa imeneyi unali Msonkhano wa “Uthenga Wabwino Wosatha,” umene unali mu Yankee Stadium, New York, mu 1963, ndipo winanso unali Msonkhano wa Mitundu wa “Mtendere Padziko Lapansi” umene unachitikira pamalo amodzimodziwo mu 1969. Pamene ndinali kumeneko, ndinasangalala kukacheza chapafupi Pamalikulu a Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York!

Ndinalinso ndi mwaŵi wakuchititsa lemba latsiku la banja la Beteli zaka khumi mosinthana ndi ena. Chikhalirechobe, mwaŵi waukulu kopambana, umene wandidzetsera chimwemwe ndi chilimbikitso chachikulu, ndiwo wa kupereka uthenga wa Ufumu kwa anthu oona mtima, monga momwe Ambuyathu, Yesu Kristu, anachitira.

Zaka zaposachedwa ndayang’anizana ndi vuto la kukhala ndi nthenda ya manjenje yotchedwa Parkinson’s. Chisamaliro chachikondi cha abale ndi alongo m’chipatala cha pa Beteli chandithandiza ndi kunditonthoza nthaŵi zonse. Ndipemphera ndi chidaliro chonse kuti Yehova andipatse nyonga kuti ndipitirize kuchita zonse zimene ndingathe chifukwa cha kulambira kwake koona.

[Chithunzi patsamba 23]

Nthambi ya Brazil pomwe ndimakhala tsopano

[Zithunzi patsamba 23]

Ndi mkazi wanga, amene anamwalira mu 1945

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena