Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/1 tsamba 6-7
  • Njira Yabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Yabwino
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko la Makhalidwe Otsimikizika
  • Kuumirira Mwambo Kodi Ndiko Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Boma Lodzalimbikitsa Mfundo za Mulungu
    Galamukani!—2003
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?
    Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupirira Chiyani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/1 tsamba 6-7

Njira Yabwino

MBONI ZA YEHOVA zikuda nkhaŵa ndi mkhalidwe wauzimu umene ukuchepa m’dziko ndi khalidwe loipa ndiponso ndi kusatsimikizika kwa chipembedzo kumene kwafala m’chitaganya. Chotero, izo nthaŵi zina zimatchedwa oumirira mwambo. Koma kodi zilidi zotero? Ayi. Pamene kuli kwakuti zili ndi zikhulupiriro zolimba zachipembedzo, sizili oumirira mwambo malinga ndi tanthauzo limene liwulo lakhala nalo. Sizimakakamiza atsogoleri andale kuti alimbikitse lingaliro linalake, ndipo sizimachita zionetsero ndi chiwawa kwa aja omwe sagwirizana nazo. Zapeza njira yabwino. Zimatsanzira Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu.

Mboni za Yehova nzotsimikiza kuti choonadi chachipembedzo chiliko, kuti chimapezeka m’Baibulo. (Yohane 8:32; 17:17) Koma Baibulo limaphunzitsa Akristu kuti azikhala okoma mtima, abwino, ofatsa, ndi ololera​—mikhalidwe imene simalola kuyaluka ndi chipembedzo. (Agalatiya 5:22, 23; Afilipi 4:5) M’buku la Baibulo la Yakobo, Akristu akulimbikitsidwa kukulitsa “nzeru yochokera kumwamba,” imene ikufotokozedwa kuti “iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino.” Yakobo anawonjeza kuti: “Chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.”​—Yakobo 3:17, 18.

Mboni za Yehova zimakumbukira kuti Yesu anali kusamala kwambiri za choonadi. Anauza Pontiyo Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Ngakhale anachirikiza choonadi molimba mtima, sanayese kukakamiza zikhulupiriro zake pa ena. M’malo mwake, anakopa maganizo awo ndi mitima yawo. Anadziŵa kuti Atate wake wakumwamba, Mulungu “wabwino ndi wolunjika mtima,” adzasankha njira ndi nthaŵi imene adzachotserapo bodza ndi chisalungamo padziko lapansi. (Salmo 25:8) Chifukwa chake, sanayese kuwakakamiza aja amene anatsutsana naye. M’malo mwake, atsogoleri achipembedzo osunga mwambo a m’tsiku lake ndiwo anayesa kumkakamiza Yesu.​—Yohane 19:5, 6.

Mboni za Yehova zili ndi zikhulupiriro zolimba paziphunzitso zachipembedzo, ndipo zimasungadi mwambo pankhani ya makhalidwe abwino. Mofanana ndi mtumwi Paulo, nzotsimikiza kuti pali chabe “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.” (Aefeso 4:5) Zimazindikiranso mawu a Yesu akuti: “Chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Komabe, sizimayesa kukakamiza ena kutsata zikhulupiriro zawo. M’malo mwake, zimatsanzira Paulo ndi ‘kupempha’ onse amene afuna kuti ‘ayanjanitsidwe ndi Mulungu.’ (2 Akorinto 5:20, NW) Imeneyi ndiyo njira yabwino. Ndiyo njira ya Mulungu.

Kuumirira mwambo wachipembedzo, malinga ndi mmene liwulo akuligwiritsira ntchito lerolino, nkosiyana kwambiri. Oumirira mwambo amagwiritsira ntchito njira zambiri​—kuphatikizapo chiwawa​—kuti aumirize zikhulupiriro zawo pa anthu. Motero, amaloŵa kwambiri m’zandale. Koma Yesu anatero kuti otsatira ake ‘saali a dziko lapansi.’ (Yohane 15:19; 17:16; Yakobo 4:4) Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, Mboni za Yehova zimasunga uchete pamikangano yonse ya ndale. Ngakhale nyuzipepala yachitaliyana Fuoripagina inavomereza kuti “sizimakakamiza aliyense; aliyense ali ndi ufulu wa kulandira kapena kukana zimene zimanena.” Zotsatira zake? Uthenga wamtendere wa m’Baibulo wa Mboni umakopa anthu a mtundu uliwonse, ngakhale aja amene kale anali oumirira mwambo.​—Yesaya 2:2, 3.

Dziko la Makhalidwe Otsimikizika

Mboni zimazindikira kuti anthu sangathe kuthetsa mavuto omwe oumirira mwambo amada nawo nkhaŵa. Sungakakamize munthu kuti akhulupirire Mulungu kapena kulandira zikhulupiriro zako za iwe mwini. Kuganiza kuti zimenezo zingatheke kunayambitsa nkhanza zoipitsitsa m’mbiri, monga Nkhondo za Mtanda, mabwalo a Inquisition a m’nyengo zapakati, ndi “kutembenuza” Aindiya a ku America. Komabe, ngati mumakhulupirira Mulungu, mudzafuna kusiya nkhani m’manja mwake.

Malinga ndi Baibulo, Mulungu waika malire a nthaŵi imene walola anthu kuswa malamulo ake ndi kudzetsa mavuto ndi zopweteka. Nthaŵiyo yatsala pang’ono kutha. Yesu wayamba kale kulamulira monga Mfumu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndipo posachedwa Ufumuwo udzachotsapo maboma a anthu ndi kuyamba kulamulira zochita za anthu zatsiku ndi tsiku. (Mateyu 24:3-14; Chivumbulutso 11:15, 18) Ndiyeno padzatsatira paradaiso wa dziko lonse amene mudzakhala mtendere ndi chilungamo chochuluka. Panthaŵiyo sipadzakhala kukayikira njira yoyenera kulambirira Mulungu woona. “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Makhalidwe osatha amenewo a kukoma mtima kwachikondi, choonadi, chilungamo, ndi ukoma adzapambana kaamba ka ubwino wa anthu onse omvera.

Poyembekezera nthaŵiyo, wamasalmo akunena mwandakatulo kuti: “Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana. Choonadi chiphukira m’dziko; ndi chilungamo chasuzumira chili m’mwamba. Inde Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake. Chilungamo chidzamtsogolera; nichidzamkonzera mapazi ake njira.”​—Salmo 85:10-13.

Pamene sitingasinthe dziko, tingathe aliyense payekha kukulitsa makhalidwe aumulungu ngakhale lerolino. Motero, tingayesetse kukhala monga anthu amene Mulungu adzafuna kuti akhale olambira ake m’dziko latsopano. Ndiyeno tidzakhala pakati pa ofatsa otchulidwa ndi wamasalmo: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Mulungu amawachirikiza ndi kuwadalitsa aja amene amachita chifuniro chake, ndipo akulonjeza kuti iwo adzakhala ndi zinthu zabwino kwambiri mtsogolo. Mtumwi Yohane anati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”​—1 Yohane 2:17.

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova zikupempha onse kuti adziŵe uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

Nyali pamasamba 3, 4, 5, ndi 6: Printer’s Ornaments/​yojambulidwa ndi Carol Belanger Grafton/​Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena